Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

M’busa Amene Amakusamalirani

M’busa Amene Amakusamalirani

Yandikirani Mulungu

M’busa Amene Amakusamalirani

Mateyo 18:12-14

‘KODI Mulungu amasamaladi za ine?’ Ngati munadzifunsapo funso limeneli, simuli nokha. Ambiri a ife tinavutikapo ndipo nthawi zina timadzifunsa ngati Mlengi wa chilengedwe chonsechi amasamaladi za ife. Koma tifunika kudziwa kuti Yehova Mulungu amasamaladi za aliyense payekhapayekha. Nthawi imene anali padziko lino lapansi, Yesu yemwe amam’dziwa bwino Yehova, ananena fanizo limene limasonyeza bwino yankho la funso limeneli.

Poyerekezera Yehova ndi mmene m’busa weniweni amasamalirira nkhosa zake, Yesu anati: “Ngati munthu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi mwa nkhosazo n’kusochera, kodi sangasiye 99 zija m’phiri ndi kupita kukafunafuna yosocherayo? Ndipo akaipeza, ndithu ndikunenetsa, amakondwera kwambiri ndi nkhosa imeneyo kusiyana ndi 99 zosasochera zija. Mofananamo Atate wanga wa kumwamba sakufuna kuti mmodzi wa aang’ono awa akawonongeke.” (Mateyo 18:12-14) Tiyeni tione momwe Yesu anafotokozera mmene Yehova amasamalirira atumiki ake aliyense payekhapayekha.

M’busa amadziwa kuti ali ndi udindo wosamalira nkhosa zake iliyonse payokhapayokha. Ngati nkhosa ina yasochera, iye amadziwa nkhosa imene yasocherayo chifukwa amadziwa dzina la nkhosa iliyonse. (Yohane 10:3) M’busa wosamala nkhosa zake sapuma mpaka ataipeza nkhosa yosocherayo. Iye akapita kukafuna nkhosa yosocherayo sikuti nkhosa 99 zotsalazo amangozisiya zokha. Nthawi zambiri abusa ankadyetsera pamodzi ziweto zawo. * Choncho m’busa amene anapita kukafuna nkhosa yosowa ija anakasiyira abusa anzakewo nkhosa zinazo. M’busayo ataipeza nkhosayo ili bwinobwino anainyamula paphewa chimwemwe chitadzaza tsaya n’kukafika nayo pagulu la nkhosa zinazo.​—Luka 15:5, 6.

Pofotokoza fanizoli, Yesu anati Mulungu safuna kuti “mmodzi wa aang’ono awa akawonongeke.” Panthawi ina Yesu asananene fanizoli anachenjeza ophunzira ake kuti asakhumudwitse “mmodzi wa aang’ono awa amene amakhulupirira mwa [iye].” (Mateyo 18:6) Nanga kodi fanizoli likutiphunzitsa chiyani za Yehova? Iye ndi M’busa amene amasamalira kwambiri nkhosa zake iliyonse payokhapayokha, kuphatikizapo “aang’ono” amene ndi anthu omwe dzikoli limawaona ngati osafunikira. Ndithudi, kwa Mulungu mtumiki wake aliyense ndi wapadera komanso ndi wofunika kwambiri.

Ngati mukufuna kutsimikizira kuti Mulungu amakukondani, bwanji osaphunzira za Yehova Mulungu amene ndi M’busa Wamkulu ndiponso zimene mungachite kuti mumuyandikire? Mukachita zimenezi, mudzakhala ndi chikhulupiriro changati cha mtumwi Petulo, amene mosakayikira analipo pamene Yesu ankakanena fanizo limeneli. Petulo kenako analemba kuti: ‘M’tulireni Mulungu nkhawa zanu zonse, pakuti amasamala za inu.’​—1 Petulo 5:7.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Zinali zosavuta kupatula nkhosa za magulu osiyana, popeza nkhosa iliyonse imadziwa bwino mawu m’busa wake.​—Yohane 10:4.