Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yendani mu Umphumphu

Yendani mu Umphumphu

Yendani mu Umphumphu

“Koma ine, ndidzayenda m’ungwiro [“umphumphu,” NW] wanga.”​—SALMO 26:11.

1, 2. (a) Kodi n’chifukwa chiyani nkhani yokayikira zoti anthu angathe kulambira Mulungu mwamphumphu ikukhudzana kwambiri ndi nkhani yokayikira kuti Mulungu ndiye woyeneradi kulamulira? (b) Kodi anthu ndiponso angelo angasonyeze motani kuti ali mbali ya ulamuliro wa Yehova?

PAMENE Satana anagalukira Mulungu m’munda wa Edene, iye anayambitsa nkhani yokhudza chilengedwe chonse. Nkhaniyi ndi ya mmene Mulungu amalamulirira zinthu zonse zimene analenga, kuti kaya amazilamulira moyenera kapena ayi. Patapita nthawi kuchokera pamene anayambitsa nkhaniyi, Satana ananena kuti anthu angatumikire Mulungu pokhapokha ngati ataona kuti iwo apezapo phindu. (Yobu 1:9-11; 2:4) Motero, nkhani yokayikira zoti anthu angathe kulambira Yehova mwamphumphu inayamba kukhudzana kwambiri ndi nkhani yokayikira kuti Yehova ndiye woyeneradi kulamulira chilengedwe chonse.

2 Ngakhale kuti ulamuliro wa Mulungu sudalira kuti azitumikiridwa mwamphumphu ndi zolengedwa zake, anthu ndiponso ana auzimu a Mulungu angasonyeze mbali imene iwo ali pankhaniyi. Kodi angasonyeze zimenezi motani? Angatero mwa kusankha kuti ayende mu umphumphu kapena ayi. Motero, aliyense adzaweruzidwa malinga ndi umphumphu wake.

3. (a) Kodi Yobu ndi Davide anafuna kuti Yehova awayang’anire ndi kuwaweruza pa chiyani? (b) Kodi pali mafunso otani okhudza umphumphu?

3 Yobu ananena motsimikiza kuti: “[Yehova] andiyese ndi muyeso wolingana, kuti Mulungu adziwe ungwiro [“umphumphu,” NW] wanga.” (Yobu 31:6) Mfumu Davide ya dziko lakale la Israyeli inali kupempha Yehova kuti ayang’anire umphumphu wake pamene inapemphera kuti: “Mundiweruze, Yehova, pakuti ndayenda m’ungwiro [“umphumphu,” NW] wanga: Ndipo ndakhulupirira Yehova, sindidzaterereka.” (Salmo 26:1) M’pofunika kwambiri kuti nafenso tiyende mu umphumphu. Koma kodi umphumphu n’chiyani, ndipo kodi kuyenda mu umphumphu kumatanthauzanji? Kodi n’chiyani chingatithandize kupitiriza kuyenda mu umphumphu?

‘Ndayenda M’umphumphu Wanga’

4. Kodi umphumphu n’chiyani?

4 Mawu akuti umphumphu amasonyeza kuti chinthu ndi chowongoka, chopanda banga, cholungama, ndiponso chopanda polakwika paliponse. Komabe, umphumphu sikuti umangotanthauza kuchita zinthu zabwino kokha koma umatanthauzanso kukhala ndi makhalidwe abwino kapena kudzipereka ndi mtima wonse kwa Mulungu. Satana anakayikira zolinga zimene Yobu anali nazo pochita zinthu, pamene anauza Mulungu kuti: “Koma tambasulani dzanja lanu, ndi kukhudza fupa lake ndi mnofu [wa Yobu], ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu.” (Yobu 2:5) Kuwonjezera pa kuchita zinthu zoyenera, munthu amene ali ndi umphumphu amafunikanso kuchita zinthu ndi zolinga zoyenera.

