Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndife Otsimikiza Kutumikira Yehova

Ndife Otsimikiza Kutumikira Yehova

Mbiri ya Moyo Wanga

Ndife Otsimikiza Kutumikira Yehova

YOSIMBIDWA NDI RAIMO KUOKKANEN

Mu 1939, nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inayamba ku Ulaya, ndipo dziko la Soviet Union linaukira dziko lathu la Finland. Bambo anga anapita kukamenya nkhondo m’gulu la asilikali a dziko la Finland. Posakhalitsa ndege za nkhondo za asilikali a dziko la Russia zinayamba kuponya mabomba mumzinda umene tinali, ndipo mayi anga ananditumiza kwa agogo anga komwe kunalibe nkhondo.

MU 1971, ndinkachita utumiki wa umishonale ku Uganda, ku East Africa. Tsiku lina ndikulalikira khomo ndi khomo, ndinaona chigulu cha anthu chikudutsa mothamanga. Ndinamva kulira kwa mfuti ndipo ndinayamba kuthamangira kunyumba. Kulira kwa mfutiko kutayamba kuyandikira, ndinadumphira m’ngalande ya m’mphepete mwa msewu. Ndinayenda chokwawa kupita kwathu kwinaku zipolopolo zikuuluka m’mwambamu.

Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse sindikanatha kuithawa, koma n’chifukwa chiyani ineyo ndi mkazi wanga tinapita m’dziko la nkhondo yapachiweniweni ku East Africa? Yankho la funso limeneli lagona poti tinali ofunitsitsa kutumikira Yehova.

Chiyambi Chake

Ndinabadwa mu 1934 mu mzinda wa Helsinki, m’dziko la Finland. Bambo anga ankagwira ntchito yopenta nyumba, ndipo tsiku lina anakagwira ntchito pa nyumba yomwe inali ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Finland. A Mboni za Yehova anawauza bambo angawo za misonkhano yawo. Bambo atafika kunyumba anauza mayi za misonkhanoyo. Mayi sanayambe kupita kumisonkhanoko panthawiyo, koma pambuyo pake anayamba kukambirana nkhani za m’Baibulo ndi mnzawo wakuntchito, yemwe anali wa Mboni. Iwo anayamba kugwiritsa ntchito zimene ankaphunzirazo, ndipo mu 1940 anabatizidwa n’kukhala a Mboni za Yehova.

Mayi atangotsala pang’ono kubatizidwa, mayi awo anapita nane kumudzi kwawo pa nthawi yonse ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Ndiye mayi anga ali ku Helsinki anayamba kulemberana makalata ndi agogo angawa komanso ndi agogo anga aang’ono n’kumawauza za zikhulupiriro za Mboni za Yehova. Onse anachita chidwi ndipo anayamba kundiuza zimene anali kuphunzira. Atumiki oyendayenda a Mboni za Yehova anafika kunyumba kwa agogo anga aja n’kutilimbikitsa, koma ine ndinali ndisanatsimikizebe mtima kutumikira Mulungu.

Ndinayamba Kuphunzira za Mulungu

Nkhondo itatha mu 1945, ndinabwerera ku Helsinki ndipo mayi anayamba kupita nane ku misonkhano ya Mboni za Yehova. Nthawi zina ndinkajomba n’kupita kukaonera filimu. Komabe mayi ankadzandiuza nkhani imene inakambidwa kumsonkhanoko, ndipo kawirikawiri ankakonda kundiuza kuti Armagedo yayandikira. Zimenezi zinandifika pamtima ndipo ndinasiya kujomba kumisonkhano. Nditayamba kumvetsa choonadi cha m’Baibulo, ndinayamba kufuna kumachita nawo zinthu zonse zochitika mumpingo.

