Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi M’tsogolomu Muli Zotani?

Kodi M’tsogolomu Muli Zotani?

Kodi M’tsogolomu Muli Zotani?

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUDZIWA YANKHO LA FUNSOLI? Mmene timaonera tsogolo lathu zimakhudza zochita zathu panopo. Mwachitsanzo, anthu amene alibe chiyembekezo cha m’tsogolo angakhale ndi moyo woti “tiyeni tidye ndi kumwa, popeza mawa tifa.” (1 Akorinto 15:32) Maganizo amenewa nthawi zambiri amapangitsa munthu kudya kwambiri, kuledzera, ndiponso kukhala ndi nkhawa. Zinthu zimenezi sizibweretsa mtendere weniweni wa mumtima.

Kunena zoona, zikanakhala kuti anthu ndi amene apatsidwa mphamvu zoyendetsa zinthu za m’tsogolo, bwenzi zimene tikuyembekezera zili zosatsimikizirika. M’dzikoli anthu awononga kwambiri mpweya, madzi ndiponso nthaka kuposa kale lonse. Anthu akuopa kwambiri zauchigawenga ndiponso nkhondo ya zida zanyukiliya. Anthu padziko lonse akuvutika ndi matenda ndi umphawi. Komabe pali zifukwa zomveka zokhulupirira kuti zinthu zidzakhala bwino.

Ngakhale kuti anthu sanganene molondola zimene zingachitike m’tsogolomu, Yehova Mulungu amati Iye ‘amalalikira za chimaliziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthawi zakale anena zinthu zimene zisanachitidwe.’ (Yesaya 46:10) Kodi Yehova amati m’tsogolomu muli zotani?

Zimene Baibulo Limanena

Yehova sadzalola kuti dzikoli kapena zamoyo zimene zilipo ziwonongedwe kotheratu. Ndipotu, Baibulo limalonjeza kuti Mulungu ‘adzawononga iwo owononga dziko lapansi.’ (Chivumbulutso 11:18) Pogwiritsa ntchito Ufumu wake, kapena kuti boma lakumwamba, Yehova adzayeretsa dzikoli mwa kuchotsa oipa onse kuti likhale monga anafunira pachiyambi. (Genesis 1:26-31; 2:8, 9; Mateyo 6:9, 10) Mavesi a m’Baibulo otsatirawa akutithandiza kuona zina mwa zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo zimene zidzakhudze wina aliyense padzikoli.

Salmo 46:8, 9“Idzani, penyani ntchito za Yehova, amene achita zopululutsa pa dziko lapansi. Aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magareta ndi moto.”

Yesaya 35:5, 6“Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilume la wosalankhula lidzayimba; pakuti m’chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m’dziko loti se.”

Yesaya 65:21, 22. “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya.”

Danieli 2:44. “Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse nudzakhala chikhalire.”

Yohane 5:28, 29. “Musadabwe nazo zimenezi, chifukwa idzafika nthawi pamene onse ali m’manda a chikumbutso adzamva mawu [a Yesu] ndipo adzatuluka.”

Chivumbulutso 21:3, 4“Mulungu mwini adzakhala nawo. Iye adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”

Baibulo Limatithandiza Kukhala ndi Mtendere wa Mumtima

Tikangoona zimene tafotokoza kumenezi, tingaganize kuti sizingachitike. Komatu Mulungu ndi amene walonjeza osati anthu. Ndipotu Yehova Mulungu “sanganame.”​—Tito 1:2.

Mukamakhulupirira zimene Mulungu walonjeza ndiponso mukamatsatira malamulo ake pamoyo wanu, mungakhale ndi mtendere wa mumtima ngakhale zinthu zitavuta kwambiri. Nkhondo, umphawi, matenda ngakhale mavuto aukalamba kapena imfa yanu yomwe, sizingachotseretu mtendere wanu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti mudzakhala ndi chikhulupiriro chonse kuti Ufumu wa Mulungu udzachotsa mavuto onsewa.

Kodi chikhulupiriro chimenechi mungachipeze bwanji? Muyenera “kusintha maganizo anu” ndi kuzindikira “chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino ndi chovomerezeka ndi changwiro.” (Aroma 12:2) N’zoonekeratu kuti mufunika umboni wina wotsimikizira kuti malonjezo a m’Baibulo ndi odalirika. Mufunikadi kufufuza zimenezi. Ndipo ndi zinthu zochepa chabe zimene mumachita pamoyo wanu zimene zingakupatseni mtendere weniweni wa mumtima.

[Zithunzi pamasamba 8, 9]

Kodi Mawu a Mulungu amati m’tsogolomu muli zotani?

Yesaya 35:5

Yesaya 35:6

Yohane 5:28, 29