Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mulungu Ndithudi Amakuganizirani

Mulungu Ndithudi Amakuganizirani

Mulungu Ndithudi Amakuganizirani

TIKAKHALA pa mavuto m’pomveka kupempha Mulungu kuti atithandize. Chifukwatu iye “ndi wa mphamvu zambiri; nzeru yake n’njosatha.” (Salmo 147:5) Iyeyu ndiye angathe kutithandiza bwino kwambiri kulimbana ndi mavuto athu. Kuphatikiza pamenepo Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘titsanulire mitima yathu’ pamaso pake. (Salmo 62:8) Motero, kodi n’chifukwa chiyani anthu ambiri amaganiza kuti Mulungu sayankha mapemphero awo? Kodi ndiye kuti iye sawaganizira?

M’malo mothamangira kuimba Mulungu mlandu mukaona ngati akunyalanyaza vuto lanu, yambani mwaganizira pamene munali mwana. Kodi makolo anu akapanda kuchita zina mwa zinthu zimene munkawapempha, munkawanena kuti sakukukondani? Ana ambiri amatero. Komabe mutakula, munazindikira kuti chikondi chimaonetsedwa m’njira zambiri ndiponso kuti kupatsa mwana chilichonse chimene angafune sikum’kondadi ayi.

N’chimodzimodzinso ndi Yehova, ngati sakuyankha mapemphero athu mmene ifeyo tikufunira, tisaganize kuti akutinyalanyaza. Chifukwatu tonsefe Mulungu amatisonyeza chikondi chake m’njira zambiri.

“Mwa Iye Tikhala ndi Moyo”

Choyamba, ifeyo ‘timakhala ndi moyo ndi kuyendayenda, ndi kupeza mkhalidwe wathu’ chifukwa cha Mulungu. (Machitidwe 17:28) Inde, potipatsa moyo iye anasonyeza chikondi chake!

Chinanso, Yehova amatipatsa zimene timafunikira kuti tikhale ndi moyo. Timaŵerenga kuti: “Ameretsa msipu ziudye ng’ombe, ndi zitsamba achite nazo munthu; natulutse chakudya chochokera m’nthaka.” (Salmo 104:14) Ndipotu, sikuti Mlengi wathu amangotipatsa zinthu zofunikira kuti tikhale ndi moyo, koma iye mowoloŵa manja amatipatsa “mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima [yathu] ndi chakudya ndi chikondwero.”​—Machitidwe 14:17.

Komabe, ena amadzifunsa kuti, ‘Ngati Mulungu amatikondadi kwambiri, kodi amaloleranji kuti tizivutika?’ Kodi yankho la funsoli inuyo mukulidziŵa?

Kodi Mulungu Ndiye Wolakwa?

Mavuto ambiri amene anthu amakumana nawo n’ngochita kuwaputa dala. Mwachitsanzo, zochita zina n’zodziŵikiratu kuti n’zangozi. Komabe, anthu amachita zachiwerewere, kumwa moŵa mwauchidakwa komanso kugwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo, kusuta fodya, kuchita maseŵera oika moyo pachiswe, kuthamangitsa kwambiri galimoto, ndiponso kuchita zinthu zina zangati zimenezi. Kodi munthu akapeza nazo mavuto zinthu zoika moyo pachiswe zoterezi ndiye kuti wolakwa ndani? Kodi ndi Mulungu kapena munthu wochita zinthu zopanda nzeruyo? Mawu ouziridwa a Mulungu amati: “Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.”​—Agalatiya 6:7.

Kuphatikizanso apo, nthaŵi zambiri anthu amachitirana zinthu zoipa. Dziko linalake likayambitsa nkhondo, anthu n’kuyamba kuvutika, sizomveka kuloza chala Mulungu. Chigaŵenga chikavulaza munthu, kodi Mulungu ndiye amachititsa kuti munthuyo avulale ngakhalenso kufa kumene? Ayi ndithu si choncho! Wolamulira wankhanza akamapondereza anthu ake, kuwazunza, ndi kuwapha, kodi tiziti wolakwa ndi Mulungu? Zimenezo sizingakhale zomveka ayi.​—Mlaliki 8:9.

Nangano, tinganenepo chiyani pa za anthu ambirimbiri amene akukhala mu umphaŵi wadzaoneni kapenanso amene alibiretu chakudya? Kodi pamenepa wolakwa ndi Mulungu? Ayi. M’dziko lathuli mumatuluka chakudya chomwe chingakwanire aliyense, china n’kutsalaponso. (Salmo 10:2, 3; 145:16) Chimene chimachititsa kuti anthu ambiri azivutika ndi njala ndiponso umphaŵi ndicho kusagaŵa bwino zinthu zochuluka zimene Mulungu amaperekazi. Ndipo chimene chimachititsa kuti vutoli lisathe n’chakuti anthu ali ndi mtima wadyera.

