Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuwomboledwa ndi ‘Mwazi wa Mtengo Wapatali’

Kuwomboledwa ndi ‘Mwazi wa Mtengo Wapatali’

“Tiyenera Kumvera Mulungu Koposa Anthu”

Kuwomboledwa ndi ‘Mwazi wa Mtengo Wapatali’

NJIRA yoposa zonse imene Yehova anasonyezera chikondi chake ndiyo kutumiza mwana wake wobadwa yekha kuti adzapereke moyo wake wangwiro kukhala dipo. Anthu ochimwafe tikufunikira kwambiri kuwomboledwa kotereku, chifukwa choti palibe munthu wopanda ungwiro amene angathe ‘kuwombola mbale wake, kapena kum’perekera dipo kwa Mulungu kuti akhale ndi moyo wosafa.’ (Salmo 49:6-9) Motero timayamikira kwambiri kuti Mulungu anapereka “Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.”​—Yohane 3:16.

Kodi dipo limatiwombola m’njira zotani? Tiyeni tione njira zinayi zimene tingapezere ufulu chifukwa cha chikondi chachikulu chimene Yehova Mulungu anasonyeza potipatsa dipo.

Kumasulidwa Chifukwa cha Dipo

Choyamba n’chakuti nsembe ya Yesu ingathe kutiwombola ku uchimo womwe tinatengera kwa makolo athu. Tonsefe timabadwa ochimwa. Inde, timakhala ochimwa ngakhale tisanafike potha kuphwanya malamulo a Yehova. Zimatheka bwanji? Lemba la Aroma 5:12 limati: “Uchimo unalowa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa mwa uchimo.” Poti ndife ana a Adamu, yemwe anachimwa, tonsefe tinatengera kupanda ungwiro kwake. Komabe, popeza kuti Kristu anatilipirira dipo tingathe kuwomboledwa ku uchimo umenewu. (Aroma 5:16) Yesu ‘analawa imfa m’malo mwa munthu aliyense,’ chifukwa anasenza zotsatirapo za uchimo m’malo mwa ana a Adamu.​—Ahebri 2:9; 2 Akorinto 5:21; 1 Petro 2:24.

Chachiwiri n’chakuti dipo lingathe kutimasula ku imfa, yomwe inabwera chifukwa cha uchimo. “Mphotho yake ya uchimo ndi imfa.” (Aroma 6:23) Chilango cha uchimo ndi imfa. Kudzera mwa imfa yake ya nsembe, Mwana wa Mulungu anachititsa kuti zikhale zotheka kwa anthu omvera Mulungu kukhala ndi moyo wosatha. Inde, “iye amene akhulupirira Mwanayo ali nawo moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo.”​—Yohane 3:36.

Onani kuti tikakhulupirira Mwana wa Mulungu m’pamene tingalanditsidwe ku zoopsa zobwera chifukwa cha uchimo. Kuti titero tiyenera kusintha moyo wathu kuti ukhale wogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Tiyenera kusiyiratu zoipa zonse zomwe tinali kuchita n’kuyesetsa kuchita zinthu zosangalatsa Mulungu. Mtumwi Petro ananena kuti tiyenera ‘kulapa, n’kubwerera kuti afafanizidwe machimo athu.’​—Machitidwe 3:19.

Chachitatu n’chakuti nsembe imene Yesu anapereka imatithandiza kukhala ndi chikumbumtima chabwino. Anthu onse amene amadzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa kukhala otsatira Mwana wake amapeza mpumulo. (Mateyu 11:28-30) Ngakhale kuti ndife anthu opanda ungwiro, timasangalala kwambiri potumikira Mulungu ndi chikumbumtima choyera. (1 Timoteo 3:9; 1 Petro 3:21) Tikaulula machimo athu n’kuwasiya, Yehova amatichitira chifundo ndipo timapeza mpumulo chifukwa choti chikumbumtima chimasiya kutipweteka.​—Miyambo 28:13.

Dipo Limatipatsa Thandizo ndi Chiyembekezo

Chotsiriza n’chakuti, tikakhulupirira dipo, timawomboledwa ku mantha oopa kuti mbiri yathu kwa Mulungu n’njoipa. Mtumwi Yohane anati: “Akachimwa wina, Nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu.” (1 Yohane 2:1) Ponena za unkhoswe wa Yesu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nawo moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.” (Ahebri 7:25) Panthawi yonse imene tili ndi uchimo, ngakhale utakhala wochepa motani, tidzafunikira kuthandizidwa ndi Mkulu wa Ansembe, Yesu Kristu kuti tikhale ndi mbiri yabwino ndi Mulungu. Kodi Yesu anakhala bwanji mkulu wa ansembe wathu?

Patatha masiku 40 Yesu ataukitsidwa, iye anapita kumwamba n’kukapereka kwa Mulungu mtengo wa “mwazi wa mtengo wake wapatali.” Motero, posachedwapa Yesu adzawombola ku uchimo ndi imfa anthu onse omvera. * (1 Petro 1:18, 19) Choncho, kodi simukuvomereza kuti Yesu Kristu tiyenera kumukonda ndi kumumvera?

Tiyeneranso kukonda ndi kulemekeza Yehova Mulungu. Iye, mwachikondi anakonza kuti ‘tiwombeledwe’ ndi dipo. (1 Akorinto 1:30) Chipanda Iyeyu ife sitikanakhala ndi moyo tili nawowu komanso sitikanakhala ndi chiyembekezo chilichonse chodzakhala ndi moyo wosatha. Motero m’pomveka kuti “tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.”​—Machitidwe 5:29.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Onani Kalendala ya Mboni za Yehova ya 2006, mwezi wa March ndi wa April.

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 9]

KODI MUKUDZIWA?

• Yesu anakwera kumwamba kuchokera pa phiri la Azitona.​—Machitidwe 1:9, 12.

• Atumwi a Yesu okhulupirika okha ndi amene anamuona akukwera kumwamba.​—Machitidwe 1:2, 11-13.