Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndinamasuka ku Mikwingwirima ya Paubwana Wanga

Ndinamasuka ku Mikwingwirima ya Paubwana Wanga

Ndinamasuka ku Mikwingwirima ya Paubwana Wanga

Yosimbidwa ndi Eusebio Morcillo

Mu September 1993, ndinapita ku ndende ina yachitetezo chokhwima kwambiri kumwambo waubatizo wa mlongo wanga wamng’ono, dzina lake Mariví. Akaidi ndiponso akuluakulu ena pandendeyo ankawonerera mwaulemu ineyo ndikuchititsa mwambowo. Ndisanafotokoze zimene zinachitika kuti ine ndi mlongo wangayu tipezeke kumeneku, ndiloleni ndifotokoze kaye za mmene tinakulira.

NDINABADWIRA ku Spain, pa May 5, 1954, ndipo ndinali mwana woyamba m’banja la ana 8. Mariví anali wachitatu. Tinakhala Akatolika olimbikira kwambiri chifukwa choleredwa ndi agogo athu aakazi, ndipo ndikukumbukira kuti panthawi imene ndinkakhala ndi agogowo ndinkadziona kuti ndine mwana wodzipereka kwambiri kwa Mulungu. Koma pakhomo pa makolo anga panalibe zoopa Mulungu. Kawirikawiri bambo ankamenya mayi anga ndiponso anafe. Tinkakhala mwamantha, ndipo zinkandiwawa kwambiri kuona mayi akuzunzidwa choncho.

Kusukulu zinthu sizinalinso bwino. Tinali ndi mphunzitsi winawake, yemwenso anali wansembe, amene ankati mwana akalakwa funso amamugwira n’kumenyetsa mutu wake kukhoma. Wansembe wina ankagwirira ana asukulu akamawachongera zinthu zomwe anawauza kuti alembe. Ndiponso, ziphunzitso za Chikatolika monga zakuti kuli moto kumwamba zinkandichititsa mantha ndipo zinkandisokoneza kwambiri. Posakhalitsa ndinayamba kufooka pa zinthu zauzimu.

Ndinalowerera

Posowa munthu wonditsogolera mwauzimu, ndinayamba kupita ku madansi, n’kumakacheza ndi anthu a makhalidwe oipa ndiponso achiwawa. Kawirikawiri kumeneku kunkachitika ndewu za mipeni, matcheni, magalasi, ndiponso mipando. Ngakhale kuti ineyo sindinkachita nawo ndewuzo, panthawi ina ndinafera za eni moti anandimenya mpaka kukomoka.

Zimenezi nditatopa nazo ndinayamba kupita ku madansi omwe sikunkakhala zachiwawa. Komabe, kumalo amenewa mankhwala osokoneza bongo anali osasowa. Mankhwalawa sanandithandize kukhala wosangalala, m’malo mwake ankandichititsa kuona zilubwelubwe ndiponso kukhala ndi nkhawa.

Ngakhale kuti moyo wangawu sunali wosangalatsa, ndinachititsa kuti mng’ono wanga José Luis, pamodzi ndi mnzanga wina wapamtima dzina lake Miguel, atengere khalidwe langali. Mofanana ndi achinyamata ambiri ku Spain panthawiyi, tinalowerera kwambiri. Ndinkalolera kuchita chilichonse kuti ndipeze ndalama zogulira mankhwala osokoneza bongo ndipo sindinkasamala za ulemu wanga.

Yehova Anandipulumutsa

Panthawi imeneyi, ndinkakonda kufunsa anzanga kuti ndidziwe ngati Mulungu alikodi ndiponso cholinga cha moyo. Ndinkafuna kum’dziwa bwino Mulungu, choncho ndinayamba kufufuza munthu woti ndizikambirana naye zinthu zimene zinkandivutitsa maganizo. Ndinaona kuti mnzanga wina wakuntchito dzina lake Francisco, anali wosiyana kwambiri ndi anzanga ena onse. Ankaoneka kuti anali munthu wosangalala, woona mtima, ndiponso wokoma mtima, motero ndinaganiza zomuuza zakukhosi kwanga. Francisco anali wa Mboni za Yehova ndipo anandipatsa magazini ya Nsanja ya Olonda yomwe inali ndi nkhani yofotokoza za mankhwala osokoneza bongo.

