Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani ndi Zolinga Zauzimu Kuti Mulemekeze Nazo Mlengi Wanu

Khalani ndi Zolinga Zauzimu Kuti Mulemekeze Nazo Mlengi Wanu

Khalani ndi Zolinga Zauzimu Kuti Mulemekeze Nazo Mlengi Wanu

“MUNTHU amene sakudziŵa doko limene akupita, alibe nazo ntchito zakuti mphepo ikuloŵera kuti panyanjapo.” Mawu ameneŵa, omwe amati ananenedwa ndi munthu wina wanzeru wa ku Roma wa m’zaka za m’ma 100 Yesu Atabwera amasonyeza kuti n’zoonadi kuti munthu ayenera kukhala ndi zolinga kuti adziŵe komwe akuloŵera ndi moyo wake.

M’Baibulo muli zitsanzo za anthu amene anali ndi zolinga. Kwa zaka pafupifupi 50, Nowa anachita khama ‘pomanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m’nyumba yake.’ Mneneri Mose “anapenyerera chobwezera cha mphotho.” (Ahebri 11:7, 26) Yoswa, yemwe analoŵa m’malo mwa Mose, anakwaniritsa cholinga chimene Mulungu anam’patsa chakuti alande dziko la Kanani.​—Deuteronomo 3:21, 22, 28; Yoswa 12:7-24.

M’zaka za m’ma 100 Kristu Atabwera, n’zosakayikitsa kuti mtumwi Paulo anakhala ndi zolinga zake zauzimu chifukwa cholimbikitsidwa ndi mawu a Yesu akuti “uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi.” (Mateyu 24:14) Polimbikitsidwa ndi mauthenga ndiponso masomphenya ochokera kwa Ambuye Yesu, kuphatikizaponso ntchito imene anam’patsa ya ‘kunyamula dzina la [Yesu] pamaso pa amitundu,’ Paulo anathandiza kwabasi pokhazikitsa mipingo yachikristu yambirimbiri ku Asiyamina konse mpaka kukafika ku Ulaya.​—Machitidwe 9:15; Akolose 1:23.

Inde, m’mbuyo monsemu atumiki a Yehova akhala ndi zolinga zabwino kwambiri ndipo azikwaniritsa, n’kulemekeza nazo Mulungu. Kodi masiku ano tingapange bwanji zolinga zauzimu? Kodi ndi zolinga zotani zimene tingakhale nazo, ndipo kodi tingatani kuti tizikwaniritsedi?

M’pofunika Kukhala ndi Maganizo Abwino

Munthu angakhale ndi zolinga zosiyanasiyana m’moyo wake, ndipo padziko pano pali anthu omwe amakonda kudziikira zolinga zosiyanasiyana. Komano zolinga zokhudza kutumikira Mulungu n’zosiyana ndi zolinga wamba. Anthu ambiri padziko pano amakhala ndi zolinga zinazake poganizira kwambiri za chuma kapena pofunitsitsa maudindo ndiponso mphamvu. Komatu kukhala ndi cholinga chinachake poganizira zofuna mphamvu kapena kutchuka n’kulakwitsa kwabasi! Zolinga zimene tingalemekeze nazo Yehova Mulungu zimakhala zokhudza kumulambira iyeyo ndiponso kuchita zinthu zothandiza pa ntchito ya Ufumu. (Mateyu 6:33) Timakhala n’zolinga zotere chifukwa chokonda Mulungu ndiponso anansi athu ndipo potero timaganizira kwambiri za kudzipereka kwathu kwa Mulungu.​—Mateyu 22:37-39; 1 Timoteo 4:7.

Maganizo athu azikhala oyenerera tikamapanga ndiponso kuyesetsa kukwaniritsa zolinga zauzimu, kaya n’zokhudza kupeza mwayi wotumikira Mulungu m’njira zinanso kapena kukula mwauzimu. Komatu, nthaŵi zina kukwaniritsa zolinga zinazake sikutheka ngakhale maganizo athu atakhala oyenera. Kodi tingapange bwanji zolinga ndi kuzikwaniritsa mosavuta?

Tiyenera Kukhala Ofunitsitsa Kuzikwaniritsa

Taganizirani mmene Yehova anakwaniritsira ntchito yolenga chilengedwe. Ponena kuti “panali madzulo ndipo panali m’maŵa,” Yehova anasonyeza kuti anagaŵagaŵa nyengo iliyonse yolengera zinthu. (Genesis 1:5, 8, 13, 19, 23, 31) Pachiyambi pa nyengo iliyonse yolengera zinthuzo, iye ankadziŵa bwinobwino cholinga chake, kapena kuti chimene anali kufuna kukwaniritsa pa nyengo imeneyo. Ndipo Mulungu anakwaniritsa cholinga chake choti alenge zinthu. (Chivumbulutso 4:11) Kholo lakale Yobu, anati chimene ‘moyo wa [Yehova] uchifuna achichita.’ (Yobu 23:13) Yehova ayenera kuti anakondwera kwambiri kuona “zonse zimene adazipanga,” ndipo ananena kuti “zinali zabwino ndithu”!​—Genesis 1:31.

