Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Lankhulani Mawu a Mulungu Molimba Mtima

Lankhulani Mawu a Mulungu Molimba Mtima

Lankhulani Mawu a Mulungu Molimba Mtima

“Muka, nenera kwa anthu anga.”​—AMOSI 7:15.

1, 2. Kodi Amosi anali ndani, ndipo kodi Baibulo limatiuza chiyani za iye?

PA NTHAWI ina pamene mboni ina ya Yehova inali mu utumiki, inakumana ndi wansembe. Wansembeyo anakuwa kuti: ‘Siya kulalikira! Choka m’dera lino!’ Kodi mboniyo inachita chiyani? Kodi inamvera zimene inauzidwazo, kapena inapitirizabe kulalikira mawu a Mulungu molimba mtima? Mungadziwe zimene zinachitika chifukwa mboniyo inalemba zimene inakumana nazo m’buku limene limadziwika ndi dzina lake. Buku lake ndi buku la m’Baibulo la Amosi. Koma tisanamve zambiri zomwe zinachitika Amosi atakumana ndi wansembeyo, choyamba tiyeni tione zinthu zingapo zokhudza Amosi ndi moyo wake.

2 Kodi Amosi anali ndani? Kodi anakhalako liti ndipo kwawo kunali kuti? Tikupeza mayankho a mafunso amenewa pa Amosi 1:1, pamene timawerenga kuti: “Mawu a Amosi, amene anali mwa oweta ng’ombe a ku Tekoa, . . . masiku a Uziya mfumu ya Yuda, ndi masiku a Yerobiamu mwana wa Yoasi mfumu ya Israyeli.” Kwawo kwa Amosi kunali ku Yuda. Tawuni ya kwawo inali Tekoa, yomwe inali pa mtunda wa makilomita 16 kum’mwera kwa Yerusalemu. Iye anakhalako cha kumapeto kwa zaka za m’ma 800 Yesu Asanabwere, panthawi imene Mfumu Uziya inali kulamulira Yuda ndiponso pamene Mfumu Yerobiamu yachiwiri inali mfumu ya ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi. Amosi anali woweta ng’ombe. Ndipo lemba la Amosi 7:14 limati Amosi sanali “woweta ng’ombe” chabe komanso anali ‘wotchera nkhuyu.’ Choncho nthawi zina pachaka anali kugwiranso ntchito yokhudzana ndi kukolola. Ankatchera, kapena kuti kubaya nkhuyuzo. Anali kuchita zimenezi ndi cholinga choti zipse msanga. Inali ntchito yotopetsa kwambiri.

“Muka, Nenera”

3. Kodi kuphunzira za Amosi kungatithandize bwanji ngati tikuona kuti siife oyenerera kulalikira?

3 Amosi ananena mosabisa kuti: “Sindinali mneneri, kapena mwana wa mneneri.” (Amosi 7:14) Iye sanali mwana wa mneneri ndiponso sanaphunzitsidwe ntchito ya uneneri. Koma mwa anthu onse a m’Yuda, Yehova anasankha Amosi kuti achite ntchito Yake. Panthawi imeneyo, Mulungu sanasankhe mfumu yamphamvu, wansembe wophunzira, kapena kalonga wolemera. Pamenepa tikupezapo phunziro lolimbikitsa kwambiri kwa ife. Mwina tingakhale ndi udindo wochepa kapenanso kukhala ndi maphuziro otsika zedi. Koma kodi tiyenera kuganiza kuti ndife osayenerera kulalikira mawu a Mulungu chifukwa cha zimenezi? Kutalitali! Yehova angatithandize kukhala okonzeka kulalikira uthenga wake, ngakhale m’gawo lovuta. Popeza Yehova anathandiza Amosi kuchita zimenezi, zingakhale zothandiza ngati anthu onse amene akufuna kulankhula mawu a Mulungu molimba mtima angaganizire bwinobwino chitsanzo cha mneneri wolimba mtima ameneyu.

4. N’chifukwa chiyani zinali zovuta kuti Amosi alosere mu Israyeli?

4 Yehova anauza Amosi kuti: “Muka nenera kwa anthu anga Israyeli.” (Amosi 7:15) Ntchito imeneyo inali yovuta. Panthawi imeneyo, ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi unali pamtendere, unali wotetezeka, ndiponso unali wolemera. Anthu ambiri anali ndi ‘nyumba za nyengo yachisanu’ komanso ‘nyumba za nyengo yadzuwa,’ zomwe sizinamangidwe ndi njerwa za dothi, koma ndi “miyala yosema” ya mtengo wapatali. Ena anali ndi katundu wa m’nyumba wokongola wopangidwa ndi minyanga, ndiponso anali kumwa vinyo wa ‘m’minda ya mpesa yabwino.’ (Amosi 3:15; 5:11) Chifukwa cha zimenezi, anthu ambiri analibe naye chidwi mneneri ameneyu. Zoonadi, gawo limene Amosi anali nalo likuoneka kuti linali lofanana ndi magawo amene ambiri a ife timalalikiramo masiku ano.