Chinkandisangalatsa kwambiri chinali misonkhano yaikulu yosiyanasiyana. Mu 1948, ndinapita ku msonkhano wa chigawo umene unachitikira kufupi ndi kunyumba kwa agogo anga, komwe ndinakachitira holide yaikulu. Mnzanga wina anabatizidwa pamsonkhano umenewu, ndipo asanabatizidwe anandipempha kuti nanenso ndibatizidwe. Ndinamuuza kuti sindinabweretse malaya oti ndingavale pobatizidwa, koma iye anati ndingathe kubwereka malaya ake iyeyu akabatizidwa. Ndinavomera ndipo ndinabatizidwa pa June 27, 1948, ndili ndi zaka 13.

Msonkhanowo utatha, anzawo ena a mayi anga anawauza kuti ndabatizidwa. Kenaka nditakumana nawo, anandifunsa kuti podziwa kuti kubatizidwa si nkhani yamasewera, n’chifukwa chiyani ineyo ndabatizidwa osawafunsa kaye iwowo. Ndinawauza kuti ndinali nditamvetsa mfundo zofunika kwambiri za m’Baibulo ndi kuti ndinkadziwa kuti Yehova akuona zochita zanga.

Ndinayamba Kulimbikira

Abale mumpingo anandithandiza kukhala otsimikiza kwambiri kutumikira Yehova. Ankapita nane mu utumiki wa nyumba ndi nyumba ndipo pafupifupi mlungu uliwonse ankandipatsa nkhani pa misonkhano. (Machitidwe 20:20) Ndili ndi zaka 16, ndinakamba nkhani ya onse, kwa nthawi yoyamba. Posakhalitsa anandisankha kukhala mtumiki wa phunziro la Baibulo mumpingo wathu. Kuchita zinthu zauzimu zonsezi kunandithandiza kukhwima maganizo, komabe ndinali ndisanathetse mantha anga oopa anthu.

Masiku amenewo, nkhani za onse za m’misonkhano ikuluikulu tinkazilengeza povala zikwangwani ziwiri zikuluzikulu. Tinkazikoleka m’khosi ndipo chimodzi chinkakhala kumaso pamene chinacho kumsana. Motero anthu ena ankatinena kuti ndife anthu ooneka ngati masangweji.

Panthawi ina, nditakolekera zikwangwani zanga n’kuima pakona pa msewu winawake wosadutsa anthu ambiri, ndinaona gulu la anzanga a kusukulu akubwera poteropo. Akuyandikira, ndinachita mantha kwambiri kuona mmene ankandiyang’anira. Ndinapemphera kuti Yehova andilimbitse mtima ndipo ndinangoima njoo ndi zikwangwani zangazo. Kulimba mtima kumeneku posaopa anthu kunandithandiza kukhala wokonzeka kulimbana ndi chiyeso chachikulu chokana kulowerera m’zandale poti ndine Mkristu.

Patapita nthawi, boma linandikakamiza kukalembetsa usilikali pamodzinso ndi anyamata ena angapo a Mboni. Tinapita ku likulu la asilikaliwo, monga anatiuzira, koma mwaulemu tinakana kuvala yunifolomu yawo. Anatimanga, ndipo posakhalitsa akhoti analamula kuti tikhale m’ndende kwa miyezi sikisi. Anatimanganso kwa miyezi isanu ndi itatu imene ankakakamiza munthu kukhala msilikali. Motero tinakhala m’ndende kwa chaka ndi miyezi iwiri chifukwa chokana kulowerera m’ndale.

M’ndendemo tinkakumana tsiku lililonse n’kumawerenga Baibulo. Pa miyezi imeneyo, ambiri mwa ife tinawerenga Baibulo lonse kawiri. Atatimasula ambirife tinali otsimikiza kwambiri kutumikira Yehova koposa kale lonse. Mpaka panopo, ambiri mwa anyamata a Mboni amenewo akutumikira Yehova mokhulupirika.

Titachoka kundende, ndinabwereranso kunyumba kwa makolo anga. Posakhalitsa ndinadziwana ndi Veera, mtsikana wa Mboni wolimbikira yemwe anali atabatizidwa chaposachedwa. Tinakwatirana mu 1957.

