Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi pa Zozizwitsa za Yesu Mungaphunzirepo Chiyani?

Kodi pa Zozizwitsa za Yesu Mungaphunzirepo Chiyani?

Kodi pa Zozizwitsa za Yesu Mungaphunzirepo Chiyani?

MUNGADABWE kudziŵa kuti m’nkhani za m’Baibulo za moyo wa Yesu padziko lapansi mulibe mawu achinenero choyambirira akuti “chozizwitsa.” Mawu a Chigiriki (dyʹna·mis) amene nthaŵi zina awamasulira kuti “chozizwitsa” kwenikweni amatanthauza “mphamvu.” (Luka 8:46) Tingawamasulirenso kuti “nzeru” kapena “ntchito zamphamvu.” (Mateyu 11:20; 25:15) Malinga ndi zimene katswiri wina ananena, mawu a Chigiriki ameneŵa “amanena za ntchito yaikulu imene yachitika, ndipo amanena makamaka mphamvu imene yachititsa ntchitoyo. Amasonyeza kuti ntchitoyo yachitika mwa mphamvu ya Mulungu.”

Mawu ena a Chigiriki (teʹras) nthaŵi zambiri amawamasulira kuti “zodabwitsa” kapena “zozizwa.” (Yohane 4:48; Machitidwe 2:19) Mawu ameneŵa amasonyeza makamaka zimene anthu amachita akaona zimenezo. Kaŵirikaŵiri, anthu ambiri oonerera ndiponso ophunzira a Yesu ankadabwa ndi kuzizwa akaona ntchito zamphamvu zimene Yesu anali kuchita.​—Marko 2:12; 4:41; 6:51; Luka 9:43.

Mawu achitatu a Chigiriki (se·meiʹon) onena za zozizwitsa za Yesu amatanthauza “chizindikiro.” Katswiri wina wamaphunziro Robert Deffinbaugh anati mawu ameneŵa “amasonyeza tanthauzo lenileni la chozizwitsa.” Ananenanso kuti: “Chizindikiro ndicho chozizwitsa chimene chimathandiza kumvetsa choonadi chinachake chonena za Ambuye wathu Yesu.”

Kodi Ankanyengeza Anthu Kapena Anali ndi Mphamvu Yochokera kwa Mulungu?

Baibulo silimanena kuti zozizwitsa za Yesu zinali zongopusitsa anthu kapena kuwanyengeza pofuna kuwasangalatsa. Zinali kusonyeza “ukulu wake wa Mulungu,” monga zinachitikira pankhani ya mnyamata amene Yesu anam’tulutsa chiwanda. (Luka 9:37-43) Kodi ntchito zamphamvu zimenezi zingakhale zosatheka kwa Mulungu Wamphamvuyonse amene amanenedwa kuti ali ndi ‘mphamvu zazikulu’? (Yesaya 40:26) Ayi, ndithu!

Mauthenga Abwino amatchula zozizwitsa za Yesu zokwana pafupifupi 35. Koma satchula zozizwitsa zonse zimene anachita. Mwachitsanzo, pa Mateyu 14:14 pamati: ‘[Yesu] anaona khamu lalikulu la anthu, nachitira iwo chifundo, nachiritsa akudwala awo.’ Sananenepo kuti ndi anthu odwala angati amene anawachiritsa panthaŵi imeneyi.

Ntchito zamphamvu zimenezi zinali zofunika kwambiri potsimikizira zimene Yesu ankanena kuti anali Mwana wa Mulungu, Mesiya wolonjezedwa. Malemba amasonyezadi kuti mphamvu zimene Mulungu anam’patsa zinamuthandiza Yesu kuchita zozizwitsa. Mtumwi Petro anatcha Yesu kuti “mwamuna wochokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndi zimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikiro, zimene Mulungu anazichita mwa iye pakati pa inu, monga mudziŵa nokha.” (Machitidwe 2:22) Panthaŵi ina, Petro ananena kuti “Mulungu anam’dzoza iye [Yesu] ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdyerekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi iye.”​—Machitidwe 10:37, 38.

