Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amakonda Chilungamo

Yehova Amakonda Chilungamo

Yehova Amakonda Chilungamo

“Ine Yehova ndikonda chiweruziro [“chilungamo,” NW].”​—YESAYA 61:8.

1, 2. Kodi mawu akuti “chilungamo” ndi “kupanda chilungamo” amatanthauza chiyani? (b) Kodi Baibulo limati chiyani za Yehova ndi khalidwe lake la chilungamo?

CHILUNGAMO chimatanthauza ‘kupanda tsankho, kusakondera, kuchita zinthu zoyenera ndiponso zabwino.’ Kupanda chilungamo kumatanthauza kukhala watsankho, wokondera, woipa mtima ndi wankhanza.

2 Kalekale, pafupifupi zaka 3,500 zapitazo, Mose ananena za Yehova, Wolamulira wa Chilengedwe Chonse, kuti: “Njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo.” (Deuteronomo 32:4) Patadutsa zaka zoposa 700, Mulungu anauza Yesaya kulemba kuti: “Ine Yehova ndikonda chiweruziro [“chilungamo”].” (Yesaya 61:8) Kenako m’nthawi ya atumwi, Paulo anati: “Kodi Mulungu alibe chilungamo? Ayi si zimenezo!” (Aroma 9:14) Nayenso Petulo anati: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” (Machitidwe 10:34, 35) Zoonadi, “Yehova akonda chiweruzo [“chilungamo,” NW].”​—Salmo 37:28; Malaki 3:6.

Kupanda Chilungamo Kuli Paliponse

3. Kodi kupanda chilungamo kunayamba bwanji padziko lapansi?

3 Masiku ano, chilungamo n’chosowa. Anthu kulikonse angatichitire zinthu zopanda chilungamo. Angachite zimenezi kaya ndi kuntchito, kusukulu, m’banja ndi m’njira zinanso. Ngakhale akuluakulu a boma angatichitire zinthu zopanda chilungamo. Kupanda chilungamo kumeneku sikunayambe lero. Anthu anayamba kukumana ndi vuto limeneli pamene makolo athu oyamba anapandukira malamulo a Mulungu, atasonkhezeredwa ndi mngelo wopanduka amene kenako anadzakhala Satana Mdyerekezi. Kunena zoona, kunalidi kupanda chilungamo kuti Adamu, Hava, ndi Satana agwiritse ntchito mosayenera ufulu wosankha zochita umene Yehova anawapatsa. Kulakwa kwawo kunabweretsa mavuto aakulu ndi imfa kwa anthu onse.​—Genesis 3:1-6; Aroma 5:12; Aheberi 2:14.

4. Kodi anthu akhala akukumana ndi kupanda chilungamo kwa zaka zingati?

4 Dziko lapansi lakhala lopanda chilungamo kwa zaka zoposa 6,000 kuchokera pamene anthu oyamba anapanduka mu Edene. Zimenezi ndi zosadabwitsa chifukwa chakuti Satana ndiye mulungu wa dzikoli. (2 Akorinto 4:4) Iye ndi wabodza komanso tate wa bodza, ndipo amaneneza ndi kutsutsa Yehova. (Yohane 8:44) Iye wakhala akusonkhezera kupanda chilungamo kosaneneka. Mwachitsanzo, Chigumula cha Nowa chisanachitike, Mulungu anaona kuti “kuipa kwa anthu kunali kwakukulu padziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yawo zinali zoipabe zokhazokha.” (Genesis 6:5) Mwa zina, chimene chinachititsa zimenezi ndi mphamvu ya Satana. Kupanda chilungamo kunalipobe ngakhale m’nthawi ya Yesu. Iye anati: “Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanira patsikulo.” Apatu anali kunena mavuto monga kupanda chilungamo. (Mateyo 6:34) Baibulo limanena zoona kuti: “Chilengedwe chonse chikubuula limodzi ndi kumva zopweteka mpaka pano.”​—Aroma 8:22.