Tsiku Limene Linasintha Moyo Wanga

Tsiku lina madzulo titapita kunyumba kwa abale ena amaudindo ku ofesi ya nthambi, mmodzi wa abalewa anatifunsa ngati tingafune kuyamba ntchito yadera. Titapemphera usiku wonse, ndinaimba foni ku ofesi ya nthambi n’kuwauza kuti tavomera. Kuti tiyambe utumiki wa nthawi zonse ndinayenera kusiya ntchito yanga, yomwe inali ya malipiro abwino kwambiri, koma tinkafunitsitsa kuika patsogolo zinthu za Ufumu m’moyo wathu. Pamene tinayamba utumiki woyendayenda mu December 1957, ineyo ndinali ndi zaka 23 ndipo Veera anali ndi zaka 19. Tinayendera ndi kulimbikitsa mipingo ya anthu a Yehova ku Finland kwa zaka zitatu.

Cha kumapeto kwa m’ma 1960, ndinalandira kalata yoitanidwa ku Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo ku Brooklyn, mumzinda wa New York. Abale atatu ochokera ku Finland tinaitanidwa kukachita maphunziro a miyezi teni a kayendetsedwe ka ofesi ya nthambi. Akazi athu anatsala ndipo ankagwira ntchito pa ofesi ya nthambi ya ku Finland.

Maphunzirowa atangotsala pang’ono kutha, ndinaitanidwa kuti ndikaonekere ku ofesi ya mbale Nathan H. Knorr, amene panthawiyo anali kuyang’anira ntchito ya Mboni za Yehova padziko lonse. Mbale Knorr anandipatsa ntchito yokachita umishonale m’dziko la Malagasy Republic, lomwe masiku ano likutchedwa kuti Madagascar. Ndinam’lembera kalata Veera, kumufunsa ngati angavomere kukachita utumiki umenewu, ndipo anayankha mwamsanga kuti, “Inde.” Nditabwerera ku Finland, tinakonzekera msangamsanga zosamukira ku Madagascar.

Tinapeza Chimwemwe Komanso Zokhumudwitsa

Mu January 1962, tinakwera ndege kupita ku Antananarivo, likulu la dzikolo, titavala zipewa za ubweya ndi makhoti otentha, chifukwa choti tinachoka ku Finland m’nyengo yozizira. Poti ku Madagascar n’kotentha, tinasintha msangamsanga kavalidwe kathu. Nyumba yathu yoyamba yaamishonale inali yaing’ono, ya chipinda chimodzi basi. Kunali kale banja limodzi la amishonale, motero ine ndi Veera tinkagona pa khonde lokhala ndi mpanda ndiponso denga.

Tinayamba kuphunzira Chifalansa, chomwe chili chizungu cha ku Madagascar. Zinali zovuta chifukwa choti Mlongo Carbonneau ankatiphunzitsa m’Chingelezi koma mkazi wanga Veera sankadziwa Chingelezi. Motero ineyo ndinkamasulira m’Chifinishi zonse zimene mlongoyu ankanena. Kenaka tinaona kuti Veera ankamvetsa bwino zinthu zokhudza malamulo a chinenero ndikamulongosolera m’Chiswidishi, motero ndinkamulongosolera malamulo a Chifalansa m’Chiswidishi. Posakhalitsa tinayamba kuchidziwa Chifalansa, ndipo tinayamba kuphunzira chinenero cha kumeneku, chotchedwa Malagasy.

Munthu amene anali woyamba kuphunzira naye Baibulo ku Madagascar ankalankhula chinenero chokhachi basi. Ndinkati ndikapeza vesi m’Baibulo langa la Chifinishi, tinkafufuzanso vesilo m’Baibulo la chinenero chakecho. Sindinkatha kumufotokozera malemba bwinobwino, koma posakhalitsa munthuyu anayamba kukonda kwambiri choonadi cha m’Baibulo, moti mpaka anabatizidwa.

Mu 1963, Mbale Milton Henschel anabwera ku Madagascar kuchoka ku likulu la Mboni za Yehova ku Brooklyn. Posakhalitsa, anakhazikitsa ofesi ya nthambi yatsopano ku Madagascar, ndipo ineyo anandiika kukhala woyang’anira ofesi ya nthambiyo, kuphatikiza pa ntchito yanga yoyang’anira madera ndi zigawo. Panthawi yonseyi, Yehova anatidalitsa kwambiri. Kuchokera mu 1962 mpaka mu 1970, ofalitsa a Ufumu anawonjezeka kuchoka pa 85 kufika pa 469.

