Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumatsitsimula Ena?

Kodi Mumatsitsimula Ena?

Kodi Mumatsitsimula Ena?

CHAKUM’MWERA kwa mapiri a Lebanon kuli phiri la Hermoni lomwe ndi lalitali mamita 2,814. Nthawi zambiri pamwamba paphirili pamakutidwa ndi chipale chofewa. Ndipo zimenezi zimachititsa kuti kudzichita mame chifukwa cha mpweya wotentha umene umadutsa usiku. Mamewa amatsikira m’munsi mwa phirili mmene muli mitengo yosiyanasiyana ndiponso minda yampesa. Kalekale ku Isiraeli, m’nyengo ya chilimwe yomwe inkakhala yaitali, mame amenewa ankathandiza kuti kuzikhala chinyezi ndipo zomera zambiri zizisangalala.

Nyimbo ina youziridwa ndi Mulungu, imayerekezera umodzi umene uli pakati pa anthu olambira Yehova ndi “mame a ku Hermoni, akutsikira pa mapiri a Ziyoni.” (Salmo 133:1, 3) Mofanana ndi phiri la Hermoni limene linkachititsa zomera kusangalala chifukwa cha mame, ifenso tingatsitsimule anthu amene timakumana nawo. Kodi tingachite motani zimenezi?

Yesu Ankatsitsimula Anthu

Anthu ankasangalala kwambiri kukhala ndi Yesu Khristu. Iwo ankatsitsimulidwa akakhala naye ngakhale kwa nthawi yochepa. Mwachitsanzo, wolemba Uthenga Wabwino Maliko anati: ‘[Yesu] anatenga ana m’manja mwake ndi kuyamba kuwadalitsa, mwa kuwaika manja.’ (Maliko 10:16) Zimenezitu zinali zotsitsimula kwambiri kwa anawo.

Patsiku lomaliza la moyo wake padziko lapansi, Yesu anasambitsa mapazi a ophunzira ake. Ophunzirawo anakhudzidwa kwambiri ndi kudzichepetsa kwake. Kenako, Yesu anawauza kuti: “Ndakupatsani chitsanzo kuti mmene ine ndachitira kwa inu, inunso muzichita chimodzimodzi.” (Yohane 13:1-17) Nawonso ophunzirawo anafunika kukhala odzichepetsa. Koma iwo sanamvetse tanthauzo la mawu a Yesu, chifukwa usiku wa tsiku lomwelo anakangana pa nkhani yakuti wamkulu ndani. Ngakhale zinali choncho, Yesu sanawapsere mtima. M’malo mwake anawathandiza moleza mtima. (Luka 22:24-27) Ngakhale “pamene anali kunenedwa zachipongwe, [Yesu] sanabwezere zachipongwe.” Ndipotu, “pamene anali kuvutika, sanawopseze, koma anali kudzipereka kwa iye amene amaweruza molungama.” Chitsanzo cha Yesu potsitsimula ena n’choyeneradi kuchitsanzira.​—1 Petulo 2:21, 23.

Yesu ananena kuti: “Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa, ndipo mudzapeza chitsitsimutso cha miyoyo yanu.” (Mateyo 11:29) Taganizirani mmene mukanamvera kuphunzitsidwa ndi Yesu pamaso ndi pamaso. Anthu akwawo atamumva akuphunzitsa m’sunagoge, anadabwa n’kunena kuti: “Kodi munthu ameneyu, nzeru komanso zamphamvu zoterezi anazitenga kuti?” (Mateyo 13:54) Kuphunzira za moyo ndi utumiki wa Yesu kungatithandize kudziwa mmene tingakhalire otsitsimula kwa ena. Tsopano tiyeni tione mmene Yesu anaperekera chitsanzo mwa kulankhula zolimbikitsa ndiponso kukhala ndi mtima wofuna kuthandiza ena.

