Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mwakonzekera Tsiku la Yehova?

Kodi Mwakonzekera Tsiku la Yehova?

Kodi Mwakonzekera Tsiku la Yehova?

“Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi, lili pafupi lifulumira kudza.”​—ZEFANIYA 1:14.

1-3. (a) Kodi Baibulo limanena chiyani za tsiku la Yehova? (b) Kodi ndi “tsiku la Yehova” liti limene tikulidikirira?

TSIKU lalikulu la Yehova si tsiku limodzi lenileni. Ndi nthawi yaitali imene Mulungu adzaweruza anthu oipa. Anthu amene satumikira Mulungu afunikira kuopa tsikuli chifukwa lidzakhala la mdima, mkwiyo, ukali, masautso ndiponso la chipasuko. (Yesaya 13:9; Amosi 5:18-20; Zefaniya 1:15) Ulosi wa Yoweli umanena kuti: “Kalanga ine, tsikuli! Pakuti layandikira tsiku la Yehova, lidzafika ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvu yonse.” (Yoweli 1:15) Komabe, patsiku lalikulu limeneli Mulungu adzapulumutsa anthu “oongoka mtima.”​—Salmo 7:10.

2 Mawu akuti “tsiku la Yehova” amatanthauza chiweruzo cha Mulungu panthawi zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, “tsiku la Yehova” linafika pamene anthu a ku Yerusalemu anawonongedwa ndi Ababulo mu 607 B.C.E. (Zefaniya 1:4-7) Chiweruzo china chinachitika mu 70 C.E. pamene Mulungu anagwiritsa ntchito Aroma kuwononga mtundu wa Yuda umene unakana Mwana wake. (Danieli 9:24-27; Yohane 19:15) Baibulo linaloseranso za “tsiku la Yehova” limene iye ‘adzachita nkhondo ndi amitundu’ onse. (Zekariya 14:1-3) Mouziridwa ndi Mulungu, mtumwi Paulo anagwirizanitsa tsiku limeneli ndi kukhalapo kwa Khristu, kumene kunayamba Yesu atangoikidwa kukhala Mfumu kumwamba mu 1914. (2 Atesalonika 2:1, 2) Popeza tsiku la Yehova layandikira kwambiri, lemba la chaka chatha la Mboni za Yehova linalidi loyenera kwambiri. Linachokera pa Zefaniya 1:14 ndipo limati: “Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi.”

3 Popeza tsiku lalikulu la Mulungu layandikira, ino ndiyo nthawi yoti mukonzekere. Kodi mungakonzekere bwanji tsiku limeneli? Kodi pali zina zimene mungachite pokonzekera tsiku la Yehova limeneli?

Khalani Okonzeka

4. Kodi Yesu anakonzekera mayesero aakulu ati?

4 Yesu Khristu polosera za mapeto a dongosolo la zinthu lino, anauza ophunzira ake kuti: “Khalani okonzeka.” (Mateyo 24:44) Pamene Yesu ankanena mawu amenewa, anali atakonzekera mayesero aakulu a imfa yake ya nsembe ya dipo. (Mateyo 20:28) Koma kodi tingaphunzirepo chiyani pa zimene Yesu anachita pokonzekera?

5, 6. (a) Kodi kukonda Mulungu ndi anthu kumatithandiza bwanji kukonzekera tsiku la Yehova? (b) Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani pankhani yokonda anansi athu?

5 Yesu ankakonda kwambiri Yehova komanso mfundo Zake zolungama. Ponena za Yesu, lemba la Aheberi 1:9 limati: “Unakonda chilungamo, unadana ndi kusamvera malamulo. Ndiye chifukwa chake Mulungu, Mulungu wako, anakudzoza ndi mafuta a chikondwerero kuposa anzako.” Yesu anakhalabe wokhulupirika chifukwa ankakonda Atate ake akumwamba. Ifenso tikamakonda Mulungu mofanana ndi Yesu komanso tikamatsatira zimene Iye amafuna, adzatiteteza. (Salmo 31:23) Chikondi ndiponso kumvera Mulungu kumeneku, zidzatithandiza kukonzekera tsiku lalikulu la Yehova.