5. N’chiyani chikusonyeza kuti kusunga umphumphu sikulira kuti tikhale angwiro?

5 Komabe, sikuti munthu amafunika kukhala wangwiro kuti azichita zinthu mwaumphumphu. Mfumu Davide inali yopanda ungwiro ndipo pamoyo wake inachita zolakwa zikuluzikulu zingapo. Koma ngakhale kuti zinali choncho, Baibulo limati Davide anayenda “ndi mtima wowona,” kapena kuti wamphumphu. (1 Mafumu 9:4) N’chifukwa chiyani limatero? Chifukwa chakuti Davide ankakonda Yehova. Anali ndi mtima wodzipereka kwa Mulungu. Anavomereza mosanyinyirika zolakwa zake, analola kudzudzulidwa, ndipo anasintha zochita zake. Zoonadi, timaona umphumphu wa Davide tikaganizira mmene iye analili wodzipereka komanso wokonda Mulungu wake, Yehova, ndi mtima wonse.​—Deuteronomo 6:5, 6.

6, 7. Kodi kuyenda mu umphumphu kumafuna chiyani?

6 Umphumphu sikuti umangokhudza mbali imodzi yokha ya khalidwe la munthu, monga kudzipereka pa chipembedzo. Koma umakhudzanso moyo wathu wonse. Davide ‘anayenda’ mu umphumphu wake. Buku lakuti The New Interpreter’s Bible limati: “Mawu akuti ‘kuyenda’ amasonyeza ‘zochita m’moyo’ kapena kuti ‘makhalidwe.’” Pofotokoza za anthu “angwiro m’mayendedwe awo,” wamasalmo anaimba kuti: “Odala iwo akusunga mboni [za Mulungu], akum’funa ndi mtima wonse; inde, sachita chosalungama; ayenda m’njira zake.” (Salmo 119:1-3) Kuti munthu azichita zinthu mwaumphumphu amafunika kuti nthawi zonse azichita zofuna za Mulungu ndi kuyenda m’njira yake.

7 Kuyenda mu umphumphu kumafuna kukhala wodzipereka ndi wokhulupirika kwa Mulungu ngakhale panthawi zovuta. Umphumphu wathu umaoneka tikamapirira mazunzo, kukhala olimba pamavuto, kapena tikakana mayesero a m’dziko loipali. Mwa kuchita zimenezi, ‘timakondweretsa mtima wa Yehova’ chifukwa chakuti iye amatha kuyankha amene amam’tonza. (Miyambo 27:11) Motero, tili ndi zifukwa zomveka zotipangitsa kutsimikiza mtima ngati mmene Yobu anachitira ponena kuti: “Mpaka kufa ine sinditaya ungwiro [“umphumphu,” NW] wanga.” (Yobu 27:5) Salmo la 26 limasonyeza zimene zingatithandize kuyenda mu umphumphu.

“Yeretsani Impso Zanga ndi Mtima Wanga”

8. Kodi mukuphunzirapo chiyani pa pempho la Davide lakuti Yehova ayese impso ndi mtima wake?

8 Davide anapemphera kuti: “Mundiyesere, Yehova, ndipo mundisunthe; yeretsani impso zanga ndi mtima wanga.” (Salmo 26:2) Impso zili m’katikati mwa thupi lathu. Impsozo, mophiphiritsira zimaimira maganizo a munthu a pansi penipeni pa mtima. Ndipo mtima wophiphiritsira umaimira m’kati mwa munthu, kapena kuti zimene zimamusonkhezera kuchita zinazake, mmene amamvera mumtima mwake, ndiponso nzeru zake. Popempha Yehova kuti amuyesere kapena kuti amuyese, Davide kwenikweni anali kupemphera kuti Yehova afufuze ndi kuyesa zoganiza zake za pansi pa mtima wake ndiponso mmene amamvera mumtima mwakemo.

