Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Musam’patse Malo Mdyerekezi

Musam’patse Malo Mdyerekezi

Musam’patse Malo Mdyerekezi

“Musam’patse mpata Mdyerekezi.”​—AEFESO 4:27, Byington.

1. N’chifukwa chiyani anthu ambiri amakayikira zoti Mdyerekezi aliko?

KWA zaka zambiri, anthu ankaganiza kuti Mdyerekezi ndi cholengedwa chofiira chokhala ndi nyanga ndi phazi ngati la ng’ombe, ndiponso chikukankhira anthu oipa mu helo wamoto pogwiritsa ntchito chifoloko. Baibulo siligwirizana ndi maganizo ngati amenewo. Ngakhale zili choncho, anthu mamiliyoni ambiri amakayikira zoti Mdyerekezi aliko kapena amaganiza kuti dzinalo limangoimira zoipa. Amatero chifukwa cha maganizo olakwika amenewa.

2. Kodi Malemba amati chiyani za Mdyerekezi?

2 Baibulo limapereka umboni wa munthu amene anaona Mdyerekezi ndi maso ndi umboni winanso wosatsutsika wakuti Mdyerekezi alikodi. Yesu Kristu anamuona kumalo a mizimu kumwamba ndipo analankhula naye ali padziko lapansi pano. (Yobu 1:6; Mateyu 4:4-11) Malemba satchula dzina loyambirira la mngelo woipayu koma amangoti iye ndi Mdyerekezi (kutanthauza “Wamiseche”) chifukwa wakhala akum’namizira Mulungu. Amatchedwanso kuti Satana (kutanthauza “Wotsutsa”), chifukwa amatsutsa Yehova. Satana Mdyerekezi amatchedwanso “njoka yokalambayo,” mwina chifukwa chakuti anagwiritsa ntchito njoka ponyenga Hava. (Chivumbulutso 12:9; 1 Timoteo 2:14) Amadziwikanso ndi mawu akuti “woipayo.”​—Mateyu 6:13. *

3. Kodi tikambirana funso liti?

3 Ifeyo atumiki a Yehova sitikufuna m’pang’ono pomwe kukhala ngati Satana, mdani wamkulu wa Mulungu yekha woona. Choncho, tiyenera kumvera langizo la mtumwi Paulo lakuti: “Musam’patse mpata Mdyerekezi.” (Aefeso 4:27, Byington) Nangano, kodi ndi makhalidwe ena ati amene Satana ali nawo amene sitiyenera kutengera?

Musatsanzire Mkulu wa Amiseche

4. Kodi “woipayo” anamudya miseche yotani Mulungu?

4 M’pake kuti “woipayo” amatchedwa Mdyerekezi, chifukwa ndi wamiseche. Miseche ndi kulankhula mabodza ndi mijedo pofuna kuipitsa mbiri ya wina. Mulungu analamula Adamu kuti: “Mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.” (Genesis 2:17) Hava anali atauzidwa zimenezi, koma Mdyerekezi, pogwiritsa ntchito njoka, anauza mkaziyo kuti: “Kufa simudzafai; chifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.” (Genesis 3:4, 5) Limeneli linali bodza lamkunkhuniza lonamizira Yehova Mulungu.

5. N’chifukwa chiyani Diotrefe anali ndi mlandu wodya ena miseche?

5 Aisrayeli analamulidwa kuti: “Usamayendayenda nusinjirira [kapena kunena miseche] mwa anthu a mtundu wako.” (Levitiko 19:16) Mtumwi Yohane ananena za wamiseche wina wa m’nthawi yake kuti: “Ndalemba kanthu kwa Mpingo; komatu Diotrefe uja, wofuna kukhala wamkulu wa iwo, satilandira ife. Momwemo, ndikadza ine, ndidzakumbutsa ntchito zake zimene achitazi, zakunena zopanda pake pa ife ndi mawu oipa.” (3 Yohane 9, 10) Diotrefe anali kumudya miseche Yohane ndipo anali ndi mlandu chifukwa cha zochita zakezo. Kodi ndi Mkristu wokhulupirika uti amene angafune kukhala ngati Diotrefe ndi kutsanzira Satana, mkulu wa amiseche?

6, 7. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kudya miseche anthu ena?

6 Kawirikawiri, anthu amawanenera zabodza atumiki a Yehova. “Ansembe aakulu ndi alembi anaimirira, nam’nenera [Yesu] kolimba.” (Luka 23:10) Mkulu wa Ansembe Hananiya ndi anthu ena anadya miseche Paulo. (Machitidwe 24:1-8) Ndipo Baibulo limanena za Satana kukhala “wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku.” (Chivumbulutso 12:10) Abalewo amene iye amawanenera zabodza ndi Akristu odzozedwa amene ali padziko lapansi pano masiku otsiriza ano.

