Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Musalekanitse Chimene Mulungu Anachimanga Pamodzi

Musalekanitse Chimene Mulungu Anachimanga Pamodzi

Musalekanitse Chimene Mulungu Anachimanga Pamodzi

“Salinso awiri, koma thupi limodzi. Choncho, chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”​—MATEYO 19:6.

1, 2. Kodi n’chifukwa chiyani zili zomveka komanso za m’Malemba kuti mwamuna ndi mkazi wake amakumana ndi mavuto?

TAYEREKEZANI kuti mukufuna kuyambapo ulendo wautali pagalimoto. Kodi mungayende ulendo wanu popanda kukumana ndi mavuto? Kuganiza choncho kungakhale kupanda nzeru. Mwina chimvula chingakupezeni ndipo mungafune kuyendetsa pang’onopang’ono mosamala. Penanso galimoto ingakufereni moti simungathe kuikonza mpaka mutaitana munthu wina kuti akuthandizeni kukonza. Kodi chifukwa cha mavuto amenewa, munganene kuti munalakwitsa kunyamuka ulendo wanu kapena mungaganize zongoinyanyala galimotoyo? Ayi, simungatero. Mukamayenda ulendo wautali, mumayembekezera mavuto ndipo mumakonzekera kuthana nawo.

2 Banjanso ndi chimodzimodzi, limakhala ndi mavuto. Ngati anthu amene akufuna kukwatirana akuganiza kuti ukwati wawo udzakhala ndi mtendere wokhawokha, sakuganiza mwanzeru. Pa 1 Akorinto 7:28, Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti mwamuna ndi mkazi wake adzakhala ndi “nsautso m’thupi mwawo.” Chifukwa chiyani? Mwachidule, ndi chifukwa chakuti mwamuna ndi mkazi wake ndi opanda ungwiro ndipo akukhala mu “nthawi yovuta.” (2 Timoteyo 3:1; Aroma 3:23) Choncho, ngakhale banja logwirizana ndi lokonda zinthu zauzimu limakumana ndi mavuto.

3. (a) Kodi anthu ambiri masiku ano banja amaliona motani? (b) Kodi n’chifukwa chiyani Akhristu amayesetsa kusunga banja lawo?

3 Masiku ano, m’banja mukabuka mavuto, anthu amangoganiza zothetsa ukwati. M’mayiko ochuluka, anthu ambiri akusudzulana. Ngakhale zili choncho, Akhristu enieni amalimbana ndi mavutowo m’malo mowathawa. Amatero chifukwa chakuti amaona kuti ukwati ndi mphatso yopatulika yochokera kwa Yehova. Ponena za ukwati, Yesu anati: “Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” (Mateyo 19:6) Kunena zoona, kutsatira mfundo imeneyi kungakhale kovuta. Mwachitsanzo, achibale ndi anthu ena, ngakhale alangizi a zabanja, amene satsatira mfundo za m’Baibulo, nthawi zambiri amalimbikitsa anthu kupatukana kapena kusudzulana pa zifukwa zosakhala za m’Malemba. * Koma Akhristu amadziwa kuti ndi bwino kukonzanso ndi kusunga banja lawo m’malo mongolithetsa. Choncho, ndi nzeru kuti poyamba penipeni, mwamuna ndi mkazi wake asankhe kutsatira njira ya Yehova osati uphungu wa anthu ena.​—Miyambo 14:12.

Mmene Mungathetsere Mavuto

4, 5. (a) Kodi ndi mavuto otani amene mungafunike kuthana nawo muukwati? (b) Kodi n’chifukwa chiyani mfundo za m’Mawu a Mulungu zimathandiza kwambiri, ngakhale pabanja pakabuka mavuto?

4 Banja lililonse limakumana ndi mavuto amene amafunikira kuwathetsa. Nthawi zambiri, mavuto amenewa amakhala a kusagwirizana pa zinthu zazing’ono. Koma mabanja ena amakhala ndi mavuto aakulu amene angasokoneze ukwati. Nthawi zina, pangafunike kupempha thandizo kwa mkulu wokwatira wodziwa bwino nkhani za m’banja. Ngati mwakumana ndi zimenezi, sindiye kuti banja lanu ndi lolephera. Zikungosonyeza kuti mukufunika kutsatira kwambiri mfundo za m’Baibulo pothetsa mavuto anuwo.

5 Yehova amadziwa kuposa wina aliyense zimene timafunika kuchita kuti ukwati wathu uyende bwino. Amatero chifukwa chakuti ndiye Mlengi wa anthu ndipo ndiye anayambitsa ukwati. Koma nkhani yagona pakuti, Kodi tidzamvera uphungu wopezeka m’Mawu ake? Tingapindule kwambiri ngati titatero. Kalelo, Yehova anauza anthu ake kuti: “Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.” (Yesaya 48:18) Kutsatira malangizo a m’Baibulo kumathandiza kuti banja liyende bwino. Tiyeni tikambirane kaye uphungu umene Baibulo limapereka kwa amuna.

