Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Malimwe ndi Dzinja Sizidzatha

Malimwe ndi Dzinja Sizidzatha

Kukongola kwa Chilengedwe cha Yehova

Malimwe ndi Dzinja Sizidzatha

DZUŴA likakula mphamvu, si mmene mumatenthera m’chipululu. M’madera ena a dziko lapansi, dzuŵa limachititsa kuti kunja kuyambe kufunda nyengo ya chisanu ikatha. Inde, chinthu chimodzi chachikulu chimene chimachititsa kuti pazikhala nyengo zosiyanasiyana ndicho kutentha kwa dzuŵa.

Nyengo zimakhala zosiyanasiyana m’madera a padziko lonse. Koma kodi nyengo zimakukhudzani bwanji inuyo? Kodi mumasangalala kunja kukayamba kugwa mvula pambuyo pa nyengo yaitali yachilimwe? Kodi mumamva bwanji nthaŵi ya chilimwe madzulo a tsiku limene kunacha bwino? Kodi simusangalala ndi nthaŵi yokolola, imene alimi amakolola zipatso za thukuta lawo?

Kodi n’chiyani chimachititsa kuti pazikhala nyengo zosiyanasiyana. Mwachidule, tingati ndi kupendekeka kwa dziko. Dziko limayenda mopendekeka pang’ono likamazungulira dzuŵa. Dziko likanapanda kukhala mopendekeka choncho sibwenzi nyengo ikumasintha. Bwenzi nyengo ikumangokhala yomweyomweyo nthaŵi zonse. Motero zomera ndiponso ulimi ukanakhala wosiyana ndi umene timachitawu.

Munthu aliyense angathe kuona kuti Mlengi ndiye anakonza zakuti nyengo izisinthasintha. Mpake kuti wamasalmo ananena mawu aŵa kwa Yehova Mulungu: ‘Munaika malekezero onse a dziko lapansi; munalenga dzinja ndi malimwe.’​Salmo 74:17. *

Kwa munthu amene ali padziko lapansi, zinthu zimene zili kumwamba monga dzuŵa, mwezi, ndi nyenyezi zimasonyeza nyengo m’njira yolondola kwambiri. Polenga mapulaneti onse amene amazungulira dzuŵa, Mulungu anati: “Pakhale zounikira pa thambo la kumwamba . . . zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku, ndi zaka.” (Genesis 1:14) Pachaka, dziko likamazungulira dzuŵa, limafika malo aŵiri amene masana dzuŵalo limadutsa pamutu penipeni m’chigawo chotentha kwambiri chimene chimagaŵa dzikoli m’zigawo ziŵiri zofanana. Zimenezi zimachititsa kuti nthaŵi imeneyi padziko lonse masana azikhala kwa nthaŵi yofanana ndi usiku ndipo m’madera ambiri ndizo zimasonyeza kuyamba kwa nyengo ya dzinja ndiponso ya masika.

Kusinthasintha kwa nyengo sikuti kumangochitika chifukwa cha kuyendayenda ndiponso malo amene pali zinthu za kumwamba monga mwezi. Kusinthasintha kwa nyengo tsiku ndi tsiku ndiponso pachaka kumakhudzidwa ndi zinthu zosiyanasiyana zimene zimathandizira kuti padziko pano pakhale zamoyo. Mtumwi wachikristu Paulo, ndi mnzake Barnaba anauza anthu okhala ku Asiyamina kuti Mulungu ndiye ‘akupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwero.’ Ambiri a anthuŵa ankadziŵa bwino zaulimi.​—Machitidwe 14:14-17.

Njira yochititsa chidwi imene zomera zimapangira chakudya chawo imathandiza kuti zinthu zizimera panthaka ndiponso m’nyanja. Chifukwa cha zimenezi nyengo imasintha kudalirana kwa zolengedwa pankhani ya chakudya ndiponso pa moyo wawo m’njira zovuta kuzifotokoza. Mpake kuti Paulo ananena kuti zonsezi amazichita ndi Yehova pamene Pauloyu anati: “Nthaka imene idamwa mvula iigwera kaŵirikaŵiri, nipatsa therere loyenera iwo amene adailimira, ilandira dalitso lochokera kwa Mulungu.”​—Ahebri 6:7.

Mawu akuti “dalitso” tanthauzo lake limamveka bwino kwambiri mukaganizira mozama zimene zimachitika m’madera a padziko lino amene panyengo ya dzinja kunja kumakhala kotenthera bwino, kunja sikuda msanga, dzuŵa limaŵala bwino, ndiponso kumagwa mvula bwino. Zomera zimayamba kutuluka maluŵa ndipo tizilombo timayamba kutuluka m’mayenje amene timabisalamo nthaŵi ya chisanu, tili tokonzeka kuthandiza mbewu kuti ziberekane. Mbalame monga imene mukuona apayi, zimachititsa kuti m’nkhalango muzikongola ndiponso kuti muzimveka tinyimbo tosangalatsa, ndipo zomera nazo zimasangalala. Zinthu zimachitika mofulumira ndiponso zamoyo zimapitiriza kuberekana, zomera zimaphukiranso ndiponso kukula. (Nyimbo ya Solomo 2:12, 13) Kumeneku n’kukonzekera nthaŵi yokolola m’nyengo ya chilimwe kapena ya masika.​—Eksodo 23:16.

Ntchito za Yehova zimaoneka kudabwitsa kwake mukaganizira za mmene anakhazikira dziko lapansi kuti pakhale masana ndi usiku, pakhale nyengo zosiyanasiyana ndiponso kuti pakhale nthaŵi yobzala ndi yokolola. Chisanu chikatha sitikayika ngakhale pang’ono kuti pabwera chilimwe. Chifukwatu ndi Mulungu amene analonjeza kuti: “Pakukhalabe masiku a dziko lapansi, nthaŵi yakubzala ndi yakukunkha, chisanu ndi mafundi, malimwe ndi msakasa, usana ndi usiku sizidzalekayi.”​—Genesis 8:22.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Onani Kalendala ya 2004 ya Mboni za Yehova pa mwezi wa July ndi wa August.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 9]

Mwezi N’ngofunika Kuti Zinthu Zikhale Bwino

Kwa zaka zambiri m’mbuyo monsemu, mwezi wakhala ukuchititsa chidwi kwambiri anthu ndiponso kuwalimbikitsa kuchita zinthu zinazake. Koma kodi mumadziŵa kuti mwezi umakhudza kusintha kwa nyengo? Mwezi umathandiza kuti nthaŵi zonse dziko likhale mopendekeka bwino pozungulira dzuŵa. Zimenezi “zimathandiza kwambiri kuti padziko lapansi pazitheka kukhala zinthu zamoyo,” anatero wolemba nkhani za sayansi Andrew Hill. Pakanakhala kuti palibe mwezi wochititsa kuti dzikoli lizipendekeka bwinobwino bwenzi kukumatentha kwambiri ndipo mosakayikira si bwenzi zili zotheka kukhala ndi zamoyo padziko pano. Motero gulu la akatswiri a zakuthambo linanena kuti: “Mwezi, tingati ndiwo umathandiza kuti nyengo izisintha mwadongosolo labwino padziko.”​—Salmo 104:19.

[Mawu a Chithunzi]

Moon: U.S. Fish & Wildlife Service, Washington, D.C./​Bart O’Gara

[Chithunzi patsamba 9]

Ngamila, kumpoto kwa Africa ndi ku Arabian Peninsula