Zozizwitsa za Yesu zinkayenderana ndi uthenga wake. Pa Marko 1:21-27 pamasonyeza zimene anthu anachita atamva zimene Yesu anali kuphunzitsa ndiponso ataona chozizwitsa chake china. Pa Marko 1:22 pamati anthu “anazizwa ndi chiphunzitso chake,” ndipo pa vesi 27 pamanena kuti anthu “anazizwa” Yesu atatulutsa chiwanda. Ntchito zamphamvu za Yesu ndi uthenga wake zinapereka umboni wakuti anali Mesiya wolonjezedwa.

Yesu sikuti anapereka umboni wakuti anali Mesiya mwa mawu okha kapenanso mwa zochita zake zina, koma iye anateronso mwa mphamvu zochitira zozizwitsa zimene Mulungu anam’patsa. Patabuka mafunso onena za ntchito ndi udindo wake, Yesu anayankha molimba mtima kuti: “Ine ndili nawo umboni woposa wa Yohane [Mbatizi]; pakuti ntchito zimene Atate anandipatsa ndizitsirize, ntchito zomwezo ndizichita zindichitira umboni, kuti Atate anandituma Ine.”​—Yohane 5:36.

Umboni Wakuti Zinali Zenizeni

Kodi tingatsimikize bwanji kuti zozizwitsa za Yesu zinali zenizeni? Onani zina zimene zikusonyeza kuti zinali zenizeni.

Pochita ntchito zamphamvu, Yesu sanafune kuti anthu azim’tama. Ankaonetsetsa kuti akachita chozizwitsa china chilichonse Mulungu apatsidwe ulemu ndi kulemekezedwa. Mwachitsanzo, asanachiritse munthu wosaona, Yesu ananena motsindika kuti munthuyo achiritsidwa “kuti ntchito za Mulungu zikaonetsedwe mwa iye.”​—Yohane 9:1-3; 11:1-4.

Mosiyana ndi anthu ochita zinthu zongonyengeza anthu, amatsenga, ndiponso ochiritsa anthu mwa kuwapempherera, Yesu sankagodomalitsa anthu maganizo, kuwanyengeza, kuchita zionetsero zofuna kugometsa anthu, zamatsenga, kapena kuchita zonyamula anthu maganizo. Sanatsatire zikhulupiriro za anthu kapena kugwiritsa nchito zinthu zimene ankati n’zopatulika. Taonani kudzichepetsa kwa Yesu pamene ankachiritsa anthu aŵiri osaona. Nkhaniyo imati: “Yesu anagwidwa ndi chifundo, nakhudza maso awo; ndipo pomwepo anapenyanso, nam’tsata iye.” (Mateyu 20:29-34) Pamenepa sanachite mwambo wina uliwonse kapena chionetsero. Yesu ankachita zozizwitsa poyera, ndipo nthaŵi zambiri ankazichita anthu ambiri akuona. Sankagwiritsa ntchito malo ochita kukonzedwa mwapadera, kapenanso zipangizo zina zapadera. Mosiyana ndi zimenezi, zimene anthu masiku ano amati n’zozizwitsa nthaŵi zambiri zimakhala zopanda umboni wotsimikizirika.​—Marko 5:24-29; Luka 7:11-15.

Nthaŵi zina Yesu ankanena kuti munthu amene wachiritsidwayo ali ndi chikhulupiriro. Koma Yesu sankalephera kuchiritsa munthu chifukwa chakuti munthuyo alibe chikhulupiriro. Ali ku Kapernao ku Galileya, anthu ‘anabwera nawo kwa iye anthu ambiri ogwidwa ndi mizimu yoipa; ndipo iye anatulutsa mizimuyo ndi mawu, nachiritsa akudwala onse.’​Mateyu 8:16.

Yesu anali kuchita zozizwitsa pofuna kuthandiza anthu pa zimene analidi kufunikira pamoyo wawo, osati kungofuna kusangalatsa anthu amene anali kuonerera. (Marko 10:46-52; Luka 23:8) Ndipo Yesu sanachite zozizwitsa kuti apeze phindu m’njira ina iliyonse.​—Mateyu 4:2-4; 10:8.

Nanga Bwanji Mauthenga Abwino?

Tadziŵa za zozizwitsa za Yesu kudzera m’Mauthenga Abwino anayi. Kodi pali zifukwa zodalirira nkhani zimenezi pamene tikupenda ngati zozizwitsa za Yesu zinali zenizeni? Inde, zifukwa zilipo.

