Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zinyama Zimalemekeza Yehova

Zinyama Zimalemekeza Yehova

Zinyama Zimalemekeza Yehova

ZINYAMA zimaonetsa ulemerero wa Yehova. Mulungu amasamalira zinyama, monganso mmene amasamalirira anthu. (Salmo 145:16) N’kulakwa kwambiri kum’pezera zifukwa Mlengi wa zinyamazi, yemwenso analenga ifeyo. Ngakhale kuti Yobu anali wosalungama, iye “anadziyesera yekha wolungama, osati Mulungu.” Motero Yobu anafunika kumuthandiza maganizo.​—Yobu 32:2; 33:8-12; 34:5.

Mulungu anam’patsa Yobu zitsanzo za zinyama pomusonyeza kuti anthu sangaloze cholakwa pa zochita za Mulungu. Mfundo imeneyi imaonekera bwino kwambiri tikaganizira zimene Yehova anauza mtumiki wakeyu.

Sizidalira Anthu

Yobu analephera kuyankha mafunso amene Mulungu anamufunsa okhudza zinyama. (Yobu 38:39-41) N’zoonekeratu kuti Yehova sathandizidwa ndi anthu kuti asamalire mikango ndiponso akhungubwi. Ngakhale kuti akhungubwi amafunafuna chakudya poulukira uku ndi uku, kwenikweni Mulungu ndi amene amawapatsa chakudya.​—Luka 12:24.

Yobu anangoti kakasi Mulungu atamufunsa za zinyama. (Yobu 39:1-8) Palibe munthu amene angateteze zinkhoma, kapena nswala zazikazi. Zinkhoma ndi nyama zovuta ngakhale kungoziyandikira chabe. (Salmo 104:18) Chifukwa cha nzeru zimene Mulungu anaipatsa, nswala yaikazi imadzipatula ikatsala pang’ono kubereka. Nswalayi imasamalira bwinobwino ana ake, koma anawo ‘akajintcha’ ‘amachoka osabwerera kwa amawo.’ Akatero amayamba kudziyang’anira okha.

Mbidzi zimangoyenda mmene zikufunira ku chipululu kumene zimakhala. Yobu sakanatha kuphunzitsa mbidzi kuti zizimunyamulira katundu. Mbidzi “ilondola chachiwisi chilichonse” pofunafuna chakudya m’mapiri. Nyama imeneyi siilola kuti igulitse ufulu wakewu pokakhala chiweto kumudzi kuti izipeza chakudya mosavuta. ‘Siimva kukuwa kwa wofulumiza nyama za m’goli,’ chifukwa choti imathawa mwamsanga munthu akaiyandikira.

Kenaka Mulungu anayamba kufotokoza za njati. (Yobu 39:9-12) Ponena za njati, katswiri wina wa mbiri yakale ku England, Austen Layard analemba kuti: “Zithunzi zakale za njati zimaonetsa kuti anthu ankaona kuti nyamayi n’njoopsa ngati mkango ndipo nayonso inkasakidwa kwambiri. Nthawi zambiri zithunzizo zimasonyeza mfumu ikulimbana ndi nyamayi, ndiponso ankhondo akuithamangitsa pa mahatchi ndiponso pansi.” (Linatero buku la Nineveh and Its Remains, 1849, Volume 2, tsamba 326) Koma palibe munthu wanzeru amene amayesa kuimika njati yoopsa yam’tchireyi.​—Salmo 22:21.

Mbalame Zimalemekeza Yehova

Kenaka Mulungu anafunsa Yobu kuti anenepo za mbalame. (Yobu 39:13-18) Chumba chimauluka m’mwamba kwambiri ndi mapiko ake amphamvu. (Yeremiya 8:7) Ngakhale kuti nthiwatiwa imakupiza mapiko ake, siitha kuuluka. Siimanga chisa mumtengo n’kumaikira mmenemo monga chimachitira chumba. (Salmo 104:17) Imakumba pamchenga n’kuikira pamenepo. Koma mbalameyi siisiya mazira akewo n’kuwaiwala. Imawakwirira mumchenga kuti asatenthedwe kapena kuzizidwa kwambiri ndipo imathandizana ndi yaimuna kusamalira mazirawo.

Mwina mungaganize kuti nthiwatiwa “anaimana nzeru” chifukwa choti ikaona chilombo choopsa imakhala ngati ikuthawa. Koma, buku la An Encyclopedia of Bible Animals linati: “[Nthiwatiwa] imachita zimenezi pofuna kuingitsa mdaniyo. Imakupiza mapiko ake kuti nyama kapena munthu aliyense amene akuiopseza aione n’kuchoka pa mazira akewo.”

Kodi nthiwatiwa ‘imaseka kavalo ndi wa pamsana pake’ m’njira yotani? Buku la The World Book Encyclopedia linati: “Nthiwatiwa siitha kuuluka, koma imathamanga liwiro la mtondowadooka. Ikamathamanga, imaponya miyendo yake yaitali mtunda woposa mamita anayi ndi theka sitepe lililonse, ndipo imatero pa liwiro la makilomita 64 pa ola limodzi.”

