Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chilengedwe N’chopandadi Mlengi?

Kodi Chilengedwe N’chopandadi Mlengi?

Kodi Chilengedwe N’chopandadi Mlengi?

PADUTSA zaka pafupifupi 150 kuchokera pamene Charles Darwin anayambitsa mfundo yakuti zamoyo zochuluka mosanenekazi zinakhalako zokha popanda kulengedwa. Komabe, posachedwapa asayansi ena amene amaona kuti zamoyo n’zopangidwa modabwitsa kwambiri, amatsutsa zoti zamoyo zinakhalako m’njira imeneyi. Ngakhale asayansi ambiri opatsidwa ulemu savomereza mfundo yoti zamoyo zosiyanasiyana za padzikoli zinakhalako pazokha.

Ena mwa asayansi amenewa amanena kuti panafunika nzeru zakuya kuti zamoyo zikhaleko. Amatero chifukwa choona kuti zamoyo zinapangidwa m’njira yoonekeratu kuti n’zochita kulengedwa komanso yogwirizana ndi sayansi ndi masamu. Asayansi amenewa akulimbikitsa zoti sukulu ziziphunzitsa zimenezi. Nkhani imeneyi yavuta kwambiri makamaka m’dziko la United States, ndi m’mayiko enanso monga England, Netherlands, Pakistan, Serbia, ndi Turkey.

Amazemba Mfundo Yoonekeratu

Komabe asayansiwa akamafotokoza mfundo yoti panafunika nzeru kuti zamoyo zikhaleko, kawirikawiri zimachita kuonekeratu kuti pali mfundo inayake imene akuizemba. Mfundo yake ndi yonena za amene anapanga zamoyozo. Kodi inuyo mumakhulupirira zoti chilengedwe chingakhaleko popanda mlengi? Nyuzipepala ina inati: “Asayansi amene amanena kuti panafunika nzeru kuti zamoyo zikhaleko, sanena momveka bwino kuti ndi ndani kapena n’chiyani chinachititsa kuti zamoyozo zikhaleko.” (The New York Times Magazine) Munthu wina wolemba mabuku, dzina lake Claudia Wallis, ananena kuti asayansi amene amalimbikitsa mfundo imeneyi “amapewa kutchula Mulungu m’zonena zawozo.” Ndipo magazini ina inati: “Asayansi amenewa sanenapo n’komwe zoti kuli mlengi ndiponso kuti mlengiyo ndi wotani.”​—Inatero Newsweek

Komatu mungathe kuona nokha kuti si nzeru kuzemba mfundo yakuti kuli mlengi. Chifukwa sizomveka kunena kuti panafunika nzeru kuti zamoyo zikhaleko, koma n’kunyalanyaza mfundo yoti pali amene anazipanga.

Kwenikweni, kuvomereza zoti kuli mlengi kungayambitse mafunso otsatirawa: Kodi zimenezi sizingalepheretse sayansi ndiponso maphunziro ena kupita patsogolo? Kodi tiyenera kungovomereza kuti kuli mlengi wanzeru chifukwa chosowa mfundo zina zogwira mtima? Ndipo kodi kuona kuti panafunika nzeru kuti zamoyo zikhaleko kumapereka umboni wokwanira woti zinachita kulengedwa? M’nkhani yotsatira tikambirana mafunso amenewa ndi enanso otero.

[Zithunzi patsamba 3]

Charles Darwin ankakhulupirira kuti zamoyo zinakhalako popanda kulengedwa

[Mawu a Chithunzi]

Darwin: From a photograph by Mrs. J. M. Cameron/​U.S. National Archives photo