Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi thawale lamkuwa la pakachisi wa Solomo linali lalikulu bwanji?

Nkhani imene ili pa 1 Mafumu 7:26 imanena kuti mu thawale la mkuwali munkalowa madzi okwana “mitsuko yaikulu zikwi ziwiri” amene ansembe ankagwiritsa ntchito. Koma nkhani yofanana ndi imeneyi ya pa 2 Mbiri 4:5 imanena kuti m’thawaleli munkalowa madzi okwana “mitsuko yaikulu zikwi zitatu.” Zimenezi zapangitsa ena kuganiza kuti wolemba buku la Mbiri analakwitsa.

Koma malemba awiriwa si otsutsana koma ndi ogwirizana. Lemba loyambirira lachiheberi la 2 Mbiri 4:5 limanena za madzi amene akanatha kulowamo pamene la 1 Mafumu 7:26 limanena za madzi amene ankaikidwa m’thawaleli. Zimenezi zikutanthauza kuti nthawi zambiri sankadzazitsa madzi m’thawalelo. Zikuoneka kuti unali mwambo wawo kungothira madzi okwana mitsuko yaikulu zikwi ziwiri m’thawaleli.

Kodi n’chifukwa chiyani Yesu ndi Petulo anangopereka ndalama imodzi pa msonkho wa pakachisi?

M’masiku a Yesu, mwamuna aliyense wachiyuda woposa zaka 20 anafunika kupereka msonkho wapachaka wa pakachisi wokwana madirakima awiri kapena ndalama imodzi yokwana madirakima awiri. Ndalama imeneyi inali yokwanira malipiro a masiku awiri. Pamene funso lokhudza kupereka msonkho umenewu linabuka, Yesu anauza Petulo kuti: “Upite kunyanja, ukaponye mbedza, ndipo ukatenge nsomba yoyambirira kuwedza. Ukakaikanula kukamwa kwake, ukapezako kobili limodzi la siliva. Ukalitenge ndi kukhomera msonkho wako ndi wanga.”​—Mateyo 17:24-27.

Akatswiri ambiri amakhulupirira kuti ndalama imeneyi inali yokwana madirakima anayi kapena yokwana kulipira msonkho wa pakachisi wa anthu awiri. Ndalama imeneyi inali yofala kuposa ndalama imodzi yokwana madirakima awiri. Ndipo buku lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo (The New Bible Dictionary) limati: “Zikuoneka kuti nthawi zambiri Ayuda ankapereka msonkho wa pakachisi wa anthu awiri.”

Koma munthu yemwe ankalipira msonkho wa iye yekha ankam’lipiritsa ndalama yapadera kuti amusinthe ndalamayo. Ndalama imeneyi inali yokwera ndithu. Koma amene anali kupereka msonkho wa anthu awiri sanali kuwalipiritsa. Motero, ngakhale pa mfundo yaing’ono imeneyi, nkhani yomwe Mateyo analemba imagwirizana ndi zinthu zomwe zinali zodziwika bwino m’masiku a Yesu.

[Chithunzi patsamba 15]

Ndalama iyi ndi yokwana madirakima anayi