6 Khalidwe lalikulu la Yesu linali kukonda anthu. Inde, “anawamvera chisoni, chifukwa anali okalikakalika ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” (Mateyo 9:36) N’chifukwa chake, Yesu analalikira uthenga wabwino kwa anthu amenewa, monga momwe chikondi chimatilimbikitsira kulalikira uthenga wa Ufumu kwa anthu ena. Kukonda Mulungu ndi anansi athu kumatipangitsa kukhala achangu mu utumiki wachikhristu ndipo zimenezi zimatithandiza kukonzekera tsiku lalikulu la Yehova.​—Mateyo 22:37-39.

7. Kodi tingatani kuti tikhale achimwemwe podikira tsiku la Yehova?

7 Yesu ankakonda kuchita zimene Yehova amafuna. (Salmo 40:8) Tikakhala ndi maganizo amenewa, tidzakhala achimwemwe potumikira Mulungu. Mofanana ndi Yesu, tidzakhala anthu opatsa moolowa manja, ndipo zimenezi zidzatithandiza kukhala anthu osangalala. (Machitidwe 20:35) Inde, “chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu [yathu].” Chimwemwe chimenechi chidzatithandiza kukonzekera bwino tsiku lalikulu la Mulungu.​—Nehemiya 8:10.

8. N’chifukwa chiyani tifunika kupemphera kwa Yehova nthawi zonse?

8 Kupemphera kwa Mulungu ndi mtima wonse kunam’thandiza Yesu kukonzekera kuyesedwa kwa chikhulupiriro chake. Iye anali kupemphera pamene Yohane anali kumubatiza. Yesu anapempheranso usiku wonse asanasankhe atumwi ake tsiku lotsatira. (Luka 6:12-16) Ndipotu aliyense amene amawerenga Baibulo amachita chidwi kwabasi ndi zimene Yesu anapempha mochokera pansi pamtima usiku womaliza wa moyo wake padziko lapansi. (Maliko 14:32-42; Yohane 17:1-26) Kodi mumakonda kupemphera ngati Yesu? Muzipemphera kwa Yehova pafupipafupi ndipo tengani kanthawi ndithu popempherapo. Pemphani mzimu woyera kuti ukuthandizeni ndipo sinthani mwamsanga mukaona kuti mzimuwo wakuthandizani kuona vuto lanu linalake. Ubwenzi wolimba ndi Atate wathu wakumwamba ndi wofunika kwambiri panthawi yovuta ino pamene tsiku lalikulu la Mulungu layandikira kwambiri. Choncho, pitirizanibe kuyandikira kwa Yehova m’pemphero.​—Yakobe 4:8.

9. Kodi kufunitsitsa kuti dzina la Yehova liyeretsedwe n’kofunika bwanji?

9 Yesu ankafuna kwambiri kuti dzina la Yehova liyeretsedwe ndipo zimenezi zinam’thandizanso kukonzekera mayesero. Ndipotu, anaphunzitsa otsatira ake kuti akamapemphera kwa Mulungu azitchula mfundo yakuti: “Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyo 6:9) Tikamafunitsitsa kuti dzina la Yehova liyeretsedwe, kapena kuti likhale lopatulika, tidzayesetsa kupewa kuchita chilichonse chimene chinganyozetse dzinali. Ndipo zimenezi zidzatithandiza kukonzekera bwino tsiku lalikulu la Yehova.

Kodi Pali Zofunika Kusintha Pamoyo Wanu?

10. N’chifukwa chiyani m’pofunika kuona bwinobwino zimene tikuchita pamoyo wathu?

10 Tsiku la Yehova litati libwere mawa, kodi ndinu wokonzeka? Aliyense ayenera kuona bwinobwino zimene akuchita pamoyo wake kuti aone ngati akufunika kusintha. Popeza moyo wathu ndi waufupi komanso wosadalirika, tifunika kukhala atcheru mwauzimu tsiku ndi tsiku. (Mlaliki 9:11, 12; Yakobe 4:13-15) Choncho tiyeni tikambirane mfundo zina zofunika kuziona bwinobwino pamoyo wathu.