Kulankhula Mawu Olimbikitsa

Kumanga nyumba n’kovuta kwambiri, koma kuigwetsa n’kosavuta. Mfundo imeneyi imagwiranso ntchito pakalankhulidwe kathu. Tonsefe ndi opanda ungwiro ndipo timalakwitsa pochita zinthu. Mfumu Solomo inalemba kuti: “Kulibe wolungama pansi pano amene achita zabwino osachimwa.” (Mlaliki 7:20) N’zosavuta kuti tione zolakwa za munthu wina n’kumulankhula mawu opweteka kwambiri. (Salmo 64:2-4) Koma sizophweka kuti mawu athu akhale olimbikitsa.

Yesu ankalankhula zinthu zolimbikitsa kwambiri. Iye ankatsitsimula anthu mwauzimu mwa kuwauza uthenga wabwino wa Ufumu. (Luka 8:1) Yesu anatsitsimulanso anthu amene anadzakhala ophunzira ake mwa kuwathandiza kudziwa bwino Atate wake. (Mateyo 11:25-27) M’pake kuti anthu ankakopeka naye.

Mosiyana ndi Yesu, alembi ndi Afarisi analibe chidwi ndi anthu. Yesu anati: “Iwo amakonda malo olemekezeka koposa pa mgonero ndi mipando yakutsogolo m’masunagoge.” (Mateyo 23:6) Iwo ankanyoza anthu n’kumanena kuti: “Khamu lonseli la anthu osadziwa Chilamulo ndi lotembereredwa.” (Yohane 7:49) Khalidwe limeneli silinali lotsitsimula.

Nthawi zambiri zolankhula zathu zimasonyeza zimene zili mu mtima mwathu ndiponso mmene timaonera anthu ena. Yesu anati: “Munthu wabwino amatulutsa zabwino m’chuma chabwino cha mtima wake, koma munthu woipa amatulutsa zoipa m’chuma chake choipa; pakuti pakamwa pamalankhula zosefukira mu mtima.” (Luka 6:45) Ndiyeno, kodi tingatani kuti tizilankhula mawu olimbikitsa?

Chinthu chimodzi chomwe tingachite ndi kuganiza kaye tisanalankhule. Lemba la Miyambo 15:28 limati: “Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe.” Sizichita kufunikira nthawi yambiri kuti tiganize. Kuganizira pang’ono tisanalankhule kungatithandize kuona ngati zimene tikufuna kunena n’zotsitsimula ena kapena ayi. Mwina tingadzifunse kuti: ‘Kodi zimene ndikufuna kunenazi zisonyeza kuti ndimakonda ena? Kodi ndi zoona kapena nkhambakamwa chabe? Kodi “ndi mawu a pa nthawi yake?” Kodi zikhala zotsitsimula ndi zolimbikitsa omwe angamve?’ (Miyambo 15:23) Ngati taona kuti mawuwo sakhala otsitsimula kapena n’ngosafunika panthawiyo, ndi bwino kuti tisawanene. Ndiyeno m’malo mongokhala duu, mungathe kulankhula mawu ena olimbikitsa ndiponso oyenera panthawiyo. Mawu osayenera amakhala ngati “kupyoza kwa lupanga,” pomwe mawu olimbikitsa ‘alamitsa’ kapena kuti kuchiritsa.​—Miyambo 12:18.

Kuona kuti okhulupirira anzathu ndi amtengo wapatali pamaso pa Mulungu kungatithandizenso. Yesu anati: “Palibe munthu angabwere kwa ine akapanda kukokedwa ndi Atate amene anandituma ine.” (Yohane 6:44) Yehova amayang’ana zinthu zabwino zimene mtumiki wake aliyense amachita ngakhale amene tingawaone kuti ndi ovuta. Ngati tiyesetsa kuona zinthu zabwino zimene iwo amachita tidzatha kulankhula za zinthu zabwino zimene iwo amachita.

