Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kumanga Nyumba Zotamandiramo Yehova

Kumanga Nyumba Zotamandiramo Yehova

Kumanga Nyumba Zotamandiramo Yehova

“Sindikukhulupirira. Sindinkaganiza kuti tingakhale ndi malo otamandira Yehova okongola kwambiri ngati amenewa. Palibe chimene chingandibweretsere chimwemwe ngati chimenechi.”​—ANATERO MARIA, WA KU MEXICO.

AMBONI ZA YEHOVA amakonda kusonkhana pamodzi pophunzira Mawu a Mulungu, Baibulo. (Salmo 27:4; Aheberi 10:23-25) Ndipo amasangalala kuchita zimenezi makamaka ngati akusonkhanira pa malo abwino. M’zaka za posachedwapa, iwo amanga malo ambirimbiri atsopano olambirira, otchedwa Nyumba za Ufumu m’mayiko ambiri padziko lonse.

N’chiyani chachititsa kuti pakhale ntchito yomanga imeneyi? Ndipo ndani amene amagwira ntchitoyi? Nanga ntchitoyi imakhudza bwanji anthu omangawo? Kuti tiyankhe mafunso amenewa, tiyeni tione zimene zakhala zikuchitika m’dziko la Mexico ndi la Belize.

Panafunika Nyumba za Ufumu Zambirimbiri

M’mbuyomu, Mboni za Yehova ku Mexico polambira Yehova zinkasonkhana m’malo aliwonse amene apezeka monga kuseri kwa nyumba, m’nyumba za Mboni, m’nyumba zosungiramo katundu, mosungira galimoto, kapena m’maholo alendi. Panthawi imeneyi, Mboni zokhulupirika zimenezi nthawi zambiri zinkaona kuti zingakhale bwino zitakhala ndi Nyumba za Ufumu zawozawo.

Pomafika mu 1994, ku Mexico kunali Mboni zokwana 388,000. Kafukufuku amene anachitika chaka chimenecho anasonyeza kuti panafunika kumangidwa Nyumba za Ufumu za tsopano 3,300 kuti anthu amenewa akhale ndi malo awoawo olambiriramo. Imeneyi inali ntchito yaikulu kwabasi.

Panthawi imeneyi mipingo yomwe inkakwanitsa inkamanga yokha Nyumba za Ufumu. Koma patadutsa zaka zisanu, anthu anayamba kuchuluka kwambiri m’mipingoyi moti zinali zoonekeratu kuti panafunika kumanga mwamsanga Nyumba za Ufumu zina zochuluka. Kodi ntchito imeneyi ikuyenda bwanji?

Antchito Aluso Ongodzipereka

Pulogalamu yatsopano yomanga Nyumba za Ufumu inayambika mu 1999. Choncho m’dziko lonse la Mexico munakhazikitsidwa Magulu Omanga Nyumba za Ufumu. Amboni za Yehova ochokera m’madera osiyanasiyana a dzikoli anadzipereka kugwira nawo ntchito yomangayi ndipo ambiri mwa amenewa anali ndi luso la zomangamanga. Padakali pano, ku Mexico kuli magulu omanga okwana 35, ndipo ku Belize kuli gulu limodzi.

Magulu Omanga Nyumba za Ufumu amenewa nthawi zambiri amakhala ndi anthu pafupifupi 8, amuna ndi akazi omwe, amene amagwira ntchito mongodzipereka ndiponso popanda malipiro. Magulu a anthu osangalala amenewa apita m’madera osiyanasiyana m’dzikoli kukatsogolera ntchito yomangayi. Aliyense mwa anthu a m’magulu amenewa amagwira ntchito maola 8 kuyambira Lolemba mpaka Lachisanu ndipo sagwira ntchito masiku ena a Loweruka. Amayamba tsiku lililonse mwa kukambirana lemba la tsiku nthawi ya 7 koloko m’mawa, kenako amadya chakudya cha m’mawa. Aliyense amakhala wofunitsitsa kugwira ntchito iliyonse imene wauzidwa. Mwachitsanzo, azimayi amagwira ntchito zimene amuna amagwira monga kupaka pulasitala, kuika matailosi, ndiponso kupenta.

Anthu a mumpingo umene uli ndi ntchito yomanga Nyumba ya Ufumu amathandiza anthu omangawo powapatsa malo ogona, kuwachapira zovala, ndi kuwaphikira zakudya. Kuwonjezera pa kugwirira limodzi ntchito yomangayi, ogwira ntchitowa amasangalala ndi Mboni za kuderalo pamisonkhano ya Chikhristu ndiponso polalikira ku nyumba ndi nyumba.