11. Kodi muli ndi cholinga chotani pankhani yowerenga Baibulo?

11 Mfundo imodzi yofunika kwambiri ndi langizo la “kapolo wokhulupirika” lakuti tiziwerenga Baibulo tsiku lililonse. (Mateyo 24:45) Mungakhale ndi cholinga chowerenga Baibulo lonse kuyambira ku Genesis mpaka ku Chivumbulutso chaka chilichonse ndipo sinkhasinkhani zimene mukuwerengazo. Mutamawerenga pafupifupi machaputala anayi patsiku, mungamalize machaputala onse a m’Baibulo okwana 1,189 m’chaka chimodzi chokha. Mfumu iliyonse ya Aisiraeli inafunika kuwerenga Chilamulo cha Yehova “masiku onse a moyo wake.” N’zachidziwikire kuti Yoswa nayenso anachita zimenezi. (Deuteronomo 17:14-20; Yoswa 1:7, 8) N’kofunikanso kwambiri kuti akulu mu mpingo aziwerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse, popeza zimenezi zidzawathandiza kuti ‘aphunzitse zopindulitsa.’​—Tito 2:1.

12. Kodi kuyandikira kwa tsiku la Yehova kuyenera kukulimbikitsani kuchita chiyani?

12 Kuyandikira kwa tsiku la Yehova kuyenera kukulimbikitsani kupezeka pa misonkhano yachikhristu mokhazikika ndiponso kutengamo mbali mmene mungathere. (Aheberi 10:24, 25) Kuchita zimenezi kudzakuthandizani kuti mukhale ndi luso kwambiri popeza ndinu wolengeza ufumu amene mumayetsetsa kuthandiza ndiponso kupeza anthu oyenera kudzalandira moyo wosatha. (Machitidwe 13:48) Mwina mungakhale achangu kwambiri mu mpingo m’njira zinanso, monga kuthandiza achikulire ndi kulimbikitsa achinyamata. Ndipo mukachita zimenezi mudzakhala wosangalala kwambiri.

Kodi Ubwenzi Wanu ndi Ena ndi Wotani?

13. Kodi tingadzifunse mafunso otani pankhani yovala umunthu watsopano?

13 Popeza tsiku la Yehova layandikira mufunikira kuyesetsa kwambiri “kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu m’chilungamo choona ndi kukhulupirika.” (Aefeso 4:20-24) Mukakhala ndi makhalidwe ofanana ndi a Mulungu, anthu ena adzaona kuti ‘mukuyenda mwa mzimu wa Mulungu’ ndiponso mukusonyeza zipatso zake. (Agalatiya 5:16, 22-25) Kodi pali zinthu zimene inuyo ndi banja lanu mwachita zosonyeza kuti mwavala umunthu watsopano? (Akolose 3:9, 10) Mwachitsanzo, kodi okhulupirira anzanu ndi anthu ena amakudziwani kuti ndinu wokoma mtima? (Agalatiya 6:10) Kuphunzira Malemba mokhazikika n’kofunika kuti mukhale ndi makhalidwe ofanana ndi a Mulungu amene angakuthandizeni kukonzekera tsiku la Yehova.

14. N’chifukwa chiyani tiyenera kupempha mzimu woyera ngati tikufuna kukhala wodziletsa?

14 Bwanji ngati simuchedwa kupsa mtima ndipo mukuona kuti mufunika kukhala wodziletsa kwambiri? Kudziletsa ndi chimodzi mwa zipatso zimene mzimu woyera wa Mulungu ungabale mwa inu. Choncho, pemphani mzimu woyera mogwirizana ndi mawu a Yesu akuti: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani; funafunanibe, ndipo mudzapeza; gogodanibe, ndipo adzakutsegulirani. . . . Ngati inu, ngakhale muli oipa, mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wakumwamba! Iye adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.”​—Luka 11:9-13.

