Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tingasonyeze Bwanji Chifundo?

Kodi Tingasonyeze Bwanji Chifundo?

Kodi Tingasonyeze Bwanji Chifundo?

“Tiyeni tichitire onse zabwino, koma makamaka achibale athu m’chikhulupiriro.”​—AGALATIYA 6:10.

1, 2. Kodi fanizo la Msamariya wachifundo limatiphunzitsa chiyani pankhani ya chifundo?

POLANKHULA ndi Yesu, munthu wina wodziwa Chilamulo anafunsa kuti: “Mnansi wanga ndani kwenikweni?” Poyankha Yesu ananena fanizo lotsatirali: “Munthu wina anali kuyenda kuchokera ku Yerusalemu kutsikira ku Yeriko, ndipo anagwa m’manja mwa achifwamba amene anam’vula ndi kum’menya koopsa. Kenako anapita, kumusiya ali pafupi kufa. Ndiye zinangochitika kuti wansembe wina anali kutsika ndi msewu womwewo, koma atamuona, anangomulambalala. Chimodzimodzinso Mlevi, atatsika ndi msewuwo n’kufika pamalo amenewo ndi kumuona, anangomulambalala. Koma panafika Msamariya wina amene anali kudutsanso msewu umenewo, ndipo atamuona, chifundo chinam’gwira. Choncho anam’yandikira ndi kumanga mabala ake. Anathira mafuta ndi vinyo m’mabalamo. Kenako anam’kweza pa chiweto chake ndi kupita naye kunyumba ya alendo kumene anam’samalira. Tsiku lotsatira anatulutsa madinari awiri ndi kupereka kwa mwininyumba ya alendo, nati, ‘Musamalireni bwino, mukawononga ndalama zina zowonjezera, ndidzakubwezerani ndikadzabwera.’” Kenako Yesu anafunsa munthu uja kuti: “Ndani mwa atatuwa amene iweyo ukuona kuti anakhala mnansi wa munthu amene anagwa m’manja mwa achifwambayu?” Munthuyo anayankha kuti: “Ndi amene anam’chitira chifundoyo.”​—Luka 10:25, 29-37a.

2 Zimene Msamariyayu anachitira munthu wovulala uja zikusonyeza bwino kwambiri tanthauzo lenileni la chifundo. Atagwidwa chisoni, Msamariyayo anathandiza munthu wovulalayo. Kuwonjezera pamenepo, Msamariyayo sankam’dziwa munthu amene anali m’mavuto uja. Munthu sangalephere kuchitira mnzake chifundo chifukwa chosiyana mafuko, zipembedzo, kapena chikhalidwe. Atatsiriza kunena fanizo la Msamariya wachifundo lija, Yesu analangiza munthu uja kuti: “Pita, iwenso uzikachita zomwezo.” (Luka 10:37b) Nafenso tingatsatire malangizo amenewa ndi kuyesetsa kukhala achifundo. Komano, kodi tingachite zimenezi motani? Nanga tingasonyeze chifundo m’njira ziti?

“Ngati M’bale . . . Ali ndi Usiwa”

3, 4. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira kwambiri nkhani yochitirana chifundo mumpingo wachikhristu?

3 Mtumwi Paulo anati: “Ngati mpata tili nawo, tiyeni tichitire onse zabwino, koma makamaka achibale athu m’chikhulupiriro.” (Agalatiya 6:10) Motero, tiyeni tione mmene tingasonyezere chifundo chachikulu kwa achibale athu m’chikhulupiriro.

4 Polimbikitsa Akhristu oona kuti azichitirana chifundo, wophunzira Yakobe anati: “Wosachita chifundo adzaweruzidwa mopanda chifundo.” (Yakobe 2:13) Nkhani imene Yakobe anali kufotokoza imatisonyeza njira zina zimene tingasonyezere chifundo. Mwachitsanzo, pa Yakobe 1:27 timawerenga kuti: “Kupembedza koyera ndi kosaipitsidwa kwa Mulungu ndi Atate wathu ndi uku: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye m’masautso awo, ndi kukhala wopanda thotho la dziko.” Lemba la Yakobe 2:15, 16 limati: “Ngati m’bale kapena mlongo ali ndi usiwa ndipo alibe chakudya chokwanira pa tsikulo, koma wina mwa inu n’kunena kuti: ‘Yendani bwino, mukhale wofunda ndi wosazizidwa, ndipo mukhale wodya bwino,’ koma osam’patsa zimene thupi lake likusowazo, kodi pali phindu lanji?”

