Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zazikulu za M’buku la Malaki

Mfundo Zazikulu za M’buku la Malaki

Mawu a Yehova Ndi Amoyo

Mfundo Zazikulu za M’buku la Malaki

PANALI patatha zaka zoposa 70 kuchokera pamene kachisi wa ku Yerusalemu anamangidwanso. Komabe m’kupita kwa nthawi, chidwi cha Ayuda pa zinthu zauzimu chinayamba kuchepa kwambiri. Ngakhale ansembe anali atayamba kuchita zachinyengo. Ndiyeno kodi ndani akanawathandiza kuzindikira vuto lawoli, kuti akhalenso paubwenzi wabwino ndi Mulungu? Yehova anauza Malaki kuti agwire ntchito imeneyi.

Buku la Malaki ndi buku lomalizira la Malemba Achiheberi lomwe muli maulosi ouziridwa ndi Mulungu ndipo linalembedwa mosabisa mawu. Kuganizira mosamala mawu a ulosi a m’bukuli kungatithandize kukonzekera bwino “tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova,” lomwe lidzakhale mapeto a dongosolo la zinthu loipali.​—Malaki 4:5.

ANSEMBE ‘ANAKHUMUDWITSA AMBIRI’

(Malaki 1:1–2:17)

Yehova anauza Aisiraeli mawu ofotokoza mmene anali kumvera m’mtima mwake ponena kuti: “Ndakukondani.” Koma ansembe ankachita zinthu zonyoza dzina lake. Ankachita zimenezi motani? ‘Popereka mkate wodetsedwa pa guwa lake la nsembe’ ndiponso popereka nsembe ‘chiweto chosimphina ndi chodwala.’​—Malaki 1:2, 6-8.

Ansembewo ‘anakhumudwitsa ambiri m’chilamulo.’ Anthu ‘anachita monyengezana yense ndi mnzake.’ Ena anakwatira akazi akunja. Ena anachita zosakhulupirika ndi ‘akazi a ubwana wawo.’​—Malaki 2:8, 10, 11, 14-16.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

2:2—Kodi Yehova ‘anatemberera bwanji madalitso a ansembe amene sankamumvera?’ Anatero m’njira yakuti madalitso amene ansembewo ankapempherera anawasandutsa matemberero.

2:3—Kodi “kuwaza chiphwidza” pa nkhope za ansembe kukutanthauza chiyani? Malinga ndi Chilamulo, chiphwidza kapena kuti ndowe za nyama yoperekedwa nsembe zinkayenera kutayidwa kunja kwa msasa n’kuziwotcha. (Levitiko 16:27) Kuwaza chiphwidza pa nkhope za ansembe kukutanthauza kuti Yehova anasiya kulandira nsembe zawo ndiponso kuti ankanyansidwa nawo anthu opereka nsembezo.

2:13—Kodi guwa la nsembe la Yehova linakutidwa ndi misozi ya ndani? Inali misozi ya akazi omwe ankabwera ku kachisi kudzapembedza Yehova ndi mitima yawo yonse. Kodi n’chifukwa chiyani akaziwa anali ndi chisoni choterechi? Chifukwa chakuti amuna awo anawasudzula popanda zifukwa zenizeni ndipo n’kutheka kuti anachita zimenezi kuti akwatire atsikana achikunja.

Zimene Tikuphunzirapo:

1:10. Yehova sankasangalala ndi nsembe zimene ansembe adyera ankapereka. Ansembewa ankafuna kuti anthu awalipire ngakhale akangowatsekera chitseko kapena kuwayatsira moto pa guwa la nsembe. M’pofunika kwambiri kuti tizilambira ndiponso kuchita utumiki wachikhristu, chifukwa chokonda Mulungu ndi anzathu, osati kufuna ndalama.​—Mateyo 22:37-39; 2 Akorinto 11:7.

1:14; 2:17. Yehova amadana ndi chinyengo.

2:7-9. Anthu omwe ali ndi mwayi wophunzitsa mumpingo azionetsetsa kuti zimene akuphunzitsazo n’zogwirizana ndi Mawu a Mulungu omwe ndi Malemba Oyera, ndiponso n’zogwirizana ndi mabuku ophunzirira Baibulo a “mdindo wokhulupirika.”​—Luka 12:42; Yakobe 3:11.

2:10, 11. Yehova amafuna kuti olambira ake asamaone mopepuka malangizo oti ayenera kukwatira kapena kukwatiwa “mwa Ambuye.”​—1 Akorinto 7:39.

2:15, 16. Olambira Yehova enieni saswa pangano la ukwati limene amapanga ndi mkazi wa ubwana wawo.