Nditawerenga nkhaniyo, ndinapemphera kwa Mulungu kuti andithandize. M’pempherolo ndinanena kuti: “Ambuye, ndikudziwa kuti mulipo, ndipo ndikufuna kukudziwani ndi kuchita chifuniro chanu. Chonde ndithandizeni.” Francisco pamodzi ndi Amboni ena anandilimbikitsa pogwiritsira ntchito Baibulo ndipo ankandipatsa mabuku ofotokoza Baibulo kuti ndiziwerenga. Ndinazindikira kuti anthuwa ankandipatsa thandizo limene ndinapempha kwa Mulungu lija. Posakhalitsa ndinayamba kuuza anzanga ndiponso José Luis zinthu zimene ndinkaphunzirazo.

Tsiku lina tikuchoka ku dansi ndi anzanga ena, ndinaima poteropo n’kumayang’ana gulu la anzangawo. Ndinadzimvera chisoni kwambiri pozindikira kuti khalidwe lathu lafika poipa kwambiri chifukwa chogwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo. Apa m’pamene ndinaganiza zosiyana nawo moyo umenewu kuti ndikhale wa Mboni za Yehova.

Ndinam’pempha Francisco kuti andipezere Baibulo, ndipo anaterodi. Anandipatsanso buku la Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya. * Nditawerenga za lonjezo la Mulungu lakuti adzapukuta misozi yonse ndi kuchotsa ngakhale imfa, sindinakayike kuti ndapeza choonadi chimene chingathe kumasula anthu. (Yohane 8:32; Chivumbulutso 21:4) Patsogolo pake ndinapita ku msonkhano ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova. Ndinadabwa kwambiri kuona anthu osangalala ndiponso achikondi omwe anali kumeneko.

Pofunitsitsa kuuza ena zimene ndinaona ku Nyumba ya Ufumu kuja, nthawi yomweyo ndinaitana José Luis ndi anzanga ena n’kuwauza za nkhaniyi. Patapita masiku angapo, tonse tinapita ku misonkhano. Mtsikana wina amene anakhala patsogolo pathu anatiyang’anitsitsa kwambiri. N’zachidziwikire kuti ankadabwa kuona gulu la anthu a tsitsi lalitali komanso lanyankhalala, ndipo sanayerekeze kutembenukanso n’kutiyang’ana. Ayenera kuti anadabwa kwambiri kutiona titabweranso ku Nyumba ya Ufumu mlungu wotsatira, chifukwa panthawiyi tinali titavala masuti ndi matayi.

Posakhalitsa, ineyo ndi Miguel tinapitanso ku msonkhano wadera wa Mboni za Yehova. Aka kanali koyamba kwa ifeyo kuona umodzi weniweni pakati pa anthu osiyanasiyana. Ndipotu zinali zochititsa chidwi kuti msonkhanowu unachitikira m’chinyumba chimene munachitikira dansi imene tinapitako ija. Kungoti panthawiyi, tinatsitsimulidwa kwabasi chifukwa cha nyimbo komanso mmene zinthu zonse zinalili pamalopo.

Gulu lathu lonse linayamba kuphunzira Baibulo. Patatha miyezi 8, pa July 26, 1974 ineyo ndi Miguel tinabatizidwa. Tonse tinali ndi zaka 20. Anzathu ena anayi a m’gululi anabatizidwa patangodutsa miyezi ingapo. Chifukwa cha zimene ndinaphunzira m’Baibulo ndinayamba kuthandiza mayi anga, amene anali munthu woleza mtima kwambiri. Ndinkawathandiza ntchito zapakhomo ndipo ndinkawauza za chikhulupiriro changa chatsopanocho. Tinayamba kugwirizana kwambiri. Ndinayambanso kuthandiza azing’ono anga ndi azilongo anga.

Patsogolo pake, mayi ndiponso azibale anga onse, kupatulapo mmodzi yekha, anaphunzira choonadi cha m’Baibulo n’kubatizidwa kukhala Mboni za Yehova. M’chaka cha 1977 ndinakwatirana ndi Soledad. Iyeyu ndiye mtsikana amene anatiyang’ana modabwa pamene tinafika koyamba ku Nyumba ya Ufumu. Patangotha miyezi yochepa, tonse tinakhala apainiya, dzina lomwe Mboni za Yehova zimatchulira alaliki a nthawi zonse a uthenga wabwino.

