Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Khalani na Zolinga Zauzimu Kuti Mulemekeze Mlengi Wanu

Khalani na Zolinga Zauzimu Kuti Mulemekeze Mlengi Wanu

Khalani na Zolinga Zauzimu Kuti Mulemekeze Mlengi Wanu

“MUNTHU amene sakudziŵa doko limene akupitako, alibe nazo nchito zakuti mphepo ikuloŵela kuti panyanjapo.” Mawu amenewa, omwe amati ananenedwa na munthu wina wanzelu wa ku Roma wa m’zaka za m’ma 100 C.E., amasonyeza kuti n’zoonadi kuti munthu ayenela kukhala na zolinga kuti adziŵe komwe akuloŵela na moyo wake.

M’Baibo muli zitsanzo za anthu amene anali na zolinga. Kwa zaka pafupifupi 50, Nowa anacita khama ‘pokhoma cingalawa copulumukilamo iye na a m’nyumba yake.’ Mneneli Mose “anapenyelela cobwezela ca mphotho.” (Ahebri 11:7, 26) Yoswa, yemwe analowa m’malo mwa Mose, anakwanilitsa colinga cimene Mulungu anam’patsa cakuti alande dziko la Kanani.—Deuteronomo 3:21, 22, 28; Yoswa 12:7-24.

M’zaka za m’ma 100 Kristu Atabwela, n’zosakayikitsa kuti mtumwi Paulo anakhala na zolinga zake zauzimu cifukwa colimbikitsidwa na mawu a Yesu akuti “uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi.” (Mateyu 24:14) Polimbikitsidwa na mauthenga ndiponso masomphenya ocokela kwa Ambuye Yesu, kuphatikizaponso nchito imene anam’patsa ya ‘kunyamula dzina la [Yesu] pamaso pa amitundu,’ Paulo anathandiza kwabasi pokhazikitsa mipingo yacikristu yambili-mbili ku Asiyamina konse mpaka kukafika ku Ulaya.—Machitidwe 9:15; Akolose 1:23.

Inde, m’mbuyo monsemu atumiki a Yehova akhala na zolinga zabwino kwambili ndipo azikwanilitsa, n’kulemekeza nazo Mulungu. Kodi masiku ano tingapange bwanji zolinga zauzimu? Kodi ni zolinga zotani zimene tingakhale nazo, ndipo kodi tingacite ciani kuti tizikwanilitsedi?

M’pofunika Kukhala na Zolinga Zabwino

Munthu angakhale na zolinga zosiyana-siyana m’moyo wake, ndipo padziko pano pali anthu omwe amakonda kudziikila zolinga zosiyana-siyana. Komabe zolinga zokhudza kutumikila Mulungu n’zosiyana na zolinga wamba. Anthu ambili padziko pano amakhala na zolinga zinazake poganizila kwambili za cuma kapena pofunitsitsa maudindo ndiponso mphamvu. Komatu kukhala na colinga cinacake poganizila zofuna mphamvu kapena kuchuka n’kulakwitsa kwabasi! Zolinga zimene tingalemekeze nazo Yehova Mulungu zimakhala zokhudza kumulambila iyeyo ndiponso kucita zinthu zothandiza pa nchito ya Ufumu. (Mateyu 6:33) Timakhala n’zolinga zotele cifukwa cokonda Mulungu ndiponso anansi athu ndipo potelo timaganizila kwambili za kudzipeleka kwathu kwa Mulungu.—Mateyu 22:37-39; 1 Timoteo 4:7.

Maganizo athu azikhala oyenelela tikamapanga ndiponso kuyesetsa kukwanilitsa zolinga zauzimu, kaya n’zokhudza kupeza mwayi wotumikila Mulungu m’njila zinanso kapena kukula mwauzimu. Komatu, nthawi zina kukwanilitsa zolinga zinazake sikutheka ngakhale maganizo athu atakhala oyenela. Kodi tingapange bwanji zolinga na kuzikwanilitsa mosavuta?

Tikhale na Mtima Wofunitsitsa Kukwanilitsa Zolinga Zathu

Taganizilani mmene Yehova anakwanilitsila nchito yolenga cilengedwe. Ponena kuti “panali madzulo ndipo panali m’mawa,” Yehova anasonyeza kuti anagawa-gawa nyengo iliyonse yolengela zinthu. (Genesis 1:5, 8, 13, 19, 23, 31) Paciyambi pa nyengo iliyonse yolengela zinthuzo, iye anali kudziŵa bwino-bwino colinga cake, kapena kuti cimene anali kufuna kukwanilitsa pa nyengo imeneyo. Ndipo Mulungu anakwanilitsa colinga cake coti alenge zinthu. (Chivumbulutso 4:11) Kholo lakale Yobu, anati cimene ‘moyo wa [Yehova] ucifuna acicita.’ (Yobu 23:13) Yehova ayenela kuti anakondwela kwambili kuona “zonse zimene adazipanga,” ndipo ananena kuti “zinali zabwino ndithu”!—Genesis 1:31.