Phindu la Kudzipereka

Kodi anthu odziperekawa amaiona bwanji ntchito yawoyi? Daniel, yemwe wakhala akugwira ntchitoyi kwa zaka zoposa zitatu anati: “N’zoona kuti timagwira ntchito kaya kunja kutenthe kapena kuzizire, timadya zakudya zimene sitinazizolowere, timasamukasamuka, timakhala kutali ndi mabanja athu, ndipo kawirikawiri sitikhala ndi zinthu zina zamakono zofunika pamoyo, koma mavuto amenewa si kanthu powayerekezera ndi madalitso amene timakhala nawo.”

Kodi ena mwa madalitsowa ndi otani? Ambiri mwa omanga odziperekawa amaphunzira luso lamakono la zomangamanga. Koma Carlos, yemwe amatsogolera gulu lina lalikulu la anthu ongodziperekawa anatchula phindu lina limene iye waona kukhala lalikulu. Iye anati: “Tsopano tangokhala ngati ndife anthu abanja limodzi la anthu 20. Timadyera pamodzi, kugwirira ntchito limodzi, kuphunzira pamodzi, kupemphera pamodzi ndipo ndife mabwenzi enieni.”

Anthu a m’magulu omangawa amakhalanso paubwenzi weniweni ndi anthu a m’mipingo imene akuithandiza. José yemwe wamanga nawo Nyumba za Ufumu zoposa 100 anati: “Ndimakhala ndi chimwemwe kwabasi kuona anthu Amboni amene tawathandiza kumanga Nyumba ya Ufumu akusangalala kwambiri.” Iye anapitiriza kuti: “Timasangalala kwambiri kuona kuti chikhulupiriro cha ena chimalimba kwambiri chifukwa cha ntchito yochepa imene timachita pomanga Nyumba ya Ufumu.”

N’zodabwitsa Kuona Ntchito Imene Yachitika

Nyumba za Ufumu zimenezi sizikhala zokongola monyanyira. M’malo mwake, n’zoyenerera ndipo zimamangidwa mwachangu komanso zosalira ndalama zambiri. Nyumba za Ufumu zimenezi amazimanga m’njira yosavuta komanso amagwiritsa ntchito zipangizo zopezeka mosavuta. Mwa njira imeneyi, amatha kumaliza kumanga Nyumba ya Ufumu m’milungu 6 yokha.

Pofika mu 2007, mpingo uliwonse wa ku Belize unali ndi Nyumba ya Ufumu yatsopano, ndipo zonse zilipo 17. Ndipo ku Mexico, Nyumba za Ufumu zoposa 1,400 zamangidwa kuyambira mu 1999.

Pakufunikabe Nyumba za Ufumu zochuluka ngakhale kuti zambiri zamangidwa kale. (Mateyo 9:37) Tsopano ku Mexico kuli Mboni zoposa 600,000, ndipo onsewa amasonkhana katatu pamlungu kuti aphunzire Mawu a Mulungu. Choncho, pakufunikabe Nyumba za Ufumu zatsopano pafupifupi 2,000. Ntchito yomangayi ikanakhala kuti ikungodalira mphamvu za anthu okha, sizingatheke kukwaniritsa zimenezi. Koma zomwe zachitika pantchito imeneyi zikusonyeza kuti “zinthu zonse n’zotheka” ndi thandizo la Yehova Mulungu.​—Mateyo 19:26.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 22]

“Amachita Zimene Amanena”

Sikuti ndi anthu a m’mipingo ya Mboni za Yehova okha amene amasangalala ndi ntchito yomanga Nyumba za Ufumu. Mwachitsanzo, pomanga Nyumba ya Ufumu ina m’dziko la Belize, mwamuna wina anauza mkazi wake yemwe ndi wa chipembedzo cha Pentekoste kuti akufuna kuti azidzapemphera ndi Mboni za Yehova zikamaliza kumanga “tchalitchi” chawo. Kodi n’chiyani chinam’chititsa kuti ayambe kufuna kupemphera ndi Mboni za Yehova? Iye anati: “Ndikutha kuona kuti Mulungu ali ndi anthu amenewa. Samenyana akamagwira ntchito limodzi. Ndipo amachita zimene amanena.”

[Chithunzi]

Nyumba ya Ufumu ku Orange Walk, m’dziko la Belize

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 23]

Ntchito ya Padziko Lonse

Magulu Omanga Nyumba za Ufumu akhazikitsidwa m’mayiko okwana 120. Awa ndi ena mwa mayiko ochepa chabe amene anthu ongodzipereka akugwira ntchito imeneyi mosangalala:

Angola, Bolivia, Croatia, Dominican Republic, Ethiopia, Fiji, Ghana, Hong Kong, India, Jamaica, Kazakhstan, Liberia, Moldova, Nigeria, Papua New Guinea, Rwanda, Tuvalu, Ukraine, Venezuela ndi Zambia.

[Zithunzi]

Nyumba ya Ufumu m’mzinda wa Tlaxcala, ku Mexico

Omanga Nyumba za Ufumu ku Mexico

[Chithunzi patsamba 23]

Nyumba ya Ufumu m’mzinda wa Acapulco, ku Mexico