5. Kodi ndi zinthu zopanda chilungamo zotani zimene Aisrayeli ena anali kuchita?

5 Sikuti zinali zolakwika kuti Aisrayeliwo akhale ndi chuma. Koma Aisrayeli ena anapeza chumacho pochita katangale. Anthu olemera anali ‘kusautsa aumphawi’ ndiponso ‘kupsinja osowa.’ (Amosi 4:1) Amalonda otchuka, oweruza, ndi ansembe ankachita kupangana kuti alande osauka. Tsopano tatiyeni tibwerere m’mbuyo pang’ono kuti tione zimene anthu amenewa anali kuchita.

Kuphwanya Chilamulo cha Mulungu

6. Kodi Aisrayeli amalonda anadyera masuku pamutu anzawo motani?

6 Choyamba tipita ku msika. Kumeneko amalonda anali “kuchepsa efa” ndi “kukulitsa sekeli,” ngakhale kugulitsa “nsadwa” m’malo mwa tirigu. (Amosi 8:5, 6) Amalondawo ankabera makasitomala awo powapatsa katundu wosakwanira mlingo wake, kuwagulitsa pamtengo wokwera kwambiri, ndiponso kuwagulitsa katundu wowonongeka. Ndiyeno, pambuyo poti amalondawo anadyera masuku pamutu osaukawo mpaka anafika pokhaliratu osowa pogwira, osaukawo sakanachitira mwina koma kudzigulitsa ngati akapolo. Kenaka, amalondawo anagula osaukawo “ndi nsapato.” (Amosi 8:6) Tangoganizani zimenezo! Amalonda adyerawo ankaona kuti Aisrayeli anzawo mtengo wawo unali wofanana ndi mtengo wa nsapato! Kumenekotu kunali kunyoza kwambiri anthu aumphawiwo, ndiponso kuphwanyiratu Chilamulo cha Mulungu! Koma amalonda omwewo ankasunga “sabata.” (Amosi 8:5) Inde, anali anthu opembedza koma mwachiphamaso chabe.

7. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti Aisrayeli amalonda aziphwanya Chilamulo cha Mulungu?

7 Kodi zinatheka bwanji kuti amalonda amenewa asalangidwe chifukwa choswa Chilamulo cha Mulungu, chimene chimanena kuti: “Uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha”? (Levitiko 19:18) Zimenezo zinatheka chifukwa chakuti oweruza, amene anayenera kusungitsa Chilamulocho, ankachita nawo zomwezo. Pachipata cha mzinda, kumene milandu inkakambidwa, oweruza anali ‘kulandira chokometsera mlandu, kukankha osowa kuchipata.’ M’malo mothandiza osauka, oweruzawo anawaipitsira mlandu wawo atapatsidwa ziphuphu. (Amosi 5:10, 12) Choncho oweruzawonso anali kunyalanyaza Chilamulo cha Mulungu.

8. Kodi ansembe oipa anali kulekerera khalidwe lotani?

8 Nanga kodi ansembe m’Israyeli anali kuchita chiyani panthawi imeneyi? Kuti tidziwe zimene anali kuchita, tiyeni tipite kumalo ena. Taonani machimo amene ansembewo analoleza “m’nyumba ya Mulungu wawo”! Kudzera mwa Amosi, Mulungu anati: “Munthu ndi atate wake amuka kwa namwali yemweyo, kuti aipse dzina langa loyera.” (Amosi 2:7, 8) Tangoganizani zimene anthuwo anali kuchita! Atate achiisrayeli ndi mwana wawo anali kuchita chiwerewere ndi mkazi mmodzi wachigololo wokhala pa kachisi. Ndipo ansembe oipa amenewo anali kulekerera chiwerewere choterocho!​—Levitiko 19:29; Deuteronomo 5:18; 23:17.

9, 10. Kodi Aisrayeli anaphwanya malamulo ati opezeka m’Chilamulo cha Mulungu, ndipo kodi masiku ano pali zinthu zotani zofanana ndi zimenezi?

