Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsiku la Mwambo Womaliza Maphunziro Linali Losaiwalika

Tsiku la Mwambo Womaliza Maphunziro Linali Losaiwalika

Tsiku la Mwambo Womaliza Maphunziro Linali Losaiwalika

“LERO kunja kwacha bwino kwabasi. Dzuwa lawala bwino. Kumwamba kulibe mitambo iliyonse. Udzu ukuoneka wobiriwira bwino. Mbalame zikuimba nyimbo zawo. Inde, zikuoneka kuti lero likhala tsiku losaiwalika kwambiri, ndipo tonse sitikhumudwa ndi zochitika za lero. Yehova si Mulungu wokhumudwitsa. Iye ndi Mulungu wopereka madalitso.”

Awa ndi mawu amene Mbale Samuel Herd, wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, ananena potsegulira mwambo womaliza maphunziro a kalasi la nambala 117 la Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo. Apa panali pa September 11, 2004. Pa mwambo wosaiwalikawu panakambidwa nkhani zolimbikitsa kwambiri zochokera m’Baibulo ndipo ophunzira anasimbapo zinthu zina zomwe anakumana nazo muutumiki wawo ali pasukuluyo komanso amishonale akale ananenaponso zinthu zina zimene anakumana nazo. Inde, tsikuli linalidi losaiwalika kwa anthu onse 6,974 amene anaonerera mwambowu, ku Likulu la Maphunziro la Watchtower ku Patterson, mumzinda wa New York, ndiponso ku maofesi ena ku Brooklyn ndi ku Wallkill, kumene anthu anaonera ndiponso kumvetsera mwambowu pa kanema ndi pawailesi.

Mawu Olimbikitsa Ophunzirawo

John Kikot yemwe ali m’Komiti Yoyang’anira Nthambi ya ku United States, ananena mawu olimbikitsa m’nkhani yake yakuti “Pitirizani Kukhala Amishonale Achimwemwe.” Iye anati ophunzira a sukulu ya Gileadi amadziwika kuti ndi anthu achimwemwe, monga mmene anali kuonekera pa mwambowu. Zimene ophunzirawa anali kuphunzira panthawi ya sukuluyi zinawapatsa chimwemwe, ndipo tsopano nawonso angathe kuthandiza anthu ena kukhala ndi chimwemwe choterocho. Kodi angatero motani? Pochita utumiki wawo waumishonale modzipereka. Yesu anati: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Potsanzira Yehova Mulungu, yemwe ndi Mulungu wopatsa komanso “wachimwemwe,” amenenso amapereka choonadi, amishonale atsopanowo angathe kukapitiriza kukhala achimwemwe.​—1 Timoteo 1:11, NW.

Kenaka Mbale David Splane, yemwenso ali m’Bungwe Lolamulira, anakamba nkhani ya mutu wakuti “Kodi Mukagwirizana Nawo Anthu?” N’zachidziwikire kuti kukhalira limodzi ndi ena n’kokoma ndiponso n’kokondweretsa ngakhale kuti kumafunika kuti munthuwe ukhale “zonse kwa anthu onse.” (1 Akorinto 9:22; Salmo 133:1) Mbale Splane analongosola kuti m’ntchito yawo yaumishonale, ophunzira omaliza maphunzirowa akakumana ndi anthu osiyanasiyana, monga anthu a m’gawo lawo, amishonale anzawo, abale ndi alongo a mumpingo umene akakhalemo, ndiponso abale a pa ofesi yanthambi amene akuyendetsa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa. Ndiyeno mbaleyu analongosolapo zimene zingakawathandize kuti akagwirizane ndi anthuwa mosavuta. Iye anati amishonalewo ayenera kukadziwa chinenero cha kumene akupitako, azikachita zinthu moganizira za chikhalidwe cha kumeneko, asamakachite zinthu zolowa m’chala amishonale anzawo, ndiponso azikamvera amene akuwatsogolera.​—Ahebri 13:17.

Kenaka, Mbale Lawrence Bowen, yemwe ndi mlangizi pa sukulu ya Gileadi, anakamba nkhani ya mutu wakuti “Kodi Mumaganiza Motani?” Iye anauza ophunzirawo kuti asaiwale kuti anthu amene ‘ankangoona maonekedwe akunja okha’ anam’kana Yesu kuti si Mesiya. (Yohane 7:24) Pakuti tonsefe ndife opanda ungwiro, tiyenera kuonetsetsa kuti tikupewa ‘maganizo a anthu’ ndipo m’malo mwake tizikhala ndi ‘maganizo a Mulungu.’ (Mateyu 16:22, 23) Ngakhale anthu amene ali achikulire mwauzimu ayenera kupitirizabe kukonza maganizo awo. Tikapanda kusintha maganizo athu, tingagwe m’vuto lalikulu lauzimu monga mmene sitima ya pamadzi ingachitire ngozi ngati ikulowera kolakwika koma wosaiwongolera. Kupitiriza kuphunzira Baibulo lonse kumatithandiza kukhala ndi “maganizo a Mulungu.”

