Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Musaiwale Kuti M’pofunika Kwambiri Kuyamikira Ena

Musaiwale Kuti M’pofunika Kwambiri Kuyamikira Ena

Musaiwale Kuti M’pofunika Kwambiri Kuyamikira Ena

KODI munamvapo munthu wina akudandaula kuti nthawi zambiri bwana wake samuyamikira? Kapena kodi inuyo munadandaulapo ndi zimenezi? Ngati muli wachinyamata, kodi munadandaulapo kuti makolo anu kapena aphunzitsi anu sakuyamikirani nthawi zambiri?

Ena omwe amadandaula ndi zimenezi angakhale ndi zifukwa zabwino. Koma munthu wina wa ku Germany amene amaphunzitsa mabwana mmene angalimbikitsire antchito awo anati, antchito akamadandaula kuti sakuyamikiridwa, chimene kwenikweni chimawadandaulitsa n’chakuti mabwana awo sachita chidwi ndi moyo wawo. Mulimonsemo, pamakhala chinachake chimene chikusoweka. Kuti tikhale osangalala pamoyo wathu, m’pofunikira kumayamikirana ndiponso kuchita chidwi ndi moyo wa anzathu.

N’chimodzimodzinso pankhani ya kupembedza. Anthu mumpingo ayenera kusonyeza kwambiri mzimu woyamikirana, kukondana, ndi kuchita chidwi ndi moyo wa ena. Amakhala ndi makhalidwe amenewa akamatsatira mfundo za m’Baibulo. Ngakhale mpingo umene ukuona kuti ukuchita bwino pambali imeneyi, ukhoza kuchita bwino kuposa pamenepo. Poganizira zimenezi, tiyeni tione zitsanzo zabwino zitatu pankhani ya kuyamikira: Elihu, amene ndi mtumiki wa Mulungu yemwe anakhalako Chikhristu chisanayambe, mtumwi Paulo, ndiponso Yesu Khristu amene.

Kupereka Uphungu Mwachikondi ndi Mwaulemu

Elihu, amene mwachionekere anali wachibale wa Abulahamu, anathandiza kwambiri Yobu kuti awongolere kaganizidwe kake pankhani yokhudza ubwenzi wake ndi Mulungu. Elihu anali munthu wokoma mtima ndi waulemu. Iye anadikira moleza mtima kuti nthawi yake yolankhula ifike. Elihu anachita zinthu mosiyana ndi anzake a Yobu achinyengo aja, amene ankangomutola zifukwa Yobuyo. N’zoona kuti iye anapereka uphungu kwa Yobu, koma anamuyamikiranso chifukwa cha khalidwe lake lolungama. Iye anatero mwachikondi ndi momuganizira ngati mnzake. Anasonyeza zimenezo pomutchula dzina Yobuyo, kusiyana ndi enawo amene sanam’tchule dzina n’komwe. Elihu anapempha Yobu mwaulemu kuti: “Komatu, Yobu, mumvere maneno anga, mutcherere khutu mawu anga.” Posonyeza kuti akumvetsa mavuto a Yobu, iye anati: “Taonani, ndikhala kwa Mulungu ngati inu; inenso ndinaumbidwa ndi dothi.” Kenako anamuyamikira kuti: “Ngati muli nawo mawu mundiyankhe. Nenani, pakuti ndifuna kukulungamitsani.”​—Yobu 33:1, 6, 32.

Kuchitira anthu ena ulemu ndi njira ina yowayamikira. Timakhala ngati tikuwauza kuti, ‘Ndinu munthu wofunikira kwa ine.’ Tikatero, timasonyeza kuti timawaganizira ndi kuwakonda.

Kusonyeza ulemu si nkhani yongotsatira mfundo za makhalidwe abwino mwamwambo basi. Kuti tiwalimbikitsedi anthu ena, chikondi chathu ndi ulemu wathu ziyenera kuchokera pansi pa mtima.

Kuyamikira Ena Mwanzeru

Mtumwi Paulo anasonyeza mmene kuyamikira ena mwanzeru kumathandizira. Mwachitsanzo, pamene iye anali kulalikira ku Atene ali pa ulendo wake wachiwiri waumishonale, ananena mfundo zoikira kumbuyo Chikhristu pamaso pa Agiriki anzeru za dziko. Taonani mmene anachitira zinthu mwanzeru. “Ena anzeru za dziko, Aepikureya ndi Asitoiki anayamba kutsutsana naye. Ndipo ena anali kunena kuti: ‘Kodi nayenso wobwetuka uyu akufuna kunena chiyani?’ Enanso anati: ‘Akuoneka kuti ndi wofalitsa milungu yachilendo.’” (Machitidwe 17:18) Ngakhale kuti ankamunyoza motero, Paulo anakhalabe wodekha ndipo anayankha kuti: “Amuna inu a mu Atene, ndaona kuti m’zinthu zonse inu mumaopa kwambiri milungu kuposa mmene ena amachitira.” Paulo sanawadzudzule anthuwo chifukwa cholambira mafano, m’malo mwake anawayamikira chifukwa chochita khama popembedza.​—Machitidwe 17:22.