5. Kodi n’chifukwa chiyani kupanda chilungamo kwafala kwambiri kuposa kale?

5 Choncho kuyambira kalekale, padziko lapansi pakhala pakuchitika zinthu zambirimbiri zopanda chilungamo. Koma panopa zinthu zafika poipa kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti dziko loipali lakhala lili “m’masiku otsiriza” kwa zaka zambiri, ndipo pamene likuyandikira mapeto ake, likukumana ndi “nthawi yovuta.” Baibulo linalosera kuti panthawi imeneyi, anthu adzakhala “odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, . . . osayamika, osakhulupirika, opanda chikondi chachibadwa, osagwirizanitsika, odyerekeza, osadziletsa, owopsa, osakonda zabwino, achiwembu, aliuma, otukumuka chifukwa cha kunyada.” (2 Timoteyo 3:1-5) Makhalidwe oipa ngati amenewa amayambitsa kupanda chilungamo kwamtundu uliwonse.

6, 7. Kodi anthu masiku ano aona zinthu zotani zopanda chilungamo?

6 Pazaka 100 zapitazi, pachitika zinthu zopanda chilungamo zimene sizinachitikepo ndi kale lonse. Tikutero chifukwa chakuti m’zaka zimenezi kwachitika nkhondo zambirimbiri. Mwachitsanzo, akatswiri a mbiri yakale amati pankhondo yachiwiri ya padziko lonse, panafa anthu pakati pa 50 ndi 60 miliyoni, ndipo ambiri anali anthu wamba, amuna, akazi, ndi ana osalakwa. Kuchokera pamene nkhondoyo inatha, anthu mamiliyoni enanso ambiri aphedwa pankhondo zosiyanasiyana, ndipo ambirinso ndi anthu wamba. Satana akulimbikitsa zinthu zopanda chilungamo ngati zimenezi chifukwa chakuti wakwiya, ndipo akudziwa kuti posachedwapa Yehova amuwononga. Baibulo linalosera zimenezi kuti: “Mdyerekezi watsikira kwa inu, ali ndi mkwiyo waukulu, podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.”​—Chivumbulutso 12:12.

7 Chaka chilichonse, ndalama zimene zimawonongedwa pa zankhondo padziko lonse ndi madola pafupifupi 1 thililiyoni. Zili choncho, pali anthu mamiliyoni ambiri amene akuvutika. Tangoganizirani zimene zingachitike ngati ndalama zonsezi atazigwiritsa ntchito pazinthu zabwino. Anthu pafupifupi 1 biliyoni amagona ndi njala, pamene ena amachita kutaya chakudya. Malinga ndi lipoti la bungwe la United Nations, pafupifupi ana 5 miliyoni amafa ndi njala chaka chilichonse. Kupanda chilungamo kwake! Komanso pali ana osalakwa ambirimbiri amene amaphedwa mwa kuchotsa mimba. Akuti mwina ana amenewa amakwana 40 kapena 60 miliyoni chaka chilichonse. Nkhanza yake!

8. Kodi chilungamo chenicheni chidzapezeka bwanji?

8 Olamulira akulephera kuthetsa mavuto a anthu; ndipo anthu mwa mphamvu zawo sangasinthe zinthu. Mawu a Mulungu ananeneratu kuti m’nthawi yathu “anthu oipa ndi onyenga adzaipiraipirabe, kusocheretsa ena ndi kusocheretsedwa.” (2 Timoteyo 3:13) Anthu sangathetse kupanda chilungamo chifukwa chakuti kwazika mizu kwambiri m’dzikoli. Amene angakuthetse ndi Mulungu yekha wachilungamo. Ndi iye yekha amene angachotse Satana, ziwanda, ndi anthu oipa.​—Yeremiya 10:23, 24.

N’zomveka Kuda Nkhawa

9, 10. Kodi n’chifukwa chiyani Asafu anakhumudwa?

9 Kale, ngakhale anthu ena olemba Baibulo ankadandaula kuti n’chifukwa chiyani Mulungu sanalowerere pa zochitika za anthu ndi kukhazikitsa chilungamo chenicheni. Mwachitsanzo, taganizirani za mwamuna wina wa nthawi za m’Baibulo. Ameneyu ndi Asafu wotchulidwa pa timawu tapamwamba ta pa Salmo 73. Asafu mwina anali Mlevi wodziwa kuimba nyimbo mu ulamuliro wa Mfumu Davide kapena akuimira chabe akatswiri oimba nyimbo a fuko la Asafu. Iye ndi mbadwa zake anapeka nyimbo zambiri zimene zinkaimbidwa polambira Mulungu kukachisi. Komabe panthawi ina, munthu amene analemba salmo limeneli anakhumudwa ndi kulambira kwake. Anaona kuti anthu oipa zinthu zinkawayendera bwino, ankaoneka osangalala ndi osadziwa mavuto.