Wallace Liverance, amenenso ali mlangizi pa Sukulu ya Gileadi, ndiye anamaliza mbali imeneyi ya mwambowu. Mutu wa nkhani yake anautenga pa Yesaya 55:1, ndipo unali wakuti “Kodi Musankha Kugula Chiyani?” Iye analimbikitsa ophunzirawo ‘kugula’ zinthu zimene uthenga wa Mulungu waulosi umatipatsa masiku ano. Zinthu zake ndizo chilimbikitso, chimwemwe, ndiponso mtima wokhutira. Mu ulosi wa Yesaya mawu a Mulungu amenewa anawayerekezera ndi madzi, vinyo, ndiponso mkaka. Kodi zinthu zoterezi tingazigule bwanji “opanda mtengo,” kapena kuti ndalama? Mbale Liverance analongosola kuti tingatero potsatira maulosi a m’Baibulo ndiponso posiya kutsatira maganizo komanso njira zoipa n’kuyamba kutsatira maganizo ndiponso njira za Mulungu. (Yesaya 55:2, 3, 6, 7) Potero, amishonale atsopanowo angathe kukakhala bwinobwino kumayiko kumene akupitako. Anthu opanda ungwirofe nthawi zambiri timaganiza kuti chimwemwe chimalira kukhala moyo wa mwanaalirenji. Mbale amene ankakamba nkhaniyi anati: “Osatengeka nawo maganizo amenewo. Ndithu, musatengeke nawo ayi. Yesetsani kukhala ndi nthawi yoti muziphunzira Mawu aulosi a Mulungu moti muzitha kuwamvetsa bwino. Mawu amenewa angathe kukulimbikitsani, kukupatsani mphamvu ndiponso chimwemwe muutumiki wanu waumishonale.”

Ophunzirawo Anasimbapo Nkhani Zawo Zosangalatsa

Ophunzirawo ankachita nawo ntchito yolalikira nthawi zonse. Mbale Mark Noumair, yemwenso ndi mlangizi pa sukulu ya Gileadi, anali ndi nkhani ya mutu wakuti “Uthenga Wabwino Sundichititsa manyazi.” (Aroma 1:16) Pankhaniyi ophunzira ena a m’kalasili anachitapo zitsanzo zosonyeza zimene anakumana nazo muutumiki. Omvetsera anasangalala kumva zimene alaliki aluso amenewa ankachita polalikira nyumba ndi nyumba, mumsewu, ndiponso m’misika ikuluikulu. Ophunzira amene ankadziwa zinenero zina anachita zotheka kuti apeze anthu olankhula zinenero zimenezo m’gawo la mpingo umene analimo. Ena anagwiritsira ntchito bwino mabuku ofotokoza za Baibulo amene Mboni za Yehova zimafalitsa, ndipo anawagwiritsira ntchito pa maulendo obwereza ndiponso poyambitsa maphunziro a Baibulo. Iwo ‘sanachite manyazi’ kulalikira uthenga wabwino.

Mbale William Nonkes, amene amagwira ntchito mu Dipatimenti ya Utumiki, anafunsa mafunso amishonale omwe akhala akuchita umishonale kwa nthawi yaitali ochokera ku Burkina Faso, Latvia, ndi Russia. Iwo anatchulapo malangizo othandiza ogwirizana ndi nkhani ya mutu wakuti “Yehova, Mwachikondi Chake, Amadalitsa Onse Okhulupirika.” Mbale wina m’gululi analimbikitsa ophunzirawo kuti asaiwale ankhondo a Gideoni 300. Aliyense mwa asilikaliwo anachita ntchito imene inathandiza kuti Gideoni apambane pankhondo. (Oweruza 7:19-21) Amishonale amene sasiya umishonale wawo amadalitsidwanso chimodzimodzi.