Kuti tikwaniritsedi zolinga zathu, nafenso tiyenera kukhala ofunitsitsa kuzikwaniritsa. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tikhale ofunitsitsa motero? Ngakhale pamene dziko lapansi linali lopanda kanthu, Yehova ankatha kuona mmene lidzakhalire akakwaniritsa cholinga chake; ankaona kuti lidzakhala ngati mwala wokongola wamtengo wapatali mumlengalengamu, ndipo lidzachititsa kuti iye alandire ulemerero ndiponso alemekezedwe. Chimodzimodzinso ifeyo, tingakhale ofunitsitsa kukwaniritsa zolinga zathu poganizira bwino za mmene tidzapindulire tikakwaniritsa cholinga chathucho. Izi n’zimene zinam’chitikira Tony, yemwe ali ndi zaka 19. Iye sanaiŵale mmene anamvera nthaŵi yoyamba imene anakaona ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova m’dziko lina la ku madzulo a ku Ulaya. Kuchokera panthaŵiyi, funso limene Tony ankangoliganizira linali lakuti, ‘Kodi ndingamve bwanji nditamakhala ndiponso kutumikira pamalo amene aja?’ Tony anapitirizabe kuganizira zodzachita zimenezi, ndipo sanasiye kuyesayesa kukwaniritsa cholinga chakechi. Patatha zaka zingapo iye anasangalala kwambiri pamene anamuvomera kukatumikira pa nthambipo!

Kucheza ndi anthu amene anakwaniritsa kale cholinga chinachake kungatilimbikitsenso kuti nafe tichikwaniritse. Jayson, yemwe ali ndi zaka 30, sankakonda kuchita utumiki wa kumunda adakali m’nyamata wa zaka zongopitirira pa 13. Koma atamaliza sukulu ya sekondale, iye anayamba kuchita utumiki waupainiya ndi mtima wonse, motero anakhala wolengeza Ufumu wa nthaŵi zonse. Kodi n’chiyani chinam’thandiza Jayson kukhala wofunitsitsa kuchita upainiya? Iye anayankha kuti: “Ndinalimbikitsidwa kwambiri chifukwa cholankhulana ndi anthu ena amene anachitapo upainiya ndiponso chifukwa choyenda nawo mu utumiki.”

Kulemba Zolinga Zathuzo Kumathandiza

Zimene timangoziganizira zimatsatirika bwino tikazilongosola m’mawu omveka bwino. Solomo anati mawu oyenerera angathe kukhala amphamvu ngati zisonga kapena zikwapu zolishira ng’ombe za pagoli chifukwa angatithandize kudziŵa koloŵera m’moyo wathu. (Mlaliki 12:11) Mawuwo tikachita kuwalemba, amatilimbikitsa ndiponso amatikhudza kwambiri. N’chifukwa chaketu Yehova anauza mafumu a Israyeli kuti azidzilembera okha Chilamulo chonse pamanja. (Deuteronomo 17:18) Motero tingachite bwino kulemba zolinga zathu ndiponso mmene tikufuna kuzikwaniritsira. Chinanso chingatithandize ndicho kuzindikira zimene tiyenera kudziŵa bwino, maluso amene tiyenera kuphunzira, ndiponso anthu amene angatithandize.

Chifukwa chokhala ndi zolinga zauzimu Geoffrey anathandizika kwambiri kukhazika mtima wake m’malo. Iyeyu wakhala mpainiya wapadera kwa nthaŵi yaitali m’gawo lakutali la m’dziko lina ku Asia. Zinthu zinam’tembenukira mkazi wake atamwalira mwadzidzidzi. Atatha kulira malirowo, Geoffrey anaganiza zopanga zolinga zinazake kuti moyo wake wonse ukhale pautumiki wa upainiya. Iye analemba kaye zolinga zakezo ndipo mothandizidwa ndi mapemphero anayesetsa kukwaniritsa cholinga choti ayambitse maphunziro atatu a Baibulo mweziwo usanathe. Tsiku lililonse likatha ankaona bwinobwino zimene wachita patsikulo, ndipo pa masiku khumi alionse, ankayang’ana m’mbuyo n’kuona mmene wachitira. Kodi anakwaniritsa cholinga chake? Inde, chifukwatu panopo ali ndi maphunziro anayi a Baibulo!