Kodi Paulo ankangowayamikira anthuwo mwachinyengo? Ayi. Anadziwa kuti sinali ntchito yake kuweruza anthuwo, ndiponso ankadziwa kuti iyenso panthawi ina sankadziwa choonadi. Ntchito yake inali kuuza anthu uthenga wa Mulungu, osati kuwaweruza ayi. Paulo ankadziwa mfundo yakuti anthu ena amene amaikira kumbuyo ziphunzitso zonyenga ndi mtima wonse, amadzakhalanso olimba kwambiri pankhani yoikira kumbuyo chipembedzo choona. Masiku anonso, Mboni za Yehova zimadziwa mfundo imeneyi.

Njira imene Paulo anagwiritsa ntchito inali yabwino ndiponso yothandizadi. Motero, “anthu ena anadziphatika kwa iye nakhala okhulupirira. Ena mwa iwo anali Diyonisiyo, woweruza m’bwalo la Areopagi, ndi mzimayi wina dzina lake Damarisi, ndi enanso.” (Machitidwe 17:34) Pamenepatu Paulo anachita zinthu mwanzeru poyamikira anthu a ku Atenewo chifukwa cha kukhulupirika pa kulambira kwawo, ngakhale kuti kunali konyenga, m’malo mowadzudzula chifukwa chosadziwa choonadi. Anthu ambiri amene amasocheretsedwa ndi mfundo zabodza amakhala a mtima wabwino ndithu.

Paulo anagwiritsanso ntchito nzeru imeneyi pamene anaitanidwa kuti akayankhe mlandu pamaso pa Herode Agiripa Wachiwiri. Zinali zodziwika kuti Herode anali pachibwenzi ndi mchemwali wake Berenike, ndipo Mawu a Mulungu amaletseratu zimenezi. Koma Paulo sanafune kunenapo chilichonse chokhudza nkhani imeneyo. M’malo mwake, anayesetsa kupeza chifukwa choyenerera kumuyamikira Herode. Iye anati: “Inu Mfumu Agiripa, ine ndili wosangalala kuti lero ndidziteteza pamaso panu, pa zinthu zonse zimene Ayuda akundineneza. Makamaka inu pokhala katswiri pa miyambo yonse, komanso pa zimene Ayuda amakangana.”​—Machitidwe 26:1-3.

Ndi bwino kuti ifenso tizigwiritsa ntchito njira yanzeru imeneyi pochita zinthu ndi anthu ena. Kuyamikira anthu amene timakhala nawo pafupi, amene timaphunzira nawo limodzi kapena amene timagwira nawo ntchito, kumathandiza kuti tizikhala mwamtendere ndi ena ndiponso kumalimbikitsa makhalidwe abwino. Tikamayamikira zenizeni anthu oona mtima, tingathe kuwathandiza kuti asiye ziphunzitso zonama n’kuyamba kutsatira choonadi.

Yesu Ndiye Chitsanzo Chabwino Kwambiri Pankhani ya Kuyamikira Ena

Yesu ankayamikira ena. Mwachitsanzo, ataukitsidwa n’kupita kumwamba, Yesu molamulidwa ndi Mulungu, anayamikira mipingo seveni ya ku Asia Minor kudzera mwa mtumwi Yohane. Iye nthawi zonse ankayamikira anthu pakafunika kutero. Kumipingo ya ku Efeso, Peregamo, ndi Tiyatira, iye ananena mawu osiyanasiyana oyamikira, monga akuti: “Ndikudziwa ntchito zako, kulimbika kwako, ndi chipiriro chako, ndi kuti sungalekelere anthu oipa”; “ukugwirabe zolimba dzina langa, ndipo sunakane kuti umakhulupirira mwa ine”; ndiponso akuti: “Ndikudziwa ntchito zako, chikondi chako, chikhulupiriro chako, utumiki wako, ndi chipiriro chako. Ndikudziwanso kuti ntchito zako zatsopano lino n’zambiri kuposa zoyamba zija.” Ngakhale kuti mpingo wa ku Sade anaupatsa uphungu wamphamvu, Yesu anayamikira anthu ena a kumeneko amene anafunikiradi kuwayamikira. Iye anati: “Ngakhale ndi choncho, uli nawo maina angapo mu Sade a amene sanaipitse malaya awo akunja. Amenewa adzayenda ndi ine atavala malaya oyera, chifukwa ali oyenerera.” (Chivumbulutso 2:2, 13, 19; 3:4) Chimenechitu n’chitsanzo chabwino choti titsatire.