Tsiku lina mu 1970, titabwera kolalikira, tinapeza chikalata pakhomo pathu, chouza amishonale onse a Mboni za Yehova kuti akapezeke ku ofesi ya nduna yoona nkhani za boma. Kumeneko anakatiuza kuti boma lalamula kuti tichoke m’dzikomo nthawi yomweyo. Nditafunsa kuti ndalakwa chiyani, mkulu wa kumeneko anati: “Bambo Kuokkanen, palibe chimene mwalakwa.”

Ndiye ndinati: “Takhala m’dziko lino kwa zaka eyiti. Kuno kwasanduka kwathu tsopano. Sitingachoke mwadzidzidzi chonchi ayi.” Zonsezi sizinaphule kanthu, moti amishonale onse anachoka m’dzikoli mlungu womwewo. Anatseka ofesi ya nthambi, ndipo Mboni ina ya kumeneku inayamba kuyang’anira ntchito yolalikira. Tisanasiyane nawo abale athu a ku Madagascar, tinapatsidwa gawo lina lokatumikirako, ku Uganda.

Kuyambanso Gawo Lina Latsopano

Patatha masiku angapo chichokereni ku Madagascar, tinafika mu mzinda wa Kampala, womwe ndi likulu la dziko la Uganda. Nthawi yomweyo tinayamba kuphunzira Chiluganda, chomwe n’chinenero chomveka ngati ukuyimba nyimbo, koma chovuta kwambiri kuphunzira. Amishonale ena anam’thandiza Veera kuphunzira kaye Chingelezi, ndipo tinalalikira bwino kwambiri m’chinenero chimenechi.

Chifukwa choti ku Kampala n’kotentha zedi, Veera anayamba kudwaladwala. Motero anatipatsa gawo la m’tauni yotchedwa Mbarara, komwe n’kozizirirako. Ifeyo tinali a Mboni oyamba kupita kumeneko, ndipo zimene tinakumana nazo m’munda tsiku lathu loyamba zinali zolimbikitsa kwambiri. Ndikulankhula ndi munthu winawake m’nyumba mwake, mkazi wake anabwera kuchokera ku khitchini. Dzina lake anali Margaret ndipo ankamvetsera zonse zimene ineyo ndimanena. Veera anayamba kuphunzira Baibulo ndi Margaret, ndipo anapita patsogolo kwambiri. Kenaka anabatizidwa n’kukhala wofalitsa wakhama kwambiri.

Nkhondo Yapachiweniweni

Mu 1971 nkhondo yapachiweniweni inasokoneza mtendere umene tinali nawo ku Uganda. Tsiku lina nkhondoyi inafika cha kufupi ndi nyumba yathu ya amishonale ku Mbarara. Panthawiyi m’pamene ndinaona zimene ndalongosola kumayambiriro kwa nkhani ino.

Pofuna kuti asilikali asandione ndinayenda mtunda wautali chokwawa m’ngalande mokhamokha mpaka kukafika kunyumba yathu ya amishonale ndipo ndinapeza Veera atafika kale. Pa kona m’nyumbayo, tinamanga malo athu obisalapo pogwiritsa ntchito matiresi, mabedi ndi mipando. Sitinatuluke m’nyumbamo kwa mlungu wathunthu, ndipo tinkangomvetsera nkhani pa wailesi. Nthawi zina zipolopolo zinkawomba khoma ifeyo n’kuthawa chokwawa kubisala pa malo athu aja. Usiku, sitinkayatsa nyali, kuti asadziwe zoti m’nyumbamo muli anthu. Nthawi ina asilikali anafika panyumbapo n’kuyamba kugogoda chitseko cha kumaso. Tonse tinangokhala duu, n’kumapemphera kwa Yehova cha mumtima. Atasiya kumenyanaku, anthu amene tinkakhala nawo pafupi anabwera kudzatithokoza kuti tawapulumutsa. Iwo ankaona kuti Yehova wawateteza pamodzi ndi ifeyo, ndipo tinavomerezana nawo.

