Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi okhulupirira nyenyezi anakaona Yesu liti?

Mu Uthenga Wabwino wa Mateyo, timawerenga kuti “okhulupirira nyenyezi ochokera madera a kum’mawa” anabwera kudzaona Yesu atatenga mphatso. (Mateyo 2:​1-12) Baibulo silinena kuti okhulupirira nyenyeziwo analipo angati, ndipo zimene ena amanena zoti analipo atatu zilibe umboni weniweni. Ndiponso Baibulo silitchula maina awo.

Ponena za mawu a pa Mateyo 2:​11, Baibulo lina (New International Version Study Bible) limafotokoza kuti: “Anthu ambiri amati okhulupirira nyenyezi anakaona Yesu ali modyera ziweto pausiku womwe iye anabadwa monga anachitira abusa aja. Zimenezi sizoona chifukwa okhulupirira nyenyeziwo anakamuona patatha miyezi ingapo. Panthawiyi n’kuti Yesu ali ‘mwana wamng’ono’ ‘kunyumba’ kwawo.” Umboni wa zimenezi ndi woti pamene Herode ankafuna kupha Yesu, analamula kuti ana onse aamuna osapitirira zaka ziwiri aphedwe ku Betelehemu ndi m’zigawo zake zonse. Kuti adziwe zaka zoyenerera, anawerengetsera bwinobwino “mogwirizana ndi nthawi imene anafunsira mosamalitsa kwa okhulupirira nyenyezi aja.”​—Mateyo 2:16.

Okhulupirira nyenyezi aja akanakhala kuti anabwera kudzaona Yesu patsiku limene anabadwa n’kudzam’patsa golidi ndi mphatso zina zamtengo wapatali, n’zokayikitsa kuti patatha masiku 40, Mariya akanapereka nsembe ya nkhunda ziwiri zokha atabwera ndi Yesu kukachisi. (Luka 2:​22-24) Anthu osauka, amene sakanakwanitsa kupereka nsembe ya mwana wankhosa ndi amene ankaloledwa kupereka nsembe ngati imeneyi mogwirizana ndi Chilamulo. (Levitiko 12:​6-8) Komabe, mphatso zamtengo wapatali zimenezi ziyenera kuti zinafika panthawi yake moti zinathandiza Yesu ndi banja lake pa zosowa zawo ali ku Iguputo.​—Mateyo 2:​13-15.

N’chifukwa chiyani Yesu anatenga masiku anayi asanafike ku manda a Lazaro?

Zikuoneka kuti kwenikweni Yesu anachita dala zimenezi. N’chifukwa chiyani tikutero? Taonani nkhani yolembedwa mu chaputala 11 cha buku la Yohane.

Lazaro anali mnzake wa Yesu ndipo ankakhala ku Betaniya. Atadwala mwakayakaya, alongo ake anatumiza uthenga kwa Yesu. (Vesi 1 mpaka 3) Panthawiyi Yesu anali kutali ndi ku Betaniya, ulendo wa masiku awiri. (Yohane 10:40) Zikuoneka kuti Lazaro anamwalira panthawi imene Yesu analandira uthengawo. Ndiyeno kodi Yesu anatani? Iye “anakhalabe masiku awiri kumalo kumene iye analiko,” kenako ananyamuka kupita ku Betaniya. (Vesi 6 ndi 7) Motero, chifukwa choti anadikira masiku awiri n’kuyendanso ulendo wa masiku awiri, anakafika ku mandako patatha masiku anayi Lazaro atamwalira.​—Vesi 17.

Nkhani ya kuukitsa Lazaro isanachitike, Yesu anali ataukitsa anthu awiri. Woyamba anamuukitsa atangofa kumene, ndipo zikuoneka kuti winayo anamuukitsa patatenga nthawi ndithu koma tsiku lomwe anafalo. (Luka 7:​11-17; 8:​49-55) Kodi Yesu akanatha kuukitsa munthu amene wakhala atamwalira kwa masiku anayi, yemwenso thupi lake layamba kuwola? (Vesi 39) N’zochititsa chidwi kuti buku lina limanena kuti Ayuda anali ndi chikhulupiriro chakuti “munthu yemwe wakhala atamwalira kwa masiku anayi sangaukenso chifukwa thupi lake limakhala litayamba kuwola ndiponso mzimu wa munthuyo, umene ankakhulupirira kuti umakhala ukuyendayenda m’mpweya kwa masiku atatu pafupi ndi thupilo, umakhala utachoka.”

Ngati kumandako kunali munthu aliyense wokayikira mphamvu za Yesu zotha kuukitsa akufa, iyi inali nthawi yoti adzionere yekha. Yesu anaima pafupi ndi khomo la mandawo, womwe anali wotsegula, n’kufuula kuti: “Lazaro, tuluka!” Kenako, munthu “amene anali wakufa uja anatuluka.” (Vesi 43 ndi 44) Chiyembekezo chenicheni cha anthu akufa ndi choti adzauka, osati maganizo olakwika akuti munthu akafa mzimu umakhalabe ndi moyo.​—Yohane 11:25.