Pamene Pagona Vuto

Komano kodi munthu akadwala kapena kufa chifukwa cha ukalamba, wolakwa amakhala ndani? Kodi zingakudabwitseni kumva kuti ngakhale pankhani imeneyi wolakwa si Mulungu? Mulungu sanalenge anthu mwakuti azikalamba kenaka n’kufa.

Anthu aŵiri oyambirira, Adamu ndi Hava, atawaika m’munda wa Edene, Yehova anawapatsa chiyembekezo chokhala ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. Komabe, n’zoonekeratu kuti iye ankafuna kuti m’dzikoli mudzaze anthu oyamikira zimene anawapatsazo. Motero, anakonza zoti chiyembekezo chawo cha m’tsogolochi chikhale chodalira mfundo inayake. Mfundoyi ndi yakuti, Adamu ndi Hava akanakhalabe m’Paradaiso pokhapokha ngati akanapitirira kumvera Mlengi wawo wachikondi.​—Genesis 2:17; 3:2, 3, 17-23.

Koma n’zomvetsa chisoni kuti Adamu ndi Hava anaukira Mulungu. Hava anasankha kumvera Satana Mdyerekezi. Satanayu anam’namiza Hava ndipo mwa zonena zakezo kwenikweni ankasonyeza kuti pali kanthu kenakake kabwino kamene Mulungu ankabisira Hava. Motero Hava anayamba kuchita zinthu mwayekha poyesa ‘kukhala ngati Mulungu, wakudziŵa zabwino ndi zoipa.’ Adamu naye anachita chimodzimodzi.​—Genesis 3:5, 6.

Atachimwa chonchi, Adamu ndi Hava anasonyeza kuti sanali oyenerera kukhala ndi moyo kosatha. Analandira malipiro owawa a kuchimwa. Nyonga yawo ndiponso moyo wawo unayamba kuchepa ndipo mapeto ake anamwalira. (Genesis 5:5) Komabe, kuukira kwawoku kunaipitsa zinthu kuposa pamenepa. Panopa tikuvutikabe chifukwa cha kuchimwa kwa Adamu ndi Hava. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Inde, chifukwa chakuti Adamu ndi Hava anaukira Mulungu, uchimo ndiponso imfa zinafalikira kwa anthu onse ngati matenda oopsa kwambiri.

Umboni Waukulu Zedi Wakuti Mulungu Amatiganizira

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti anthu olengedwa ndi Mulungufe, tinaipitsidwa moti sitingakonzekenso? Ayi, ndipotu mfundoyi imatifikitsa pa umboni waukulu zedi wakuti Mulungu amatiganiziradi. Ngakhale kuti zinali zomuvuta kwambiri, Mulungu anakonza njira yowombolera anthu kuchoka ku uchimo ndi imfa. Mtengo wowombolera anthuwu unali moyo wangwiro wa Yesu, womwe iye anaupereka mochita kufuna kuti atipulumutse. (Aroma 3:24) Motero, mtumwi Yohane analemba kuti: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Chifukwa cha chikondi chachikulu choterechi, ifeyo tili ndi chiyembekezo chokhalanso ndi moyo wosatha. Paulo analembera Aroma kuti: “Mwa chilungamitso chimodzi chilungamo cha moyo chinafikira anthu onse.”​—Aroma 5:18.

Tisakayike n’komwe kuti nthaŵi ya Mulungu ikadzakwana, padziko lapansi pano sipadzakhalanso kuvutika kapena imfa. M’malo mwake, zinthu zonse zidzakhala ngati mmene ulosi wa m’buku la Chivumbulutso umanenera kuti: “Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.” (Chivumbulutso 21:3, 4) Mwina mukuganiza kuti, ‘Sindidzakhala ndidakali moyo zimenezi zikamadzachitika.’ Komatu zoona zake n’zakuti n’kutheka kuti mudzakhala mudakali moyo. Ndipo ngakhale mutamwalira, Mulungu angathe kudzakuukitsani. (Yohane 5:28, 29) Zimenezi n’zimene Mulungu akufuna kudzatichitira, ndipo n’zimene zidzachitikedi. Ndithu, kunena kuti Mulungu saganizira anthu ndi bodza lamkunkhuniza!