9. Kodi Yehova amayeretsa motani impso ndi mtima wathu wophiphiritsira?

9 Davide anapempha kuti impso ndi mtima wake ziyeretsedwe. Kodi Yehova amatiyeretsa motani m’kati mwathu? Davide anaimba kuti: “Ndidzadalitsa Yehova, amene anandichitira uphungu: Usikunso impso zanga zindilangiza.” (Salmo 16:7) Kodi izi zikutanthauzanji? Zikutanthauza kuti malangizo a Mulungu anam’fika pamtima Davide n’kukhazikika mumtimamo, ndi kukonza maganizo am’katikati mwa mtima wake. Zimenezi zingatichitikirenso ifeyo ngati timasinkhasinkha ndi mtima woyamikira malangizo amene timalandira kudzera m’Mawu a Mulungu, anthu omuimira, ndiponso gulu lake, ndi kulola kuti malangizowo akhazikike mumtima mwathu. Kupemphera nthawi zonse kwa Yehova kuti atiyeretse moteremu kungatithandize kuti tiyende mu umphumphu.

“Chifundo Chanu Chili Pamaso Panga”

10. Kodi n’chiyani chinathandiza Davide kuyenda m’choonadi cha Mulungu?

10 Davide anapitiriza motere: “Chifundo chanu chili pamaso panga, ndipo ndayenda m’choona chanu.” (Salmo 26:3) Mosakayikira, Davide ankadziwa zinthu zosiyanasiyana zimene Mulungu anachita posonyeza chifundo chake, ndipo ankasinkhasinkha zimenezi ndi mtima woyamikira. Iye anaimba kuti: “Lemekeza Yehova, moyo wanga, ndi kusaiwala zokoma zake zonse atichitirazi.” Pokumbukira chimodzi mwa ‘zochita’ za Mulungu, Davide anapitiriza motere: “Yehova achitira onse osautsidwa chilungamo ndi chiweruzo. Analangiza Mose njira zake, ndi ana a Israyeli machitidwe ake.” (Salmo 103:2, 6, 7) N’kutheka kuti Davide anali kuganizira za mmene Aisrayeli anasautsidwira ndi Aigupto m’masiku a Mose. Ngati ndi choncho, Davide ayenera kuti anakhudzidwa mtima poganizira mmene Yehova anasonyezera Mose njira zake zopulumutsira anthu ndiponso zimenezi ziyenera kuti zinamulimbikitsa kukhalabe wotsimikiza mtima kuyenda m’choonadi cha Mulungu

11. Kodi n’chiyani chingatithandize kuyenda mu umphumphu?

11 Nakonso kuphunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse ndiponso kusinkhasinkha zimene timaphunzira m’mawuwo kungatithandize kuyenda mu umphumphu. Mwachitsanzo, kukumbukira kuti Yosefe anathawa pamene mkazi wa Potifara ankafuna kuti agone naye, mosakayikira kungatilimbikitse kuthawa anthu ena akamatinyengerera m’njira yangati imeneyi, kaya n’kuntchito, kusukulu, kapenanso kwina kulikonse. (Genesis 39:7-12) Kodi tili ndi zitsanzo zomwe tingaziganizire panthawi imene mwayi wopeza chuma kapena kutchuka ndiponso kukhala amphamvu m’dzikoli ukutiika pachiyeso? Tili ndi chitsanzo cha Mose, amene anakana ulemerero wa mu Igupto. (Ahebri 11:24-26) Mosakayikira, kukumbukira za kupirira kwa Yobu kungatilimbikitse kutsimikiza mtima kuti tipitirize kukhala okhulupirika kwa Yehova ngakhale titadwala kapena kukumana ndi mavuto. (Yakobo 5:11) Nanga bwanji ngati tikuzunzidwa? Kukumbukira zimene zinachitikira Danieli m’dzenje la mikango kungatithandize kukhala olimba mtima.​—Danieli 6:16-22.

“Sindinakhala Pansi ndi Anthu Achabe”

12, 13. Kodi tiyenera kupewa kugwirizana ndi anthu otani?

