Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukumbukira “Anthu Oiwalika Amene Anazunzidwa”

Kukumbukira “Anthu Oiwalika Amene Anazunzidwa”

Olengeza Ufumu Akusimba

Kukumbukira “Anthu Oiwalika Amene Anazunzidwa”

KUMAYAMBIRIRO kwa chaka cha 2001, Haykaz, mnyamata wa zaka 15 amene ali Mboni ya Yehova, anapita ku Bern, Switzerland, kukaona chionetsero chotchedwa “Anthu Oiwalika Amene Anazunzidwa” chokhudza mmene a Nazi anazunzira Mboni za Yehova. Pomaliza pa ulendo wakewo, Haykaz anati: “Ndinali nditamvapo za nkhanza ndi chizunzo chimene Mboni za Yehova zinakumana nazo mu ulamuliro wa Nazi, koma aka n’koyamba kuti ndione zikalata zenizeni ndi zithunzi zokhudza nthaŵi imeneyo. Zimene anasonyeza pachionetseropo, ndiponso zimene ananena anthu amene anaona zinthuzo zikuchitika maso ndi maso, komanso zimene ananena akatswiri a mbiri yakale pachionetserocho zinandikhudza mtima kwambiri.”

Patapita nthaŵi, pamene Haykaz anapatsidwa ntchito yoti alembere lipoti anthu a m’kalasi mwake kusekondale kwawo, anasankha kulemba nkhani yoti “Mboni za Yehova​—Anthu Oiwalika Amene Anazunzidwa pa Ulamuliro wa Nazi.” Aphunzitsi ake anamuvomera kuti alembe nkhaniyo, koma anamuuza kuti afunika kuphatikizapo mfundo zochokera m’mabuku olembedwa ndi anthu ena. Haykaz anavomera zimenezi. “Ndinalemba mwachidule mfundo zochokera m’mabuku amene ndinaŵerenga onena zimene zinachitikira Mboni za Yehova panthaŵi ya ulamuliro wa Nazi. Ndinafotokozanso zimene ndinaona ndekha pachionetsero cha ‘Anthu Oiwalika Amene Anazunzidwa’. Mu lipoti la masamba 43 limene ndinalembalo munalinso zithunzi.”

Mu November 2002, Haykaz anaonetsa lipoti lake kwa ana asukulu anzake, aphunzitsi, anthu a m’banja mwake, ndi anzake. Atamaliza, panali nthaŵi ya mafunso ndi mayankho, imene inamupatsa mpata wofotokoza zikhulupiriro zake zochokera m’Baibulo. Mtsikana wina amene anali nawo pamenepo atamufunsa chifukwa chimene anasankhira nkhani imeneyi, Haykaz anafotokoza kuti mabuku ambiri a mbiri yakale satchula Mboni za Yehova ndipo iye anafuna kuti anthu adziŵe kulimba mtima kumene Mbonizo zinasonyeza poikira kumbuyo chikhulupiriro chawo chachikristu. Kodi chinachitika n’chiyani atapereka lipoti lakelo?

Haykaz anati: “Ana asukulu anzanga anachita chidwi kwambiri. Iwo sankadziŵa kuti Mboni za Yehova zinazunzidwa kwambiri. Ndiponso ambiri sankadziŵa kuti Mboni zimene zinali m’misasa yachibalo ya Nazi zinkavala chizindikiro chofiirira cha makona atatu.”

Atamaliza kusonyeza lipoti lakelo, Haykaz anakhala ndi mipata ina yolankhula ndi anthu a m’kalasi mwake ndi kukambirana nawo zinthu zochokera m’Baibulo zimene Mboni zimakhulupirira zokhudza kuthiridwa magazi, kumwa moŵa, ndi makhalidwe abwino. Haykaz anati: “Palibe ana asukulu anzanga amene anandinyoza kapena kundiseka.” Kuwonjezera apo, lipoti lakelo tsopano akulisunga m’laibulale ya pasukulupo. Zimenezi zithandiza kuti kulimba mtima kwa Mboni za Yehova kusaiwalike.