Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zazikulu za M’buku la Mlaliki

Mfundo Zazikulu za M’buku la Mlaliki

Mawu a Yehova Ndi Amoyo

Mfundo Zazikulu za M’buku la Mlaliki

YOBU anati: “Munthu wobadwa ndi mkazi ngwa masiku owerengeka, nakhuta mavuto.” (Yobu 14:1) Ndi bwinotu kusawononga moyo wathu waufupiwu poganizira ndiponso kuchita zinthu zopanda ntchito. Koma kodi ndi zinthu zotani zimene tiyenera kutherapo nthawi yathu, mphamvu zathu, ndiponso zinthu zathu? Nanga ndi zinthu zotani zimene tiyenera kuzipewa? Mawu anzeru olembedwa m’buku la m’Baibulo la Mlaliki amapereka malangizo odalirika pa nkhaniyi. Uthenga wa m’malangizowa ‘umathanso kuzindikira malingaliro ndi zolinga za mtima’ ndipo ungatithandize kukhala ndi moyo wosangalatsa.​—Aheberi 4:12.

Buku la Mlaliki linalembedwa ndi Mfumu Solomo wa ku Isiraeli wakale, munthu wodziwika chifukwa cha nzeru zake, ndipo lili ndi malangizo othandiza munthu kudziwa zinthu zimene zili zopindulitsadi pa moyo ndi zimene zili zopanda phindu. Popeza kuti Solomo akutchula m’buku la Mlaliki za nyumba zina zimene anamanga, ayenera kuti analemba bukuli atamaliza kumanga nyumbazo koma asanapatuke pa kulambira koona. (Nehemiya 13:26) Izi zikutanthauza kuti analemba bukuli chaka cha 1000 B.C.E. chisanakwane, cha kumapeto kwa ulamuliro wake wa zaka 40.

KODI N’CHIYANI CHIMENE SICHILI CHACHABE?

(Mlaliki 1:1–6:12)

“Zonse ndi chabe,” anatero mlaliki, ndipo anafunsa kuti: “Kodi ntchito zake zonse munthu asauka nazo zim’pindulira chiyani? . . . Palibe kanthu katsopano pansi pano. Ndaona ntchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi chabe ndi kungosautsa mtima.” (Mlaliki 1:2, 3, 9, 14) Mawu akuti “chabe” ndi “pansi pano” kapenanso “kunja kuno” amapezeka kambirimbiri m’buku la Mlaliki. Mawu a Chiheberi otanthauza kuti “chabe” kwenikweni amatanthauza “mpweya” kapena “nthunzi” ndipo amasonyeza kuti chinthucho n’chopanda ntchito, n’chosakhalitsa, kapena n’chosapindulitsa kwa nthawi yaitali. Mawu akuti “pansi pano” kapena “kunja kuno” amatanthauza “padziko lapansi pano” kapena “m’dzikoli.” Motero, zonse, kapena kuti zinthu zonse zimene anthu amachita mosaganizira chifuniro cha Mulungu, n’zachabe.

Solomo anati: “Samalira phazi lako popita ku nyumba ya Mulungu; [ndipo pakhale] kuyandikira kumvera.” (Mlaliki 5:1) Kuchita zinthu zokhudza kulambira koona kwa Yehova Mulungu si kwachabe. Kwenikweni, kuganizira za ubwenzi wathu ndi iye ndiyo njira yokhalira ndi moyo wopindulitsa.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

1:4-10​—Kodi zinthu zochitika mobwerezabwereza zam’chilengedwe “n’zolemetsa” m’njira yotani? Mlaliki akutchula zitatu zokha mwa zinthu zikuluzikulu zimene zimathandiza kuti padziko pano pakhale moyo. Zinthu zake ndi dzuwa, kayendedwe ka mphepo, ndi kayendedwe ka madzi kobwerezabwereza. Kwenikweni, zinthu zochitika mobwerezabwereza m’chilengedwe n’zambiri, ndipo n’zovuta kwambiri kuzimvetsa. Munthu angathe moyo wake wonse akuzifufuza komabe osazimvetsa. Zimenezi zingakhaledi “zolemetsa.” Komanso n’zofooketsa kuyerekezera moyo wathu waufupiwu ndi kubwerezabwereza kosatha kwa kayendedwe ka zinthu zam’chilengedwezi. Ngakhale kuyesa kutulukira zinthu zatsopano n’kolemetsa. Chifukwatu zinthu zatsopano zimene anthu amatulukira, kwenikweni zimakhala zozikidwa pa mfundo zimene Mulungu woona anakhazikitsa ndipo wazigwiritsirapo kale ntchito m’chilengedwe.