12 Pofotokoza chinthu chinanso chomwe chinalimbitsa umphumphu wake, Davide anati: “Sindinakhala pansi ndi anthu achabe; kapena kutsagana nawo anthu othyasika. Ndidana nawo msonkhano wa ochimwa, ndipo sindidzakhala nawo pansi ochita zoipa.” (Salmo 26:4, 5) Davide sankakhala pansi, ngakhale pang’ono chabe, ndi anthu oipa. Sankafuna kugwirizana nawo.

13 Nanga bwanji ifeyo? Kodi timakana kukhala ndi anthu achabe, kudzera m’mapulogalamu a pa TV, m’mavidiyo, m’makanema, pa Intaneti, kapena m’njira zina? Kodi timapewa anthu amene amabisa umunthu wawo? Anthu ena kusukulu kapena kuntchito kwathu anganamizire kuti ndi anzathu pamene ali ndi zolinga zachabe. Ndithudi, sitingafune kugwirizana ndi anthu amene sayenda m’choonadi cha Mulungu. Ngakhale kuti ampatuko amati ndi anthu oona mitima, nawonso angabise cholinga chawo pofuna kuti atisiyitse kutumikira Yehova. Kodi tingatani ngati mumpingo wachikristu muli ena amene ali ndi moyo wachiphamaso? Nawonso ndiye kuti amabisa umunthu wawo weniweni. Jayson, yemwe tsopano ndi mtumiki wotumikira, anali ndi anzake ngati amenewa ali wamng’ono. Pofotokoza za anthu amenewa, iye anati: “Tsiku lina mmodzi wa anzangawa anandiuza kuti: ‘Zimene timachita panopa zilibe ntchito chifukwa dziko latsopano likamadzafika, tidzakhala titafa basi. Sitidzadziwa kuti tikumanidwa chilichonse.’ Zimene ananenazi zinandigalamutsa. Ineyo sindikufuna kuti ndidzakhale nditafa dziko latsopano likamadzabwera.” Jayson anachita zanzeru posiya kugwirizana ndi anthu amenewa. Mtumwi Paulo anachenjeza motere: “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Motero kupewa kugwirizana ndi anthu oipa n’kofunika kwambiri.

‘Ndidzalalikira Ntchito Zanu Zonse Zozizwa’

14, 15. Kodi ‘tingazungulire guwa la nsembe la [Yehova]’ motani?

14 Davide anapitiriza motere: “Ndidzasamba manja anga mosalakwa; kuti ndizungulire guwa la nsembe lanu, Yehova.” Chifukwa? “Kuti ndimveketse mawu a chiyamiko, ndi kulalikira ntchito zanu zonse zozizwa.” (Salmo 26:6, 7) Davide anafuna kuti apitirize kukhala ndi makhalidwe abwino kuti azilambira Yehova ndi kulengeza za kudzipereka kwake kwa Mulungu.

15 Chilichonse chokhudza kulambira koona pa chihema ndiponso pa kachisi amene anamangidwa pambuyo pake chinali ‘mthunzi wa zakumwamba.’ (Ahebri 8:5; 9:23) Guwa la nsembe linkatanthauza zimene Yehova anali kufuna zoti alandire nsembe ya Yesu Kristu yowombolera anthu. (Ahebri 10:5-10) Tikamakhulupirira nsembe imeneyo timakhala tikusamba m’manja mwathu mosalakwa ndi ‘kuzungulira guwa la nsembe la [Yehova].’​—Yohane 3:16-18.