‘AMBUYE ADZADZA KU KACHISI WAKE’

(Malaki 3:1–4:6)

“Ambuye [Yehova Mulungu] adzadza ku kachisi wake modzidzimutsa” ndi “mthenga wa chipangano [Yesu Khristu].” Mulungu ‘adzayandikiza anthu ake kuti awaweruze’ ndipo adzafulumira kupereka umboni wodzudzula anthu onse ochita zoipa. Komanso padzalembedwa “buku la chikumbutso” la anthu oopa Yehova.​—Malaki 3:1, 3, 5, 16.

“Tsiku lotentha ngati ng’anjo” lidzabwera ndipo lidzawononga anthu onse oipa. Koma tsiku limeneli lisanabwere, mneneri adzatumizidwa ‘kudzabwezera mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate awo.’​—Malaki 4:1, 5, 6.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

3:1-3—Kodi “Ambuye” ndiponso “mthenga wa chipangano” anafika liti kukachisi, ndipo ndani anatumizidwa ku kachisiko iwowo asanafike? Munthu woimira Yehova anafika ku kachisi Wake n’kumuyeretsa pa Nisani 10, 33 C.E. Izi zinachitika pamene Yesu analowa m’kachisi n’kuthamangitsa anthu amene ankagula ndi kugulitsa zinthu. (Maliko 11:15) Apa n’kuti patatha zaka zitatu ndi theka kuchokera pamene Yesu anadzozedwa kukhala Mfumu yosankhidwiratu. Zikuonekanso kuti patatha zaka zitatu ndi theka kuchokera pamene Yesu anaikidwa kukhala Mfumu kumwamba, iye anaperekeza Yehova ku kachisi wauzimu ndipo anapeza kuti anthu a Mulungu ankafunikira kuyeretsedwa. M’nthawi ya atumwi, Yohane M’batizi anatumizidwa kuti akonzekeretse Ayuda za kubwera kwa Yesu Khristu. M’nthawi yathu ino, wamthenga anatumizidwa pasanakhale kuti akonze njira ya kubweranso kwa Yehova kukachisi wake wauzimu. Kuyambira kale m’ma 1880, gulu la Ophunzira Baibulo linayamba ntchito yophunzitsa anthu Baibulo n’cholinga chophunzitsa anthu oona mtima zinthu zambirimbiri zofunika zokhudza choonadi cha m’Baibulo.

3:10—Kodi kubweretsa “limodzi lonse la khumi,” kapena kuti kupereka chachikhumi, kumaimira kupereka kwa Yehova zinthu zonse zimene tili nazo? Chilamulo cha Mose chinathetsedwa chifukwa cha imfa ya Yesu, motero masiku ano sitilamulidwa kupereka chachikhumi chenicheni. Komano kupereka chachikhumi kuli ndi tanthauzo lina lophiphiritsa. (Aefeso 2:15) Sikutanthauza kupereka zonse zimene tili nazo. Chachikhumi chinkaperekedwa chaka chilichonse, koma ifeyo timapereka zinthu zathu zonse kwa Yehova kamodzi kokha, panthawi imene tikudzipereka kwa iyeyo n’kusonyeza zimenezi pobatizidwa. Kuchokera panthawi imeneyi, chilichonse chimene tili nacho chimakhala cha Yehova. Komabe, iye amatilola kusankhapo pa zinthu zimene tili nazozo n’kuzigwiritsa ntchito pom’tumikira. Motero zimene tasankhazo zimakhala ngati chachikhumi. M’gulu limeneli muli zinthu zonse zimene timachitira Yehova mogwizana ndi mmene zinthu zilili pamoyo wathu komanso mmene mtima wathu ukutiuzira. Nsembe zimene timapereka kwa Yehova ndi zinthu monga nthawi yathu, mphamvu zathu, ndiponso zinthu zonse zimene timagwiritsira ntchito polalikira za Ufumu ndi kupanga ophunzira. M’gulu limeneli mulinso zinthu monga kupezeka pa misonkhano, kuyendera Akhristu anzathu omwe akudwala kapenanso omwe ndi achikulire, ndiponso kuthandiza nawo pantchito yopititsa patsogolo kulambira koona mwa kupereka ndalama zathu.

4:3—Kodi anthu a Yehova ‘adzapondereza oipa’ m’njira yotani? Anthu a Mulungu padziko lapansi ‘sadzapondereza oipa’ popereka chilango cha Mulungu kwa oipawo. M’malo mwake, mawu amenewa akusonyeza kuti atumiki a Yehova apadziko lapansi adzachita zimenezi m’njira yophiphiritsa pochita nawo mwamtima wonse chikondwerero chimene chidzakhalepo dziko la Satanali likadzachotsedwa.​—Salmo 145:20; Chivumbulutso 20:1-3.