15. Kodi muyenera kuchita chiyani ngati mwasemphana maganizo ndi wokhulupirira mnzanu?

15 Nanga bwanji ngati mwasemphana maganizo ndi wokhulupirira mnzanu wina wake? Ngati zili choncho, yesetsani kuthetsa nkhaniyo, chifukwa mukatero mudzathandiza kuti mumpingo mukhale mtendere ndi mgwirizano. (Salmo 133:1-3) Tsatirani malangizo a Yesu a pa Mateyo 5:23, 24 kapena Mateyo 18:15-17. Ngati mumakonda kukwiya mpaka dzuwa kulowa, muziyesetsa kuthetsa nkhaniyo mwamsanga. Nthawi zambiri zimene zimangofunika ndi kukhala wofunitsitsa kukhululukira ena basi. Paulo analemba kuti: “Khalani okomerana mtima wina ndi mnzake, achifundo chachikulu, okhululukirana ndi mtima wonse, monga mmene inunso anakukhululukirani Mulungu ndi mtima wonse kudzera mwa Khristu.”​—Aefeso 4:25, 26, 32.

16. Kodi anthu okwatirana angasonyezane chifundo m’njira ziti?

16 Anthu okwatirana amafunikanso kusonyezana chifundo ndipo nthawi zina kukhululukirana kumene. Ngati mukufuna kuti muzikondana ndi kusonyezana chifundo kwambiri, dalirani Mulungu ndi Mawu ake. Kodi pali zimene inuyo mungachite potsatira malangizo a pa 1 Akorinto 7:1-5, kuti muchepetse nkhawa ndiponso kupewa chimasomaso? Ndithudi izi n’zimene anthu okwatirana ayenera kuchita kuti asonyezane “chifundo chachikulu.”

17. Kodi n’chiyani chimene tiyenera kuchita ngati tachita tchimo lalikulu?

17 Bwanji ngati mwachita tchimo linalake lalikulu? Yesetsani kukonza zinthu mwamsanga. Musazembe, auzeni akulu achikhristu kuti akuthandizeni chifukwa mapemphero ndi malangizo awo ndi ofunika kuti muchire mwauzimu. (Yakobe 5:13-16) Pempherani kwa Yehova ndi mtima wolapadi. Mukalephera kuchita zimenezi muzingodziimba mlandu ndipo chikumbumtima chanu chizingokuvutitsani. Davide anachita zimenezi ndipo anapepukidwa kwambiri mumtima mwake atalapa pamaso pa Yehova. Iye analemba kuti: “Wodala munthuyo wokhululukidwa tchimo lake; wokwiriridwa choipa chake. Wodala munthuyu Yehova samuwerengera mphulupulu zake; ndimo mumzimu mwake mulibe chinyengo.” (Salmo 32:1-5) Yehova amakhululukira anthu ochimwa amene alapa moona mtima.​—Salmo 103:8-14; Miyambo 28:13.

Musakhale Mbali ya Dziko

18. Kodi dzikoli muziliona bwanji?

18 Sitikukayika kuti mukuyembekezera mwachidwi dziko lapansi latsopano limene Atate wathu wakumwamba analonjeza. Ndiyeno kodi mumaliona bwanji dziko la anthu osalungama amene Mulungu amadana nawo? Satana yemwe ndi “wolamulira wa dzikoli” analibe mphamvu pa Yesu Khristu. (Yohane 12:31; 14:30) Zoonadi inunso simungafune kuti Mdyerekezi ndi dziko lakeli akulamulireni. Chotero tsatirani mawu a mtumwi Yohane akuti: “Musamakonde dziko kapena za m’dziko.” Ndi bwino kuchita zimenezi chifukwa, “dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake, koma wochita chifuniro cha Mulungu akhalabe kosatha.”​—1 Yohane 2:15-17.

19. Kodi achinyamata achikhristu akulimbikitsidwa kukhala ndi zolinga zotani?

19 Kodi mukuthandiza ana anu ‘kukhala opanda thotho [kapena kuti banga] la dziko’? (Yakobe 1:27) Satana akunyengerera ana anu kuti awagwire monga mmene msodzi amachitira akamawedza nsomba. Magulu ndi mabungwe ambiri amapangidwa ndi cholinga chakuti achinyamata akhale mbali ya dziko la Satanali. Koma atumiki a Yehova ali kale m’gulu lokhalo limene lidzapulumuke mapeto a dongosolo loipa la zinthu lino. Chotero achinyamata achikhristu ayenera ‘kukhala ndi zochita zochuluka m’ntchito ya Ambuye.’ (1 Akorinto 15:58) Makolo achikhristu ayenera kuthandiza ana awo kukhala ndi zolinga zimene zidzawathandiza kuti akhale ndi moyo wosangalala komanso wopindulitsa. Moyo umenewu umalemekeza Mulungu ndipo ungawathandize kukonzekera tsiku la Yehova.