9 Pofotokoza khalidwe lina loipa, Yehova anati: “Nagona pansi pa zofunda za chikole ku maguwa a nsembe alionse, ndi m’nyumba ya Mulungu wawo akumwa vinyo wa iwo olipitsidwa.” (Amosi 2:8) Inde, ansembe ndi anthuwo anaswa lamulo la pa Eksodo 22:26, 27, lakuti chovala chotengedwa ngati chikole chiyenera kubwezedwa dzuwa lisanalowe. M’malo mwake anagwiritsa ntchito chofundacho ngati pogonapo akamadyerera ndi kumwa polambira milungu yonyenga pakachisi. Ndipo ndalama zimene ankabera anthu osauka zija, ankagulira vinyo kuti azimwa pa madyerero opembedza milungu yonyenga. Anatalikiranadi zedi ndi kulambira koyera!

10 Aisrayeli anaswa mopanda manyazi malamulo awiri aakulu kwambiri a Chilamulo, lakuti uzikonda Yehova ndiponso lakuti uzikonda munthu mnzako. Ndicho chifukwa chake Mulungu anatuma Amosi kuti akawadzudzule chifukwa cha kusakhulupirika kwawoko. Masiku ano mayiko a gawo la Matchalitchi Achikristu ndi ena onse aipa mofanana ndi Israyeli wakale. Ngakhale kuti anthu ena akulemera, ena ambiri akungosaukirasaukirabe ndiponso amapwetekedwa kwambiri mumtima chifukwa cha khalidwe loipa la atsogoleri osaona mtima m’zamalonda, ndale, ndiponso m’chipembedzo chonyenga. Komabe, Yehova amadera nkhawa anthu amene akuvutika ndi amene akum’funafuna. Choncho, wapatsa atumiki ake amakono ntchito yofanana ndi ya Amosi yoti agwire, yolalikira mawu Ake molimba mtima.

11. Kodi chitsanzo cha Amosi chikutiphunzitsa chiyani?

11 Chifukwa chakuti ntchito ya Amosi ndi yathu n’njofanana, timapindula kwambiri mwa kupenda chitsanzo chake. Zoonadi, Amosi akutisonyeza (1) uthenga umene tiyenera kulalikira, (2) mmene tiyenera kuulalikirira, ndiponso (3) chifukwa chake otsutsa sangaimitse ntchito yathu yolalikira. Tiyeni tipende mfundo zimenezi imodziimodzi.

Mmene Tingatsanzirire Amosi

12, 13. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti sanali kukondwera nawo Aisrayeli, ndipo kodi iwo anachitapo chiyani?

12 Monga Mboni za Yehova, utumiki wathu wachikristu wagona pa ntchito yolalikira za Ufumu ndi kupanga ophunzira. (Mateyu 28:19, 20; Marko 13:10) Komabe, timalalikiranso za machenjezo a Mulungu, monga mmene Amosi ananenera kuti Yehova adzaweruza ndi kulanga oipa. Mwachitsanzo, lemba la Amosi 4:6-11 likusonyeza kuti Yehova anachenjeza Aisrayeli mobwerezabwereza powauza kuti sanali kum’kondweretsa. Iye anapatsa anthu “kusowa mkate,” ‘anawamana mvula,’ anawakantha ndi “chinsikwi ndi chinoni,” ndiponso anawatumizira “mliri.” Kodi zinthu zimenezi zinapangitsa Israyeli kusintha? “Simunabwerera kudza kwa Ine,” anatero Mulungu. Indedi, Aisrayeli anakana Yehova mobwerezabwereza.

13 Yehova analanga Aisrayeli osalapawo. Koma choyamba iwo analandira machenjezo kudzera m’maulosi. Mogwirizana ndi zimenezi, Mulungu anati: “Ambuye Yehova sadzachita kanthu osaulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.” (Amosi 3:7) Mulungu anaululira Nowa kuti kudzabwera Chigumula, ndipo anamuuza kuti achenjeze anthu. Mofanana ndi zimenezo, Yehova anauza Amosi kuti apereke chenjezo lomaliza. Zomvetsa chisoni n’zakuti Israyeli ananyalanyaza uthenga wa Mulungu umenewo ndipo sanachite zimene zinali kufunika.