“Yandikirani kwa Mulungu”

N’zolimbikitsa kudziŵa kuti Mulungu anaika njira yodzathetseratu mavuto a anthu mpaka kalekale. Nanga bwanji panopa? Kodi tingatani munthu amene timam’konda akamwalira kapena mwana wathu akadwala? Nthaŵi yoti Mulungu adzachotse matenda ndiponso imfa sinakwane. Baibulo limasonyeza kuti tiyenera kudikira pang’ono kuti zimenezi zidzachitike. Komano sikuti Mulungu wangotisiya popanda thandizo. Wophunzira Yakobo anati: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.” (Yakobo 4:8) Inde, Mlengi wathu akutipempha kuti tizikondana naye kwambiri, ndipotu anthu amene amatero, nthaŵi zonse amaona kuti iye amawathandiza ngakhale akakhala pamavuto adzaoneni.

Kodi tingayandikire motani kwa Mulungu? Mfumu Davide anafunsa funso langati lomweli, pafupifupi zaka 3,000 zapitazo. Iye anati: “Yehova, . . . adzagonera ndani m’phiri lanu lopatulika?” (Salmo 15:1) Davide anayankha yekha funso lakeli pamene anati: “Iye wakuyendayo mokwanira, nachita chilungamo, nanena zoonadi mumtima mwake. Amene sasinjirira ndi lilime lake, sachitira mnzake choipa.” (Salmo 15:2, 3) Tingoti, Yehova amalandira aliyense amene amatsatira njira imene Adamu ndi Hava anakana kutsatira. Iye amayandikira kwa anthu amene amachita chifuniro chake.​—Deuteronomo 6:24, 25; 1 Yohane 5:3.

Kodi tingachite bwanji chifuniro cha Mulungu? Tiyenera kudziŵa “chokoma ndi cholandirika pamaso pa Mulungu Mpulumutsi wathu” ndipo kenaka n’kutsimikiza mtima kuchitadi zimenezo. (1 Timoteo 2:3) Ndiye kuti tiyenera kudziŵa molondola Mawu a Mulungu, omwe ndi Baibulo. (Yohane 17:3; 2 Timoteo 3:16, 17) Izi sizikutanthauza kuŵerenga Baibulo mwamwambo chabe. Tiyenera kutsanzira Ayuda a ku Bereya a m’zaka 100 zoyambirira amene anamva Paulo akulalikira. Timaŵerenga za Ayudaŵa kuti: “Ameneŵa anali mfulu koposa a m’Tesalonika, popeza analandira mawu ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m’malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.”​—Machitidwe 17:11.

Masiku anonso, kuŵerenga Baibulo mosamalitsa kumalimbitsa chikhulupiriro chathu mwa Mulungu ndipo kumatithandiza kuti tiyambe kugwirizana naye kwambiri. (Ahebri 11:6) Kumatithandizanso kumvetsetsa bwinobwino mmene Yehova amachitira zinthu ndi anthu, osati poganizira zimene angapindule kwa nthaŵi yochepa koma makamaka poganizira zimene anthu onse owongoka mtima angapindule nazo mpaka kalekale.

Taonani mawu otsatiraŵa omwe Akristu angapo okondana kwambiri ndi Mulungu ananena. Danielle, yemwe ali ndi zaka 16 anati: “Yehova ndimam’konda kwambiri, ndipo pali zifukwa zambiri zimene ndimam’thokozera. Anandipatsa makolo amene amandikonda omwenso amam’kondadi iyeyo ndiponso amene andiphunzitsa m’njira yogwirizana ndi Mawu ake.” Mkristu wina wa ku Uruguay anati: “Ndimam’thokoza Yehova mochoka pansi pamtima chifukwa cha chisomo chake ndiponso chifukwa chokhala mnzanga.” Mulungu amalandira ngakhale tiana. Gabriela, yemwe ali ndi zaka seveni anati: “Ndimakonda Mulungu koposa china chilichonse m’dziko lonse lino! Ndili ndi Baibulo langalanga. Ndimakonda kuphunzira za Mulungu ndiponso za Mwana wake.”

Masiku ano, anthu ambirimbiri padziko lonse amavomerezana ndi wamasalmo amene anati: “Kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu.” (Salmo 73:28) Iwoŵa athandizidwa kupirira mavuto awo panopa, ndipo sakayika kuti adzakhala kosatha m’Paradaiso padziko lapansi. (1 Timoteo 4:8) Nanga inuyo mulekeranji kukhala n’cholinga ‘choyandikira kwa Mulungu’? Baibulotu limatitsimikizira kuti: “[Iye] sakhala patali ndi yense wa ife.” (Machitidwe 17:27) N’zoonadi, Mulungu amakuganiziranidi!

[Zithunzi patsamba 5]

Timaona m’njira zambiri kuti Yehova amatiganizira

[Chithunzi patsamba 7]

Ngakhale ana aang’ono angathe kuyandikira kwa Mulungu

[Zithunzi patsamba 7]

Masiku ano, Yehova amatithandiza kupirira. Panthaŵi yake, iye adzachotsa matenda ndiponso imfa