Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Yesu Kristu Tiyenera Kumam’kumbukira Motani?

Kodi Yesu Kristu Tiyenera Kumam’kumbukira Motani?

Kodi Yesu Kristu Tiyenera Kumam’kumbukira Motani?

Yesu Kristu ‘mosakayikira anali mmodzi mwa anthu otchuka kwambiri pa dziko lonse lapansi,’ linatero buku la “The World Book Encyclopedia.”

KAWIRIKAWIRI anthu otchuka amakumbukiridwa chifukwa cha ntchito zawo. Nanga n’chifukwa chiyani anthu ambiri amakumbukira Yesu chifukwa cha kubadwa kwake m’malo mom’kumbukira chifukwa cha ntchito zake? M’Matchalitchi onse Achikristu, anthu amatha kunena pamtima zinthu zonse zokhudza kubadwa kwake, chimodzi ndi chimodzi. Koma ndi angati angathe kukumbukira ndi kugwiritsa ntchito m’moyo mwawo zinthu zamtengo wapatali zimene Yesuyo anaphunzitsa mu Ulaliki wa pa Phiri?

Zoona, kubadwa kwa Yesu kunali kofunika, koma ophunzira ake oyambirira ankaganizira kwambiri zinthu zimene iye anachita ndiponso zimene anaphunzitsa. Ndithudi Mulungu sanafune kuti kubadwa kwa Kristu kukhale kofunika kuposa zimene anachita monga munthu wachikulire. Komabe, ntchito za Kristu zaiwalikiratu chifukwa cha nthano za Khirisimasi.

Funso lina lothetsa nzeru limene munthu angafunse n’lokhudza zimene zimachitika pa chikondwerero cha Khirisimasi. Ngati Yesu akanabweranso padziko lero, kodi akanaganiza chiyani poona mmene anthu asandutsira Khirisimasi kukhala bizinesi yotentha? Zaka 2000 zapitazo, Yesu anapita ku kachisi m’Yerusalemu. Iye anakwiya ndi anthu osintha ndalama ndiponso ochita malonda potengerapo mwayi wopanga ndalama pa mwambo winawake wa Chiyuda. Yesu anati: “Chotsani izi muno; musamayesa nyumba ya Atate wanga nyumba ya malonda.” (Yohane 2:13-16) Mwachionekere, Yesu sanagwirizane nazo zophatikiza malonda ndi chipembedzo.

Akatolika ambiri oona mtima a ku Spain amada nkhawa ndi mmene khalidwe logwiritsa ntchito Khirisimasi pochita malonda likukulira. Komabe, n’kovuta kupewa khalidweli tikaganizira mmene Khirisimasi inayambira. Juan Arias yemwe ndi mtolankhani anati: “Mkristu aliyense amene sagwirizana ndi mmene anthu asandutsira Khirisimasi kukhala ‘yachikunja,’ kapenanso kukhala chikondwerero wamba ndiponso nyengo yochita malonda m’malo mokhala mwambo wachipembedzo sadziwa kuti ngakhale pamene mwambowu unkayamba . . . anali ataphatikizamo kale miyambo yambiri ya chikondwerero chachikunja cha Aroma [chokondwerera dzuwa].”​—El País, December 24, 2001.

M’zaka zaposachedwapa, atolankhani ambiri ku Spain komanso mabuku ambiri athirirapo ndemanga zoti chikondwerero cha Khirisimasi n’chachikunja ndiponso anenapo chifukwa chake amachigwiritsa ntchito m’zamalonda. Pokambapo za deti la chikondwerero cha Khirisimasi, buku lofotokoza za Chikatolika la Enciclopedia de la Religión Católica limanena mosapita m’mbali kuti: “Zikuoneka kuti deti la chikondwerero limeneli analisankha chifukwa chakuti Tchalitchi cha Roma chili ndi chizolowezi chosanduliza zikondwerero zachikunja kukhala zachikristu. . . . Tikudziwa kuti ku Roma panthawiyo, akunja anapatula deti la December 25 monga tsiku la chikondwerero cha natalis invicti, cha kubadwa kwa ‘dzuwa losagonjetseka.’”