4:4—N’chifukwa chiyani tiyenera “kukumbukira chilamulo cha Mose”? Chilamulo chimenechi sichigwira ntchito kwa Akhristu, komano ‘chinali mthunzi chabe wa zinthu zabwino zimene zinali kubwera.’ (Aheberi 10:1) Motero kuganizira mozama Chilamulo cha Mose kungatithandize kuona mmene zinthu zimene zinalembedwa mmenemo zikukwaniritsidwira panopo. (Luka 24:44, 45) Komanso, m’Chilamulochi muli “zifaniziro za zinthu za kumwamba.” Kuphunzira Chilamulo chimenechi n’kofunika kuti tithe kumvetsa ziphunzitso ndiponso makhalidwe achikhristu.​—Aheberi 9:23.

4:5, 6—Kodi “Eliya mneneri” akuimira ndani? Ulosi unati “Eliya” adzachita ntchito yokonzanso zinthu. Ntchito yake inali yokonzekeretsa mitima ya anthu. M’nthawi ya atumwi, Yesu Khristu ananena kuti Yohane M’batizi ndiye anali “Eliya” wamuulosi. (Mateyo 11:12-14; Maliko 9:11-13) Anzake a masiku ano anatumizidwa “lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.” Masiku ano Eliya si munthu winanso ayi, koma “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyo 24:45) Gulu la Akhristu odzozedwali lakhala likugwira ntchito yokonzanso zinthu mwauzimu.

Zimene Tikuphunzirapo:

3:10. Tikamapanda kum’patsa Yehova zonse zomwe tingathe timakhala tikudzimana tokha madalitso ake.

3:14, 15. Chifukwa cha chitsanzo choipa cha ansembe, Ayuda anayamba kuona kuti kutumikira Mulungu n’kosafunika kwenikweni. Abale amene ali ndi maudindo mumpingo ayenera kupereka chitsanzo chabwino.​—1 Petulo 5:1-3.

3:16. Yehova amasunga mayina a anthu onse amene amamuopa ndiponso amene ali okhulupirika. Amawakumbukira ndipo adzawapulumutsa akamadzawononga dziko loipa la Satanali. Motero, tisafooke koma tichite khama kuti tikhalebe okhulupirika kwa Mulungu.​—Yobu 27:5.

4:1. Patsiku loweruzidwa ndi Yehova, “nthambi” ndi “muzu” zidzaweruzidwa mofanana, kutanthauza kuti ana aang’ono adzalandira chiweruzo chofanana ndi chamakolo awo. Apatu zikusonyeza kuti makolo ali ndi udindo waukulu kwambiri wolera bwino ana awo. Makolo achikhristu ayenera kuchita khama kwambiri pochita zinthu zosangalatsa Mulungu ndiponso pokhala ndi dzina labwino kwa iye.​—1 Akorinto 7:14.

“Opa Mulungu”

Kodi ndani adzapulumutsidwa pa “tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova”? (Malaki 4:5) Yehova anati: “Inu akuopa dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakutulukirani, muli kuchiritsa m’mapiko mwake; ndipo mudzatuluka ndi kutumphatumpha ngati ana a ng’ombe onenepa.”​—Malaki 4:2.

Yesu Khristu ndiye “dzuwa la chilungamo” ndipo amawala kwa anthu amene amaopa ndi kulemekeza dzina la Mulungu, ndipo Yehova amasangalala nawo anthu otero. (Yohane 8:12) Komanso kwa iwowa, “muli kuchiritsa m’mapiko mwake.” Uku ndi kuchiritsidwa kwauzimu komwe kukuchitika panopo, ndipo m’tsogolo muno anthuwa adzachiritsidwanso matenda awo onse akuthupi ndiponso amaganizo, m’dziko latsopano la Mulungu. (Chivumbulutso 22:1, 2) Iwowa ndi osangalala ndiponso ndi achimwemwe chodzaza tsaya, motero amatumphatumpha “ngati ana a ng’ombe onenepa.” Poganizira madalitso amenewa, tiyeni timvere malangizo a Mfumu Solomo akuti: “Opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.”​—Mlaliki 12:13.

[Chithunzi patsamba 26]

Mneneri Malaki anali mtumiki wa Mulungu wakhama ndiponso wodzipereka kwambiri

[Chithunzi patsamba 29]

Tiziphunzitsa zinthu zogwirizana ndi Baibulo

[Chithunzi patsamba 29]

Atumiki a Yehova saswa pangano lawo laukwati