Zinthu zinali bwino mpaka tsiku lina m’mawa pamene tinamva pawailesi kuti boma la Uganda laletsa gulu la Mboni za Yehova. Muulutsi wa pa wailesi anati a Mboni za Yehova onse ayenera kubwerera ku zipembedzo zawo zakale. Ndinayesetsa kulankhulana ndi akuluakulu aboma pankhaniyi koma sizinaphule kanthu. Kenaka ndinapita ku ofesi ya Pulezidenti Idi Amin n’kupempha kuti ndikufuna kukumana naye. Wolonjera alendo mu ofesiyo anandiuza kuti pulezidenti watanganidwa kwambiri. Ndinapitako nthawi zambirimbiri, koma pulezidentiyo sindinaonane naye. Mapeto ake, mu July 1973 tinachoka ku Uganda.

Chaka Chimodzi Chinakhala Zaka Teni

Atatithamangitsa ku Uganda tinalinso achisoni kwambiri posiyana ndi abale athu kumeneko monga mmene tinachitira atatithamangitsa ku Madagascar. Tisanapite ku gawo lathu latsopano ku Senegal, tinapita ku Finland. Koma tili ku Finland tinauzidwa kuti zopita ku Senegal zija zalephereka, motero anatiuza kuti tikhale ku Finland komweko. Zitatero tinaona ngati kuti ntchito yathu ya umishonale yathera pompo. Ku Finland, tinatumikira mu ntchito ya upainiya wapadera ndipo kenaka tinatumikira mu ntchito yadera.

Pofika m’chaka cha 1990 ntchito yathu inali itatsegulidwa ku Madagascar, ndipo tinadabwa kuuzidwa ndi likulu ku Brooklyn kuti tipite ku Madagascar kukakhala amishonale kwa chaka chimodzi. Tinafuna kupita koma tinali ndi mavuto awiri akuluakulu. Bambo anga ankafunika chisamaliro chifukwa cha ukalamba, ndipo Veera anali wodwaladwala. Ndinamva chisoni kwambiri bambo anga atamwalira mu November 1990, koma Veera anayamba kupezako bwino moti tinayamba kuganiza zoti mwina tingakwanitsenso ntchito yaumishonale. Tinabwerera ku Madagascar mu September 1991.

Tinapita ku Madagascar tikuganiza kuti tikakhalako chaka chimodzi, koma tinakhalako zaka teni. Panthawiyi, ofalitsa anawonjezeka kuchokera pa 4,000 kufika pa 11,600. Ndinasangalala kwambiri kuchita ntchito yaumishonale. Koma nthawi zina ndinkafooka poganiza kuti mwina ndikunyalanyaza mkazi wanga posakhala naye kwa nthawi zonse n’kumamulimbikitsa. Yehova anatilimbikitsa tonse awiri kuti tipitebe patsogolo. Potsiriza pake, mu 2001 tinabwerera ku Finland, komwe takhala tikugwira ntchito pa ofesi yanthambi. Panopo tikuchitabe mwakhama zinthu za Ufumu ndipo timaganizirabe kwambiri za ku Africa. Ndife ofunitsitsa kwambiri kuchita chifuniro cha Yehova kulikonse kumene angatitumizeko.​—Yesaya 6:8.

[Mapu patsamba 12]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

FINLAND

ULAYA

[Mapu patsamba 14]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

AFRICA

MADAGASCAR

[Mapu patsamba 15]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

AFRICA

UGANDA

[Chithunzi patsamba 14]

Tsiku la ukwati wathu

[Zithunzi pamasamba 14, 15]

Kuchoka ku ntchito yadera ku Finland, mu 1960 . . .

. . .  kupita ku ntchito yaumishonale ku Madagascar, mu 1962

[Chithunzi patsamba 16]

Ineyo ndi Veera panopo