Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ambuye, Tiphunzitseni Ife Kupemphera”

“Ambuye, Tiphunzitseni Ife Kupemphera”

“Ambuye, Tiphunzitseni Ife Kupemphera”

“Wina wa ophunzira ake anati kwa Iye, Ambuye, tiphunzitseni ife kupemphera.”​—LUKA 11:1.

1. N’chifukwa chiyani m’modzi wa ophunzira a Yesu anapempha kuti Yesu awaphunzitse kupemphera?

PA NTHAŴI ina mu 32 C.E., wophunzira wina wa Yesu anamuona Yesuyo akupemphera. Sanamve zimene Yesu amanena kwa Atate wake, chifukwa mwina linali pemphero la mumtima. Komabe, Yesu atamaliza kupempherako, wophunzirayo anamuuza kuti: “Ambuye, tiphunzitseni ife kupemphera.” (Luka 11:1) Kodi n’chiyani chinamuchititsa kupempha motero? Ayuda anali ndi chizolowezi chopemphera ndipo inali mbali ya kulambira kwawo. Malemba Achihebri ali ndi mapemphero ambiri m’buku la Masalmo ndi mabuku ena. Motero wophunzirayo sankapempha kuti am’phunzitse chimene sankadziŵa kapena chimene anali asanachiteko. Mosakayikira, ankadziŵa mapemphero a mwambo a atsogoleri achipembedzo Achiyuda. Koma tsopano anali ataona Yesu akupemphera, ndipo mosakayikira anaona kusiyana kwakukulu pakati pa mapemphero a atsogoleri achipembedzo odzionetsera ngati olungama ndi mmene Yesu anapempherera.​—Mateyu 6:5-8.

2. (a) Kodi n’chiyani chimene chikusonyeza kuti Yesu sanatanthauze kuti tizingobwereza pemphero lachitsanzo monga mmene analinenera? (b) N’chifukwa chiyani tili ndi chidwi chofuna kudziŵa mmene tingapempherere?

2 Pafupifupi chaka chimodzi ndi theka zimenezi zisanachitike, pa Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu anali atapatsa ophunzira ake pemphero lachitsanzo loti azitsatira akamapemphera. (Mateyu 6:9-13) Mwina wophunzira ameneyu panalibe panthaŵiyo, motero Yesu mokoma mtima anabwereza mfundo zofunika mu pemphero lachitsanzolo. Chochititsa chidwi n’chakuti sanabwereze mawu ake ndendende mmene anawanenera poyamba, zimene zikusonyeza kuti pemphero limene anawapatsalo silinali loti aliloweze pamtima n’kumalitchula mobwerezabwereza. (Luka 11:1-4) Mofanana ndi wophunzira amene sanatchulidwe dzinayo, ifenso tikufuna kuphunzitsidwa mmene tingapempherere kuti mapemphero athu atiyandikizitse kwa Yehova. Motero tiyeni tipende pemphero lonse lachitsanzo, monga mmene analilembera mtumwi Mateyu. Lili ndi mapempho asanu ndi aŵiri, amene atatu akukhudza zolinga za Mulungu ndipo mapempho anayi akukhudza zinthu zimene timafuna pamoyo wathu ndiponso zauzimu. Mu nkhani ino, tikambirana mapempho atatu oyambirira.

Atate Wachikondi

3, 4. Kodi timatanthauzanji tikamatchula Yehova kuti “Atate wathu”?

3 Kungoyambira pachiyambi, Yesu anasonyeza kuti mapemphero athu afunika kusonyeza kuti tili pa ubwenzi ndi Yehova ndipo timamukonda kwambiri komanso timamulemekeza. Polankhula makamaka n’cholinga choti ophunzira ake amene anali atasonkhana naye pafupi m’mphepete mwa phiri apindule, Yesu anawauza kuti azitchula Yehova kuti “Atate wathu wa Kumwamba.” (Mateyu 6:9) Malinga ndi zimene katswiri wina wamaphunziro ananena, kaya Yesu ankalankhula m’Chihebri chimene chinali chodziŵika kwambiri kapena m’Chialamu, mawu amene anagwiritsa ntchito a “Atate” ndi ofanana ndi amene ‘mwana’ amanena kwa Atate wake. Kutchula Yehova kuti “Atate wathu” kumasonyeza kuti tili naye paubale wabwino ndiponso kuti timamudalira.