Monga taonera, zozizwitsa za Yesu zinkachitikira pagulu, anthu ambiri akuona. Mabuku a Mauthenga Abwino amene analembedwa chakoyambirira analembedwa ambiri mwa anthu amene anaona zozizwitsazi ali ndi moyo. Pankhani yakuti olemba Mauthenga Abwino anali oona mtima, buku lakuti The Miracles and the Resurrection linati: “N’kulakwa kwambiri kunena kuti olemba Mauthenga Abwino ankalemba dala nkhani zambirimbiri za zozizwitsa pofuna kubisa zimene zinachitikadi n’cholinga chofalitsa chikhulupiriro chawo. . . . Iwo ankangofuna kulemba zoona zokhazokha.”

Anthu achiyuda otsutsa Chikristu sanakayikirepo ntchito zamphamvu za m’Mauthenga Abwino. Iwo ankakayikira mphamvu imene inkachititsa zimenezi basi. (Marko 3:22-26) Ngakhale amene anadzakhala otsutsa analephera kutsutsadi zozizwitsa za Yesu. M’malomwake, zisanakwane zaka 100 ndiponso pambuyo pa zaka 100 Kristu Atabwera, panali maumboni a zozizwitsa zimene Yesu anachita. Ndithudi, tili ndi zifukwa zokwanira zokhulupirira kuti nkhani za m’Mauthenga Abwino zonena za zozizwitsa za Yesu n’zenizeni.

Khalidwe la Munthu Amene Ankachita Zozizwitsazi

Kuti timvetse zozizwitsa za Yesu sitingalekere pamfundo yakuti zozizwitsa zake zinali zenizeni. Pofotokoza ntchito zamphamvu zimene Yesu anachita, Mauthenga Abwino amanena za munthu amene anali kukhudzidwa mtima kwambiri ndiponso wachifundo koposa, wochita chidwi ndi moyo wa anthu anzake.

Taonani nkhani ya munthu wodwala khate amene anafika kwa Yesu ndi kum’chonderera momvetsa chisoni kuti: “Ngati mufuna mukhoza kundikonza.” Yesu ‘atagwidwa chifundo,’ anatansa dzanja ndi kukhudza munthu wodwala khateyo, nanena kuti: “Ndifuna; khala wokonzedwa.” Munthuyo anachiritsidwa nthaŵi yomweyo. (Marko 1:40-42) Chotero, Yesu anasonyeza kuti chisoni n’chimene chinkamupangitsa kugwiritsira ntchito mphamvu zimene Mulungu anamupatsa zochitira zozizwitsa.

Kodi chinachitika n’chiyani Yesu atakumana ndi anthu amene ananyamula maliro akuchokera m’mudzi wa Nayini? Mnyamata amene anali atamwalirayo anali mwana mmodzi yekhayo wa mkazi wina wa masiye. Yesu ‘atagwidwa chifundo’ ndi mayiyo, anam’yandikira nanena kuti: “Usalire.” Ndiyeno anaukitsa mwana wa mayiyo.​—Luka 7:11-15.

Phunziro lolimbikitsa kwambiri limene tikuphunzira pa zozizwitsa za Yesu n’lakuti anali ‘kugwidwa chifundo’ ndipo ankachita zinthu kuti athandize anthu. Koma zozizwitsa zimenezi sikuti ndi mbiri chabe. Pa Ahebri 13:8 pamati: “Yesu Kristu ali yemweyo dzulo, ndi lero, ndi ku nthaŵi zonse.” Panopo akulamulira monga Mfumu kumwamba, ndipo ndi wokonzeka ndiponso angagwiritse ntchito mphamvu zimene Mulungu anam’patsa zochitira zozizwitsa m’njira yaikulu zedi kuposa mmene anachitira ali padziko lapansi pano. Posachedwapa, Yesu adzagwiritsira ntchito mphamvuzo kuchiritsira anthu omvera. Mboni za Yehova zidzasangalala kukuthandizani kuphunzira zambiri ponena za chiyembekezo cha m’tsogolo chabwino kwambiri chimenechi.

[Zithunzi pamasamba 4, 5]

Zozizwitsa za Yesu zinali kusonyeza “ukulu wake wa Mulungu”

[Chithunzi patsamba 7]

Yesu anali munthu amene amakhudzidwa mtima kwambiri