Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Linalembedwa Kuti Litilangize’

‘Linalembedwa Kuti Litilangize’

‘Linalembedwa Kuti Litilangize’

“SALEKA kulemba mabuku ambiri.” (Mlaliki 12:12) Mawu amenewa ndi oonanso masiku ano monga mmene analili nthawi imene analembedwa. Zili choncho chifukwa cha mabuku ochuluka amene asindikizidwa masiku ano. Ndiyeno, kodi munthu wozindikira angasankhe bwanji mabuku oti awerenge?

Anthu ambiri akamaganizira zowerenga buku amafuna kudziwa kaye amene analemba. Ofalitsa mabuku amafotokoza mwachidule kumene wolemba buku akuchokera, maphunziro ake ndiponso mabuku ena amene analemba. Kudziwa wolemba n’kofunika, monga mmene zinkachitikira kale kuti akazi olemba mabuku ankakonda kuika mayina a amuna ngati ndiwo analemba bukulo kuti anthu owerenga asalidelere kuti lalembedwa ndi mkazi.

Monga mmene taonera m’nkhani yapitayi, n’zomvetsa chisoni kuti anthu ena sawerenga Malemba Achiheberi chifukwa amaganiza kuti Mulungu amene amafotokozedwa mmenemu ndi wankhanza ndipo ankapha adani ake mopanda chifundo. * Tiyeni tione zimene Malemba Achiheberi ndi Malemba Achigiriki Achikristu akutiuza za Wolemba Baibulo.

Zimene Akutiuza za Wolemba Baibulo

Malemba Achiheberi amafotokoza zimene Mulungu anauza mtundu wa Isiraeli kuti: “Ine Yehova sindisinthika.” (Malaki 3:6) Patatha zaka pafupifupi 500, wolemba Baibulo Yakobe anati, ponena za Mulungu: “Iye sasintha ngati kusuntha kwa mthunzi.” (Yakobe 1:17) Ndiyeno, n’chifukwa chiyani anthu ena amaganiza kuti Mulungu amene amafotokozedwa m’Malemba Achiheberi amasiyana ndi amene ali m’Malemba Achigiriki Achikristu?

Yankho lake n’lakuti mbali zosiyanasiyana za umunthu wa Mulungu zimafotokozedwa m’zigawo zosiyanasiyana za Baibulo. Mwachitsanzo, buku la Genesis lokha limafotokoza kuti Mulungu “anavutika m’mtima mwake,” ndiye “mwini kumwamba ndi dziko lapansi” ndiponso ndi “Woweruza wa dziko lonse lapansi.” (Genesis 6:6; 14:22; 18:25) Kodi mawu onsewa akunena za Mulungu mmodzi yemweyo? Inde.

Mwachitsanzo: Woweruza angadziwike ndi anthu amene wawaweruzira milandu kuti ndi wolimbikitsa kwambiri malamulo. Koma ana ake kunyumba angamuone kuti ndi bambo wachikondi ndi wowolowa manja. Ndipo mabwenzi ake apamtima angamuone kuti ndi munthu wochezeka ndiponso wansangala. Munthu mmodzi yemweyo ndi woweruza, bambo komanso bwenzi. Iye wangosonyeza khalidwe lake pazinthu zosiyanasiyana.

Mofanana ndi zimenezi, Malemba Achiheberi amafotokoza Yehova kuti ndi “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi.” Koma timaphunziranso kuti iye ‘samasula wopalamula.’ (Eksodo 34:6, 7) Mbali ziwirizi zikusonyeza tanthauzo la dzina la Mulungu. Dzina lakuti “Yehova” limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhala.” Zimenezi zikusonyeza kuti, Mulungu akhoza kukhala chilichonse chimene akufuna kuti akwaniritse malonjezo ake. (Eksodo 3:13-15) Koma iye amakhalabe Mulungu yemweyo. Yesu anati: “Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.”​—Maliko 12:29.

Kodi Malemba Achiheberi Analowedwa M’malo?

Nthawi zambiri anthu amasintha mabuku akapeza mfundo zina zatsopano kapena maganizo a anthu akasintha. Kodi Malemba Achigiriki Achikristu analowa m’malo Malemba Achiheberi mwa njira imeneyi? Ayi.