4 Ponena kuti “Atate wathu,” timakhalanso tikuvomereza kuti ndife mbali ya banja lalikulu la amuna ndi akazi amene amazindikira kuti Yehova ndiye Wopereka Moyo. (Yesaya 64:8; Machitidwe 17:24, 28) Akristu odzozedwa ndi Mzimu atengedwa kukhala “ana a Mulungu,” ndipo iwo ‘angafuule kuti: Abba, Atate.’ (Aroma 8:14, 15) Anthu mamiliyoni ambiri akhala mabwenzi awo okhulupirika. Ameneŵa apatulira miyoyo yawo kwa Yehova ndipo asonyeza kudzipatulira kwawo mwa kubatizidwa. Onse a “nkhosa zina” ameneŵa angafikenso kwa Yehova m’dzina la Yesu ndipo angatchule Yehova kuti “Atate wathu.” (Yohane 10:16; 14:6) Tingapemphere kwa Atate wathu wakumwamba nthaŵi zonse pofuna kuti tim’tamande, timuthokoze chifukwa cha zabwino zonse zimene amatichitira, ndiponso kuti timuuze nkhaŵa zathu, tikukhulupirira kuti amatiganizira.​—Afilipi 4:6, 7; 1 Petro 5:6, 7.

Kukonda Dzina la Yehova

5. Kodi pempho loyamba mu pemphero lachitsanzo n’loti chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani pempho limeneli n’loyenera?

5 Pempho loyamba mosapita m’mbali likuika zinthu zofunika kwambiri pa malo oyamba. Likunena kuti: “Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Inde, kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova kuyenera kukhala chinthu chofunika kwambiri kuposa china chilichonse chifukwa timamukonda ndipo sizitisangalatsa kuona mmene dzina lake ladetsedwera. Kupanduka kwa Satana ndiponso kuchititsa kwake banja loyamba la anthu kuti lisamvere Yehova Mulungu kunanyozetsa dzina Lake poyambitsa kukayikira njira imene Mulungu amachitira ulamuliro wake m’chilengedwe chonse. (Genesis 3:1-6) Kuwonjezera apo, kuchokera pamene anthu anapanduka, dzina la Yehova lanyozedwa chifukwa cha makhalidwe ochititsa manyazi ndi ziphunzitso za amene amati amamuimira.

6. Ngati timapemphera kuti dzina la Yehova liyeretsedwe, sitidzachita chiyani?

6 Pempho lathu loti dzina la Yehova liyeretsedwe limasonyeza mbali imene ife tili, kuti tili kumbali yoti Yehova ndiye woyenera kulamulira chilengedwe chonse. Yehova akufuna kuti m’chilengedwe chonse mukhale zolengedwa zanzeru zimene zingagonjere mwakufuna kwawo ndiponso mosangalala ku ulamuliro wake wolungama chifukwa chakuti zimamukonda ndipo zimakonda zimene dzina lake limaimira. (1 Mbiri 29:10-13; Salmo 8:1; 148:13) Kukonda kwathu dzina la Yehova kudzatithandiza kupeŵa kuchita zinthu zimene zinganyozetse dzina loyera limenelo. (Ezekieli 36:20, 21; Aroma 2:21-24) Chifukwa chakuti mtendere wa chilengedwe chonse ndi zinthu zimene zilimo umadalira pa kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova ndiponso kugonjera mwachikondi ku ulamuliro wake, pempho lathu loti “dzina lanu liyeretsedwe” limasonyeza kuti timakhulupirira kuti zolinga za Yehova zidzachitika ndipo iye adzalemekezedwa.​—Ezekieli 38:23.

Ufumu Umene Timapempherera

7, 8. (a) Kodi Ufumu umene Yesu anatiphunzitsa kuti tizipempherera n’chiyani? (b) Kodi tikuphunzira chiyani za Ufumu umenewu m’mabuku a Danieli ndi Chivumbulutso?

