Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi udindo wa mpingo n’ngotani Mkristu amene anali kuyendetsa galimoto akachita ngozi anthu ena n’kufapo?

Mpingo uyenera kuona ngati dalaivala ali ndi mlandu wakupha pofuna kupewa kuti mpingo wonse ukhale ndi mlandu wakupha. (Deuteronomo 21:1-9; 22:8) Dalaivala amene wachita ngozi yomwe anthu ena afapo, angakhale ndi mlandu wakupha ngati anali kuyendetsa mosasamala kapena ngati anaswa mwadala malamulo a Kaisara kapena malamulo a pamsewu oteteza ngozi. (Marko 12:14) Komabe, pali mfundo zinanso zofunika kuziganizira.

Munthu wopha mnzake n’kuthawira ku umodzi mwa midzi yopulumukirako ku Israyeli ankafunika kuzengedwa mlandu. Ngati am’peza kuti anapha mnzakeyo mwangozi, ankaloledwa kukhala m’mudziwo, ndipo wolipsira mwazi sakanam’chita chilichonse. (Numeri 35:6-25) Motero, ngati Mkristu waphetsa munthu pangozi, akulu ayenera kufufuza nkhaniyo ndi kuona ngati ali ndi mlandu wakupha. Sikuti maganizo a boma kapena chigamulo cha akhoti pazokha n’zimene zingathandize mpingo kudziwa zoti uchite ayi.

Mwachitsanzo, khoti lingapeze kuti munthu ali ndi mlandu wa kuswa malamulo a pamsewu, koma mwina akulu omwe akufufuza nkhaniyo angaone kuti palibe mlandu wakupha, chifukwa chakuti zinali zovuta kwambiri kuti dalaivalayo apewe ngoziyo kapenanso zinali zosatheka n’komwe kuipewa. Komanso, ngakhale akhoti atagamula kuti munthu alibe mlandu, mwina akuluwo angam’peze ndi mlandu wakupha.

Akulu ofufuza nkhaniyo ayenera kusankha zochita mogwirizana ndi Malemba ndiponso mfundo zina zotsimikizika bwino. Mfundo zake zingakhale monga izi, dalaivala kuvomera yekha kuti ndi wolakwa, umboni wa anthu odalirika awiri kapena atatu omwe anaona ngoziyo ikuchitika, kapena zonse ziwirizi pamodzi. (Deuteronomo 17:6; Mateyu 18:15, 16) Ngati papezeka kuti munthu ali ndi mlandu wakupha, komiti ya chiweruzo iyenera kupangidwa. Ngati komitiyo yaona kuti munthu yemwe ali ndi mlandu wakuphayo ndi wolapa, ayenera kudzudzulidwa mogwirizana ndi Malemba ndipo sangapatsidwe mwayi wochita nawo zinthu zina mu mpingo. Sangakhalenso mkulu kapena mtumiki wothandiza. Angathenso kupatsidwa ziletso zina ndi zina. Ndipo ali ndi mlandu kwa Mulungu chifukwa cha kusasamala, kapena kunyalanyaza kwake komwe kwachititsa ngozi imene pafa anthu.​—Agalatiya 6:5, 7.

Tipereke chitsanzo ichi: Ngati nyengo sinali bwino panthawi ya ngoziyo, dalaivalayo anafunika kuyendetsa mosamala kwambiri. Ngati anali ndi tulo, anayenera kuima ndi kupumula mpaka tuloto titam’thera, kapena akanapatsa wina kuti ayendetse galimotoyo.

Tiyerekeze kuti dalaivalayo anali kuthamanga kwambiri. Mkristu aliyense akapitirira mlingo wa liwiro loyenera kuyendetsera galimoto, amakhala akulephera ‘kupatsa Kaisara, zake za Kaisara.’ Komanso zimasonyeza kuti amanyalanyaza mfundo yakuti moyo ndi wopatulika, chifukwa chakuti n’zotheka kuti mwa zochita zakezo aphetse anthu. (Mateyu 22:21) Taonani mfundo inanso pankhani imeneyi. Kodi mkulu angakhale akusonyeza chitsanzo chotani kwa nkhosa ngati sasamala malamulo a pamsewu a Kaisara kapena ngati akuchita kuwaswa mwadala?​—1 Petro 5:3.

Akristu asamapemphe anzawo kuti afike pamalo enaake pamene zili zoonekeratu kuti sangathe kutero popanda kuswa malamulo othamangitsira galimoto pamsewu. Koma nthawi zambiri, pamangofunika kunyamuka mwamsanga kapena kusintha nthawi n’cholinga chokhala ndi nthawi yokwanira yoyendera. Mkristu akachita zimenezo, sangakakamizike kuthamangitsa kwambiri galimoto, m’malo mwake angathe kutsatira malamulo a pamsewu oikidwa ndi “maulamuliro a akulu,” kapena kuti boma. (Aroma 13:1, 5) Izi zingathandize dalaivala kusamala kuti asachite ngozi yophetsa anthu, mpaka mwina kukhala ndi mlandu wakupha. Komanso zingam’thandize kusonyeza chitsanzo chabwino ndiponso kukhala ndi chikumbumtima chabwino.​—1 Petro 3:16.