Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi ndi bwino kuti Mkhristu wa Mboni za Yehova akakhale nawo pamwambo wa ukwati wa wachibale wake kapena mnzake amene si Mboni?

Mwambo wa ukwati umakhala wosangalatsa kwambiri ndipo n’zomveka kuti Akhristu amafuna kukhala nawo pachisangalalo chimenechi. N’zodziwikiratu kuti ana ang’onoang’ono ayenera kumvera malangizo a makolo kapena munthu amene akukhala nawo pankhani yoti apite kapena asapite ku ukwati. (Aefeso 6:1-3) Nanga bwanji mkazi wachikhristu atapemphedwa ndi mwamuna wake yemwe si wa Mboni kuti apite naye kuukwati umene ukachitikira m’tchalitchi? Mwina chikumbumtima chake chingamulole kupita ndi kukangoonerera popanda kuchita nawo mwambo uliwonse wachipembedzo umene ungachitike paukwatiwo.

Pamenepa, munthu aliyense angasankhe yekha kupita kapena kusapita ku ukwati winawake. Komabe, Mkhristu aliyense ayenera kudziwa kuti Yehova akuona zimene wasankha kuchita, ndiponso ayenera kuganizira mfundo zingapo za m’Malemba pamene akufuna kupita ku ukwati wa munthu yemwe si Mboni.

Chinthu chofunika kwambiri kwa Mkhristu aliyense chiyenera kukhala kukondweretsa Mulungu. Yesu anati: “Mulungu ndiye Mzimu, ndipo onse omulambira ayenera kumulambira ndi mzimu ndi choonadi.” (Yohane 4:24) Motero, Mboni za Yehova sizichita nawo zinthu monga mapemphero kapena miyambo yotsutsana ndi choonadi cha m’Baibulo imene zipembedzo zina zimachita.​—2 Akorinto 6:14-17.

Mkhristu ayenera kukumbukiranso kuti zimene wasankha zingakhudze anthu ena. Tiyerekeze kuti mwapita ku ukwatiwo, kodi achibale anu sangakhumudwe ataona kuti simukuchita nawo zinthu zina? Komanso ndi bwino kuganizira mmene zosankha zanu zingakhudzire Akhristu anzanu. (Aroma 14:13) Ngakhale inuyo ndi achibale anu mutaona kuti palibe vuto kupita ku ukwati wa munthu yemwe si Mboni, kodi zimenezo sizingakhumudwitse Akhristu anzanu? Kodi sizingavulaze chikumbumtima cha ena?

Pamwambo wa ukwati wa m’bale wathu yemwe si Mboni pangakhale zinthu zina zovuta kwambiri. Mwachitsanzo, kodi mungatani atakupemphani kuti mukhale woperekeza mkwati kapena mkwatibwi? Nanga mungatani ngati mwamuna kapena mkazi wanu yemwe si wa Mboni akufuna kukachita nawo zinthu zina kumeneko? Ngati ukwatiwo ukuchitika mogwirizana ndi malamulo, ndipo ukuchititsidwa ndi woweruza milandu kapena munthu wina wochokera kuboma, kupezekapo kungatanthauze kungoonerera mwambo waboma basi.

Koma ukwati wochitikira m’tchalitchi kapena wochititsidwa ndi mkulu wachipembedzo umakhala ndi mavuto enanso. Choncho, pofuna kuti mutsatire chikumbumtima chanu chophunzitsidwa Baibulo ndiponso zinthu zimene mumakhulupirira, komanso kuti musakachititse manyazi anthu amene angakapezeke pa mwambowo mungasankhe kuti musapite. (Miyambo 22:3) Kuti inuyo komanso abale anu asakhumudwe ndi bwino kufotokoza pasadakhale mfundo za m’Baibulo zimene mumakhulupirira. Ndiponso mungafotokozeretu zinthu zimene mungachite nawo ndi zimene simungachite komanso zinthu zina zimene iwo angachite m’malo mwa zimene akufuna kuchita.

Akhristu ena ataganizira bwinobwino mfundo zimenezi, aona kuti palibe vuto ngati atapita ku mwambo wa ukwati wa munthu yemwe si Mboni chifukwa azikangoonerera. Koma ngati Mkhristu aona kuti zingakamuvute kutsatira mfundo za Mulungu pamwambowo angasankhe kuti asapite. Ngati angasankhe kuti asapite ku mwambowo koma n’kupita ku phwando lochitika pambuyo pake, ayenera kukhala wotsimikiza kukachita “zonse ku ulemerero wa Mulungu.” (1 Akorinto 10:31) Posankha zochita pankhani imeneyi “aliyense ayenera kunyamula katundu wakewake.” (Agalatiya 6:5) Choncho, pazilizonse zimene mungasankhe kuchita, kumbukirani kuti kukhala ndi chikumbumtima chabwino pamaso pa Yehova Mulungu n’kofunika kwambiri.