Buku la Enciclopedia Hispánica limanena chimodzimodzi kuti: “Deti la December 25, pamene anthu amakondwerera Khirisimasi, silinaikidwe mogwirizanadi ndi tsiku limene Yesu anabadwa, koma linaikidwa pofuna kuti zikondwerero zachikunja za Aroma zokondwerera nthawi imene dzuwa limabwereranso pa liwombo m’nyengo ya chisanu zisanduke za Chikristu.” Kodi anthu ku Roma ankakondwerera motani mwambo umenewu? Ankakondwerera mwa kuchita madyerero, kuchita chisangalalo mwaphokoso ndi kupatsana mphatso. Popeza akuluakulu a tchalitchi sanafune kuthetsa mwambo wachikunjawu, anausandutsa wa “Chikristu” n’kumanena kuti ndi tsiku limene Yesu anabadwa osati limene dzuwa linabadwa.

Chakumayambiriro kwa chikondwererochi, m’zaka za pakati pa 300 ndi 400, anthu anali asanasiyiretu kulambira dzuwa ndipo zinali zovuta kuti miyambo yake itheretu. Augustine “Woyera” wa Chikatolika (yemwe anabadwa mu 354 n’kumwalira mu 430 C.E.) anafika polimbikitsa Akatolika anzake kuti asamakondwerere December 25 m’njira yofanana ndi mmene akunja ankakondwerera dzuwa. Ngakhale masiku ano zikuoneka kuti miyambo yakale yachiroma yokhudza kulambira dzuwa ndiyo ikutenga malo.

Nyengo ya Chisangalalo ndi Malonda Basi

Kwa zaka mazana ambiri, pakhala zifukwa zingapo zomwe zachititsa kuti padziko lonse lapansi Khirisimasi ikhale nyengo yotchuka, yosangalala ndiponso yochita malonda. Komanso, miyambo ya zikondwerero zomwe zinkachitika nyengo yachisanu makamaka kumpoto kwa Ulaya pang’onopang’ono inalowa mu chikondwererochi chomwe chinayambira ku Roma. * Ndipo, m’zaka za m’ma 1900 anthu ogulitsa ndi otsatsa malonda anachita khama kulimbikitsa miyambo iliyonse imene ikanawabweretsera phindu lalikulu pamalonda.

Zotsatira zake zakhala zotani? Chikondwerero cha kubadwa kwa Kristu ndicho chakhala chofunika kwambiri kuposa phindu lake lenileni la kubadwako. Nthawi zambiri, Kristu samutchula n’komwe m’zochitika za pa Khirisimasi. “[Khirisimasi] ndi chikondwerero chabanja chomwe chimachitika padziko lonse, ndipo aliyense amakondwerera mmene iye mwini akufunira,” inatero nyuzipepala ya ku Spain ya El País.

Zimene nyuzipepalayi inanena n’zimene zikuchitikadi ku Spain ndi m’mayiko ena ambiri padziko lonse. Pamene anthu akupitiriza kumwaza ndalama zochuluka pa Khirisimasi, m’pamenenso zimene amadziwa ponena za Kristu zikucheperachepera. Choonadi chake n’chakuti zochitika za pa Khirisimasi zabwerera mwakale monga mmene zinkachitikira m’nthawi yachiroma chifukwa zasandukanso chikondwerero chaphokoso, madyerero, ndi kupatsana mphatso.

Mwana Watibadwira

Ngati mwambo wa Khirisimasi sukhudzana n’komwe ndi kubadwa kwa Kristu, nanga Akristu angamakumbukire motani kubadwa ndiponso moyo wa Kristu? Zaka 700 Yesu asanabadwe, Yesaya analosera za Yesu kuti: “Kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake.” (Yesaya 9:6) N’chifukwa chiyani Yesaya anasonyeza kuti kubadwa kwa Yesu limodzi ndi ulamuliro umene anadzakhala nawo pambuyo pake zinali zofunika kwambiri? Chifukwa chakuti Yesu anadzakhala mtsogoleri wamphamvu. Anadzatchedwa Kalonga wa Mtendere, ndipo mtendere ndi ufumu wake n’zopanda malire. Komanso, ulamuliro wa Yesu udzakhazikika chifukwa cha “chiweruziro ndi chilungamo.”​—Yesaya 9:7.

Mngelo Gabrieli anabwereza uthenga wa Yesaya pamene anauza Mariya za kubadwa kwa Yesu. Mngeloyu analosera kuti: “Iye adzakhala wamkulu, nadzatchedwa Mwana wa Wamkulukulu: ndipo Ambuye Mulungu adzam’patsa Iye mpando wachifumu wa Davide atate wake: ndipo Iye adzachita ufumu pa banja la Yakobo ku nthawi zonse; ndipo ufumu wake sudzatha.” (Luka 1:32, 33) Mwachionekere, kufunika kwenikweni kwa kubadwa kwa Yesu kwagona pa ntchito imene Kristu anadzakwaniritsa monga Mfumu yodzozedwa ya Ufumu wa Mulungu. Anthu onse, kuphatikizapo inuyo ndi enanso amene mumawakonda angathandizidwe kwambiri ndi ulamuliro wa Kristu. Ndithudi, angelo anasonyeza kuti kubadwa kumeneku kudzabweretsa “mtendere pansi pano mwa anthu amene [Mulungu] akondwera nawo.”​—Luka 2:14.