Mulungu Apatsa Kavalo Mphamvu

Kenaka Mulungu anafunsa Yobu za kavalo. (Yobu 39:19-25) Kale, ankhondo ankamenyana atakwera pa kavalo, ndipo akavalo ankakoka magaleta okhala ndi oyendetsa mmodzi mwinanso ndi asilikali awiri. Mtima wa kavalo wankhondo umakhala dyokodyoko pofuna kupita kunkhondo ndipo amalilima n’kumapalasa dothi. Sachita mantha ndipo sabwerera m’mbuyo poopa lupanga. Akamva kulira kwa lipenga, kavalo wankhondo amasangalala mokhala ngati akunena kuti, “Hee!” Amathamangira kutsogolo, ‘n’kumeza nthaka.’ Komatu chonsecho, kavalo wankhondoyu amamvera munthu amene wamukwera.

Katswiri wa mbiri yakale uja, Layard, analemba za kavalo kuti: “Akavalo akale a ku Arabiya anali omvera ngati mwana wankhosa, ndipo ankawawongolera ndi chingwe basi. Koma akavalowa akamva mkuwe wa nkhondo, n’kuona mkondo wanyezinyezi wa munthu amene wawakwera, maso awo ankasintha n’kuoneka psuu ngati moto, mphuno zawo zofiira zinkanyevuka, ndipo ankapendeketsa makosi awo, n’kukweza michira yawo m’mwamba ndipo ubweya wawo wapakhosi unkaimirira.”​—Linatero buku la Discoveries Among the Ruins of Nineveh and Babylon, 1853, tsamba 330.

Ganizirani za Kabawi ndi Chiwombankhanga

Kenaka Yehova anayamba kumuuza Yobu za mbalame zinazake. (Yobu 39:26-30) Akabawi ‘amatambasula mapiko awo kumka kumwera,’ kapena kuti komwe mphepo ikuchokera. Buku la The Guinness Book of Records linatchula mtundu winawake wa akabawi omwe amathamanga kwambiri kuposa mbalame zina zonse, n’kunena kuti liwiro la akabawiwa “limafika pachimake akamapita pansi kuchokera m’mwamba kwambiri panthawi imene akufuna kuti ena aone dera lawo, kapena akamathamangitsa mbalame inayake imene akufuna kuigwira.” Mbalamezi zimatha kuuluka liwiro lokwana mtunda wa makilomita 349 pa ola limodzi zikutsetsereka pansi.

Ziwombankhanga zimauluka liwiro lopitirira makilomita 130 pa ola limodzi. Yobu anayerekezera kufulumira kwa moyo ndi liwiro la chiwombankhanga chikamasaka nyama. (Yobu 9:25, 26) Mulungu amatipatsa mphamvu zoti tipirire, ngati kuti tikuuluka ndi mapiko a chiwombankhanga, omwe amaoneka ngati satopa. (Yesaya 40:31) Ziwombankhanga zikamauluka, zimagwiritsira ntchito mphepo yofunda. Mbalamezi zimazungulira pamene pakuwomba mphepo yofundayi ndipo mphepoyo imazinyamula mpaka kufika m’mwamba kwambiri. Chiwombankhanga chikafika pamwamba, chimangotsatira mphepo yofundayi moti chimatha kukhala mlengalenga kwa maola ambiri popanda kukupiza kwambiri mapiko.

Chiwombankhanga ‘chimamanga chisanja [kapena kuti chisa] chake m’mwamba’ mosafikirika, kuti ana ake akhale otetezeka. Yehova ndiye anapatsa chiwombankhanga nzeru zachibadwa zoterezi. Ndipo ndi amenenso anachilenga m’njira yoti ‘maso ake azitha kuchipenyetsa chili kutali.’ Chiwombankhanga chili ndi maso otha kuona nyama imene chikufuna kugwira kapena imene yafa kale ngakhale chili pamwamba kwambiri. Chiwombankhanga chimatha kudya nyama yakufa imene chapeza, moti “pomwe pali ophedwa, apo pali icho,” kapena kuti nachonso chimapezekapo. Chiwombankhanga chimagwira nyama zazing’ono n’kukadyetsa anapiye ake.

Yehova Analangiza Yobu

Asanapitirize kumufunsa mafunso okhudza zinyama, Mulungu analangiza kaye Yobu. Kodi zitatero Yobu anatani? Iye anadzichepetsa ndipo anamvera malangizo ena onse amene anapatsidwa.​—Yobu 40:1-14.

Pamenepa nkhani youziridwa ya Yobu, imatiphunzitsa mfundo yofunika kwambiri. Mfundo yake ndi iyi: Palibe munthu amene angakhale ndi mfundo zomveka zomupezera zifukwa Mulungu Wamphamvuyonse. Tiyenera kulankhula ndi kuchita zinthu m’njira yosangalatsa Atate wathu wakumwamba. Chifukwatu tiyenera kuganizira kwambiri za kuyeretsa dzina la Yehova ndi kukweza ulamuliro wake.