16. Kodi timapindula motani tikamalengeza kwa ena ntchito zozizwitsa za Mulungu?

16 Tikaganizira zinthu zonse zimene zimatheka chifukwa cha dipo, kodi mitima yathu siyamikira Yehova ndiponso Mwana wake wobadwa yekha? Motero, ndi mitima yoyamikira, tiyeni tidziwitse ena ntchito zozizwitsa za Mulungu, kungoyambira pa kulengedwa kwa munthu m’munda wa Edene mpaka kufika panthawi imene zinthu zonse zidzabwerere mwakale m’dziko latsopano la Mulungu. (Genesis 2:7; Machitidwe 3:21) Ndiponsotu, ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira imeneyi imatiteteza mwauzimu. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Kugwira ntchito imeneyi kumathandiza kukhala ndi chiyembekezo chachikulu cha zinthu zam’tsogolo, kukhulupirira kwambiri malonjezo a Mulungu, ndiponso kupitiriza kukonda Yehova ndiponso anthu ena.

‘Ndikonda Kukhala M’nyumba Yanu’

17, 18. Kodi tiziiona motani misonkhano yachikristu?

17 Chihema, pamodzi ndi ntchito zake za nsembe, chinali likulu lolambirirapo Yehova ku Israyeli. Pofotokoza mmene ankasangalalira ndi malo amenewo, Davide anapemphera kuti: “Yehova, ndikonda chikhalidwe cha nyumba yanu, ndi malo akukhalamo ulemerero wanu.”​Salmo 26:8.

18 Kodi timakonda kusonkhana pamalo amene timaphunzira za Yehova? Nyumba ya Ufumu iliyonse, chifukwa cha maphunziro auzimu amene amachitikirapo, imakhala likulu la kulambira koona m’dera limene muli nyumbayo. Komanso, chaka n’chaka timakhala ndi misonkhano yachigawo, yadera, ndiponso masiku a misonkhano yapadera. Pamisonkhanoyi pamafotokozedwa “mboni,” kapena kuti zikumbutso za Yehova. Tikaphunzira ‘kuzikonda kwambiri’ zikumbutsozi, timakhala ofunitsitsa kupita kumisonkhano ndi kukatchera khutu tikafika kumisonkhanoko. (Salmo 119:167) N’zotsitsimutsa kwambiri kukhala ndi okhulupirira anzathu amene amadera nkhawa za moyo wathu ndiponso amene amatithandiza kupitiriza kuyenda mu umphumphu.​—Ahebri 10:24, 25.

‘Musandichotsere Moyo Wanga’

19. Kodi Davide sanafune kukhala ndi machimo ati?

19 Pozindikira vuto la kusiya kuyenda m’choonadi cha Mulungu, Davide anapempha kuti: “Musandichotsere mzimu wanga pamodzi ndi olakwa, kapena moyo wanga pamodzi ndi anthu okhetsa mwazi: Amene m’manja mwawo muli mphulupulu, ndi dzanja lawo lamanja ladzala ndi zokometsera mlandu.” (Salmo 26:9, 10) Davide sanafune kuikidwa m’gulu la anthu osapembedza, amphulupulu kapena kuti amakhalidwe otayirira kapena anthu aziphuphu.

20, 21. Kodi n’chiyani chingachititse kuti tiyende m’njira ya osakonda Mulungu?

20 Dzikoli masiku ano ladzala ndi makhalidwe oipa. Ma TV, magazini, ndiponso mafilimu ake amalimbikitsa anthu kukhala ndi makhalidwe otayirira, omwe ndi “dama, chodetsa, kukhumba zonyansa.” (Agalatiya 5:19) Ena amakonda kwambiri zinthu zolaula, zomwe kawirikawiri zimapangitsa munthu kukhala wamakhalidwe oipa. Achinyamata ndiwo amene amakodwa mosavuta ndi zinthu zimenezi. M’mayiko ena, kukhala ndi chibwenzi n’kofala kwambiri ndipo achinyamata amakakamizika kutengera maganizo okhala ndi chibwenzi. Achinyamata ambiri amakhala ndi chibwenzi, ngakhale kuti sanafike n’komwe msinkhu wokwatira. Pofuna kukwaniritsa chikhumbo cha kugonana chomwe chimakhala chitangoyamba kumene m’matupi mwawo, achinyamatawa satenga nthawi yaitali, amachita zoipa mpaka kufika pochita chiwerewere.