Khalani ndi Zolinga Zing’onozing’ono Kuti Mudziŵe Pamene Mwafika

Zolinga zina poyamba zimaoneka ngati zosatheka kuzikwaniritsa. Kwa Tony, amene tam’tchula kale uja, zotumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova zinkangooneka ngati maloto basi. Zinali choncho chifukwa chakuti ankakhala moyo woloŵelera, ndipo anali asanadzipatulire n’komwe kwa Mulungu. Komano Tony anaganiza zoti moyo wake ukhale wogwirizana ndi njira za Yehova ndipo anakhala ndi cholinga choti adzabatizidwe. Atakwaniritsa cholinga chimenecho, iye anakhala ndi cholinga chochita upainiya wothandiza ndipo kenaka wokhazikika, moti analemberatu pa kalendala yake madeti odzayambira zimenezi. Atachita upainiya kwa kanthaŵi, kutumikira pa ofesi ya nthambi sanakuone ngati cholinga chosatheka.

Nafenso tingachite bwino kugaŵa zolinga zathu zikuluzikulu kuti zikhale zolinga zingapo zing’onozing’ono. Zolinga zing’onozing’onozo zingatithandize kuona pamene tafika pa ulendo wathu wofuna kukwaniritsa cholinga chathu chachikulucho. Kuyang’ana m’mbuyo kaŵirikaŵiri kuti tione pamene tafika nazo zolingazi kungatithandize kuti tisasokonezeke pa zolinga zathuzo. Kupemphera kwa Yehova kaŵirikaŵiri n’kumamuuza zolinga zathuzo kungatithandizenso kuti tisasokonezeke. Mtumwi Paulo analimbikitsa kuti: “Pempherani kosaleka.”​—1 Atesalonika 5:17.

M’pofunika Khama Ndiponso Kuikirapo Mtima

Ngakhale titaganizira bwinobwino zonse zofunika n’kukhala wofunitsitsa kuzikwaniritsa, pali zolinga zina zimene sitingathebe kuzikwaniritsa. Wophunzira wotchedwa Yohane Marko ayenera kuti anakhumudwa kwambiri pamene mtumwi Paulo anakana kum’tenga pa ulendo wake wachiŵiri waumishonale. (Machitidwe 15:37-40) Marko anayenera kuphunzirapo kanthu pa kukhumudwitsidwa kumeneku ndipo anayenera kusintha zolinga zake zokhudza njira zinanso zotumikirira Mulungu. Zikuoneka kuti iye anaterodi. Pambuyo pake, Paulo ananena zinthu zabwino zokhudza Marko ndipo Marko anakakhala ndi mtumwi Petro mogwirizana kwambiri ku Babulo. (2 Timoteo 4:11; 1 Petro 5:13) Mwina mwayi wake waukulu kwambiri unali wolemba buku louziridwa lonena za moyo ndiponso utumiki wa Yesu.

Tikamakhala ndi zolinga zauzimu, nafenso tingathe kukumana ndi mikwingwirima. M’malo mongolekera panjira, tiyenera kuona kuti tafika pati, kuona ngati zolingazo tingazikwanitsebe ndiponso tiyenera kusintha ngati pakufunika kutero. Tikakumana ndi mikwingwirima tiyenera kuyesetsa kuti tisafooke ngakhale pang’ono. Mfumu yanzeru Solomo ikutilimbikitsa kuti: “Pereka zochita zako kwa Yehova, ndipo zolingalira zako zidzakhazikika.”​—Miyambo 16:3.

Komano, nthaŵi zina zimakhala zovuta kukwaniritsa zolinga zinazake. Mwachitsanzo ngati sitili bwino m’thupi, kapena ngati tili ndi maudindo enaake m’banja mwathu, zolinga zinazake sitingathe kuzikwaniritsa. Komabe tisaiŵale kuti mphotho yathu yaikulu kwambiri ndiyo moyo wosatha, kaya n’kumwamba kapena m’Paradaiso padziko lapansi. (Luka 23:43; Afilipi 3:13, 14) Kodi tingaipeze motani mphothoyi? Mtumwi Yohane analemba kuti: “Iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.” (1 Yohane 2:17) Motero, ngakhale titalephera kukwaniritsa cholinga chinachake chifukwa cha mmene zinthu zilili m’moyo wathu, tingathebe ‘kuopa Mulungu, ndi kusunga malamulo ake.’ (Mlaliki 12:13) Zolinga zauzimu zimatithandiza kuganizira kwambiri zomachita chifuniro cha Mulungu. Motero tiyeni tikhale ndi zolinga zauzimu kuti tilemekeze Mlengi wathu.

[Bokosi patsamba 22]

Zolinga Zauzimu Zimene Tingaziganizire

○ Kuŵerenga Baibulo tsiku lililonse

○ Kuŵerenga magazini iliyonse ya Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!

○ Kusintha mapemphero athu kuti azikhala abwino kwambiri

○ Kusonyeza chipatso cha mzimu

○ Kulimbikira kuti tipeze njira zinanso zotumikirira ena

○ Kukhala aluso kwambiri polalikira ndiponso pophunzitsa

○ Kuphunzira maluso ena monga ulaliki wa patelefoni, wamwamwayi, ndiponso wa m’malo antchito