Ganizirani Zimene Zidzachitike Tsiku Lalikulu la Yehova Likadzadutsa

20. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kumaganizira za moyo wosatha?

20 Mukamaganizira za moyo wosatha nthawi zonse, mudzatha kudikira tsiku la Yehova modekha. (Yuda 20, 21) Muziyembekezeranso moyo wosatha m’Paradaiso, pamene mudzabwerere ku unyamata. Panthawiyi mudzakhalanso ndi nthawi yambiri yochita zinthu zabwino ndiponso yophunzira zambiri za Yehova. Ndipotu mudzaphunzira za Mulungu mpaka kalekale chifukwa zimene panopa tikudziwa ponena za “njira zake,” n’zochepa kwambiri. (Yobu 26:14) Koma ndiye n’zosangalatsa bwanji!

21, 22. Kodi anthu amene adzaukitsidwe adzatiuza zotani ndipo ife tidzawaphunzitsa chiyani?

21 M’Paradaiso, anthu amene adzaukitsidwe adzatiuza zinthu zina zakale zimene sitikuzidziwa. Mwachitsanzo, Enoke adzatiuza chimene chinamuthandiza kulimba mtima kuti alalikire uthenga wa Yehova kwa anthu osaopa Mulungu. (Yuda 14, 15) Nowa nayenso adzatiuza mmene zinalili pomanga chingalawa. Abulahamu ndi Sara adzafotokoza mmene anamvera mu mtima mwawo atauzidwa kusiya moyo wa mwanaalirenji ku Uri ndi kumakakhala m’mahema. Taganizirani za Estere akutiuza mmene anatetezera anthu a mtundu wake ku chiwembu chimene Hamani anakonza. (Estere 7:1-6) Ndiyeno taganiziraninso za Yona akutiuza za masiku atatu amene anakhala m’mimba mwa chinsomba kapena Yohane M’batizi akutiuza mmene anamvera mu mtima mwake pamene ankabatiza Yesu. (Luka 3:21, 22; 7:28) Koma ndiye padzakhaladi zambiri zoti tiphunzire.

22 Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, mungadzakhale ndi mwayi wothandiza anthu amene adzaukitsidwe kuti ‘am’dziwedi Mulungu.’ (Miyambo 2:1-6) Masiku ano, n’zosangalatsa zedi kuona anthu akuphunzira ndi kutsatira Mawu a Yehova Mulungu. Koma taganizirani chisangalalo chimene mudzakhale nacho Yehova akadzadalitsa khama lanu lophunzitsa anthu omwe anakhalako kale. Ndipo mudzasangalalanso kuwaona akuyamikira zimene mudzawaphunzitsezo.

23. Kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani?

23 Madalitso amene ife atumiki a Yehova tili nawo panopo ndi ochuluka zedi moti sitingathe n’komwe kuwawerenga. (Salmo 40:5) Timayamikira makamaka zogawira zauzimu zimene Mulungu watipatsa. (Yesaya 48:17, 18) Kaya moyo wathu ndi wotani, tiyeni tim’tumikire Yehova ndi mtima wonse pamene tikudikira tsiku lake lalikulu.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi “tsiku la Yehova” limatanthauza chiyani?

• Kodi mungakonzekere bwanji tsiku la Yehova?

• Popeza tsiku lalikulu la Mulungu layandikira kwambiri, kodi tiyenera kusintha zinthu zotani pamoyo wathu?

• Kodi inuyo mukuyembekezera chiyani tsiku la Yehova likadzadutsa?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 12]

Yesu anakonzekera mayesero

[Chithunzi patsamba 15]

Udzakhala mwayi waukulu kuthandiza anthu omwe adzaukitsidwe kuphunzira za Yehova