Mvuu Imalemekeza Mulungu

Mulungu anabwereranso ku nkhani ya zinyama ija ndipo anafunsa Yobu za mvuu. (Yobu 40:15-24) Mvuu ikakula imatha kutalika mamita 4 mpaka 5 ndipo imatha kulemera makilogalamu 3,600. “Mphamvu yake ili m’chuuno mwake,” kapena kuti m’mitsempha ya msana wake. Chikopa chochindikala cha pa mimba pake chimaithandiza kwambiri nyama yaifupi miyendoyi ikamayenda m’miyala m’mphepete mwa mitsinje. N’zoonekeratu kuti palibe munthu angaimitsane ndi mvuu, tikaganizira za kukula kwa chithupi chake, kukamwa kwake, ndiponso mphamvu za nsagwada zake.

Mvuu imatuluka m’madzi kuti ikadye “udzu” wobiriwira. Zimangokhala ngati kuti mvuu imafunika zomera za m’phiri lonse lathunthu kuti ikhute. Tsiku lililonse imadya zomera zolemera makilogalamu 90 mpaka mwina 180. Ikakhuta, mvuu imagona pansi pa mitengo yamthunzi monga misondozi. Mtsinje umene imakhalamo ukasefukira, mvuu imatha kutulutsa mutu n’kumasambira molowera kumene kukuchokera madzi amphamvu osefukirawo. Yobu akanakumana ndi chimvuu chitayasama kukamwa kwake n’kumaonetsa mano ake akuluakulu, omwe ndi oopsa, sakanayerekeza n’komwe kuchikola poponya mbedza kuti iboole mphuno yake.

Ng’ona Imatamanda Mulungu

Kenaka Mulungu anayamba kumuuza Yobu za ng’ona. (Yobu 41:1-34) Kodi Yobu akanatha kutenga ng’ona n’kuisandutsa choseweretsa ana? Ayi, sakanayerekeza dala kutero. Nthawi zambiri nyama imeneyi ikakumana ndi anthu imachita zinthu zoonetsa kuti n’njoopsa. Ndithudi, munthu atati ayese kulimbana ndi ng’ona, angakhaule kwambiri moti mwina kameneko kangakhale koyamba n’komaliza.

Ng’ona ikatukula mutu wake n’kutumphuka m’madzi m’mawa, maso ake amathwanima ngati “zikope za m’mawa,” kapena kuti cheza cha kuwala kwa mbandakucha. Mamba a ng’ona n’ngothithikana kwambiri ndipo chikopa chake chili ndi timafupa. Motero nthawi zina ngakhale zipolopolo zimakanika kulowa pa chikopachi, nanji malupanga kapena mikondo! Mamba a kumimba kwake ali ndi nsonga zakuthwa moti amasiya mkukuluzi wooneka ngati anadutsitsapo “chopunthira.” Ng’ona ikalilima ili pansi pa madzi, pamwamba pa madziwo pamaoneka thovu. Ndipo chifukwa cha kukula kwake ndi zida zake monga kukamwa kwake koopsa ndiponso mchira wake wamphamvu, ng’ona siiopa kanthu.

Yobu Anabweza Mawu

Yobu anavomereza kuti anayankhula ‘mosazindikira zodabwitsa zimene iyeyo sanazidziwe.’ (Yobu 42:1-3) Mulungu atamukonza pa zonena zake, iye anavomereza kulakwa kwake, ndipo anabweza mawu n’kulapa. Anzake anawadzudzula, koma iye anamudalitsa kwambiri.​—Yobu 42:4-17.

N’chinthu chanzeru kwambiri kukumbukira nkhani ya Yobuyi. Sitingathe kuyankha mafunso onse amene Mulungu anamufunsa. Koma tingathe kusonyeza kuyamikira zinthu zambiri zodabwitsa zachilengedwe zimene zimalemekeza Yehova ndipo tiyenera kutero.

[Chithunzi patsamba 13]

Chinkhoma

[Chithunzi patsamba 13]

Khungubwi

[Chithunzi patsamba 13]

Mkango waukazi

[Chithunzi patsamba 14]

Mbidzi

[Chithunzi patsamba 14]

Nthiwatiwa imasiya mazira ake, koma sikuti imawaiwala

[Chithunzi patsamba 14]

Mazira a nthiwatiwa

[Chithunzi pamasamba 14, 15]

Kabawi

[Mawu a Chithunzi]

Falcon: © Joe McDonald/​Visuals Unlimited

[Chithunzi patsamba 15]

Kavalo wa ku Arabiya

[Chithunzi patsamba 15]

Chiwombankhanga

[Chithunzi patsamba 16]

Mvuu

[Chithunzi patsamba 16]

Ng’ona