“Pitirizani Kukonda Akazi Anu”

6. Kodi Malemba amapereka uphungu wotani kwa amuna?

6 Kalata imene mtumwi Paulo analembera Aefeso ili ndi malangizo omveka bwino kwa amuna. Iye analemba kuti: “Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu, monga Khristu anakonda mpingo nadzipereka yekha chifukwa cha mpingowo. Mwa njira imeneyi amuna akonde akazi awo monga matupi awoawo. Amene akonda mkazi wake adzikonda iye mwini, pakuti palibe munthu anadapo thupi la iye mwini; koma amalidyetsa ndi kulisamala, mmenenso Khristu amachitira ndi mpingo. Komabe, aliyense wa inu akonde mkazi wake monga adzikonda iye mwini.”​—Aefeso 5:25, 28, 29, 33.

7. (a) Kodi n’chiyani chimene chiyenera kukhala maziko a banja lachikhristu? (b) Kodi amuna azitani kuti apitirize kukonda akazi awo?

7 Paulo sanafotokoze mavuto onse amene mwamuna ndi mkazi wake angakumane nawo. Koma anatchula chinthu chofunika kwambiri, chimene tingati ndi maziko a banja lachikhristu. Chinthucho ndi chikondi. Ndipotu, chikondi chikutchulidwa ka 6 m’mavesi ali pamwambawo. Onaninso kuti Paulo akuuza amuna kuti: “Pitirizani kukonda akazi anu.” Tingatero kuti Paulo anazindikira kuti kukopeka ndi munthu, n’kuyamba kumukonda, ndi kosavuta kusiyana ndi kupitirizabe kumukonda. Zimenezi zili choncho makamaka “m’masiku otsiriza” ano, pamene anthu ambiri ndi “odzikonda” ndiponso “osagwirizanitsika.” (2 Timoteyo 3:1-3) Makhalidwe oipa ngati amenewa akuwononga mabanja ambiri masiku ano, koma mwamuna amene amakonda mkazi wake salola kutengera khalidwe lodzikonda la dzikoli.​—Aroma 12:2.

Kodi Kudyetsa Mkazi Wanu Kumatanthauza Chiyani?

8, 9. Kodi mwamuna wachikhristu amadyetsa bwanji mkazi wake?

8 Ngati ndinu mwamuna wachikhristu, kodi mungapewe bwanji mtima wodzikonda n’kusonyeza mkazi wanu chikondi chenicheni? M’kalata imene analembera Aefeso ija, Paulo anatchula zinthu ziwiri zimene muyenera kuchitira mkazi wanu. Anati muyenera kum’dyetsa ndi kumusamala ngati mmene mumachitira ndi thupi lanu. Kodi kudyetsa mkazi wanu kumatanthauza chiyani? Choyamba, kumatanthauza kumupezera zinthu zofunika pamoyo wake. Paulo analembera Timoteyo kuti: “Ndithudi, ngati munthu sasamalira ake a iye mwini, makamaka a m’banja lake, wakana chikhulupiriro ndipo ndi woipa kuposa munthu wopanda chikhulupiriro.”​—1 Timoteyo 5:8.

9 Komabe, kudyetsa mkazi wanu kumatanthauza zambiri, osati kungomupezera chakudya, zovala, ndi pogona. Tikutero chifukwa chakuti mwamuna angapezere mkazi wake zinthu zambiri pamoyo wake koma angalephere kumukonda kapena kumusamala mwauzimu. Zinthu ziwiri zotsirizazi ndi zofunikanso kwambiri. Ndi zoona kuti amuna ambiri achikhristu amatanganidwa ndi zinthu za mumpingo. Koma mwamuna amene ali ndi udindo waukulu mumpingo asaone ngati atha kunyalanyaza udindo umene ali nawo pabanja pake. (1 Timoteyo 3:5, 12) Zaka zingapo zapitazo, magazini ino inanenapo za nkhani imeneyi kuti, malinga ndi zimene Baibulo limanena, “‘kuweta kumayambira panyumba.’ Ngati mkulu anyalanyaza banja lake, iye angaike pangozi kuikidwa kwake.” * Choncho, n’zofunika kwambiri kuti mupatse mkazi wanu zinthu zakuthupi, muzimukonda ndipo makamaka muzimusamala mwauzimu.

Kodi Kusamala Mkazi Wanu Kumatanthauza Chiyani?