14. Kodi pali kufanana kotani pakati pa nthawi ya Amosi ndi nthawi yathu ino?

14 Mosakayika inu mukuvomereza kuti pali mbali zina zofanana kwambiri pakati pa nthawi ya Amosi ndi nthawi yathu. Yesu Kristu ananeneratu za masoka ambiri odzachitika m’nthawi ya mapeto. Ananenanso za ntchito yolalikira ya padziko lonse. (Mateyu 24:3-14) Koma monga zinalili mu nthawi ya Amosi, anthu ambiri masiku ano akunyalanyaza chizindikiro cha nthawi ino ndi uthenga wa Ufumu. Zomwe zidzachitikire anthu amenewa n’zofanana ndi zomwe Aisrayeli osalapa aja anakumana nazo. Yehova anawachenjeza kuti: ‘Konzekera kukumana ndi Mulugu wako.’ (Amosi 4:12) Aisrayeli anakumana ndi Mulungu pamene anawaweruza ndi kuwalanga nthawi imene asilikali a Asuri anawagonjetsa. Masiku ano, dziko losaopa Mulunguli ‘lidzakumana ndi Mulungu’ pa Armagedo. (Chivumbulutso 16:14, 16) Koma pakadali pano, pamene kuleza mtima kwa Yehova kukupitirirabe, tikulimbikitsa anthu ambiri kuti: “Funani Yehova, ndipo mudzakhala ndi moyo.”​—Amosi 5:6.

Kutsutsidwa Ngati Amosi

15-17. (a) Kodi Amaziya anali ndani, ndipo kodi anachita chiyani atamva zimene Amosi anali kunena? (b) Kodi Amaziya anamuimba Amosi milandu yotani?

15 Tingatsanzire Amosi osati potengera uthenga umene tiyenera kulalikira wokha, komanso mmene tiyenera kulalikirira. Mfundo imeneyi yafotokozedwa m’chaputala 7, pamene tikumva za wansembe amene watchulidwa pachiyambi cha nkhani yathuyi. Wansembeyo anali “Amaziya wansembe wa ku Beteli.” (Amosi 7:10) Mzinda wa Beteli unali likulu la chipembedzo champatuko cha Aisrayeli, kumene ankalambira mwana wa ng’ombe. Motero Amaziya anali wansembe wa chipembedzo cha bomalo. Kodi iye anachita chiyani pamene Amosi anapereka machenjezo molimba mtima?

16 Amaziya anauza Amosi kuti: “Mlauli iwe, choka, thawira ku dziko la Yuda, nudye, nunenere komweko; koma usaneneranso ku Beteli; pakuti pamenepo m’pamalo opatulika a mfumu, ndiyo nyumba yachifumu.” (Amosi 7:12, 13) Kwenikweni Amaziya anati: ‘Bwerera kwanu! Ife tili ndi chipembedzo chathu kuno.’ Anayesanso kuuza boma kuti liletse ntchito ya Amosi, ndipo anauza Mfumu Yerobiamu yachiwiri kuti: “Amosi wapangira inu chiwembu pakati pa nyumba ya Israyeli.” (Amosi 7:10) Indedi, Amaziya anaimba Amosi mlandu woukira boma! Iye anauza mfumuyo kuti: “Atero Amosi, Yerobiamu adzafa ndi lupanga, ndi Israyeli adzatengedwadi ndende, kuchoka m’dziko lake.”​—Amosi 7:11.

17 M’mawu amenewa, Amaziya ananena zinthu zitatu zimene sizinali zoona kwenikweni. Iye anati: “Atero Amosi.” Koma Amosi sananenepo n’kamodzi komwe kuti ulosi umenewo unachokera kwa iye. M’malo mwake, iye nthawi zonse anali kunena kuti: “Atero Yehova.” (Amosi 1:3) Amosi anaimbidwanso mlandu wonena kuti: “Yerobiamu adzafa ndi lupanga.” Koma tikaona Amosi 7:9, tiona kuti Amosi analosera kuti: “[Ine Yehova] ndidzaukira nyumba ya Yerobiamu ndi lupanga.” Mulungu ananeneratu kuti tsoka loterolo lidzagwera “nyumba” ya Yerobiamu, kapena kuti mbadwa zake. Ndiponso, Amaziya ananenanso kuti Amosi ananena kuti: “Israyeli adzatengedwadi ndende.” Koma Amosi anali ataloseranso kuti Mwisrayeli aliyense wobwerera kwa Mulungu adzalandira madalitso. N’zoonekeratu kuti Amaziya anagwiritsa ntchito mfundo zomveka ngati zoona koma zili zopotoka n’cholinga choti boma liletse ntchito yolalikira ya Amosi.

18. Kodi pali kufanana kotani pakati pa njira zimene Amaziya anagwiritsa ntchito ndi zimene atsogoleri achipembedzo amagwiritsa ntchito masiku ano?