7 Pempho lachiŵiri mu pemphero lachitsanzo n’lakuti: “Ufumu wanu udze.” (Mateyu 6:10) Pempho limeneli n’logwirizana ndi pempho loyamba lija. Chida cha Yehova choyeretsera dzina lake loyera ndicho Ufumu wa Mesiya, boma lake lakumwamba, limene Mwana wake, Yesu Kristu, ndiye Mfumu yake yosankhidwa. (Salmo 2:1-9) Ulosi wa Danieli umasonyeza Ufumu wa Mesiya kukhala “mwala” umene unasemedwa “m’phiri.” (Danieli 2:34, 35, 44, 45) Phiri limaimira ulamuliro wa Yehova pa chilengedwe chonse, pamene Ufumu umene ukuimiridwa ndi mwala ndiyo njira yatsopano yosonyezera ulamuliro wa Yehova pa chilengedwe chonse. Mu ulosiwu, mwala, kenako ‘unasanduka phiri lalikulu, nudzaza dziko lonse lapansi,’ kusonyeza kuti Ufumu wa Mesiya udzaimira ulamuliro wachilengedwe chonse wa Mulungu polamulira dziko lapansi.

8 Amene akugwirizana ndi Kristu m’boma limeneli la Ufumu ndi a 144,000, amene “anagulidwa mwa anthu” kuti akalamulire ndi Kristu monga mafumu ndi ansembe. (Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1-4; 20:6) Danieli anawatcha ameneŵa kuti ndi “opatulika a Wam’mwambamwamba,” amene pamodzi ndi Kristu Mtsogoleri wawo adzalandira “ufumu, ndi ulamuliro, ndi ukulu wa maufumu, pansi pa thambo lonse . . . ufumu wake ndiwo ufumu wosatha, ndi mayiko onse adzam’tumikira ndi kum’mvera.” (Danieli 7:13, 14, 18, 27) Limeneli ndi boma lakumwamba limene Kristu anaphunzitsa otsatira ake kupempherera.

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupemphererabe Kuti Ufumu Udze?

9. N’chifukwa chiyani n’koyenera kuti tizipemphera kuti Ufumu wa Mulungu udze?

9 M’pemphero lake lachitsanzo, Kristu anatiphunzitsa kupemphera kuti Ufumu wa Mulungu udze. Kukwaniritsidwa kwa maulosi a m’Baibulo kumasonyeza kuti Ufumu wa Mesiya unakhazikitsidwa kumwamba mu 1914. * Kodi n’koyenera kuti tizipemphererabe kuti Ufumu umenewo “udze”? Tiyeneradi kutero, chifukwa chakuti, mu ulosi wa Danieli, Ufumu wa Mesiya, wophiphiritsidwa ndi mwala, ukulimbana mwachindunji ndi maboma a ndale a anthu, amene akuphiphiritsidwa ndi fano lalikulu kwambiri. Mwalawo udzabwerabe kuti udzaphwanye fanolo, n’kulipera. Ulosi wa Danieli umati: “Ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse nudzakhala chikhalire.”​—Danieli 2:44.

10. N’chifukwa chiyani tikufunitsitsa kuti Ufumu wa Mulungu udze?

10 Tikufunitsitsa kuona Ufumu wa Mulungu ukuthetsa dongosolo la Satana loipali chifukwa zimenezi zidzatanthauza kuyeretsedwa kwa dzina lopatulika la Yehova ndi kuchotsedwa kwa onse amene amatsutsa ulamuliro wa Mulungu. Timapemphera ndi mtima wonse kuti: “Ufumu wanu udze,” ndipo mogwirizana ndi mtumwi Yohane, tikuti: “Amen; idzani, Ambuye Yesu.” (Chivumbulutso 22:20) Inde, Yesu abweredi kudzayeretsa dzina la Yehova ndiponso kudzatsimikizira kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira. Zikadzatero mawu a Wamasalmo adzakwaniritsidwa, omwe amati: “Kuti adziŵe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.”​—Salmo 83:18.

“Kufuna Kwanu Kuchitidwe”

11, 12. (a) Kodi timapempha chiyani tikamapemphera kuti chifuno cha Mulungu ‘chichitike, monga Kumwamba chomwecho pansi pano’? (b) Kodi timatanthauzanso chiyani tikamapemphera kuti chifuno cha Yehova chichitike?

11 Kenako Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kupemphera kuti: “Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:10) Chilengedwe chonse chinakhalapo chifukwa cha kufuna kwa Yehova. Zolengedwa zamphamvu zakumwamba zimalengeza kuti: “Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.” (Chivumbulutso 4:11) Yehova ali ndi cholinga chokhudza zinthu “za kumwamba, ndi za padziko.” (Aefeso 1:8-10) Tikamapemphera kuti chifuno cha Mulungu chichitike, timakhala tikupempha Yehova kuti akwaniritse cholinga chake. Kuwonjezera apo, timakhalanso tikusonyeza kuti tikufunitsitsa kuona chifuno cha Mulungu chikuchitika mu chilengedwe chonse.