21 Nawonso akuluakulu angathe kutengera zinthu zoipa. Malonda achinyengo ndiponso kuchita zinthu mwadyera n’chizindikiro chakuti munthu sakuyenda mu umphumphu. Komatu kutengera zochita za dzikoli kungangotipangitsa kuti tikhale adani a Yehova. Tiyeni ‘tidane nacho choipa, ndi kukonda chokoma’ ndi kupitiriza kuyenda mu umphumphu.​—Amosi 5:15.

“Mundiwombole, Ndipo Ndichitireni Chifundo”

22-24. (a) Kodi m’mawu omaliza a Salmo 26 mumapezamo zinthu ziti zolimbikitsa? (b) Kodi m’nkhani yotsatirayi mwafotokozedwa za msampha wotani?

22 Davide anamaliza motere kufotokozera Mulungu maganizo ake: “Koma ine, ndidzayenda m’ungwiro [“umphumphu,” NW] wanga; mundiwombole, ndipo ndichitireni chifundo. Phazi langa liponda pachidikha: M’masonkhano ndidzalemekeza Yehova.” (Salmo 26:11, 12) Onani kuti pamenepa Davide akusonyeza kuti akufunitsitsa kuchita zinthu mwaumphumphu koma panthawi yomweyo akupemphanso kuti awomboledwe. Izitu ndi zolimbikitsa kwambiri. Ngakhale kuti ndife ochimwa, Yehova angatithandize ngati tatsimikiza mtima kuyenda mu umphumphu.

23 Tiyeni tionetse mwa makhalidwe athu kuti timalemekeza ulamuliro wa Mulungu ndipo timauona kuti ndi wofunika m’moyo wathu wonse. Tonsefe tingapemphere kwa Yehova kuti ayese ndi kuyeretsa maganizo am’katikati mwa mtima wathu. Kuti nthawi zonse tisamaiwale choonadi chake tizichita khama pophunzira Mawu ake. Motero, tiyeni tiyesetse kupewa kugwirizana ndi anthu oipa koma tilimbikire kudalitsa Yehova m’misonkhano. Tiyeni tikhale akhama pa ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira, ndipo tisalole dzikoli kusokoneza ubwenzi wathu ndi Mulungu, womwe n’ngwamtengo wapatali. Pamene tikuyesetsa kuyenda mu umphumphu, tingakhale ndi chikhulupiriro chakuti Yehova atichitira chifundo.

24 Popeza kuti umphumphu umakhudza mbali zonse za moyo, tiyenera kukhala tcheru ndi msampha wina woopsa kwambiri. Msampha uwu ndi wa kumwa mowa mopyola malire. Izi zafotokozedwa m’nkhani yotsatirayi.

Kodi Mukukumbukira?

• N’chifukwa chiyani pali poyenera kuti anthu ndiponso angelo adzaweruzidwe malinga ndi umphumphu wawo?

• Kodi umphumphu n’chiyani, ndipo kodi kuyenda mu umphumphu kumafuna chiyani?

• Kodi n’chiyani chingatithandize kuyenda mu umphumphu?

• Kodi tiyenera kudziwa ndiponso kupewa chiyani kuti tipitirize kuchita zinthu mwaumphumphu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 14]

Kodi mumapempha Yehova nthawi zonse kuti ayese maganizo am’katikati mwa mtima wanu?

[Chithunzi patsamba 14]

Kodi mumaganizira nthawi zonse za ntchito zimene Yehova anachita chifukwa cha chifundo?

[Zithunzi patsamba 15]

Yehova amasangalala tikamapitiriza kuchita zinthu mwaumphumphu pamene tikuyesedwa

[Zithunzi patsamba 17]

Kodi mumagwiritsa ntchito zinthu zimene Yehova wapereka zoti zikuthandizeni kuyenda mu umphumphu?