7 Mkristu sayenera kukhala wamiseche kapena kunamizira anzake. Komatu, zimenezo n’zimene zingachitike ngati tipereka umboni wotsutsa munthu wina pamene sitikudziwa mfundo zonse za nkhaniyo. Malinga ndi Chilamulo cha Mose, munthu amene mwadala wapereka umboni wabodza anayenera kuphedwa. (Eksodo 20:16; Deuteronomo 19:15-19) Ndipo Yehova amanyansidwanso ndi “mboni yonama yonong’ona mabodza.” (Miyambo 6:16-19) Ndiyetu, tisatengere khalidwe la mkulu wa amiseche ndi wabodza uja.

Pewani Njira za Wambanda Woyambirira

8. Kodi Mdyerekezi anakhala bwanji “wambanda kuyambira pachiyambi”?

8 Mdyerekezi ndi wambanda. “Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi,” anatero Yesu. (Yohane 8:44) Kuchokera pachiyambi pamene anapatutsa Adamu ndi Hava kuwachotsa kwa Mulungu, Satana wakhala wambanda. Anadzetsa imfa pa iwo ndi ana awo. (Aroma 5:12) Onani kuti cholengedwa chamoyo ndicho chingathe kuchita zimenezi, osati mphamvu inayake yoipa.

9. Malinga ndi 1 Yohane 3:15, kodi zingatheke bwanji kuti tikhale ambanda?

9 “Usaphe.” Limatero limodzi la Malamulo Khumi amene Israyeli anapatsidwa. (Deuteronomo 5:17) Polembera Akristu, mtumwi Petro anati: “Asamve zowawa wina wa inu ngati wambanda.” (1 Petro 4:15) Chotero ife atumiki a Yehova sitingachite mbanda, kapena kuti kupha munthu. Ngakhale zili choncho, tingakhale ndi mlandu kwa Mulungu ngati tidana ndi Mkristu mnzathu n’kumalakalaka kuti iye atafa. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Yense wakudana ndi mbale wake ali wakupha munthu; ndipo mudziwa kuti wakupha munthu aliyense alibe moyo wosatha wakukhala mwa iye.” (1 Yohane 3:15) Aisrayeli analamulidwa kuti: “Usamamuda mbale wako mumtima mwako.” (Levitiko 19:17) Ndiye, tizifulumira kuthetsa mavuto alionse amene angakhalepo pakati pa ife ndi wokhulupirira mnzathu, kuti Satana wambanda uja asawononge umodzi wathu wachikristu.​—Luka 17:3, 4.

M’kaneni Zolimba Mkulu wa Bodza

10, 11. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tim’kane Satana, mkulu wa bodza?

10 Mdyerekezi ndi wabodza. “Pamene alankhula bodza,” anatero Yesu, “alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.” (Yohane 8:44) Satana ananamiza Hava, koma Yesu anadza m’dziko lapansi kudzapereka umboni wa choonadi. (Yohane 18:37) Kuti ife otsatira Kristu tim’kane Mdyerekezi, tipewe mabodza ndi chinyengo. ‘Tizinena choonadi.’ (Zekariya 8:16; Aefeso 4:25) “Yehova, Mulungu wa choonadi” amadalitsa Mboni zake zokhazo zimene zimalankhula zoona. Oipa alibe ufulu womuimira.​—Salmo 31:5; 50:16; Yesaya 43:10.

11 Ngati timanyadira ufulu wauzimu umene tili nawo chifukwa chomasuka ku mabodza a Satana, tidzamamatira Chikristu, chimene ndi “njira ya choonadi.” (2 Petro 2:2; Yohane 8:32) Ziphunzitso zonse zachikristu ndizo “choonadi cha Uthenga Wabwino.” (Agalatiya 2:5, 14) Ndipotu chipulumutso chathu chimadalira ‘kuyenda kwathu m’choonadi,’​—kuchimamatira ndi kum’kana “atate wake wa bodza.”​—3 Yohane 3, 4, 8.

Kanizani Mkulu wa Mpatuko

12, 13. Kodi ampatuko tiyenera kutani nawo?

12 Nthawi inayake mngelo amene anakhala Mdyerekezi anali m’choonadi. Koma “sanaima m’choonadi,” anatero Yesu, “pakuti mwa iye mulibe choonadi.” (Yohane 8:44) Mkulu wa mpatuko ameneyu wailimbikira njira yotsutsa “Mulungu wa choonadi.” Akristu ena oyambirira anakodwa mu “msampha wa Mdyerekezi,” mwina chifukwa chakuti anasokeretsedwa n’kupatuka pa choonadi. N’chifukwa chake Paulo analimbikitsa wantchito mnzake Timoteo kuwalangiza iwo mofatsa kuti achire mwauzimu n’kuwonjokamo mu msampha wa Satana. (2 Timoteo 2:23-26) Koma ndi bwino kwambiri ngati munthu nthawi zonse ungamamatire choonadi popanda kukopeka ndi maganizo ampatuko.