12 Mu pemphero limeneli timasonyezanso kufunitsitsa kwathu kusintha miyoyo yathu kuti ikhale yogwirizana ndi zofuna za Yehova. Yesu anafotokoza kuti: “Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake.” (Yohane 4:34) Mofanana ndi Yesu, ife pokhala Akristu odzipatulira, timasangalala kuchita zimene Mulungu amafuna. Kukonda kwathu Yehova ndi Mwana wake kumatilimbikitsa kukhala ndi moyo ‘wosatsata zilakolako za anthu, koma chifuniro cha Mulungu.’ (1 Petro 4:1, 2; 2 Akorinto 5:14, 15) Timayesetsa kupeŵa kuchita zinthu zimene tikudziŵa kuti n’zosemphana ndi zimene Yehova amafuna. (1 Atesalonika 4:3-5) Mwa kuwombola nthaŵi yoŵerenga Baibulo ndi kuphunzira, timakhala ‘tikudziŵa chifuniro cha Ambuye nchiyani,’ chimene chimaphatikizapo kuchita nawo kwathu ntchito yolalikira “uthenga uwu wabwino wa Ufumu” nthaŵi zonse.​—Aefeso 5:15-17; Mateyu 24:14.

Zofuna za Yehova Zokhudza Kumwamba

13. Kodi zofuna za Mulungu zinkachitika motani kale kwambiri Satana asanapanduke?

13 Zofuna za Yehova zinkakwaniritsidwa kumwamba kale kwambiri m’modzi mwa ana ake auzimu asanapanduke kukhala Satana. Buku la Miyambo limasonyeza Mwana woyamba kubadwa wa Mulungu kukhala nzeru imene aifotokoza monga munthu. Zimenezi zimasonyeza kuti kwa zaka zambiri, Mwana wobadwa yekha wa Mulungu anali “kukondwera pamaso pake nthaŵi zonse,” kuchita zofuna za Atate wake mosangalala. M’kupita kwa nthaŵi, anakhala “mmisiri” wa Yehova polenga zinthu zonse “za m’mwamba, ndi za padziko, zooneka ndi zosaonekazo.” (Miyambo 8:22-31; Akolose 1:15-17) Yehova anagwiritsa ntchito Yesu ngati Mawu, kapena kuti Wom’lankhulira.​—Yohane 1:1-3.

14. Kodi tingaphunzire chiyani mu Salmo 103 za mmene angelo amakwaniritsira zofuna za Yehova kumwamba?

14 Wamasalmo akusonyeza kuti ulamuliro wa Yehova ndiye waukulu pa maulamuliro onse ndiponso kuti angelo miyandamiyanda amamvera malangizo ndi malamulo ake. Timaŵerenga kuti: “Yehova anakhazika mpando wachifumu wake Kumwamba; ndi ufumu wake uchita mphamvu ponsepo. Lemekezani Yehova, inu angelo ake; a mphamvu zolimba, akuchita mawu ake, akumvera liwu la mawu ake. Lemekezani Yehova, inu makamu ake onse; inu atumiki ake akuchita chom’kondweretsa Iye. Lemekezani Yehova, inu, ntchito zake zonse. Ponse ponse pali ufumu [kapena kuti, ulamuliro] wake.”​—Salmo 103:19-22.

15. Kodi kulandira mphamvu za Ufumu kwa Yesu kunakhudza bwanji zolinga za Mulungu kumwamba?

15 Satana atapanduka, ankathabe kupita kumwamba, monga mmene buku la Yobu likusonyezera. (Yobu 1:6-12; 2:1-7) Komabe, buku la Chivumbulutso linalosera kuti nthaŵi idzafika pamene Satana ndi ziŵanda zake adzachotsedwa kumwamba. Zikuoneka kuti nthaŵi imeneyo inafika Yesu Kristu atangolandira mphamvu za Ufumu mu 1914. Kuyambira nthaŵi imeneyo, opanduka amenewo alibenso malo kumwamba. Iwo amakhala malo ozungulira padziko lapansi. (Chivumbulutso 12:7-12) Pakali pano kumwamba sikumvekanso mawu otsutsa. Mawu amene amamveka ndi otamanda “Mwanawankhosa,” Kristu Yesu, komanso ogonjera molemekeza Yehova. (Chivumbulutso 4:9-11) Kunena zoona, zofuna za Yehova zikukwaniritsidwa kumwamba.