18 Kodi mwaona kufanana kwa njira zimene Amaziya anagwiritsa ntchito ndi njira zimene otsutsa anthu a Yehova amagwiritsa ntchito masiku ano? Mofanana ndi mmene Amaziya anayesera kuletsa ntchito ya Amosi, masiku anonso ansembe, mabishopu, ndi abambo achipembedzo amayesetsa kuletsa ntchito yolalikira ya atumiki a Yehova. Amaziya anaimba Amosi mlandu wabodza wakuti anali kufuna kuukira boma. N’zomwenso atsogoleri achipembedzo ena amachita masiku ano ponamizira Mboni za Yehova kuti zimasokoneza chitetezo cha dziko. Ndiponso mofanana ndi zimene Amaziya anachita popita kwa mfumu kuti imuthandize kulimbana ndi Amosi, atsogoleri achipembedzo masiku ano amagwirizananso ndi andale kuti awathandize kuzunza Mboni za Yehova.

Otsutsa Sangaimitse Ntchito Yathu Yolalikira

19, 20. Kodi Amosi anachita chiyani atatsutsidwa ndi Amaziya?

19 Kodi Amosi anachita chiyani Amaziya atamutsutsa? Choyamba, Amosi anafunsa wansembeyo kuti: “Iwe ukuti, Usamanenera chotsutsana ndi Israyeli”? Ndiyeno mosazengereza, mneneri wolimba mtima wa Mulunguyo analankhula mawu amene Amaziya sanafune kuwamva m’pang’ono pomwe. (Amosi 7:16, 17) Amosi sanaope. Chimenechi n’chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife. Pa nkhani yolankhula mawu a Mulungu, ifenso tidzamvera Mulungu wathu ndipo sitidzagonja ngakhale m’mayiko amene anthu ofanana ndi Amaziya akulimbikitsa chizunzo chankhanza. Monga Amosi timanenabe kuti: “Atero Yehova.” Ndipo otsutsa sangaimitse ntchito yathu, chifukwa “dzanja la [Yehova]” lili nafe.​—Machitidwe 11:19-21.

20 Ndithudi, Amaziya anayenera kudziwa kuti mawu ake oopseza sadzaphula kanthu. Amosi anali atafotokozeratu chifukwa chake padziko lapansi sipakanapezeka ngakhale munthu mmodzi wom’letsa kulankhula, ndipo imeneyi ndiyo mfundo yathu yachitatu imene tipende. Malinga ndi Amosi 3:3-8, Amosi anagwiritsa ntchito mafunso ndi mafanizo kusonyeza kuti palibe chinthu chimene chimayamba chokha. Kenako anasonyeza mfundo ya zomwe anali kunenazo. Anati: “Mkango ukabangula, ndani amene saopa? Ambuye Yehova wanena, ndani amene sanenera?” M’mawu ena, Amosi anauza omvera akewo kuti: ‘Monga momwe mumachitira mantha mukamva kubangula kwa mkango, inenso sindingasiye kulalikira mawu a Mulungu, chifukwa chakuti ndamva lamulo la Yehova loti nditero.’ Kuopa Mulungu, kapena kuti kumulemekeza kwambiri Yehova, kunalimbikitsa Amosi kulankhula molimba mtima.

21. Kodi timachitapo chiyani tikamva lamulo la Mulungu loti tilalikire uthenga wabwino?

21 Nafenso timamva lamulo la Yehova loti tilalikire. Kodi timachitapo chiyani? Mofanana ndi Amosi ndi otsatira oyambirira a Yesu, timalankhula mawu a Yehova molimba mtima, ndi thandizo Lake. (Machitidwe 4:23-31) Chizunzo chimene adani athu amayambitsa kapena kusalabadira kwa anthu amene timawalalikira sizingatiletse kulankhula. Posonyeza changu monga cha Amosi, Mboni za Yehova padziko lonse lapansi zikupitiriza kulalikira uthenga wabwino molimba mtima. Tili ndi udindo wochenjeza anthu za kubwera kwa chiweruzo cha Yehova. Kodi chiweruzo chimenecho chikuphatikizapo chiyani? Nkhani yotsatira iyankha funso limeneli.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi zinthu zinali bwanji panthawi imene Amosi anachita ntchito imene Mulungu anamupatsa?

• Mofanana ndi Amosi, kodi tiyenera kulalikira chiyani?

• Kodi tiyenera kukhala ndi mtima wotani tikamagwira ntchito yathu yolalikira?

• N’chifukwa chiyani otsutsa sangaimitse ntchito yathu yolalikira?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 10]

Mulungu anasankha Amosi, wotchera nkhuyu, kuti achite ntchito Yake

[Zithunzi patsamba 13]

Mofanana ndi Amosi, kodi mukulalikira uthenga wa Yehova molimba mtima?