Yesu akanafuna kuti nkhani zokhudza utumiki wake ndiponso zomwe ophunzira ake analemba zilowe m’malo Malemba Achiheberi, mosakayikira iye akanena zimenezi. Koma ponena za Yesu atangotsala pang’ono kupita kumwamba, Luka anati: “Anayamba kuwasanthulira Zolemba za Mose ndi za aneneri [m’Malemba Achiheberi] zonse akumawatanthauzira [ophunzira ake awiri] zinthu zokhudza iye m’Malemba onse.” Kenako, Yesu anaonekera kwa atumwi ake okhulupirika ndi anthu ena. Nkhaniyo inapitiriza kuti: “Ndiyeno anati kwa iwo: “Awa ndi mawu anga amene ndinakuuzani pamene ndinali nanu pamodzi, kuti zonse zokhudza ine zolembedwa m’chilamulo cha Mose, m’Zolemba za aneneri ndi m’Masalimo zikwaniritsidwe.” (Luka 24:27, 44) Yesu sakanagwiritsa ntchito Malemba Achiheberi pamapeto a utumiki wake wa padziko lapansi ngati malembawo anali atatha ntchito.

Mpingo wachikhristu utakhazikitsidwa, otsatira a Yesu ankagwiritsabe ntchito Malemba Achiheberi pofotokoza maulosi amene anali asanakwaniritsidwe ndi mfundo za m’Chilamulo cha Mose zomwe zinali zothandiza. Ankawagwiritsanso ntchito pofotokoza nkhani za atumiki a Mulungu akale, omwe zitsanzo zawo zabwino zimalimbikitsa Akhristu kukhalabe okhulupirika. (Machitidwe 2:16-21; 1 Akorinto 9:9, 10; Aheberi 11:1–12:1) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Malemba onse anawauzira ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa.” * (2 Timoteyo 3:16) Kodi Malemba Achiheberi ndi othandiza motani masiku ano?

Malangizo Othandiza Pamoyo wa Tsiku ndi Tsiku

Taganizirani za vuto la masiku ano la kusankhana mtundu. Mumzinda wina womwe uli kum’mawa kwa Ulaya, mwamuna wina wa ku Ethiopia wa zaka 21 anati: “Tikamafuna kupita kulikonse timafunikira kuyenda kagulu. Timaona kuti tikakhala kagulu sangatiukire.” Ndipo iye anapitiriza kuti: “Sitingayende nthawi ikapitirira 6 koloko madzulo, makamaka m’timisewu tapansi. Anthu akamatiyang’ana amangoona khungu lathu basi.” Kodi Malemba Achiheberi amati chiyani pavuto limeneli?

Aisiraeli akale anauzidwa kuti: “Mlendo akagonera m’dziko mwanu, musamam’sautsa. Mlendo wakugonera kwa inu mumuyese pakati pa inu monga wa m’dziko momwemo; um’konde monga udzikonda wekha; popeza munali alendo m’dziko la Aigupto.” (Levitiko 19:33, 34) Kalelo Aisiraeli ankafunika kulemekeza anthu ochokera kwina kapena kuti “alendo,” ndipo lamulo limeneli lili m’Malemba Achiheberi. Kodi simukuvomereza kuti mfundo zomwe zili m’lamuloli zingathandize kuthetsa vuto la kusankhana mitundu masiku ano?

Ngakhale kuti Malemba Achiheberi safotokoza kwambiri nkhani zachuma, ali ndi mfundo zothandiza za mmene tingagwiritsire ntchito ndalama mwanzeru. Mwachitsanzo, lemba la Miyambo 22:7 limati: “Wokongola ndiye kapolo wa wom’kongoletsa.” Alangizi ambiri a zachuma amavomereza kuti kugula zinthu pangongole mosaganizira bwino kungalowetse munthu m’mavuto a zachuma.

Kuwonjezera pamenepo, kusakasaka chuma mosaganizira zotsatirapo zake, komwe ndi kofala kwambiri m’dziko lomwe anthu akukonda chumali, kunafotokozedwa bwino kwambiri ndi Mfumu Solomo, yemwe anali wolemera kwambiri. Iye analemba kuti: “Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu; ichinso ndi chabe.” (Mlaliki 5:10) Limeneli ndi chenjezo labwino kwambiri.

Chiyembekezo cha M’tsogolo

Baibulo lonse lili ndi mfundo imodzi yokha yakuti: Ufumu womwe wolamulira wake ndi Yesu Khristu ndiwo udzasonyeze kuti Mulungu ndiye woyenera kulamulira ndiponso ndiwo udzayeretsa dzina Lake.​—Danieli 2:44; Chivumbulutso 11:15.

