Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi Chaka Choliza Lipenga chotchulidwa m’chaputala 25 cha buku la Levitiko chimasonyeza zinthu zotani za m’tsogolo?

Chilamulo cha Mose chinanena kuti “chaka chachisanu ndi chiŵiri chikhale sabata lakupumula la dziko.” Ponena za chaka chimenechi, Aisrayeli analamulidwa kuti: “Usamabzala m’munda mwako, usamadzombola mipesa yako. Zophuka zokha zofikira masika usamazitchera, ndi mphesa za mipesa yako yosadzombola usazicheka; chikhale chaka chopumula dziko.” (Levitiko 25:4, 5) Motero chaka chachisanu ndi chiŵiri chilichonse chinali chaka cha Sabata la dziko. Ndipo chaka cha makumi asanu chilichonse, chomwe chinali kutsatira chaka cha Sabata chachisanu ndi chiŵiri, chinkakhala Chaka Choliza Lipenga. Kodi chaka chimenecho pankachitika zotani?

Yehova anauza Israyeli kudzera mwa Mose kuti: “Muchipatule chaka cha makumi asanu, ndi kulalikira kwa onse okhala m’dzikomo kuti akhale aufulu; muchiyese chaka choliza lipenga; ndipo mubwerere munthu aliyense ku zakezake, ndipo mubwerere yense ku banja lake. Muchiyese chaka cha makumi asanucho choliza lipenga, musamabzala, kapena kucheka zophuka zokha m’mwemo; kapena kucheka mphesa zake za mipesa yosadzombola.” (Levitiko 25:10, 11) Motero pa Chaka Choliza Lipenga dzikolo linkakhala ndi zaka za Sabata ziŵiri zotsatizana. Koma kwa anthu a m’dzikomo, chakachi chinkawapatsa ufulu. Ayuda onse omwe anali atagulitsidwa kukhala akapolo anali kumasulidwa. Katundu wa choloŵa amene mwina munthu anali atakakamizika kum’gulitsa anali kubwezedwa ku banja lake. Kwa Aisrayeli akale, Chaka Choliza Lipenga chinali chaka chobwezeretsa zinthu mwakale ndiponso chobweretsa ufulu. Kodi kwa Akristu chakachi chimaimira zinthu zotani?

Kupanduka kwa munthu woyambirira, Adamu, kunachititsa anthu kukhala akapolo a uchimo. Nsembe ya dipo ya Yesu Kristu ndiyo chinthu chimene Mulungu anakonza pofuna kumasula anthu ku ukapolo wa uchimo. * (Mateyu 20:28; Yohane 3:16; 1 Yohane 2:1, 2) Kodi ndi liti pamene Akristu amamasulidwa ku lamulo la uchimo? Polankhula ndi Akristu odzozedwa, mtumwi Paulo anati: “Chilamulo cha mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu chandimasula ine ku lamulo la uchimo ndi la imfa.” (Aroma 8:2) Anthu oyembekezera kukakhala ndi moyo kumwamba amalandira ufulu umenewu akadzozedwa ndi mzimu woyera. Ngakhale kuti matupi awo ndi anyama ndi mwazi ndiponso ndi opanda ungwiro, Mulungu amawaona kuti ndi olungama ndipo amawatenga kukhala ana ake auzimu. (Aroma 3:24; 8:16, 17) Kwa odzozedwa onse monga gulu limodzi, Chaka Choliza Lipenga chachikristu chinayamba pa Pentekoste m’chaka cha 33 Kristu Atabwera.

Nanga bwanji za “nkhosa zina,” zimene zikuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi? (Yohane 10:16) Kwa ankhosa zina, Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu udzakhala nthaŵi yobwezeretsa zinthu mwakale ndiponso yobweretsa ufulu. M’Chaka Choliza Lipenga cha Zaka 1,000 chimenechi, Yesu adzagwiritsira ntchito phindu la nsembe yake ya dipo kwa anthu okhulupirira ndipo adzathetsa zoipa zonse zobwera chifukwa cha uchimo. (Chivumbulutso 21:3, 4) Podzafika kumapeto kwa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu, anthu adzafika pokhala angwiro ndipo adzamasukiratu ku uchimo ndi imfa zomwe amabadwa nazo. (Aroma 8:21) Zimenezi zikadzachitika, Chaka Choliza Lipenga chachikristu chidzathera pomwepo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Kwenikweni Yesu anatumidwa ‘kudzalalikira kwa am’nsinga mamasulidwe.’ (Yesaya 61:1-7; Luka 4:16-21) Iye analalikira za kumasulidwa mu ukapolo wauzimu.

[Chithunzi patsamba 26]

Chaka Choliza Lipenga cha Zaka 1,000 chidzakhala nthaŵi yobwezeretsa zinthu mwakale ndiponso yomasula “nkhosa zina” ku ukapolo