2:1, 2—N’chifukwa chiyani akunena kuti kuseka ndi “misala?” Kuseka kungatithandize kuiwala mavuto athu kwakanthawi, ndipo kusangalala kungachititse kuti mavuto athu tisawaone ngati aakulu kwambiri. Komabe, kuseka sikuchotsa zovuta zathu. N’chifukwa chake akuti kuganiza kuti kuseka kungam’pezetse munthu chimwemwe ndi “misala.”

3:11—Kodi n’chiyani chimene Mulungu “anachikongoletsa pa mphindi yake”? Zinthu zina zimene Yehova Mulungu ‘anazikongoletsa,’ kapena kuti kuzipanga moyenerera ndi mopindulitsa panthawi yake ndizo kulengedwa kwa Adamu ndi Hava, pangano la utawaleza, pangano limene anapanga ndi Abrahamu, pangano la Davide, kubwera kwa Mesiya, ndi kulongedwa ufumu kwa Yesu Khristu monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Komabe pali chinthu chinanso chimene Yehova ‘achikongoletse’ posachedwapa. Chinthu chake ndicho dziko latsopano lolungama lomwe lifike panthawi yake yoyenera, ndipo tisakayike za zimenezi ayi.​—2 Petulo 3:13.

5:9—Kodi ‘phindu la dziko lipindulira onse’ m’njira yotani? Anthu onse padziko lapansi amadalira ‘phindu la dziko,’ kapena kuti zinthu zimene dziko limatulutsa. Ngakhale mfumu imadalira zomwezo. Kuti ilandire dzinthu dza m’munda mwake, mfumu iyenera kuthandizidwa ndi ntchito yolimba ya atumiki ake amene amalima mundawo.

Zimene Tikuphunzirapo:

1:15. Kutaya nthawi ndi mphamvu zathu poyesa kulimbana ndi khalidwe lopondereza ena ndiponso losowa chilungamo limene timaona masiku anoli n’kungodzivutitsa. Ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene ungathe kuchotsa zoipa.​—Danieli 2:44.

2:4-11. Zinthu zimene anthu amachita pamoyo, monga kumanga nyumba, kulima, ndi kuimba nyimbo, ndiponso kukhala moyo wawofuwofu ndi “kungosautsa mtima” chifukwa choti sizithandiza kuti moyo ukhale wopindulitsa ndipo sizipereka chimwemwe chokhalitsa.

2:12-16. Nzeru zimaposa kupusa chifukwa choti zingatithandize kuthetsa mavuto enaake. Koma pa nkhani ya imfa, nzeru za anthu zilibe phindu lililonse. Ndipo ngakhale munthu atatchuka chifukwa chokhala ndi nzeru zoterezi, posakhalitsa munthuyo amadzaiwalika.

2:24; 3:12, 13, 22. Kusangalala ndi zipatso za thukuta lathu si kulakwa.

2:26. Nzeru za Mulungu, zomwe zimabweretsa chimwemwe, zimapatsidwa kwa ‘yemwe Yehova amuyesa wabwino.’ N’zosatheka kupeza nzeru zimenezi popanda kukhala ndi ubwenzi wabwino ndi Mulungu.

3:16, 17. Tisamayembekeze kuti nthawi zonse anthu aziyendetsa zinthu mwachilungamo. Tisamavutike kuganizira kwambiri zinthu zimene zikuchitika m’dzikoli, koma tiziyembekeza kuti Yehova ndiye adzakonze zinthu.

4:4. Munthu angakhale wosangalala polimbikira ntchito ndi kuichita mwaluso. Koma kulimbikira ntchito n’cholinga chongofuna kuposa ena, kumalimbikitsa mpikisano ndipo kungayambitse mtima wa njiru ndi nsanje. Ntchito yolimba imene timachita muutumiki wachikhristu tiziichita ndi zolinga zabwino.

4:7-12. Ubwenzi wathu ndi anthu ena n’ngofunika kwambiri kuposa katundu, ndipo tisamalolere kuwononga ubwenzi umenewu pofuna chuma.

4:13. Sikuti nthawi zonse munthu amalemekezeka chifukwa cha udindo ndi msinkhu wake. N’chifukwa chake anthu okhala ndi udindo ayenera kuchita zinthu mwanzeru.

4:15, 16. ‘Mwana wachiwiri,’ kapena kuti mwana amene adzalowe m’malo mwa mfumu, poyamba angathe kukondedwa ndi anthu ‘onse amene akuwalamulira,’ koma “amene akudza m’mbuyo [mwake] sadzakondwera naye.” N’zoona, kutchuka sikuchedwa kutha.