Mbale Samuel Robertson, amene ali mlangizi ku Patterson, anafunsanso abale ena mafunso ogwirizana ndi mutu wa nkhani yake yakuti “Khalani Zonse kwa Anthu Onse.” Iyeyu anafunsa mafunso abale anayi a m’Makomiti a Nthambi a ku Senegal, Guam, Liberia, ndi Madagascar. M’mayiko amenewa muli amishonale 170. Ophunzira amene amamaliza maphunzirowa anadzimvera okha mmene Makomiti a Nthambi amathandizira amishonale atsopano kuti azolowere utumiki wawo. Nthawi zambiri kuti amishonalewa atero, amayenera kuphunzira chikhalidwe cha m’maderawo chimene kwa azungu chingaoneke ngati chodabwitsa kwambiri. Mwachitsanzo, m’madera ena sizachilendo kuona amuna, ngakhale a Mboni za Yehova, akuyenda atagwirana manja posonyeza kuti n’ngogwirizana. M’madera ena oyang’aniridwa ndi ofesi ya nthambi ya ku Guam, anthu amadya zakudya zachilendo kwambiri. Komano ena anafika pongozolowera ndipo zimenezi zikusonyeza kuti amishonale atsopanowa angathenso kutero.

Guy Pierce, yemwe ali m’Bungwe Lolamulira, anakamba nkhani ya mutu wakuti “Khalani Okhulupirika ku ‘Ufumu wa Ambuye Wathu.’” Iye anauza anthuwo kuti: “Yehova anali n’cholinga polenga zinthu. Ndithu, sikuti Iye anangolenga zinthuzi popanda cholinga chilichonse. Cholinga chake polenga dzikoli sichinasinthe ayi. Chidzakwaniritsidwa mosapeneka ngakhale pang’ono. Palibe chingaletse zimenezi kuchitika.” (Genesis 1:28) Mbale Pierce analimbikitsa aliyense kuti akhale wokhulupirika pomvera ulamuliro wa Mulungu ngakhale kuti aliyense amakhudzidwa ndi mavuto obwera chifukwa cha tchimo la Adamu, munthu woyamba. Polimbikitsa anthuwo, Mbale Pierce anati: “Tikukhala m’nthawi yachiweruzo. Tatsala ndi nthawi yochepa kwambiri yoti tithandize anthu oona mtima kudziwa choonadi. Nthawi imeneyi tiigwiritsire ntchito bwino pouza ena uthenga wabwino.” Anthu amene akutumikira Ufumu wa Mulungu mokhulupirika asamakayike kuti Mulunguyo amawathandiza.​—Salmo 18:25.

Pomaliza mwambowu, tcheyamani anawerenga makalata a mafuno abwino ochokera ku maofesi a nthambi a padziko lonse. Kenaka anapereka masatifiketi kwa ophunzirawo, ndipo m’modzi mwa ophunzirawo anawerenga kalata imene ophunzira am’kalasiyo analemba poyamikira kwambiri zimene anaphunzirazo. Kalatayi inali njira yabwino kwambiri yomalizira mwambo wosaiwalikawu, kwa aliyense amene anauonera.

[Bokosi patsamba 23]

ZIWERENGERO ZA KALASI

Chiwerengero cha mayiko kumene ophunzira anachokera: 11

Chiwerengero cha mayiko kumene anawatumiza: 22

Chiwerengero cha ophunzira: 48

Avareji ya zaka zakubadwa: 34.8

Avareji ya zaka zimene akhala m’choonadi: 18.3

Avareji ya zaka zimene akhala mu utumiki wa nthawi zonse: 13.4

[Chithunzi patsamba 24]

Kalasi la nambala 117 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo

Pa m’ndandanda umene uli pansipa, mizera yayambira kutsogolo kupita kumbuyo, ndipo mayina tawandandalika kuyambira kumanzere kupita kumanja mumzera uliwonse.

(1) Thompson, E.; Norvell, G.; Powell, T.; Kozza, M.; McIntyre, T. (2) Reilly, A.; Clayton, C.; Allan, J.; Blanco, A.; Muñoz, L.; Rustad, N. (3) Guerrero, Z.; Garcia, K.; McKerlie, D.; Ishikawa, T.; Blanco, G. (4) McIntyre, S.; Cruz, E.; Guerrero, J.; Ritchie, O.; Avellaneda, L.; Garcia, R. (5) Powell, G.; Fiskå, H.; Muñoz, V.; Baumann, D.; Shaw, S.; Brown, K.; Brown, L. (6) Shaw, C.; Reilly, A.; Peloquin, C.; Münch, N.; McKerlie, D.; Ishikawa, K. (7) Münch, M.; Peloquin, J.; Kozza, T.; Avellaneda, M.; Allan, K.; Ritchie, E.; Norvell, T. (8) Cruz, J.; Baumann, H.; Clayton, Z.; Fiskå, E.; Thompson, M.; Rustad, J.