5, 6. Kodi tingatani kuti tisonyeze kwambiri chifundo pa zimene timachitira Akhristu a mumpingo wathu?

5 Kusamalira ena ndiponso kuthandiza ovutika ndi chizindikiro cha kupembedza koona. Chifukwa cha kulambira kwathu, kuganizira anthu ovutika sikufunika kungokhala kwa mawu chabe owafunira zabwino. Koma, kuwamvera chisoni kwambiri kumatilimbikitsa kuwathandiza. (1 Yohane 3:17, 18) Inde, zina mwa njira zimene tingasonyezere chifundo ndi kuphikira odwala, kuthandiza okalamba pantchito zapakhomo, kuthandiza ena kayendedwe popita ku misonkhano yachikhristu ngati m’pofunika kutero, ndiponso kukhala wowolowa manja kwa ena.​—Deuteronomo 15:7-10.

6 Chinthu chofunika kwambiri kuposa kupatsa ena zinthu zakuthupi ndicho kuthandiza mwauzimu Akhristu a mumpingo umene ukupitiriza kukula. Timalangizidwa kuti: “Lankhulani molimbikitsa kwa a mtima wachisoni, thandizani ofooka.” (1 Atesalonika 5:14) “Akazi achikulire” akulimbikitsidwa kuti akhale “aphunzitsi a zinthu zabwino.” (Tito 2:3) Ponena za oyang’anira achikhristu, Baibulo limati: “Munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo.”​—Yesaya 32:2.

7. Malingana ndi zimene ophunzira a ku Antiokeya wa ku Suriya anachita, kodi tikuphunzirapo chiyani pankhani yosonyeza chifundo?

7 Nthawi zina anthu a m’mipingo ya m’nthawi ya atumwi ankakonza zopereka chithandizo kwa Akhristu a m’madera ena. Iwo ankachita izi kuwonjezera pa kuthandiza akazi amasiye, ana amasiye, ndiponso anthu ena ovutika ndi ofunika kulimbikitsidwa a mumpingo mwawo. Mwachitsanzo, mneneri Agabo atalosera kuti “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, padzagwa njala yaikulu,” ophunzira a ku Antiokeya wa ku Suriya “aliyense wa iwo anatsimikiza mtima . . . kutumiza thandizo lililonse limene akanatha kwa abale okhala ku Yudeya.” Anatumiza zinthu zimenezi kwa akulu ku Yudeya “kudzera kwa Baranaba ndi Saulo.” (Machitidwe 11:27-30) Nanga bwanji masiku ano? “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” anakhazikitsa makomiti opereka chithandizo kuti azisamalira abale athu omwe angakhudzidwe ndi masoka achilengedwe, monga mphepo zamkuntho, zivomezi, kapena tsunami. (Mateyo 24:45) Kudzipereka kugwiritsa ntchito nthawi, nyonga, ndiponso chuma chathu mogwirizana ndi dongosolo limeneli ndi njira yabwino kwambiri yosonyezera chifundo.

“Mukapitiriza Kukhala Okondera”

8. Kodi kukondera kumasokoneza motani mtima wachifundo?

8 Pochenjeza za khalidwe limene lingalepheretse munthu kukhala wachifundo ndiponso kulephera kutsatira “lamulo lachifumu” la chikondi, Yakobe analemba kuti: “Koma mukapitiriza kukhala okondera, mukuchita tchimo, chifukwa lamulo likukutsutsani monga ochimwa.” (Yakobe 2:8, 9) Kukonda munthu chifukwa chakuti ndi wolemera kapena wotchuka, kungachititse kuti tisamamve ‘kulira kwa waumphawi.’ (Miyambo 21:13) Kukondera kumasokoneza mtima wachifundo. Choncho kuti tisonyeze chifundo tisamakondere munthu aliyense.