5:2. Mapemphero athu azikhala osonyeza ulemu, osati ongochulukitsa mawu.

5:3-7. Kufunitsitsa kukhala ndi chuma kungachititse munthu kumangoganizira zochita zinthu zom’pindulira iyeyo basi. Kungachititsenso kuti munthuyo azilephera kugona tulo tabwino chifukwa chomangoganizira zomwe angapeze. Kuchulutsa zonena kungachititse munthu kuti ena azimuona ngati wopusa ndipo kungam’chititse kulumbira kwa Mulungu mopupuluma. ‘Kuopa Mulungu woona’ kumatithandiza kusachita zinthu zonsezi.

6:1-9. Kodi chuma, ulemerero, moyo wautali, ngakhalenso banja lalikulu, zili ndi ntchito yanji ngati sitikusangalala nazo chifukwa cha mmene zinthu zilili pamoyo wathu? Ndipotu “kupenya kwa maso,” kapena kuti kuvomereza mmene zinthu zilili, “kuposa kukhumba kwa mtima,” kapena kuti kulimbana ndi zilakolako zimene sitingathe kuzikhutiritsa. Motero, moyo wabwino ndiwo moyo wokhutira ndi “zakudya ndi zofunda” ndi kusangalala ndi zinthu zabwino pamoyo wathu n’kumaganizira kwambiri zopitiriza kukhala ndi ubwenzi wapamtima ndi Yehova.​—1 Timoteyo 6:8.

MALANGIZO KWA ANZERU

(Mlaliki 7:1–12:8)

Kodi tingatani kuti tisunge bwino dzina lathu kapena kuti mbiri yathu? Kodi tiziona motani anthu olamulira ndiponso kupanda chilungamo kumene timaona? Popeza kuti anthu akufa sadziwa kanthu, kodi moyo wathu tiziugwiritsa ntchito bwanji panopo? Kodi achinyamata angatani kuti agwiritsire ntchito mwanzeru nthawi yawo ndi mphamvu zawo? Malangizo anzeru a mlaliki pa nkhani zimenezi ndi nkhani zinanso akupezeka m’machaputala 7 mpaka 12 a buku la Mlaliki.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

7:19—Kodi nzeru imaposa bwanji ‘akulu khumi olamulira’? Baibulo likatchula nambala ya khumi mophiphiritsira, nambalayi imaimira kuti zinthuzo zilipo zonse kapena kuti zokwanira. Motero, Solomo akunena kuti nzeru imateteza moposa asilikali onse oteteza mzinda.

10:2—Kodi kunena kuti mtima wa munthu uli “ku dzanja lake lamanja” kapena “kulamanzere” kumatanthauza chiyani? Chifukwa choti nthawi zambiri dzanja lamanja limaimira kuchita bwino, kunena kuti mtima wa munthu uli kudzanja lake lamanja kumatanthauza kuti mtimawo umam’limbikitsa kuchita zinthu zabwino. Koma mtima ukamam’limbikitsa munthu kuchita zinthu zoipa, tinganene kuti mtimawo uli kudzanja lake lamanzere.

10:15—Kodi “ntchito ya zitsiru izitopetsa zonsezo” m’njira yotani? Ngati munthu saganiza mwanzeru, ntchito yake yonse siiphula kanthu kalikonse kopindulitsa. Sasangalala nayo. Moti chintchito chonsecho chimangom’topetsa.

11:7, 8—Kodi mawu akuti “kuunika n’kokoma, maso napeza bwino m’kuona dzuwa,” amatanthauza chiyani? Kuunika ndiponso dzuwa limasangalatsa zinthu zamoyo. Pamenepa Solomo akunena kuti ndi bwino kukhala ndi moyo ndi kuti ‘tizikondwereratu’ panopo tisanafike pofooka chifukwa cha masiku amdima, kapena kuti aukalamba.

11:10—Kodi “ubwana ndi unyamata” n’ngwachabe m’njira yotani? Zinthu zimenezi tikapanda kuzitenga bwino, zimakhala zachabe chifukwa choti, monga imachitira nthunzi, masiku amene munthu amakhala ndi mphamvu zaunyamata sachedwa kutha.

Zimene Tikuphunzirapo:

7:6. Kuseka panthawi yolakwika sikusangalatsa ndiponso n’kopanda ntchito mofanana ndi kuthetheka kwa minga pansi pa mphika. Ndi bwino kupewa kuseka kotereku.