Thandizani Ena

Yesu ankadziwa mavuto amene anthu oponderezedwa ankakumana nawo. Ndipo iye, “poona chikhamu cha anthu, anawamvera chisoni, chifukwa anali okalikakalika ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” (Mateyo 9:36) Yesu sanangoona mavuto awo, koma anachitapo kanthu kuti awathandize. Iye anawaitana kuti: “Bwerani kwa ine, nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani.” Ndipo anawatsimikizira kuti: “Goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.”​—Mateyo 11:28, 30.

Panopa tikukhala mu “nthawi yovuta.” (2 Timoteyo 3:1) Anthu ambiri akuvutika maganizo chifukwa cha “nkhawa za m’dongosolo lino la zinthu.” (Mateyo 13:22) Ena ali ndi nkhawa chifukwa cha mavuto amene akukumana nawo. (1 Atesalonika 5:14) Kodi ife tingatani kuti titsitsimule anthu amene akufunika thandizo? Tingawathandize kuti katundu wawo apepuke ngati mmene Khristu anachitira.

Anthu ena amayesa kupepukitsa katundu wawo mwa kuuzako ena za mavuto awo. Kodi mumapatula nthawi yomvetsera mwatcheru, anthu oterewa akabwera kwa inu kuti akuuzeni mavuto awo? Kuti mukhale womvera ena chifundo mufunika kudziletsa. M’malo mongoganizira mmene mungayankhire kapena mmene mungathetsere vutolo, yesetsani kumvetsera zimene munthuyo akunena. Mukamamvetsera mosamala, n’kumamuyang’ana, n’kumamwetulira pamene kuli koyenera, zimasonyeza kuti mumasamala za iye.

Mumpingo wachikhristu timakhala ndi mwayi wolimbikitsa okhulupirira anzathu. Mwachitsanzo, tikapita ku misonkhano ku Nyumba ya Ufumu, tingayang’ane anthu amene akuvutika ndi matenda. Nthawi zina chinthu chofunika ndi kupatula nthawi misonkhano isanayambe kapena itatha kuti tiwalimbikitse. Komanso ndi bwino kuona anthu amene alephera kufika ku Phunziro la Buku la Mpingo m’gulu limene timasonkhana. Mwina tingathe kuwaimbira foni kuti tidziwe mmene alili kapena kuona mmene tingawathandizire.​—Afilipi 2:4.

Akulu mumpingo wachikhristu ali ndi udindo waukulu kwambiri. Tingawathandize kuti katundu wawo apepuke mwa kugwirizana nawo komanso kuchita modzichepetsa utumiki uliwonse umene atipempha kuchita. Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti: “Muzimvera amene akutsogolera pakati panu ndipo muziwagonjera. Iwo amayang’anira miyoyo yanu monga anthu amene adzayankha mlandu. Teroni kuti achite ntchito yawo mwa chimwemwe, osati modandaula, pakuti akatero zingakhale zokuwonongani.” (Aheberi 13:17) Tikakhala ndi mtima wodzipereka tidzatsitsimula anthu amene ‘amatsogolera bwino.’​—1 Timoteyo 5:17.

Pitirizani Kulankhula ndi Kuchita Zinthu Zolimbikitsa

Mame amene amatsitsimula amapangidwa ndi timadontho tamadzi tambirimbiri timene munthu sangadziwe kumene tachokera. Choncho, munthu amatsitsimula ena osati chifukwa chongochita chinthu chabwino kamodzi kokha, koma chifukwa chokhala ndi makhalidwe a Khristu nthawi zonse.

Mtumwi Paulo analemba kuti: “Posonyezana chikondi chaubale khalani ndi chikondi chenicheni kwa wina ndi mnzake. Posonyezana ulemu wina ndi mnzake, khalani patsogolo.” (Aroma 12:10) Choncho, mogwirizana ndi mawu a Paulo, tiyeni tiyesetse kutsitsimula ena ndi mawu komanso zochita zathu.

[Zithunzi patsamba 16]

Mame a m’phiri la Hermoni ankachititsa kuti zomera zizisangalala

[Chithunzi patsamba 17]

Munthu amene amamvetsera mwachifundo amatsitsimula ena