9. N’chifukwa chiyani kukonda mwapadera anthu ena sikulakwa?

9 Kodi kukhala wosakondera kumatanthauza kuti sitiyenera kukonda mwapadera munthu aliyense? Ayi si choncho. Pofotokoza za wantchito mnzake Epafurodito, mtumwi Paulo analembera Akhristu a ku Filipi kuti: “Anthu a mtundu umenewu muziwalemekeza kwambiri.” Chifukwa chiyani? Iye anati: “Chifukwa cha ntchito ya Ambuye, anatsala pang’ono kufa. Anaika moyo wake pachiswe, kuti anditumikire bwino lomwe m’malo mwanu, popeza simuli kuno.” (Afilipi 2:25, 29, 30) Epafurodito anafunika kukondedwa mwapadera chifukwa choti anali kutumikira mokhulupirika. Komanso, pa 1 Timoteyo 5:17, timawerenga kuti: “Akulu otsogolera bwino apatsidwe ulemu wowirikiza, makamaka amene amachita khama kulankhula ndi kuphunzitsa.” Nawonso anthu amakhalidwe abwino achikhristu amafunika kuwakonda mwapadera. Kukonda munthu mwapadera chifukwa cha zinthu ngati zimenezi si kukondera ayi.

“Nzeru Yochokera Kumwamba . . . Ndi . . . Yodzala Chifundo”

10. N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala ndi lilime lathu?

10 Pofotokoza za lilime, Yakobe anati: “Ndiko kanthu kamodzi kosalamulirika ndi kovulaza, kodzala ululu wakupha. Inde, lilime timatamanda nalo Yehova, amenenso ndi Atate, komanso ndi lilime lomwelo timatemberera anthu amene analengedwa ‘mu chifaniziro cha Mulungu.’ Pakamwa pamodzimodzipo pamatuluka mawu otamanda ndi otemberera.” Yakobe anapitiriza motere: “Ngati m’mitima mwanu muli nsanje ya kaduka ndi ndewu, musadzitamande pakuti kutero n’kunamizira choonadi. Imeneyo si nzeru yochokera kumwamba, koma ya padziko lapansi, yaumunthu ndi yauchiwanda. Pakuti pamene pali nsanje ndi mtima wandewu, palinso chisokonezo ndi zoipa za mtundu uliwonse. Koma nzeru yochokera kumwamba, choyamba, ndi yoyera, kenako yamtendere, yololera, yokonzeka kumvera, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yopanda chinyengo.”​—Yakobe 3:8-10a, 14-17.

11. Kodi tingasonyeze bwanji chifundo pa zolankhula zathu?

11 Motero, mmene timalankhulira zingasonyeze ngati tili ndi nzeru “yodzala chifundo.” Koma bwanji ngati chifukwa cha nsanje kapena mkangano tiyamba kudzitama, kunama, kapena kufalitsa miseche? Lemba la Salmo 94:4 limati: “Adzitamandira onse ochita zopanda pake.” Ndipo mawu oipa sachedwa kuwononga mbiri ya munthu wonenedwayo. (Salmo 64:2-4) Komanso taganizirani za kuopsa kwa ‘mboni yonyenga yolankhula zonama.’ (Miyambo 14:5; 1 Mafumu 21:7-13) Atatsiriza kufotokoza za kulankhula zosayenera, Yakobe anati: “N’kosayenera abale anga kuti zinthu izi zipitirire kumachitika motere.” (Yakobe 3:10b) Tikakhala achifundo chenicheni timalankhula zoyera, zamtendere ndi zololera. Yesu anati: “Ndikukuuzani kuti pa Tsiku la Chiweruzo, anthu adzayankha mlandu pa mawu alionse opanda pake amene iwo amalankhula.” (Mateyo 12:36) Choncho, tikufunika kuyesetsa kukhala achifundo pa zolankhula zathu!