Zofuna za Yehova Zokhudza Dziko Lapansi

16. Kodi pemphero lachitsanzo limatsutsa bwanji chiphunzitso cha Matchalitchi Achikristu chokhudza chiyembekezo cha anthu?

16 Matchalitchi Achikristu amapatula dziko lapansi pa zofuna za Mulungu, ponena kuti anthu onse abwino amapita kumwamba. Koma Yesu anatiphunzitsa kupemphera kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:10) Kodi tinganene n’komwe kuti cholinga cha Yehova chikuchitika masiku ano padziko lapansi limene likukumana ndi mavuto osaneneka a chiwawa, kusoŵa chilungamo, matenda ndi imfa? Sitingatero! Motero tiyenera kupemphera mochokera pansi pamtima kuti zofuna za Mulungu zichitike padziko lapansi, mogwirizana ndi malonjezo amene analemba mtumwi Petro kuti: “Monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano [boma la Ufumu wa Mesiya lolamulidwa ndi Kristu], ndi dziko latsopano [anthu olungama] m’menemo mukhalitsa chilungamo.”​—2 Petro 3:13.

17. Kodi cholinga cha Yehova cha dziko lapansi n’chiyani?

17 Yehova anali ndi cholinga polenga dziko lapansi. Anauzira mneneri Yesaya kulemba kuti: “Atero Yehova amene analenga kumwamba, Iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenga mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu; Ine ndine Yehova; ndipo palibenso wina.” (Yesaya 45:18) Mulungu anaika anthu aŵiri oyamba m’munda wa paradaiso, ndipo anawalamula kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse.” (Genesis 1:27, 28; 2:15) N’zachionekere kuti cholinga cha Mlengi n’chakuti m’dziko lapansi mukhale anthu angwiro amene amagonjera mosangalala ulamuliro wa Yehova ndi kukhala m’Paradaiso mpaka kalekale, amene Kristu analonjeza.​—Salmo 37:11, 29; Luka 23:43.

18, 19. (a) Kodi payenera kuchitika chiyani chifuno cha Mulungu chisanachitike mokwanira padziko lapansi? (b) Kodi ndi mbali zina ziti m’pemphero lachitsanzo la Yesu zimene tikambirane mu nkhani yotsatira?

18 Zimene Yehova akufuna zokhudza dziko lapansi sizingakwaniritsidwe zonse pamene padziko lapansili pakukhalabe amuna ndi akazi amene samvera ulamuliro wake. Mwakugwiritsa ntchito angelo amphamvu mu ulamuliro wa Kristu, Mulungu ‘adzawononga iwo akuwononga dziko.’ Dongosolo lonse loipa la Satana, pamodzi ndi chipembedzo chake chonyenga, ndale zoipa, malonda adyera ndi achinyengo, ankhondo ankhanza, zidzachotsedwa ndipo sizidzakhalakonso mpaka kalekale. (Chivumbulutso 11:18; 18:21; 19:1, 2, 11-18) Posachedwapa zidzatsimikizidwa kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira ndipo dzina lake lidzayeretsedwa. Zonse zimenezi n’zimene timapempherera tikamanena kuti: “Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.”​—Mateyu 6:9, 10.

19 Komabe, m’pemphero lake lachitsanzo, Yesu anasonyeza kuti tingapemphererenso zinthu zokhudza ifeyo. Mu nkhani yotsatira tikambirana mbali zimenezi za malangizo ake okhudza pemphero.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Onani mutu 6 wa buku la Samalani Ulosi wa Danieli!, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kubwereza

• N’chifukwa chiyani n’koyenera kutchula Yehova kuti “Atate wathu”?

• N’chifukwa chiyani n’kofunika kwambiri kuti tizipempherera kuti dzina la Yehova liyeretsedwe?

• N’chifukwa chiyani timapemphera kuti Ufumu wa Mulungu udze?

• Kodi zimatanthauza chiyani tikamapemphera kuti chifuno cha Mulungu chichitike pa dziko lapansi monga kumwamba?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 9]

Mapemphero a Yesu ankasiyana kwambiri ndi mapemphero a Afarisi odzionetsera kuti ndi olungama

[Chithunzi patsamba 10]

Akristu amapempherera Ufumu wa Mulungu kuti udze, dzina lake liyeretsedwe, ndiponso kuti kufuna kwake kuchitidwe