10. Kodi mwamuna angasamale bwanji mkazi wake?

10 Kusamala mkazi wanu kumatanthauza kumukonda. Pali njira zambiri zochitira zimenezi. Choyamba, muzipeza nthawi yokwanira yocheza ndi mkazi wanu. Mukanyalanyaza zimenezi, mkazi wanu angasiye kukukondani. Mwina mungaone kuti nthawi ndi chisamaliro zimene mukupereka ndi zokwanira kwa mkazi wanu, koma mwina si zimene iyeyo akufuna. Apa mfundo si yakuti muzingonena kuti ndimasamala mkazi wanga. Mkazi wanuyo aziona kuti mumamusamala. Paulo analemba kuti: “Aliyense asamangodzifunira zopindulitsa iye yekha basi, komanso zopindulitsa wina.” (1 Akorinto 10:24) Pokhala mwamuna wachikondi, muzionetsetsa kuti mukumvetsa zofuna zenizeni za mkazi wanu.​—Afilipi 2:4.

11. Ngati mwamuna sasamala mkazi wake, kodi ubwenzi wake ndi Mulungu umatani, nanga zimamuyendera bwanji mumpingo?

11 Njira ina yosonyezera kuti mumasamala mkazi wanu ndi kulankhula ndi kuchita naye zinthu mokoma mtima. (Miyambo 12:18) Paulo analembera anthu a ku Kolose kuti: “Amuna inu, musaleke kukonda akazi anu ndipo musawapsere mtima.” (Akolose 3:19) Buku lina limati mawu otsirizira a lembali angamasuliridwenso kuti “musamutenge ngati wantchito” kapena “musamuyese kapolo.” Mwamuna amene amachitira nkhanza mkazi wake, kaya pagulu kapena m’seri, sasamala mkazi wake. Amawononganso ubwenzi wake ndi Mulungu. Kwa amuna, mtumwi Petulo anati: “Pitirizani kukhala nawo [akazi anu] mowadziwa bwino, kupatsa ulemu mkazi monga chiwiya chosalimba, kuti mapemphero anu asatsekerezedwe, pakutinso mudzalandira nawo limodzi mphatso yachisomo ya moyo.” *​—1 Petulo 3:7.

12. Kodi mmene Yesu ankachitira ndi mpingo, zimaphunzitsa chiyani amuna achikhristu?

12 Musamaganize kuti mulimonse mmene mungachitire, mkazi wanu adzangopitirizabe kukukondani. Muzimutsimikizira kuti mumamukonda. Mmene Yesu ankachitira zinthu ndi mpingo wachikhristu, zimapereka chitsanzo chabwino kwa amuna achikhristu. Anali wofatsa, wokoma mtima, ndi wokhululuka, ngakhale pamene otsatira ake anasonyeza makhalidwe oipa. N’chifukwa chake Yesu anatha kuuza ena kuti: “Bwerani kwa ine, . . . pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa, ndipo mudzapeza chitsitsimutso cha miyoyo yanu.” (Mateyo 11:28, 29) Mwamuna wachikhristu amene amatsatira Yesu, amachita zinthu ndi mkazi wake mofanana ndi mmene Yesu anachitira ndi mpingo. Mwamuna amene amasamaladi mkazi wake m’mawu ndi m’zochita, amamutsitsimutsa kwambiri.

Akazi Azitsatira Mfundo za M’Baibulo

13. Kodi m’Baibulo muli mfundo zotani zothandiza akazi?

13 Baibulo lili ndi mfundo zothandizanso akazi. Lemba la Aefeso 5:22-24, 33 limati: “Akazi agonjere amuna awo monga kugonjera Ambuye, chifukwa mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake monganso Khristu alili mutu wa mpingo, pokhala iye mpulumutsi wa thupilo. Ndipotu, monga mpingo umagonjera Khristu, akazinso agonjere amuna awo m’chilichonse. . . . Mkazi akhale ndi ulemu waukulu kwa mwamuna wake.”

14. Kodi n’chifukwa chiyani mfundo ya m’Malemba yoti akazi azigonjera amuna awo siwachotsera ulemu?

14 Onani kuti Paulo ananena za kugonjera ndi kukhala ndi ulemu. Anakumbutsa akazi kugonjera amuna awo. Limeneli ndi dongosolo limene Mulungu anakhazikitsa. Zolengedwa zonse, kaya zakumwamba kapena zapadziko, zili ndi winawake amene ziyenera kumugonjera. Ngakhale Yesu amene amagonjera Yehova Mulungu. (1 Akorinto 11:3) Koma zimakhala zosavuta kuti mkazi azigonjera mwamuna wake ngati mwamunayo ali mutu wabwino.

