Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ntchito Yomanga Mwauzimu ku “Nyumba ya Miyala”

Ntchito Yomanga Mwauzimu ku “Nyumba ya Miyala”

Ntchito Yomanga Mwauzimu ku “Nyumba ya Miyala”

Dzina la dziko linalake la mu Africa limatanthauza “Nyumba ya Miyala.” Dziko limeneli limadziwika kwambiri chifukwa cha mathithi a Victoria Falls komanso mitundu yosiyanasiyana ya nyama zakuthengo. Komabe, m’dzikoli mulinso nyumba zakalekale zazikulu kwambiri kuposa dziko lina lililonse la kum’mwera kwa chipululu cha Sahara. Pakati pa dzikoli palinso phiri la miyala. Kudera la kuphirili kuli nyengo yabwino yomwe yachititsa kuti kukhale nthaka yachonde ndi mitengo yambiri. Limeneli ndi dziko la Zimbabwe, kumene kuli anthu okwana 12 miliyoni.

N’CHIFUKWA chiyani dziko limeneli lili ndi dzina lotanthauza Nyumba ya Miyala? M’chaka cha 1867, Adam Renders, yemwe anali mlenje ndi wofufuza malo atsopano, anatulukira nyumba za miyalazi zomwe zili pa malo okwana maekala 1,800. Munthu ameneyu anakhala akuyenda m’tchire la mu Africa, komwe nyumba zambiri zinali zophoma zofolera ndi udzu. Koma kenako anatulukira mabwinja a miyala a mzinda waukulu omwe tsopano amatchedwa Great Zimbabwe.

Mabwinja amenewa ali kum’mwera kwa tawuni yomwe masiku ano imatchedwa Masvingo. Makoma ena a mabwinjawo n’ngopangidwa ndi miyala yongosanjikiza popanda matope ndipo n’ngaatali kupitirira mamita 9. M’mabwinjawa muli nsanja yozungulira mochititsa chidwi yaitali mamita 11, ndipo kuyeza pansi pake mopingasa pamakwana mamita 6. Cholinga cha nsanjayi sichikudziwika mpaka pano. Mabwinja amenewa anamangidwa m’zaka za m’ma 700 C.E., koma pali umboni woti kumalo amenewa kunkakhala anthu kuyambira kalekale nthawi imeneyi isanafike.

Poyamba dzikoli linkatchedwa Rhodesia, koma litalandira ufulu wake wodzilamulira kuchokera ku dziko la Britain m’chaka cha 1980, linasintha n’kukhala Zimbabwe. Anthu a ku Zimbabwe ndi a mafuko awiri makamaka. Fuko lalikulu ndi la Ashona ndipo lachiwiri lake ndi la Andebele. Anthu ake n’ngodziwa kuchereza alendo ndipo Mboni za Yehova zikamalalikira ku nyumba ndi nyumba zimaona zimenezi. Nthawi zina, mlendo akagogoda pa khomo asanamudziwe n’komwe amangoti “Lowani” kenako “Khalani pansi.” Anthu ambiri ku Zimbabwe amalemekeza kwambiri Baibulo ndipo mukamakambirana nawo Malemba amafunitsitsa kuti ana awonso akhalepo.

Kupereka Uthenga Wolimbikitsa ndi Wotonthoza

Mawu akuti “Edzi” ndi “chilala” samasowa mu nkhani zokhudza Zimbabwe zikamakambidwa pa wailesi, pa TV ndi m’nyuzipepala. Kufalikira kwa Edzi kwabweretsa mavuto aakulu kwa anthu ndiponso kwasokoneza chuma cha mayiko ambiri a kum’mwera kwa Sahara. M’mayiko amenewa, anthu ambiri amene amagonekedwa ku chipatala amakhala odwala matenda okhudzana ndi HIV. Nthenda ya Edzi yasokoneza moyo wa mabanja ambiri.

Pofuna kuthandiza anthu ku Zimbabwe, Mboni za Yehova zikuyesetsa kuuza anthu kuti angakhale ndi moyo wabwino kwambiri akatsatira malangizo a Mulungu opezeka m’Baibulo. Mwachitsanzo, Mawu a Mulungu amaphunzitsa kuti ndi anthu okwatirana okha amene angamagonane komanso kugonana kwa amuna okhaokha kapena akazi okhaokha n’koletsedwa. Amaphunzitsanso kuti kuthiridwa magazi ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo n’koletsedwa ndi Yehova. (Machitidwe 15:28, 29; Aroma 1:24-27; 1 Akorinto 7:2-5; 2 Akorinto 7:1) Mbonizo zimalengezanso uthenga wa chiyembekezo chodalirika wakuti posachedwa Ufumu wa Mulungu udzathetsa matenda onse.​—Yesaya 33:24.