13 Popeza kuti banja loyamba linamvera Mdyerekezi ndipo silinakane mabodza ake, linakhala lampatuko. Ndiye, kodi ndi bwino kumvetsera kwa ampatuko, kuwerenga mabuku awo, kapena kufufuza zonena zawo pa Intaneti? Ngati timakonda Mulungu ndi choonadi, sitidzachita zimenezo. Tisalole ampatuko kulowa m’nyumba zathu kapena kuwapatsa moni, chifukwa tikatero ‘timayanjana nazo ntchito zawo zoipa.’ (2 Yohane 9-11) Tisagonjere machenjera a Mdyerekezi n’kusiyana nayo “njira ya choonadi” chachikristu n’kutsata aphunzitsi onyenga amene amafuna kuyambitsa “ziphunzitso zonama ndi zowononga” ndipo amayesa ‘kutidyera chuma chathu potiuza nkhani zongopeka.’​—2 Petro 2:1-3, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.

14, 15. Kodi Paulo anawachenjeza zoti chiyani akulu a ku Efeso ndi wantchito mnzake Timoteo?

14 Paulo anauza akulu achikristu a ku Efeso kuti: “Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang’anira, kuti muwete Eklesia wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa [Mwana wake]. Ndidziwa ine kuti, nditachoka ine, adzalowa mimbulu yosautsa, yosalekerera gululo; ndipo mwa inu nokha adzauka anthu, olankhula zokhotakhota, kupatutsa ophunzira awatsate.” (Machitidwe 20:28-30) Patapita nthawi, panabukadi ampatuko ngati amenewo ndipo ‘analankhula zokhotakhota.’

15 Cha m’ma 65 C.E., mtumwiyo analimbikitsa Timoteo ‘kulunjika nawo bwino mawu a choonadi.’ Paulo analemba kuti: “Koma pewa nkhani zopanda pake; pakuti adzapitirira kutsata chisapembedzo, ndipo mawu awo adzanyeka chilonda; a iwo ali Humenayo ndi Fileto; ndiwo amene adasokera kunena za choonadi, ponena kuti kuuka kwa akufa kwachitika kale, napasula chikhulupiriro cha ena.” Mpatuko unali utayamba kale! Paulo anawonjezera kuti: “Koma ndithu maziko a Mulungu aimika pokhazikika.”​—2 Timoteo 2:15-19.

16. Ngakhale kuti pali machenjera a mkulu wa mpatuko, n’chifukwa chiyani takhala okhulupirika kwa Mulungu ndi Mawu ake?

16 Nthawi zambiri Satana wagwiritsa ntchito ampatuko pofuna kuwononga kupembedza koona koma walephera. Cha m’ma 1868, Charles Taze Russell anayamba kuunika bwinobwino zinthu zomwe Matchalitchi Achikristu anakhala akuphunzitsa kwa nthawi yaitali ndipo anapeza kuti zinali zopotoza Malemba. Russell ndi anthu ena ochepa ofuna choonadi anapanga kagulu ka ophunzira Baibulo ku Pittsburgh, Pennsylvania, U.S.A. Pa zaka pafupifupi 140 chichokereni nthawiyo, atumiki a Yehova adziwa zambiri ndipo chikondi chawo pa Mulungu ndi Mawu ake chakula. Chifukwa chokhala maso mwauzimu, gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru lathandiza Akristu oona amenewa kukhala okhulupirika kwa Yehova ndi Mawu ake ngakhale pali machenjera a mkulu wa mpatuko.​—Mateyu 24:45.

Wolamulira wa Dzikoli Asakhale ndi Mphamvu pa Inu

17-19. Kodi dziko limene lili m’manja mwa Mdyerekezi ndi liti, ndipo n’chifukwa chiyani sitiyenera kulikonda?

17 Njira ina imene Satana amayesa kutikola nayo ndiyo kutikopa kuti tikonde dzikoli, kutanthauza anthu oipa otalikirana ndi Mulungu. Yesu anatcha Mdyerekezi “wolamulira wa dziko lapansi” ndipo anati: “Alibe mphamvu pa Ine.” (Yohane 14:30, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Satana asakhale ndi mphamvu pa ife! Koma tikudziwa kuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) N’chifukwa chake Mdyerekezi anati apatse Yesu “mayiko onse a dziko lapansi” ngati Yesuyo akanachita mpatuko kamodzi kokha mwa kum’gwadira. Koma Mwana wa Mulungu anakana zimenezo kwamtuwagalu. (Mateyu 4:8-10) Dziko limene Satana akulamulira limadana ndi otsatira a Kristu. (Yohane 15:18-21) M’pake kuti mtumwi Yohane anatichenjeza kuti tisakonde dzikoli.