15. Kodi Baibulo lili ndi uphungu wotani kwa akazi?

15 Paulo ananenanso kuti mkazi “akhale ndi ulemu waukulu kwa mwamuna wake.” Mkazi wachikhristu azikhala ndi “mzimu wabata ndi wofatsa,” ndipo asapikisane ndi mwamuna wake kapena kumangoyendera zake. (1 Petulo 3:4) Mkazi woopa Mulungu amalimbikira kugwira ntchito kuti athandize banja lake ndipo potero mwamuna wake amalemekezedwa. (Tito 2:4, 5) Amayesetsa kunena zabwino za mwamuna wake ndipo sachita chilichonse chimene chingamuchotsere ulemu. Amathandizanso mwamuna wake pa zimene wagamula kuti zitheke.​—Miyambo 14:1.

16. Kodi akazi achikhristu angaphunzire chiyani kwa Sara ndi Rebeka?

16 Sikuti mkazi wachikhristu akakhala ndi mzimu wabata ndi wofatsa ndiye kuti alibe mfundo kapena amaganiza moperewera. Kale, akazi oopa Mulungu, monga Sara ndi Rebeka, ananena maganizo awo ndipo Baibulo limasonyeza kuti Yehova anagwirizana nawo. (Genesis 21:8-12; 27:46–28:4) Akazi achikhristu nawonso ayenera kunena maganizo awo. Koma azichita zimenezi mwaulemu osati monyoza. Mkazi akamalankhula maganizo ake mwaulemu, mwamuna amasangalala ndipo amamvetsera.

Ukwati N’kukhulupirika

17, 18. Kodi amuna ndi akazi angachite chiyani kuti asalole Satana kuwononga ukwati wawo?

17 Ukwati umafuna kukhulupirika kwa moyo wonse. Choncho, mwamuna ndi mkazi wake ayenera kukhala ndi mtima wofuna kukhala ndi ukwati wolimba. Ngati mwamuna ndi mkazi wake akulephera kulankhulana zakukhosi, mavuto amakula. Nthawi zambiri, mwamuna ndi mkazi amasiya kulankhulana pakabuka mavuto ndipo amangokwiyirana. Ena mpaka amafuna kuthetsa banja, mwinanso kuyamba kukondana ndi munthu wina. Yesu anachenjeza kuti: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka wachita naye kale chigololo mumtima mwake.”​—Mateyo 5:28.

18 Mtumwi Paulo analangiza Akhristu onse, ndi apabanja omwe, kuti: “Kwiyani, koma musachimwe. Dzuwa lisalowe muli chikwiyire, ndipo musam’patse malo Mdyerekezi.” (Aefeso 4:26, 27) Satana, mdani wathu wamkulu, amapezerapo mwayi akaona Akhristu akukangana. Musamulole kupambana! Pakabuka mavuto, fufuzani maganizo a Yehova pankhaniyo m’Baibulo, pogwiritsa ntchito mabuku olifotokoza. Pakakhala kusamvana, kambiranani modekha ndi moona mtima. Yesetsani kugwiritsa ntchito mfundo za Yehova zimene mukudziwazo. (Yakobe 1:22-25) Ndithudi, tsimikizani mtima kuyendabe ndi Mulungu paukwati wanu, ndipo musalole aliyense kapena chilichonse kulekanitsa chimene Mulungu anachimanga pamodzi.​—Mika 6:8.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Onani bokosi lakuti “Kusudzulana Ndiponso Kupatukana” mu Galamukani! ya February 8, 2002, tsamba 28, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 9 Onani Nsanja ya Olonda ya May 15, 1989, tsamba 12.

^ ndime 11 Kuti mwamuna apatsidwe udindo mumpingo, sayenera kukhala “womenya” anzake ndi mawu kapena zibakera. N’chifukwa chake Nsanja ya Olonda ya September 1, 1990, tsamba 25 inati: “Mwamunayo samayeneretsedwa ngati achita zinthu mwanjira yaumulungu kumalo ena komabe nakhala wotsendereza panyumba.”​—1 Timoteyo 3:2-5, 12.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi n’chifukwa chiyani ngakhale mabanja achikhristu amakhala ndi mavuto?

• Kodi mwamuna amadyetsa ndi kusamala mkazi wake motani?

• Kodi mkazi angachite chiyani kusonyeza kuti ali ndi ulemu waukulu kwa mwamuna wake?

• Kodi mwamuna ndi mkazi angachite chiyani kuti asasiye kukhala okhulupirika muukwati?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 20]

Mwamuna ayenera kudyetsa mkazi wake mwakuthupi ndi mwauzimu

[Chithunzi patsamba 21]

Mwamuna amene amasamala mkazi wake amamutsitsimutsa kwambiri

[Chithunzi patsamba 23]

Akazi Achikhristu amanena maganizo awo mwaulemu