7:21, 22. Tisamavutike n’kuganizira kwambiri zomwe anthu akutinena.

8:2, 3; 10:4. Woyang’anira ntchito kapena bwana akatidzudzula kapena kutikonza penapake, n’chinthu chanzeru kuugwira mtima. Ndi bwino kutero kusiyana ndi ‘kukangaza kum’chokera,’ kapena kuti kungosiya ntchitoyo mopupuluma.

8:8; 9:5-10, 12. Moyo wathu ungathe kutha mwadzidzidzi monga zimachitira nsomba pogwidwa muukonde kapena mbalame pogwidwa mumsampha. Ndiponso palibe munthu amene angaletse kuti mphamvu ya moyo isachoke pakufa, ndipo palibe aliyense amene angalephere kukhudziwa ndi nkhondo imene imfa ikumenya polimbana ndi anthu. Motero, tisawononge nthawi pochita zinthu zosafunikira. Yehova akufuna kuti moyo tiziuona kuti n’ngofunika kwambiri ndiponso kuti tizisangalala nawo. Kuti titero, tiyenera kuika patsogolo utumiki wa Yehova pamoyo wathu.

8:16, 17. Zinthu zonse zimene Mulungu wachita ndiponso zimene walola kuti zichitike kwa anthu n’zosasanthulika, ngakhale titachita kusowa nazo tulo kuti tizimvetsetse. Kudandaula chifukwa cha zolakwa zambirimbiri zimene zakhala zikuchitika kungathe kungotilepheretsa kusangalala pamoyo.

9:16-18. Nzeru tiziiona kuti n’chinthu chofunika ngakhale anthu ambiri atakhala kuti sakuganiza choncho. Mawu oleza mtima onenedwa ndi munthu wanzeru tiziwaona kuti n’ngofunika kusiyana ndi mawu amphamvu onenedwa ndi wopusa.

10:1. Tizisamala ndi zolankhula komanso zochita zathu. Kuchita chinthu chimodzi chokha mosaganizira bwino, monga kuchita zinthu mwamtima wapachala, kuledzera, kapena kuchita zinazake zosayenera ndi mkazi kapena mwamuna, kungathe kuwononga mbiri yabwino ya munthu wolemekezeka.

10:5-11. Munthu waudindo waukulu koma wosagwira ntchito molongosoka n’ngosakhumbirika. Kusagwira bwino ntchito, ngakhale itakhala yaing’ono, kungabweretse mavuto. Koma ndi bwino ‘kugwiritsa ntchito nzeru kuti itipindulitse.’ Kukhala aluso pa ntchito yolalikira za Ufumu ndi kupanga ophunzira n’kofunika kwambiri.

11:1, 2Tiziyesetsa ndi mtima wonse kukhala owolowa manja. Zimenezi zimachititsa kuti tizikhala anthu okonda kupatsa.​—Luka 6:38.

11:3-6. Zovuta za pamoyo zisamatipangitse kukhala osasangalala.

11:9; 12:1-7. Achinyamata azidziwa kuti Yehova amaona zimene amachita. Motero, ayenera kugwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zawo muutumiki wa Mulungu asanafike pofooka ndi ukalamba.

“MAWU A ANZERU” OTITSOGOLERA

(Mlaliki 12:9-14)

Kodi tiyenera kuona motani “mawu okondweretsa” amene mlaliki anafunafuna ndi kulemba? Mosiyana ndi “mabuku ambiri” a nzeru za anthu, “mawu a anzeru akunga zisonga, omwe akundika mawu amene mbusa mmodzi awapatsa mawu awo akunga misomali yokhomedwa zolimba.” (Mlaliki 12:10-12) Mawu anzeru ochokera kwa “mbusa mmodzi,” yemwe ndi Yehova, amathandiza munthu kukhala moyo wokhazikika.

Kutsatira malangizo anzeru opezeka m’buku la Mlaliki kungatithandizedi kukhala moyo wopindulitsa ndiponso wosangalatsa. Komanso tikulimbikitsidwa ndi mawu akuti: ‘Omwe aopa Mulungu adzapeza bwino.’ Motero tiyesetse ndi mtima wonse ‘kuopa Mulungu, ndi kusunga malamulo ake.’​—Mlaliki 8:12; 12:13.

[Chithunzi patsamba 15]

Imodzi mwa ntchito zokongola kwambiri za Mulungu idzakwaniritsidwa pa nthawi yake yoyenera

[Chithunzi patsamba 16]

Pa mphatso za Mulungu pali zinthu monga zakudya, zakumwa, ndiponso kusangalala ndi ntchito imene takhetserapo thukuta lathu