Mlongo Wanga Wokondedwa Anamasulidwa

Mlongo wanga Mariví anagwiriridwa ali mwana, ndipo zimenezi zinamusokoneza maganizo kwambiri. Ali mtsikana, analowerera kwambiri moti ankagwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo, ankaba ndiponso ankachita uhule. Ali ndi zaka 23 anamangidwa, ndipo anapitirizabe khalidwe lakelo kundendeko.

Apa n’kuti ineyo ndili woyang’anira dera, kapena kuti mtumiki woyendera mipingo ya Mboni za Yehova. M’chaka cha 1989, ineyo ndi mkazi wanga Soledad tinatumizidwa ku dera la kufupi ndi ndende imene kunali Mariví. Aboma anali atangomulanda mwana wake, ndipo anasokonezeka kwambiri, moti moyo sankaufunanso ngakhale pang’ono. Tsiku lina nditapita kukamuona ndinam’pempha kuti ndiziphunzira naye Baibulo, ndipo anavomera. Nditaphunzira naye kwa mwezi umodzi, iye anasiya kugwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo ndi kusuta fodya. Zinandisangalatsa kwambiri kuona kuti Yehova anam’patsa mphamvu zotha kusintha chonchi.​—Aheberi 4:12.

Kuchokera pa nthawi imene anayamba kuphunzira Baibulo, Mariví sanatenge nthawi kuti ayambe kuuza akaidi anzake ndiponso oyang’anira ndende za choonadi cha m’Baibulo. Ngakhale kuti iye ankasamukasamuka, ndende iliyonse imene wapitako ankapitiriza kulalikira. Pandende ina anafika pomalalikira selo iliyonse. Kwa zaka zambiri Mariví anayambitsa maphunziro a Baibulo ndi akaidi ambiri m’ndende zosiyanasiyana.

Tsiku lina Mariví anandiuza kuti akufuna kupereka moyo wake kwa Yehova n’kubatizidwa. Koma sanaloledwe kuchoka pa ndendeyo ndipo palibe aliyense amene analoledwa kuti afike pa ndendepo kukam’batiza. Iye anakhala zaka zinayi akuvutika ndi anthu a makhalidwe oipa m’ndendemo. Kodi chinam’thandiza n’chiyani kuti chikhulupiriro chake chikhalebe cholimba? Panthawi yeniyeni imene mpingo wadera limenelo unkachita misonkhano, m’pamene nayenso ankawerenga nkhani za misonkhanoyo ali mu selo. Komanso tsiku ndi tsiku ankawerenga Baibulo ndiponso kupemphera.

M’kupita kwa nthawi, Mariví anamusamutsira ku ndende ina ya chitetezo chokhwima kwambiri yomwenso inali ndi dziwe losambira. Iye anaona kuti malo atsopanowa am’patsa mwayi woti abatizidwe. Ndipo ndi zimene zinachitikadi. Zimenezi ndi zimene zinandichititsa kuti ndipezeke kumeneku kukakamba nkhani yake yaubatizo. Ndinasangalala kuti ndinali naye limodzi panthawi yofunika kwambiri pamoyo wakeyi.

Mariví anatenga matenda a Edzi chifukwa cha makhalidwe ake akale. Kenako, chifukwa chakuti anayamba kusonyeza khalidwe labwino kundendeko, anamutulutsa mu March 1994, nthawi yomwe analamulidwa kukhala m’ndende isanathe. Atatuluka anakakhala ndi mayi athu ndipo anali wolimbikira kwambiri pa moyo wachikhristu mpaka pamene iye anamwalira patatha zaka ziwiri atatuluka ku ndende.

Kulimbana ndi Maganizo Ofoola

Inenso ndikukumanabe ndi mavuto chifukwa cha mmene ndinakulira. Moyo wanga unakhudzidwa kwambiri chifukwa cha nkhanza za bambo anga komanso chifukwa chokhala ndi khalidwe lotayirira ndili mnyamata. Ndakhala ndikudziimba mlandu ndiponso kudziona kuti ndine munthu wosafunika. Nthawi zinanso ndimakhala wopsinjika maganizo kwambiri. Komabe, Mawu a Mulungu andithandiza kwambiri kulimbana ndi maganizo ovutitsa amenewa. Kusinkhasinkha malemba monga Yesaya 1:18 ndi Salmo 103:​8-13 kwandithandiza kwa zaka zambiri kuti ndichepetse kumadziimba mlandu.

