Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi Yesu ankatanthauza chiyani ponena kuti kapolo wake wokhulupirika adzakhala “wanzeru”?

Yesu anafunsa kuti: “Ndani kwenikweni amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amene mbuye wake anamuika kuyang’anira antchito ake a pakhomo, kuwapatsa chakudya chawo panthawi yoyenera?” (Mateyo 24:45) “Kapolo” wopereka “chakudya” chauzimu ameneyu ndi gulu la Akhristu odzozedwa. N’chifukwa chiyani Yesu anawatcha kuti anzeru? *

Tingamvetse bwino tanthauzo la mawu akuti “wanzeru” tikaona zimene Yesu mwiniyo anaphunzitsa. Mwachitsanzo, pamene anali kunena za “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” Yesu ananena fanizo la anamwali khumi amene ankadikirira mkwati. Anamwaliwo akutikumbutsa za Akhristu odzozedwa amene analipo chaka cha 1914 chisanafike. Iwowa ankadikira mwatcheru kubwera kwa Mkwati wamkulu, Yesu Khristu. Mwa anamwali khumiwo, asanu analibe mafuta okwanira panthawi imene mkwati anafika, ndipo sanalowe kumadyerero a ukwatiwo. Koma anamwali asanu enawo anali ochenjera. Iwowa anali ndi mafuta okwanira, choncho nyale zawo sizinazime mpaka mkwati anafika, ndipo analoledwa kulowa ku madyerero a ukwati.​—Mateyo 25:10-12.

Yesu atabwera mu ulamuliro wa Ufumu wake mu 1914, ambiri mwa Akhristu odzozedwa ankayembekezera kuti akayamba kulamulira naye kumwamba nthawi yomweyo. Komabe, panthawi imeneyi n’kuti padziko pano pali ntchito yambiri yoti achite, ndipo ena mwa iwo sankafuna kugwira ntchitoyo. Mofanana ndi anamwali opusa aja, Akhristuwo sanali okonzeka kupititsa patsogolo zinthu zauzimu, choncho sanathenso kupitiriza kunyamula nyale zawo. Ngakhale zinali choncho, ambiri mwa odzozedwawo anali ochenjera, anachita zinthu mwanzeru ndiponso moyang’ana m’tsogolo, motero anakhalabe olimba mwauzimu. Atadziwa kuti ntchito yawo idakalipo yambiri, anapitirizabe kuigwira ntchitoyo ndi mtima wonse. Pochita zimenezi, anasonyeza kuti iwo ndiwo “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.”

Taganiziraninso mawu akuti “wochenjera” a pa Mateyo 7:24, amene amatanthauzanso kuti “wanzeru.” Yesu anati: “Aliyense wakumva mawu angawa ndi kuwachita adzafanizidwa ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe.” Munthuyu anamanga nyumba yake pathanthwe kuti isadzagwe ndi chimvula champhamvu. Koma munthu wopusa anamanga pa mchenga, ndipo nyumbayo inagwa. Motero, munthu amene amatsatira Yesu mwanzeru ndi amene amaoneratu mavuto omwe angabwere chifukwa chotsatira nzeru za anthu. Chifukwa chokhala munthu wanzeru ndi wozindikira, munthuyo amakhulupirira kwambiri Yesu. Komanso zimene amaphunzitsa ndiponso kuchita, zimakhala zochokera pa zimene Yesu anaphunzitsa. Nayenso “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amachita zimenezi.

Taonaninso mmene mawu akuti “wanzeru” awagwiritsira ntchito m’malemba osiyanasiyana a Chiheberi. Mwachitsanzo, Farao anasankha Yosefe kukhala mkulu woyang’anira zakudya mu Iguputo monse. Imeneyi inali njira imene Yehova anakonza kuti anthu ake Aheberi akhale ndi zakudya. N’chifukwa chiyani Yosefe anaikidwa pa udindo umenewu? Farao anauza Yosefe kuti: “Palibe wina wakuzindikira ndi wanzeru ngati iwe.” (Genesis 41:33-39; 45:5) Baibulo limanenanso za Abigayeli kuti anali “wa nzeru yabwino.” Iye anapereka chakudya kwa Davide, yemwe anali wodzozedwa wa Yehova, pamodzi ndi anyamata a Davidewo. (1 Samueli 25:3, 11, 18) Tinganene kuti Yosefe ndi Abigayeli anali anthu anzeru chifukwa choti ankazindikira chifuniro cha Mulungu ndipo anachita zinthu moyang’ana m’tsogolo ndiponso moganiza bwino.

Motero, pofotokoza kuti kapolo wokhulupirika adzakhala wanzeru, Yesu anasonyeza kuti gulu limene kapolo ameneyu akuimira lidzakhala lochita zinthu mozindikira, moyang’ana m’tsogolo, ndiponso moganiza bwino. Lidzatero chifukwa choti chikhulupiriro chake, zochita zake ndiponso ziphunzitso zake zidzakhala zochokera m’Mawu a Mulungu a choonadi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Mawu akuti “wanzeru” anamasuliridwa kuchokera ku mawu a Chigiriki akuti phroʹni·mos. Buku lina (lotchedwa Word Studies in the New Testament) lolembedwa ndi M. R. Vincent, limati mawuwa kwenikweni amatanthauza kuchita zinthu mwanzeru ndiponso mochenjera.