‘Muzikhululukira Anthu Zolakwa Zawo’

12, 13. (a) M’fanizo la kapolo amene anali ndi ngongole yaikulu kwa mbuye wake, kodi tikuphunzira chiyani za chifundo? (b) Kodi kukhululukira m’bale wathu “mpaka nthawi 77” kumatanthauza chiyani?

12 Fanizo la Yesu la kapolo amene anali ndi ngongole ya madinari 60 miliyoni kwa mbuye wake, amene anali mfumu, limasonyeza njira inanso imene tingasonyezere chifundo. Popeza analibe njira yobwezera ngongoleyo, kapoloyo anapempha kuti am’chitire chifundo. ‘Pomumvera chisoni,’ mbuyeyo anakhululukira kapoloyo ngongole yake. Koma kapoloyo anapita kwa kapolo mnzake amene anali naye ngongole ya madinari 100 okha ndipo sanam’chitire chifundo, mpaka anam’mangitsa. Mbuye uja atamva zimene zinachitika, anaitanitsa kapolo amene anam’khululukira uja n’kumuuza kuti: “Kapolo woipa iwe, ine ndakhululukira iwe ngongole yonse ija utandidandaulira. Kodi nawenso sukanam’chitira chifundo kapolo mnzako, monga momwe ine ndinakuchitira iwe chifundo?” Atatero, mbuyeyo anam’pereka kwa oyang’anira ndende. Yesu anamaliza fanizoli ndi mawu awa: “Momwemonso Atate wanga wa kumwamba adzathana ndi inu ngati simukhululukira aliyense m’bale wake ndi mtima wonse.”​—Mateyo 18:23-35.

13 Fanizo tangofotokozali likusonyezeratu kuti munthu wachifundo amakhala wokonzeka kukhululukira ena. Yehova watikhululukira ife ngongole yaikulu ya uchimo. Kodi si bwino kuti nafenso ‘tizikhululukira anthu zolakwa zawo’? (Mateyo 6:14, 15) Yesu asananene fanizo la kapolo wopanda chifundo lija, Petulo anam’funsa kuti: “Ambuye, kodi m’bale wanga angandichimwire kangati ndipo ine n’kumukhululukira? Mpaka nthawi 7 kodi?” Yesu anamuyankha kuti: “Ndikukuuza kuti, osati nthawi 7 zokha ayi, koma, Mpaka nthawi 77.” (Mateyo 18:21, 22) Zoonadi, munthu wachifundo amakhala wokonzeka kukhululuka “mpaka nthawi  77,” zimene zikutanthauza kuti mopanda malire.

14. Malinga ndi Mateyo 7:1-4, kodi tingasonyeze bwanji chifundo nthawi zonse?

14 Pa ulaliki wa paphiri Yesu anatchulanso njira ina imene tingasonyezere chifundo. Iye anati: “Lekani kuweruza ena kuti inunso musaweruzidwe; pakuti chiweruzo chimene mukuweruza nacho ena inunso mudzaweruzidwa nacho . . . Nanga n’chifukwa chiyani umayang’ana kachitsotso m’diso la m’bale wako, koma osaganizira mtanda wa denga umene uli m’diso lako? Kapena ungauze bwanji m’bale wako kuti, ‘Taima ndikuchotse kachitsotso m’diso lako’; pamene iwe m’diso lako muli mtanda wa denga?” (Mateyo 7:1-4) Choncho tingasonyeze chifundo nthawi zonse mwa kulolera zophophonya za ena m’malo mowaweruza.

“Tiyeni Tichitire Onse Zabwino”

15. N’chifukwa chiyani sitimangochitira chifundo okhulupirira anzathu okha?

15 Ngakhale kuti buku la m’Baibulo la Yakobe limalimbikitsa kuchitira chifundo okhulupirira anzathu, sizikutanthauza kuti tizingochitira chifundo anthu a mumpingo wachikhristu okha. Lemba la Salmo 145:9 limati: “Yehova achitira chokoma onse; ndi nsoni zokoma zake zigwera ntchito zake zonse.” Timalangizidwanso kuti, ‘tikhale akutsanza a Mulungu’ ndiponso kuti “tichitire onse chokoma.” (Aefeso 5:1; Agalatiya 6:10) Ngakhale kuti ‘sitikonda dziko lapansi, kapena za m’dziko lapansi,’ timaganizira zofunika za anthu a m’dzikoli.​—1 Yohane 2:15.