M’Malemba Achiheberi timawerenga mmene moyo udzakhalira mu Ufumu wa Mulungu. Zimenezi zimatitonthoza ndipo zimatithandiza kuyandikira kwambiri kwa Yehova Mulungu, yemwe ndi Gwero la chitonthozo chimenechi. Mwachitsanzo, mneneri Yesaya ananeneratu kuti, anthu ndi nyama adzakhala pa mtendere. Iye anati: “Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng’ombe ndi mwana wa mkango ndi choweta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera.” (Yesaya 11:6-8) Chimenechi n’chiyembekezo chosangalatsa kwabasi.

Nanga bwanji anthu amene akuvutika chifukwa cha kusankhana mitundu kapena fuko, matenda aakulu, kapenanso mavuto a zachuma? Ponena za Yesu Khristu, Malemba Achiheberi ananeneratu kuti: “Adzapulumutsa waumphawi wopfuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphawi, nadzapulumutsa moyo wa aumphawi.” (Salmo 72:12, 13) Malonjezo amenewo ndi othandiza chifukwa amalimbikitsa anthu amene amawakhulupirira kuti akhale ndi chiyembekezo komanso chidaliro.​—Aheberi 11:6.

N’chifukwa chake mtumwi Paulo analemba kuti: “Zonse zimene zinalembedweratu zinalembedwa kuti zitilangize ife, kuti mwa chipiriro chathu ndi mwa chitonthozo cha m’Malemba tikhale ndi chiyembekezo.” (Aroma 15:4) N’zoona, Malemba Achiheberi adakali ofunika kwambiri monga Mawu a Mulungu ouziridwa. Malembawa ndi othandiza kwambiri masiku ano. Tikukhulupirira kuti muyesetsa kuphunzira zochuluka za zimene Baibulo lonse limaphunzitsa kwenikweni ndipo motero mudzayandikira kwa Yehova Mulungu, amene analilemba.​—Salmo 119:111, 112

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 M’nkhani ino, “Chipangano Chakale” chikutchedwa Malemba Achiheberi. (Onani bokosi loti “Chipangano Chakale kapena Malemba Achiheberi?” patsamba 6.) Mboni za Yehova zimatchulanso “Chipangano Chatsopano” kuti Malemba Achigiriki Achikristu.

^ ndime 13 Malemba Achiheberi ali ndi mfundo zambiri zothandiza masiku ano. Koma, tiyenera kudziwa kuti Akhristu sali pansi pa Chilamulo chimene Mulungu anapereka ku mtundu wa Isiraeli kudzera mwa Mose.

[Bokosi patsamba 6]

KODI TIZITI “CHIPANGANO CHAKALE” KAPENA MALEMBA ACHIHEBERI?

Mawu akuti “chipangano chakale” akupezeka pa 2 Akorinto 3:14 m’Baibulo la King James Version. M’Baibulo limeneli mawu akuti “chipangano” amaimira mawu Achigiriki akuti di·a·theʹke. Kodi mawu akuti “chipangano chakale” opezeka pa 2 Akorinto 3:14 amatanthauza chiyani?

Wolemba mabuku otanthauzira mawu dzina lake Edward Robinson anati: “Popeza pangano lakale lili m’mabuku a Mose, [mawu akuti di·a·theʹke] amaimira buku la chipangano, Zolemba za Mose, kapena kuti chilamulo.” Pa 2 Akorinto 3:14, mtumwi Paulo ankanena za Chilamulo cha Mose, chomwe ndi kachigawo ka Malemba Achiheberi.

Motero, kodi dzina loyenera la mabuku 39 oyambirira a m’Malemba Oyera ndi liti? M’malo monena kuti mbali imeneyi ya Baibulo inatha ntchito kapena kuti ndi yakale, Yesu Khristu ndi otsatira ake anaitcha kuti “Malemba” ndiponso “Malemba oyera.” (Mateyo 21:42; Aroma 1:2) Choncho, mogwirizana ndi mawu ouziridwa amenewa, Mboni za Yehova zimatchula “Chipangano Chakale” kuti Malemba Achiheberi chifukwa chakuti mbali yaikulu ya Baibulo imeneyi poyamba inalembedwa m’Chiheberi. Ndiyeno, malemba omwe anthu ambiri amati Chipangano Chatsopano, Mboni za Yehova zimawatcha Malemba Achigiriki Achikristu, chifukwa chakuti anthu omwe Mulungu anawauzira kulemba anagwiritsa ntchito Chigiriki.

[Zithunzi patsamba 4]

Munthu angadziwike kuti ndi woweruza wotsatira malamulo, bambo wachikondi ndiponso bwenzi

[Chithunzi patsamba 5]

Yesu anagwiritsa ntchito Malemba Achiheberi m’nthawi yonse ya utumiki wake

[Zithunzi patsamba 7]

Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zomwe zingathandize munthu kusankha bwino zochita?