18 Yohane analemba kuti: “Musakonde dziko lapansi, kapena za m’dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichili mwa iye. Pakuti chilichonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi. Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthawi zonse.” (1 Yohane 2:15-17) Tisakonde dziko lapansi, chifukwa moyo wake umakopa thupi lathu lochimwa ndipo umasemphana kotheratu ndi miyezo ya Yehova Mulungu.

19 Nanga bwanji ngati mtima wathu ukukonda dzikoli? Ndiye tipemphere kwa Mulungu kuti atithandize kugonjetsa chikondicho ndi zilakolako zake za thupi. (Agalatiya 5:16-21) Kunena zoona, ngati tikumbukira kuti makamu a mizimu yoipa ndi amene akulamulira dziko la anthu oipa, tidzayesetsa kukhala “wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.”​—Yakobo 1:27; Aefeso 6:11, 12; 2 Akorinto 4:4.

20. N’chifukwa chiyani tingati ‘sitili a dziko lapansi’?

20 Ponena za ophunzira, Yesu anati: “Siali a dziko lapansi monga Ine sindili wa dziko lapansi.” (Yohane 17:16) Akristu odzozedwa ndi anzawo odzipereka amayesetsa kukhala oyera m’makhalidwe ndi mwauzimu, kusiyana ndi dzikoli. (Yohane 15:19; 17:14; Yakobo 4:4) Dziko loipali limatida chifukwa timasiyana nalo ndipo ‘timalalikira chilungamo.’ (2 Petro 2:5) Inde, timakhala ndi anthu onse m’dzikoli, kuphatikizapo adama, achigololo, olanda, opembedza mafano, mbava, amabodza, ndi zidakwa. (1 Akorinto 5:9-11; 6:9-11; Chivumbulutso 21:8) Koma sitipuma nawo “mzimu wa dziko lapansi,” chifukwa sitilamulidwa ndi mphamvu yoipa imeneyi.​—1 Akorinto 2:12.

Musam’patse Malo Mdyerekezi

21, 22. Kodi mungagwiritse ntchito motani langizo la Paulo limene lili pa Aefeso 4:26, 27?

21 M’malo molamulidwa ndi “mzimu wa dziko lapansi,” ife timatsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu, umene umatithandiza kukhala ndi makhalidwe monga chikondi ndi kudziletsa. (Agalatiya 5:22, 23) Makhalidwe amenewa amatithandiza kulimbana ndi Mdyerekezi pamene ayesa kuwononga chikhulupiriro chathu. Iye akufuna kuti ‘tivutike mtima n’kuchita choipa,’ koma mzimu wa Mulungu umatithandiza ‘kuleka kupsa mtima, ndi kutaya mkwiyo.’ (Salmo 37:8) N’zoona kuti nthawi zina tingakwiye pachifukwa chabwino, koma Paulo akutilangiza kuti: “Kwiyani, koma musachimwe; dzuwa lisalowe muli chikwiyire, ndiponso musam’patse malo Mdyerekezi.”​—Aefeso 4:26, 27.

22 Ngati tikhalabe okwiya, tingachimwe. Mkwiyowo ungapatse Mdyerekezi mpata wobweretsa chisokonezo mu mpingo kapena kutisonkhezera kuchita zoipa. N’chifukwa chake ngati sitikumvana ndi ena, tifunika kuthetsa msanga vutolo mwa njira yaumulungu. (Levitiko 19:17, 18; Mateyu 5:23, 24; 18:15, 16) Choncho, tiyeni titsogozedwe ndi mzimu wa Mulungu, tikhale odziletsa ndipo tisalole ngakhale mkwiyo umene tili nawo pachifukwa chabwino kukhala dumbo, kapena chidani.

23. Kodi tidzakambirana mafunso otani m’nkhani yotsatira?

23 Takambirana makhalidwe ena a Mdyerekezi amene sitiyenera kutengera. Koma ena amene awerenga zimenezi angafunse kuti: Kodi Satana tizimuopa? Nanga n’chifukwa chiyani amasonkhezera anthu kuzunza Akristu? Ndipo tingachite chiyani kuti Mdyerekezi asatichenjerere?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Onani nkhani yoyambira pachikuto yakuti “Kodi Mdyerekezi Alikodi?” mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 2005.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kudya miseche aliyense?

• Malinga ndi 1 Yohane 3:15, kodi tingapewe bwanji kukhala opha munthu?

• Kodi ampatuko tiziwaona bwanji, ndipo chifukwa chiyani?

• N’chifukwa chiyani sitiyenera kukonda dziko lapansi?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 23]

Sitidzalola Mdyerekezi kuwononga umodzi wathu wachikristu

[Zithunzi patsamba 24]

N’chifukwa chiyani Yohane anatilimbikitsa kusakonda dziko lapansi?