Kuti tikwanilitsedi zolinga zathu, nafenso tiyenela kukhala ofunitsitsa kuzikwanilitsa. Kodi n’ciani cingatithandize kuti tikhale ofunitsitsa motelo? Ngakhale pamene dziko lapansi linali lopanda kanthu, Yehova anali kutha kuona mmene lidzakhalile akakwanilitsa colinga cake; anali kuona kuti lidzakhala ngati mwala wokongola wamtengo wapatali m’mlengalengamu, ndipo lidzacititsa kuti iye alandile ulemelelo ndiponso alemekezedwe. Cimodzi-modzinso ifeyo, tingakhale ofunitsitsa kukwanilitsa zolinga zathu poganizila bwino za mmene tidzapindulile tikakwanilitsa colinga cathuco. Izi n’zimene zinam’citikila Tony, yemwe ali na zaka 19. Iye sanaiwale mmene anamvela nthawi yoyamba imene anakaona ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova m’dziko lina la ku madzulo a ku Ulaya. Kucokela panthawiyi, funso limene Tony anali kungoliganizila linali lakuti, ‘Kodi ningamve bwanji nitamakhala ndiponso kutumikila pamalo amene aja?’ Tony anapitilizabe kuganizila zodzacita zimenezi, ndipo sanasiye kuyesa-yesa kukwanilitsa colinga cakeci. Patatha zaka zingapo iye anasangalala kwambili pamene anamuvomela kukatumikila pa nthambipo!

Kuceza na anthu amene anakwanilitsa kale colinga cinacake kungatilimbikitsenso kuti nafe ticikwanilitse. Jayson, yemwe ali na zaka 30, sanali kukonda kucita utumiki wa kumunda akali m’nyamata wongopitilila pa zaka 13. Koma atamaliza sukulu ya sekondale, iye anayamba kucita utumiki waupainiya na mtima wonse, motelo anakhala wolengeza Ufumu wa nthawi zonse. Kodi n’ciani cinam’thandiza Jayson kukhala wofunitsitsa kucita upainiya? Iye anayankha kuti: “Ninalimbikitsidwa kwambili cifukwa colankhulana na anthu ena amene anacitapo upainiya ndiponso cifukwa coyenda nawo mu utumiki.”

Kulemba Zolinga Zathuzo Kumathandiza

Zimene timangoziganizila zimatsatilika bwino tikazilongosola m’mawu omveka bwino. Solomo anati mawu oyenelela angathe kukhala amphamvu ngati zisonga kapena zikwapu zolishila ng’ombe za pagoli cifukwa angatithandize kudziŵa koloŵela m’moyo wathu. (Mlaliki 12:11) Mawuwo tikacita kuwalemba, amatilimbikitsa ndiponso amatikhudza kwambili. N’cifukwa cake Yehova anauza mafumu a Israyeli kuti azidzilembela okha Cilamulo conse pamanja. (Deuteronomo 17:18) Motelo tingacite bwino kulemba zolinga zathu ndiponso mmene tikufuna kuzikwanilitsila. Cinanso cingatithandize ndico kuzindikila zimene tiyenela kudziŵa bwino, maluso amene tiyenela kuphunzila, ndiponso anthu amene angatithandize.

Cifukwa cokhala na zolinga zauzimu Geoffrey anathandizika kwambili kukhazika mtima wake m’malo. Iyeyu wakhala mpainiya wapadela kwa nthawi yaitali m’gawo lakutali la m’dziko lina ku Asia. Zinthu zinam’tembenukila mkazi wake atamwalila mwadzidzidzi. Atatha kulila malilowo, Geoffrey anaganiza zopanga zolinga zinazake kuti moyo wake wonse ukhale pautumiki wa upainiya. Iye analemba coyamba zolinga zakezo ndipo mothandizidwa na mapemphelo anayesetsa kukwanilitsa colinga coti ayambitse maphunzilo atatu a Baibo mweziwo usanathe. Tsiku lililonse likatha anali kuona bwino-bwino zimene wacita patsikulo, ndipo pa masiku khumi alionse, anali kuyang’ana m’mbuyo n’kuona mmene wacitila. Kodi anakwanilitsa colinga cake? Inde, cifukwa panopa ali na maphunzilo anayi a Baibo!