Kupereka Chithandizo kwa Osowa

Ku Zimbabwe kwakhala kuli chilala chachikulu pazaka 10 zapitazi. Nyama zakuthengo zafa chifukwa cha njala ndi ludzu. Ng’ombe zambirimbiri zafanso. Nkhalango zambiri zapsa ndi moto. Ana ndi anthu okalamba ambiri afa chifukwa cha kuperewera kwa zakudya m’thupi. Ngakhale madzi a mumtsinje waukulu wa Zambezi anaphwa kwambiri mpaka kusokoneza ntchito za magetsi.

Pothandizapo, Mboni za Yehova zinakhazikitsa makomiti 8 achithandizo m’madera osiyanasiyana m’dzikoli. Oyang’anira oyendayenda ankapita ku mipingo kukaona mavuto omwe anthu akukumana nawo. Abale amenewa ankakanena zimene apeza ku makomiti achithandizo oyenerera. Woyang’anira woyendayenda wina anati: “M’zaka zisanu zapitazi, tagawira matani oposa 1000 a chimanga, matani 10 a nsomba zouma, ndi matani 10 enanso a nyemba. Abale athu auzimu anafutsa ndiwo zamasamba zokwana matani awiri. Tinaperekanso zovala zambiri ndi ndalama zomwe zinkafunikira.” Woyang’anira woyendayenda winanso anati: “Ndikaganizira mavuto amene takumana nawo popempha chilolezo kudziko la Zimbabwe ndi South Africa kuti tilowetse katunduyu m’dzikoli komanso kusowa kwa mafuta a galimoto zonyamula katundu, n’zodabwitsa kuti takwanitsa kuchita zonsezi. Umenewu ndi umboni wa mawu a Yesu akuti Atate wathu wakumwamba amadziwa kuti tikusowa zinthu zonsezi.”​—Mateyo 6:32.

Koma oyang’anira oyendayendawa amatha bwanji kugwira ntchito yawo m’madera a chilala ngati amenewa? Ena amanyamula chakudya chawo ndi cha banja lomwe azikakhala nalo. Woyang’anira woyendayenda wina anati, alongo ena ankakambirana kuti alekeze pa njira kulalikira n’cholinga choti akakhale nawo pamzera wa anthu amene anali kudikirira chithandizo cha boma. Koma kenako, anaganiza zodalira Yehova ndi kupitirizabe kulalikira kuti aone mmene zinthu zikhalire. Tsiku limenelo chithandizo cha boma sichinafike.

Tsiku lotsatira linali tsiku la misonkhano, ndipo alongowa anafunikiranso kuganiza chochita. Kodi apita ku misonkhano kapena kukadikira chithandizo? Anasankha mwanzeru, chifukwa anapita ku Nyumba ya Ufumu kukakhala nawo pamisonkhano. (Mateyo 6:33) Akuimba nyimbo yomaliza, anamva chigalimoto chikufika. Thandizo linawapeza komweko, kudzera mwa abale awo auzimu a m’komiti ya chithandizo. Mboni zokhulupirika zomwe zinali pa msonkhanopo zinasangalala kwambiri.

Chikondi Chimamangirira

Kuchitira chifundo anthu omwe si Mboni kwapereka mipata yabwino kwambiri yolalikira. Woyang’anira woyendayenda wina akulalikira pamodzi ndi Mboni zina za ku Masvingo, anapeza mtsikana wina atagona pa msewu. Mbonizo zinaona kuti mtsikanayo anali kudwala kwambiri, chifukwa ankalephera kulankhula bwinobwino. Dzina la mtsikanayo linali Hamunyari, lomwe m’Chishona limatanthauza “Kodi Simukuchita Manyazi?” Abalewo anauzidwa kuti mtsikanayo anasiyidwa ndi anthu a kutchalitchi chake omwe anali kupita kukapemphera ku phiri. Mbonizo zinam’thandiza kwambiri mtsikanayo ndipo zinapita naye kumudzi wina wapafupi.

Kumudziko, anthu ena anamuzindikira Hamunyari ndipo anakauza achibale ake kuti adzamutenge. Pokambapo za Mbonizo, anthu a m’mudzimo anati: “Chipembedzo choona n’chimenechi. Akhristu ayenera kusonyeza chikondi chotere.” (Yohane 13:35) Abalewo asanachoke, anam’patsa Hamunyari kapepala kakuti, Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? *

Mlungu wotsatira, woyang’anira woyendayenda uja anakayendera mpingo wakudera komwe Hamunyari ankakhala. Anafuna kudziwa ngati Hamunyari anafika ku nyumba kwawo bwinobwino. Banja lonse la mtsikanayu linasangalala kwambiri kuonana ndi mbaleyu ndi abale ena a komweko. Makolo a Hamunyari anati: “Anthu inu muli m’chipembedzo choona. Munapulumutsa mwana wathu, yemwe anasiyidwa akufa pa njira.” Makolowo anafunsa anthu a kutchalitchi kwawo kuti: “Kodi simunachite manyazi, monga mwa dzina lake, kumusiya akufa?” Mbonizo zinakambirana ndi banjalo nkhani za m’Baibulo ndipo zinalisiyira mabuku ofotokoza za m’Baibulo. Ndipo anthuwo anavomera kuti Mbonizo zidzabwerenso kudzaphunzira nawo Baibulo. Achibale awo ena omwe ankatsutsa kwambiri Mboni, anasintha maganizo. Mmodzi mwa iwo anali mlamu wake wa Hamunyari, yemwe anali mtsogoleri wa tchalitchi cha kuderalo. Iye anavomeranso kuphunzira Baibulo.

