Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi “Chipangano Chakale” Chinatha Ntchito?

Kodi “Chipangano Chakale” Chinatha Ntchito?

Kodi “Chipangano Chakale” Chinatha Ntchito?

MU 1786 dokotala wina wa ku France anasindikiza buku lonena za mmene thupi linapangidwira ndiponso mmene limagwirira ntchito (Traité d’anatomie et de physiologie). Bukuli amaliona kuti linalembedwa bwino kwambiri. Posachedwapa, buku limodzi lotereli linagulitsidwa madola opitirira 27,000 a ku America chifukwa choti masiku ano mabukuwa n’ngovuta kupeza. Ngakhale zili choncho, masiku ano ndi odwala ochepa amene angadalire dokotala wogwiritsa ntchito buku la zachipatala la makedzana limeneli. Kutchuka kwa bukuli komanso mmene linalembedwera sikupangitsa odwala kuliona kuti n’lothandiza.

Umu ndi mmenenso anthu ambiri amaonera “Chipangano Chakale.” Iwo amaona kuti nkhani zokhudza mbiri ya Isiraeli n’zothandiza ndiponso amachita chidwi ndi ndakatulo zake. Koma amaganiza kuti si nzeru kutsatira malangizo olembedwa zaka 2,400 zapitazo. Amaona kuti sayansi, malonda ndiponso moyo wabanja zasintha kwambiri kusiyana ndi mmene zinalili pamene Baibulo linalembedwa. Philip Yancey, yemwe anali mkonzi wa magazini ina (Christianity Today), analemba m’buku lake (The Bible Jesus Read) kuti: “Nkhani zambiri za m’Chipangano Chakale sizimveka ndipo zomwe zimamveka n’zogonthetsa m’makutu. Zifukwa zimenezi ndiponso zina zimachititsa kuti anthu asamawerenge Chipangano Chakale, chomwe ndi mbali yaikulu ya Baibulo lonse.” Maganizo oterowo sikuti ndi achilendo.

Pasanathe zaka 50 kuchokera pamene mtumwi Yohane anaphedwa cha m’ma 100 C.E, wachinyamata wina wolemera dzina lake Marcion ananena poyera kuti, Akhristu ayenera kukana Chipangano Chakale. Katswiri wa mbiri yakale wa ku England, Robin Lane Fox anati, Marcion ananena kuti, “‘Mulungu’ wa m’Chipangano Chakale anali mbuli yotheratu yankhanza yomwe inali kukonda mbava ndi zigawenga monga Mfumu Davide wa Isiraeli. Koma Khristu anasonyeza kuti iye anali Mulungu wabwino kwambiri yemwe anali wosiyana ndi wa m’Chipangano Chakale.” Fox ananenanso kuti zikhulupiriro zimenezi “zinatchedwa ‘Mfundo za Marcion’ ndipo anthu ambiri anali kuzikonda kwambiri, makamaka olankhula Chisuriya a kum’mawa, mpaka zaka za m’ma 300.” Ndipo anthu ena akutsatira mfundo zimenezi mpaka pano. Patatha zaka 1,600, zimenezi zinachititsa Philip Yancey kulemba kuti: “Chipangano Chakale chikutha mphamvu mofulumira pakati pa Akhristu ndipo changotsala pang’ono kusiyiratu kugwira ntchito masiku ano.”

Kodi “Chipangano Chakale” chalowedwa m’malo ndi “Chipangano Chatsopano”? Kodi mawu oti “Yehova wa makamu” mu “Chipangano Chakale” tingawagwirizanitse bwanji ndi mawu oti “Mulungu wachikondi ndi wamtendere” mu “Chipangano Chatsopano”? (Yesaya 13:13; 2 Akorinto 13:11) Kodi “Chipangano Chakale” chingakuthandizeni masiku ano?