10 Timawerenga kuti: “Ndinachitira nsanje odzitamandira, pakuona mtendere wa oipa. Pakuti palibe zomangira pakufa iwo: Ndi mphamvu yawo n’njolimba. Savutika monga anthu ena; sasautsika monga anthu ena.” (Salmo 73:2-8) Koma patapita nthawi, mwamuna ameneyu anazindikira kuti maganizo akewo anali olakwika. (Salmo 73:15, 16) Wamasalmoyo ankayesetsa kusintha maganizo ake, koma sankamvetsabe chifukwa chake anthu oipa ankaoneka ngati salangidwa pa zoipa zawo pamene anthu abwino ankavutika.

11. Kodi Asafu wamasalmo anazindikira chiyani?

11 Komabe, munthu wokhulupirika ameneyu anazindikira zimene zidzachitikire oipa, ndi kuti Yehova adzakonza zinthu. (Salmo 73:17-19) Davide analemba kuti: “Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko: Pakudulidwa oipa udzapenya.”​—Salmo 37:9, 11, 34.

12. (a) Kodi cholinga cha Yehova n’chiyani pankhani ya kuipa ndi kupanda chilungamo? (b) Kodi mukuganiza bwanji za njira imeneyi yothetsera kupanda chilungamo?

12 Ndithu, cholinga cha Yehova ndicho kuthetseratu kuipa ndi kupanda chilungamo padziko lapansili panthawi yake. Ngakhale Akhristu okhulupirika ayenera kukumbukira mfundo imeneyi nthawi zonse. Yehova adzawononga anthu amene sachita chifuniro chake, koma adzadalitsa amene amachita chifuniro chakecho. “Apenyerera ndi maso ake, ayesa ana a anthu ndi zikope zake. Yehova ayesa wolungama mtima: Koma moyo wake umuda woipa ndi iye wakukonda chiwawa. Adzagwetsa pwatapwata misampha pa oipa; moto ndi miyala yasulfure, ndi mphepo yoopsa . . . Pakuti Yehova ndiye wolungama; akonda zolungama.”​—Salmo 11:4-7.

Dziko Latsopano Lachilungamo

13, 14. Kodi n’chifukwa chiyani chilungamo chidzakhala paliponse m’dziko latsopano?

13 Yehova akadzawononga dziko lopanda chilungamoli lolamulidwa ndi Satana, adzakhazikitsa dziko latsopano laulemerero. Lidzalamulidwa ndi Ufumu wakumwamba wa Mulungu, umene Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti aziupempherera. M’malo mwa kuipa ndi kupanda chilungamo, padzakhala chilungamo chokhachokha. Nthawi imeneyo, pemphero limene anaphunzitsa otsatira ake kuti ‘ufumu wanu ubwere, chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chomwechonso pansi pano,’ lidzayankhidwa lonse.​—Mateyo 6:10.

14 Baibulo limatiuza za boma limenelo, ndipo ndi boma limene anthu onse olungama akhala akuliyembekezera. Panthawiyo lemba la Salmo 145:16 lomwe limati, “[Yehova] muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo,” lidzakwaniritsidwa. Ndipo lemba la Yesaya 32:1 limati: “Taonani mfumu [Khristu Yesu ali kumwamba] idzalamulira m’chilungamo, ndi akalonga [anthu oimira Khristu padziko lapansi] adzalamulira m’chiweruzo.” Ponena za Mfumu Yesu Khristu, lemba la Yesaya 9:7 linalosera kuti: “Za kuwonjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.” Kodi mukutha kudziona nokha mukulamulidwa ndi boma lolungama limenelo?

15. Kodi Yehova adzawachitira chiyani anthu m’dziko latsopano?

15 M’dziko latsopano la Mulungu limenelo, sitidzakhala ndi chifukwa chonena mawu a pa Mlaliki 4:1, akuti: “Ndinabweranso tsono ndi kupenyera nsautso zonse zimachitidwa kunja kuno; ndipo taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwowa analibe wakuwatonthoza.” Kunena zoona, ndi zovuta kuganizira ndi nzeru zathu zopanda ungwiro mmene zinthu zidzakhalira bwino m’dziko latsopano lachilungamo limenelo. Kuipa sikudzakhalakonso, koma tsiku lililonse padzakhala zinthu zabwino zokhazokha. Yehova adzachotsa zinthu zoipa zonse, ndipo adzachita zimenezi m’njira imene sitingaiyerekezere n’komwe. M’pake kuti Yehova Mulungu anauza mtumwi Petulo kulemba kuti: “Pali miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekeza malinga ndi lonjezo lake, ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.”​—2 Petulo 3:13.