Kumanga Nyumba Zolambirira

Wolemba ndakatulo wina wa m’Baibulo analemba kuti: “Inu Mulungu, . . . moyo wanga ukumva ludzu la kwa Inu, . . . m’dziko louma ndi lotopetsa, lopanda madzi.” (Salmo 63:1) Zimenezi zachitikiradi anthu ambiri ku Zimbabwe. Avutikadi ndi chilala, koma mwauzimu moyo wawo ukumva ludzu lofuna kudziwa za Mulungu ndi ubwino wake. Ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova ikusonyeza bwino zimenezi. Pamene dziko la Zimbabwe linalandira ufulu wake wodzilamulira mu 1980, kunali Mboni zokwana 10,000 m’mipingo 476. Tsopano, patapita zaka 27, chiwerengero cha Mbonizo chachuluka kuwirikiza katatu ndipo mipingo yachulukanso kuwirikiza kawiri.

Ndi mipingo yochepa chabe yomwe inali ndi malo olambirira. Pofika mu January 2001, pamipingo yoposa 800 ya ku Zimbabwe, 98 yokha inali ndi malo olambirira kapena kuti Nyumba za Ufumu. Mipingo yambiri inkachitira misonkhano yawo pansi pa mitengo kapena m’nyumba zophoma zofolera ndi udzu.

Koma panopa Mboni za ku Zimbabwe zikumanga Nyumba za Ufumu zosafuna ndalama zambiri koma zolemekezeka. Zimenezi zatheka chifukwa cha zopereka za abale a padziko lonse komanso ntchito yawo yodzipereka. Mboni zambiri zochokera kumayiko akutali zomwe zili ndi luso la zomangamanga zinadzipereka kukagwira ntchito pamodzi ndi Mboni zinanso zodzipereka za ku Zimbabwe komweko. Mbale wina wa ku Zimbabwe analemba kuti: “Tikuthokoza ndi mtima wonse abale ndi alongo onse omwe abwera ku Zimbabwe kuno kuchokera kumayiko osiyanasiyana kudzamanga nawo Nyumba za Ufumu zokongolazi. Tikuthokozanso ena nonsenu chifukwa cha zopereka zanu ku Thumba la Nyumba za Ufumu, zomwe zathandiza kuti ntchito imeneyi itheke.”

Kudera lina la kummawa kwa dzikoli, abale ankachitira misonkhano yawo pansi pamtengo wa malambe kwa zaka 50. Akulu a mumpingowo atauzidwa kuti kudera lawo kumangidwa nyumba yolambirira, mkulu wina mpaka anakhetsa misozi. Pampingo wina woyandikana nawo, mkulu wina wa zaka 91, anati: “Ndakhala ndikum’lilira Yehova kwa zaka zambiri kuti zinthu ngati zimenezi zichitike.”

Anthu ambiri anenapo za changu chimene chimakhalapo pomanga nyumba zokongolazi. Munthu wina yemwe anaona nyumbazi zikumangidwa anati: “Anthu inu mukumanga masana, ndipo Mulungu ayenera kuti akumanga usiku.” Anthu achitanso chidwi ndi mgwirizano komanso chimwemwe cha anthu ogwira ntchitoyi. Pakali pano, Nyumba za Ufumu zoposa 350 zamangidwa m’dzikoli. Zimenezi zachititsa kuti mipingo 534 izichitira misonkhano yawo m’Nyumba za Ufumu zolimba zomangidwa ndi njerwa.

Ntchito yofunika kwambiri yomanga mwauzimu ikupitirirabe ku Zimbabwe. Tikaganizira zimene zachitika, timayamikira Yehova, yemwe wachititsa kuti zonsezi zitheke. Inde, “akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe.”​—Salmo 127:1.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 16 Kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mapu patsamba 9]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

ZIMBABWE

HARARE

Masvingo

Great Zimbabwe

[Chithunzi patsamba 9]

Nsanja yozungulira

[Chithunzi patsamba 12]

Nyumba ya Ufumu yatsopano ya mpingo wa Concession

[Chithunzi patsamba 12]

Anthu a mumpingo wa Lyndale kunja kwa Nyumba ya Ufumu yawo yatsopano

[Mawu a Chithunzi patsamba 9]

Ruins with steps: ©Chris van der Merwe/​AAI Fotostock/​age fotostock; tower inset: ©Ingrid van den Berg/​AAI Fotostock/​age fotostock