Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yesetsani Kusonyeza Chifundo M’dziko Lankhanzali

Yesetsani Kusonyeza Chifundo M’dziko Lankhanzali

Yesetsani Kusonyeza Chifundo M’dziko Lankhanzali

MWAMUNA wina ku Burundi anadwala kwambiri malungo. Ndipo anafunika kupita naye ku chipatala mwamsanga. Koma kodi akanapita bwanji popeza panalibe galimoto? Anzake apamtima awiri anam’thandiza. Anam’kweza pa njinga ndipo anayenda naye ulendo wotopetsa wa m’mapiri kwa maola asanu. Anafika naye pamalo okwerera basi ndipo anam’kweza basi yomwe inakam’fikitsa kuchipatala. Patangopita masiku angapo anapeza bwino.

Mu August 2005, kudera lina la ku United States kunagwa mvula yamkuntho yotchedwa Hurricane Katrina yomwe inawononga kwambiri derali. Ndiyeno, anthu angapo ongodzipereka anapeza nyumba ina itawonongeka chifukwa cha mitengo imene inagwera pa nyumbapo. Anthuwa omwe sankamudziwa n’komwe mwini wake wa nyumbayo anakhala tsiku lonse akuchotsa zogumukagumuka za nyumbayo ndiponso mitengo yomwe inagwayo. Mwininyumbayo anati: “Ndikuthokoza kwambiri anthu amenewa.”

Nkhani zokhudza nkhanza n’zimene zimakambidwa kwambiri m’nyuzipepala, pa TV ndi m’mawailesi. Ndipo nkhani zimenezi zimapangitsa kuti zinthu zachifundo zimene anthu amachita tsiku ndi tsiku zisaoneke kapena kumveka. Koma zimenezi sizisintha mfundo yakuti anthu kulikonse amafuna kuwasonyeza chikondi ndi chifundo. Timafunikadi chifundo. Ndipo anthu ambiri amanena zimenezi makamaka panyengo ya khirisimasi imene anthu ambiri amanena kapena amaimba za ‘mtendere pakati pa anthu amene amakondwera nawo.’​—Luka 2:14.

N’kovuta kusonyeza chifundo m’dziko limene anthu ambiri ndi opanda chikondi ndiponso osafuna kuthandiza ena. Ndipo anthu ambiri amaona kuti kukhala wankhanza ndi wosaganizira ena n’kumene kungachititse munthu kukhala ndi moyo wabwino. Zikuoneka kuti anthu ambiri amatsatira mfundo yoti, ndibwino kukhala wankhanza kusiyana ndi kukhala wachifundo. Dyera ndi kudzikonda kumachititsa anthu kuti asakhale achifundo.

Chifukwa cha zimenezi, anthu ambiri amangofuna zawo zokha mosaganizira zofuna za anzawo. Nthawi zambiri amuna omwe amachita masewera ena ndi zisudzo amaonedwa kukhala “amuna enieni” amene sasonyeza chikondi. N’zimenenso atsogoleri ena andale amachita.

Choncho, tingachite bwino kufunsa kuti: N’chifukwa chiyani tiyenera kusonyeza chifundo? Kodi kusonyeza chifundo kuli ndi ubwino uliwonse? Ndipo n’chiyani chimene chingatithandize kusonyeza chifundo? Nkhani yotsatira iyankha mafunsowa.

[Bokosi patsamba 3]

•Kodi kusonyeza chifundo n’kufooka?

•Kodi kusonyeza chifundo kuli ndi ubwino uliwonse?

•Kodi tingasonyeze chifundo m’njira ziti?