16. Kodi pochitira ena chifundo tiyenera kuganizira zinthu ziti?

16 Monga Akhristu, sitizengereza kuthandiza anthu amene akhudzidwa ndi zinthu ‘zongowagwera m’nthawi mwake,’ kapena omwe ali pa mavuto aakulu. (Mlaliki 9:11) N’zoona kuti, timathandiza anthu mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wathu. (Miyambo 3:27) Komabe, tikamathandiza ena timafunika kusamala kuti thandizo lathu lisalimbikitse ulesi. (Miyambo 20:1, 4; 2 Atesalonika 3:10-12) Motero, munthu yemwe ali ndi chifundo chenicheni amachita zinthu chifukwa chomva chisoni komanso kuganiza bwino.

17. Kodi njira yabwino kwambiri yosonyezera chifundo kwa anthu amene saali mu mpingo wachikhristu ndi iti?

17 Kulalikira choonadi cha m’Baibulo kwa anthu omwe saali mu mpingo wachikhristu ndi njira yabwino kwambiri yosonyezera chifundo. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa choti anthu ambiri masiku ano ali mu mdima wauzimu. Ndipo ndi “okalikakalika ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa,” chifukwa choti alibe njira yothetsera mavuto amene amakumana nawo, komanso alibe chiyembekezo. (Mateyo 9:36) Uthenga wa Mawu a Mulungu ungakhale ngati ‘nyali ya ku mapazi awo,’ powathandiza kulimbana ndi mavuto awo. Uthengawu ungakhalenso ‘kuunika kwa panjira pawo’ chifukwa chakuti Baibulo linaneneratu chifuniro cha Mulungu cham’tsogolo, zimene zingawapatse chiyembekezo cha tsogolo labwino. (Salmo 119:105) Kunena zoona, ndi mwayi waukulu kulengeza uthenga wabwino wa choonadi kwa anthu omwe akuufunitsitsa. Popeza kuti “chisautso chachikulu” chayandikira, panopa tikufunika kukhala achangu kwambiri pantchito yolalikira za Ufumu ndi kupanga ophunzira. (Mateyo 24:3-8, 21, 22, 36-41; 28:19, 20) Palibenso njira ina yosonyezera chifundo koposa imeneyi.

Kupereka “Zimene Zili M’kati”

18, 19. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kwambiri kukhala achifundo?

18 Yesu ananena kuti: “Perekani zimene zili m’kati monga mphatso za chifundo.” (Luka 11:41) Zinthu zabwino zimene munthu wachita, zingasonyeze chifundo chenicheni ngati zili zochokera mumtima wachikondi ndi wofunadi kuthandiza. (2 Akorinto 9:7) Kuchitirana chifundo kotereku kumakhala kolimbikitsa kwambiri chifukwa chakuti m’dzikoli masiku ano mwadzaza nkhanza, kudzikonda ndiponso kusaganizira mavuto a ena.

19 Choncho, tiyeni tiyesetse kukhala achifundo. Tikamayesetsa kwambiri kukhala achifundo, timafanana kwambiri ndi Mulungu. Izi zimatithandiza kusangalala kwambiri ndi moyo.​—Mateyo 5:7.

Kodi Mwaphunzira Chiyani?

• Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kukhala achifundo makamaka kwa okhulupirira anzathu?

• Kodi tingasonyeze bwanji chifundo mumpingo wachikhristu?

• Kodi tingawachitire motani zabwino anthu amene saali mu mpingo wachikhristu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 26]

Msamariya anasonyeza chifundo

[Zithunzi patsamba 27]

Akhristu amachita zinthu zambiri zosonyeza chifundo

[Chithunzi patsamba 30]

Kulalikira choonadi cha m’Baibulo kwa anthu omwe saali mu mpingo wachikhristu ndi njira yabwino kwambiri yosonyezera chifundo