Ndani kodi safuna kukhala m’dziko lamtendere ndi chilungamo? Koma kuti tidzathe kusangalala ndi mtendere umene ulamuliro wa Kristu udzabweretse timafunika kukondweretsa Mulungu ndi kukhala naye paubwenzi wabwino. Yesu ananena kuti chinthu choyamba kuti tikhazikitse ubwenzi umenewu ndicho kudziwa bwinobwino za Mulungu ndi Kristu. Yesu anati: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.”​—Yohane 17:3.

Tikaphunzira ndi kudziwa bwino za Yesu, sitingachite kufunsa kuti kodi iye akanakonda kuti tizim’kumbukira motani. Kodi iye akanakonda kuti tizim’kumbukira mwa kudyerera, kumwerera ndi kupatsana mphatso pa tsiku la chikondwerero lakalekale ndi lachikunja? Ayi ndithu. Usiku woti akufa mawa lake, Yesu anauza ophunzira ake zimene iye mwini wake ankafuna. Yesu anati: “Iye wakukhala nawo malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo Ine ndidzam’konda.”​—Yohane 14:21.

A Mboni za Yehova aphunzira mozama Malemba Opatulika ndipo zimenezi zawathandiza kumvetsetsa chimene malamulo a Mulungu ndiponso Yesu amanena. Iwo angakonde kukuthandizani kuti mumvetsetse malamulo ofunika amenewo kuti muzitha kukumbukira Yesu m’njira yoyenera.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Zitsanzo zabwino kwambiri pankhaniyi ndizo kugwiritsira ntchito mtengo wa pa Khirisimasi ndiponso zidole za Santa Claus kapena kuti Tate Khirisimasi.

[Bokosi/​Zithunzi pamasamba 6, 7]

Kodi Baibulo Limaletsa Mapwando ndi Kupatsana Mphatso?

Kupatsana Mphatso

Baibulo limavomereza kupatsana mphatso, ndipo Yehova mwiniyo amatchedwa Wopatsa “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro.” (Yakobo 1:17) Yesu ananena kuti makolo abwino amapatsa ana awo mphatso zabwino. (Luka 11:11-13) Mabwenzi a Yobu ndi achibale ake anam’patsa mphatso atachira. (Yobu 42:11) Komabe, anthu onse tawatchulawa sankachita kudikirira masiku apadera a chikondwerero kuti apatse ena mphatsozo. M’malo mwake, ankazipereka mochokera pansi pa mtima.​—2 Akorinto 9:7.

Mapwando a Pabanja

Kuchita phwando pamodzi monga banja kumagwirizanitsa banjalo, makamaka ngati anthuwo amakhala motalikirana. Yesu ndi ophunzira ake anakapezekapo pa madyerero a ukwati ku Kana komwe mosakayikira mabwenzi ndi achibale anakumana pamodzi. (Yohane 2:1-10) Ndiponso m’fanizo la Yesu la mwana wolowerera, atate wake anachita phwando la pabanja limene panalinso nyimbo ndiponso kuvina pokondwerera kubwera kwa mwana wawo.​—Luka 15:21-25.

Kudya Chakudya Chosowa

Baibulo limasimba kawirikawiri nkhani za atumiki a Mulungu akudya chakudya chokoma ndi a pabanja, mabwenzi kapena okhulupirira anzawo. Pamene angelo atatu anafika ku nyumba kwa Abrahamu, anawakonzera phwando lomwe mwa zina panali zakudya monga nyama ya ng’ombe, mkaka, batala ndi mikate. (Genesis 18:6-8) Solomo anati ‘kudya, kumwa, ndi kusekerera’ ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.​—Mlaliki 3:13; 8:15.

Mwachionekere, Mulungu amafuna kuti ife tizisangalala kumadyera pamodzi chakudya chokoma ndi a pabanja pathu ndiponso ndi mabwenzi anthu ndipo satiletsa kupatsana mphatso. Pali nthawi yochuluka yochitira zimenezi m’chaka chonse chathunthu.