Potsanzira Yesu, tisamangodzudzula gulu lonse la anthu chifukwa cha anthu ochepa amene akulakwitsa pa gulupo. Komanso tisamangopereka uphungu koma osayamikira poyenera kuyamikira. Ndi bwinonso kukumbukira kuti ngati nthawi zonse timayamikira ena pamene tikufuna kuwapatsa uphungu basi, nthawi zina anthuwo samva n’komwe zimene tikuwayamikirazo. Musamaumire kuyamikira ena akachita zabwino kuti asadzavutike kulandira uphungu wanu nthawi ina.

Akulu Amene Amayamikira Ena Moyenera

Mlongo wina amene tsopano akutumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Ulaya, dzina lake Cornelia, akukumbukira zimene zinachitika m’ma 1970. Woyang’anira woyendayenda anam’funsa mmene pulogalamu yake yophunzira payekha ndi kuwerenga magazini inali kuyendera. Iye anati: “Ndinachita manyazi pang’ono.” Komabe iye anavomereza kuti sakwanitsa kuwerenga nkhani zonse za m’magazini athu. Iye akukumbukira kuti: “M’malo mondidzudzula, anandiyamikira chifukwa ndimayesetsabe kuwerenga nkhani zimene ndimatha. Mawu ondiyamikirawo anandilimbikitsa kwambiri, moti kuchokera nthawi imeneyo ndimayesetsa kuwerenga nkhani iliyonse m’magazini athu.”

Ray, amenenso akutumikira pa nthambi ina ya ku Ulaya, akukumbukira tsiku limene anayamba kuchita upainiya. Woyang’anira wotsogolera wa mpingo wawo, amene anali munthu wotanganidwa kwambiri ndi ntchito yake, kusamalira banja lake, komanso ntchito za mumpingo, analowa mu Nyumba ya Ufumu madzulowo ndi kupita pamene panali iyeyo n’kum’funsa kuti: “Kaya mwauyamba bwanji upainiya?” Tsopano padutsa zaka zopitirira 60, koma Ray akukumbukirabe chidwi chimenechi, chomwe mkuluyo anam’sonyeza.

Monga taonera pa nkhani za anthu awirizi, kuyamikira ena moona mtima pa zimene achita, osati kungowayamikira mwamwambo chabe kapena mwachinyengo, kungawalimbikitse kwambiri. Mumpingo, timakhala ndi zifukwa zambiri zoyamikirira okhulupirira anzathu. Tingawayamikire chifukwa cha mtima wawo wofuna kutumikira Yehova ndiponso mayankho awo amene amawakonzekera bwino. Tingawayamikirenso chifukwa cha mmene ayesetsera kuthetsa mantha pokamba nkhani papulatifomu kapena pochita chitsanzo, khama lawo pantchito yolalikira ndi yophunzitsa, komanso kuyesetsa kwawo kuika patsogolo zinthu za Ufumu ndi zolinga zauzimu. Tikamayamikira ena, ifenso timakhala osangalala kwambiri pamoyo wathu.​—Machitidwe 20:35.

Ndi bwino kuti akulu mumpingo aziyamikira mpingo pantchito zabwino zimene ukuchita. Ndipo uphungu ukakhala wofunikira, aziupereka mwachikondi. Komabe, iwo asayembekezere kuti abale ndi alongo azichita zonse mosalakwitsa ngakhale pang’ono.

Akulu amene amatengera chitsanzo cha Elihu chosonyeza ena ulemu ndi chikondi, cha Paulo chochita zinthu mwanzeru, ndiponso cha Yesu chochita zinthu moganizira ena, amalimbikitsa kwambiri abale awo. Kuyamikirana kumathandiza kuti anthu azichita zinthu bwino kwambiri ndiponso kuti azikhala mosangalala ndi mogwirizana. Yesu anakondwera kwambiri paubatizo wake pamene anamva Atate wake wakumwamba akumuyamikira kuti: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndimakondwera nawe.” (Maliko 1:11) Tiyeni tionetsetse kuti tikuthandiza abale athu kukhala osangalala mwa kuwayamikira mochokera pansi pa mtima.

[Zithunzi patsamba 15]

Kuyamikira ena mwanzeru kunathandiza kwambiri Paulo, choncho ifenso kungatithandize

[Chithunzi patsamba 16]

Kuyamikira ena mochokera pansi pa mtima kungawathandize kwambiri kuyamba kuchita zinthu bwino