Khalani na Zolinga Zing’ono-zing’ono Kuti Mudziŵe Pamene Mwafika

Zolinga zina poyamba zimaoneka ngati zosatheka kuzikwanilitsa. Kwa Tony, amene tam’chula kale uja, zotumikila pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova zinali kungooneka ngati maloto basi. Zinali conco cifukwa cakuti anali kukhala moyo woloŵelela, ndipo anali asanadzipatulile n’komwe kwa Mulungu. Koma Tony anaganiza zoti moyo wake ukhale wogwilizana na njila za Yehova ndipo anakhala na colinga coti adzabatizike. Atakwanilitsa colinga cimeneco, iye anakhala na colinga cocita upainiya wothandiza ndipo kenaka wokhazikika, moti analembelatu pa kalendala yake madeti odzayambila zimenezi. Atacita upainiya kwa kanthawi, kutumikila pa ofesi ya nthambi sanakuone ngati colinga cosatheka.

Nafenso tingacite bwino kugawa zolinga zathu zikulu-zikulu kuti zikhale zolinga zingapo zing’ono-zing’ono. Zolinga zing’ono-zing’onozo zingatithandize kuona pamene tafika pa ulendo wathu wofuna kukwanilitsa colinga cathu cacikuluco. Kuyang’ana m’mbuyo kaŵili-kaŵili kuti tione pamene tafika nazo zolingazi kungatithandize kuti tisasokonezeke pa zolinga zathuzo. Kupemphela kwa Yehova kaŵili-kaŵili n’kumamuuza zolinga zathuzo kungatithandizenso kuti tisasokonezeke. Mtumwi Paulo analimbikitsa kuti: “Pemphelani kosaleka.”—1 Atesalonika 5:17.

M’pofunika Khama Ndiponso Kuikilapo Mtima

Ngakhale titaganizila bwino-bwino zonse zofunika n’kukhala wofunitsitsa kuzikwanilitsa, pali zolinga zina zimene sitingathebe kuzikwanilitsa. Wophunzila wochedwa Yohane Marko ayenela kuti anakhumudwa kwambili pamene mtumwi Paulo anakana kum’tenga pa ulendo wake waciŵili waumishonale. (Machitidwe 15:37-40) Marko anayenela kuphunzilapo kanthu pa kukhumudwitsidwa kumeneku ndipo anayenela kusintha zolinga zake zokhudza njila zinanso zotumikilila Mulungu. Zikuoneka kuti iye anatelodi. Pambuyo pake, Paulo ananena zinthu zabwino zokhudza Marko ndipo Marko anakakhala na mtumwi Petro mogwilizana kwambili ku Babulo. (2 Timoteo 4:11; 1 Petro 5:13) Mwina mwayi wake waukulu kwambili unali wolemba buku louzilidwa lonena za moyo ndiponso utumiki wa Yesu.

Tikamakhala na zolinga zauzimu, nafenso tingathe kukumana na mikwingwilima. M’malo mongolekela panjila, tiyenela kuona kuti tafika pati, kuona ngati zolingazo tingazikwanitsebe ndiponso tiyenela kusintha ngati pakufunika kutelo. Tikakumana na mikwingwilima tiyenela kuyesetsa kuti tisafooke ngakhale pang’ono. Mfumu yanzelu Solomo ikutilimbikitsa kuti: “Peleka zocita zako kwa Yehova, ndipo zolingalila zako zidzakhazikika.”—Miyambo 16:3.

Komabe, nthawi zina zimakhala zovuta kukwanilitsa zolinga zinazake. Mwacitsanzo ngati sitili bwino m’thupi, kapena ngati tili na maudindo enaake m’banja mwathu, zolinga zinazake sitingathe kuzikwanilitsa. Komabe tisaiwale kuti mphotho yathu yaikulu kwambili ndiyo moyo wosatha, kaya n’kumwamba kapena m’Paradaiso padziko lapansi. (Luka 23:43; Afilipi 3:13, 14) Kodi tingaipeze motani mphothoyi? Mtumwi Yohane analemba kuti: “Iye amene acita cifunilo ca Mulungu akhala ku nthawi zonse.” (1 Yohane 2:17) Motelo, ngakhale titalephela kukwanilitsa colinga cinacake cifukwa ca mmene zinthu zilili m’moyo wathu, tingathebe ‘kuopa Mulungu, na kusunga malamulo ake.’ (Mlaliki 12:13) Zolinga zauzimu zimatithandiza kuganizila kwambili zomacita cifunilo ca Mulungu. Motelo tiyeni tikhale na zolinga zauzimu kuti tilemekeze Mlengi wathu.

[Bokosi]

Zolinga Zauzimu Zimene Tingaziganizile

○ Kuŵelenga Baibo tsiku lililonse

○ Kuŵelenga magazini iliyonse ya Nsanja ya M’londa na Galamuka!

○ Kusintha mapemphelo athu kuti azikhala abwino kwambili

○ Kusonyeza makhalidwe a cipatso ca mzimu

○ Kulimbikila kuti tipeze njila zinanso zotumikilila ena

○ Kukhala aluso kwambili polalikila ndiponso pophunzitsa

○ Kuphunzila maluso ena monga ulaliki wa patelefoni, wamwamwayi, ndiponso wa m’malo anchito