Pemphero ndi chida china chimene chandithandiza kuthana ndi maganizo odziona ngati ndine wosafunika. Nthawi zambiri ndikamapemphera kwa Yehova ndimagwetsa misozi. Koma ndimalimbikitsidwa ndi mawu a pa 1 Yohane 3:​19, 20 akuti: “Umu ndi mmene tidzadziwira kuti ndife ochokera m’choonadi, ndipo tidzatsimikizira mitima yathu pamaso pake za chilichonse chimene mitima yathu ingatitsutse, chifukwa Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziwa zonse.”

Chifukwa chopemphera kwa Yehova moona mtima ndiponso ndi “mtima wosweka,” ndazindikira kuti si bwino kumadziona kuti ndine munthu woipa kwambiri. Anthu onse amene amafunafuna Yehova asamakayikire mfundo ya m’Baibulo yakuti, iye sataya anthu amene ayamba kuchita zimene iyeyo amafuna amene panopo akunong’oneza bondo chifukwa cha khalidwe lawo loipa limene anali nalo poyamba.​—Salmo 51:17.

Maganizo ofoola akandifikira, ndimayamba kuganizira zinthu zolimbikitsa, monga zinthu zauzimu zotchulidwa pa Afilipi 4:8. Ndalowezanso pamtima Salmo 23 ndiponso ulaliki wa paphiri. Ndikayamba kuganizira zinthu zofoola, ndimanena mokweza Malemba amenewa. Kuchita zimenezi kumandithandiza kwambiri makamaka ndikamasowa tulo.

Chinthu chinanso chomwe chandithandiza kwambiri ndi mawu oyamikira ochokera kwa mkazi wanga ndiponso Akhristu okhwima mwauzimu. Poyamba zinkandivuta kukhulupirira kuti akundiyamikira mochokera pansi pa mtima, komabe Baibulo landithandiza kumvetsa mfundo yakuti chikondi “chimakhulupirira zinthu zonse.” (1 Akorinto 13:7) Pang’onopang’ono, ndaphunziranso kuvomereza modzichepetsa zolephera zanga ndiponso kudziwa kuti pali zinthu zina zomwe sindingathe kuchita.

Komabe, chosangalatsa ndi chakuti kulimbana ndi maganizo ofoola kwandithandiza kwambiri kukhala mtumiki wadera womvera ena chifundo. Ine ndi mkazi wanga tatha zaka pafupifupi 30 mu utumiki wanthawi zonse monga alaliki a uthenga wabwino. Chisangalalo chimene ndimapeza chifukwa chotumikira ena chandithandiza kuti ndithane ndi maganizo ofoola ndiponso kuti ndisamaganizire kwambiri mavuto amene ndinakumana nawo pamoyo wanga.

Ndikayang’ana m’mbuyo n’kuganizira za madalitso amene Yehova wandipatsa, ndimanena mawu ofanana ndi a wamasalmo akuti: “Lemekeza Yehova, . . . amene akhululukira mphulupulu zako zonse; nachiritsa nthenda zako zonse; amene awombola moyo wako ungawonongeke; nakuveka korona wa chifundo ndi nsoni zokoma.​—Salmo 103:​1-4.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma tsopano anasiya kulisindikiza.

[Mawu Otsindika patsamba 30]

Ndakhala ndikudziimba mlandu ndiponso kudziona kuti ndine munthu wosafunika. Komabe, Mawu a Mulungu andithandiza kwambiri kulimbana ndi maganizo ovutitsa amenewa

[Zithunzi patsamba 27]

Mchimwene wanga José Luis ndiponso mnzanga Miguel anatengera chitsanzo changa choipa ndi chabwino chomwe

[Chithunzi pamasamba 28, 29]

Banja la a Morcillo mu 1973

[Chithunzi patsamba 29]

Mariví pamene anali ku ndende

[Chithunzi patsamba 30]

Ndili ndi mkazi wanga, Soledad