16. Kodi “miyamba yatsopano” yakhazikitsidwa bwanji, nanga n’chiyani chikuchitika pokonzekera “dziko lapansi latsopano”?

16 Tikunena pano, “miyamba yatsopano” imeneyi, yomwe ndi boma lakumwamba la Mulungu lolamulidwa ndi Khristu, lakhazikitsidwa kale. Anthu amene tingati ndi maziko a “dziko lapansi latsopano,” kutanthauza dziko la anthu olungama, akusonkhanitsidwa m’masiku otsiriza ano. Panopa anthuwa alipo pafupifupi 7 miliyoni, m’mayiko pafupifupi 235 komanso m’mipingo pafupifupi 100,000. Padziko lonse lapansi, anthu amenewa akhala akuphunzira za njira zolungama za Yehova, ndipo pakati pawo pali umodzi umene umalimbikitsidwa ndi chikondi chachikhristu. Umodzi umene uli pakati pawo umachita kuonekeratu ndipo sunayambe wathapo m’mbiri yawo yonse. Umenewu ndi umodzi umene ngakhale anthu olamulidwa ndi Satana sanauonepo. Chikondi ndi umodzi umenewu zili ngati kulawako madalitso a m’dziko latsopano la Mulungu, limene lidzalamuliridwa mwachilungamo.​—Yesaya 2:2-4; Yohane 13:34, 35; Akolose 3:14.

Satana Sadzapambana

17. Kodi n’chifukwa chiyani Satana akadzaukira anthu a Yehova komaliza, sadzapambana?

17 Posachedwapa, Satana ndi anthu ake adzaukira anthu a Yehova ndi cholinga chowawonongeratu. (Ezekieli 38:14-23) Zimenezi zidzakhala mbali ya zimene Yesu anati ndi “chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pachiyambi cha dziko kufikira lerolino, ndipo sichidzachitikanso.” (Mateyo 24:21) Kodi Satana adzapambana? Ayi, chifukwa Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti: “Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa: Asungika kosatha: Koma adzadula mbumba za oipa. Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”​—Salmo 37:28, 29.

18. (a) Kodi Mulungu adzatani Satana akadzaukira anthu ake? (b) Kodi kukambirana nkhani ya m’Baibulo imeneyi ya kupambana kwa chilungamo kwakuthandizani bwanji?

18 Satana ndi gulu lake akadzaukira atumiki a Yehova, umenewo udzakhala mwano womaliza. Yehova, kudzera mwa Zekariya, analosera kuti: “Iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m’diso [langa].” (Zekariya 2:8) Zili ngati kuti winawake akumutosa Yehova ndi chala m’diso mwake. Nthawi yomweyo iye adzafafaniziratu adaniwo. Atumiki a Yehova ndi anthu achikondi, ogwirizana, amtendere, ndi omvera malamulo kwambiri padziko lonse. Choncho kuwaukira kumeneko sikudzakhala komveka, kudzakhala kupanda chilungamo. Mulungu ‘wokonda chilungamo’ kwambiri ameneyu, sadzalola zimenezi. Powamenyera nkhondo, adzawononga kotheratu adani a anthu ake, kuti chilungamo chipambane, ndipo adzapulumutsa anthu onse amene amalambira Mulungu yekhayo woona. Posachedwapa, tiona zinthu zodabwitsa komanso zosangalatsa kwambiri.​—Miyambo 2:21, 22.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi n’chifukwa chiyani kupanda chilungamo kwachuluka?

• Kodi Yehova adzathetsa bwanji kupanda chilungamo padziko lapansi?

• Kodi phunziroli la kupambana kwa chilungamo lakukhudzani bwanji?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 23]

Kuipa kunali kochuluka Chigumula chisanachitike, ndipo kwachulukanso “m’masiku otsiriza” ano

[Chithunzi pamasamba 24, 25]

M’dziko latsopano la Mulungu, mudzakhala chilungamo m’malo mwa kuipa