Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zazikulu za M’buku la Luka

Mfundo Zazikulu za M’buku la Luka

Mawu a Yehova Ndi Amoyo

Mfundo Zazikulu za M’buku la Luka

ZIKUONEKA kuti uthenga wabwino wa Mateyo analembera Ayuda ndipo uthenga wabwino wa Maliko analembera anthu omwe sanali Ayuda. Koma uthenga wabwino wa Luka analembera anthu a mitundu yonse. Buku la Luka linalembedwa cha m’ma 56 mpaka 58 C.E., ndipo limafotokoza mwatsatanetsatane nkhani za moyo ndi utumiki wa Yesu.

Luka anali dokotala wachifundo ndi wosamala ndipo ‘anafufuza zinthu zonse mosamala kwambiri kuchokera pachiyambi.’ Iye amafotokoza zinthu zimene zinachitika zaka 35 kuyambira mu 3 B.C.E. mpaka mu 33 C.E. (Luka 1:3) Nkhani zambiri za uthenga wabwino wa Luka sizipezeka m’mabuku ena a uthenga wabwino.

KUCHIYAMBI KWA UTUMIKI WAKE

(Luka 1:1–9:62)

Atafotokoza mwatsatanetsatane za kubadwa kwa Yohane Mbatizi ndiponso kwa Yesu, Luka akutiuza kuti Yohane anayamba utumiki wake m’chaka cha 15 cha ulamuliro wa Kaisara Tiberiyo, kutanthauza kumayambiriro kwa 29 C.E. (Luka 3:1, 2) Yohane anabatiza Yesu chakumapeto kwa chaka chimenecho. (Luka 3:21, 22) Pofika chaka cha 30 C.E., ‘Yesu anabwerera ku Galileya ndipo anayamba kuphunzitsa m’masunagoge awo.’​—Luka 4:14, 15.

Paulendo wake woyamba wokalalikira ku Galileya, Yesu anauza makamu a anthu kuti: “Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu ku mizinda inanso.” (Luka 4:43) Limodzi naye, anatenga Simoni msodzi ndi anzake, ndipo anati: ‘Kuyambira lero muzisodza anthu amoyo.’ (Luka 5:1-11; Mat. 4:18, 19) Atumwi 12 anapita ndi Yesu paulendo wake wachiwiri wokalalikira ku Galileya. (Luka 8:1) Paulendo wake wachitatu, iye anatumiza atumwi 12 “kukalalikira ufumu wa Mulungu ndi kuchiritsa.”​—Luka 9:1, 2.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

1:35—Kodi dzira la Mariya linagwira ntchito kuti iye akhale ndi pathupi? Kuti mwana wa Mariya akhaledi mbadwa ya Abulahamu, Yuda ndi Davide, malinga ndi lonjezo la Mulungu, dzira la Mariya linafunikira kugwira ntchito kuti iye akhale ndi pathupi. (Gen. 22:15, 18; 49:10; 2 Sam. 7:8, 16) Komabe, mzimu woyera wa Yehova ndi umene unagwira ntchito yosamutsira mwa Mariya moyo wangwiro wa Mwana wa Mulungu kuti Mariyayo akhale ndi pathupi. (Mat. 1:18) Zikuoneka kuti zimenezi zinafafaniza kupanda ungwiro kulikonse kumene kunali m’dzira la Mariya ndi kuteteza mwana wosabadwayo ku choipa chilichonse kuyambira pa chiyambi.

1:62—Kodi Zekariya anakhala wosalankhula ndi wogontha? Ayi. Iye anangosiya kulankhula. Anthu ena anamufunsa “mwa kulankhula ndi manja” kuti akufuna kuti dzina la mwana wake likhale ndani. Sikuti iwo anachita zimenezi chifukwa chakuti Zekariya anali wogontha. Iye ayenera kuti anamva zimene mkazi wake ananena zokhudza dzina la mwana wawo. Mwina anthu ena anafunsa Zekariya za nkhaniyi mwa kumulankhula ndi manja. Popeza anangofunikira kuti lilime lake limasuke kuti ayambenso kulankhula, zikusonyeza kuti Zekariya sanasiye kumva.​—Luka 1:13, 18-20, 60-64.

2:1, 2—Kodi mawu akuti ‘kulembetsa m’kaundula koyamba’ akutithandiza bwanji kudziwa chaka chimene Yesu anabadwa? Nthawi imene Kaisara Augusito anali kulamulira, kulembetsa m’kaundula kunachitika kawiri. Koyamba kunachitika mu 2 B.C.E. kukwaniritsa lemba la Danieli 11:20 ndipo kwachiwiri mu 6 kapena 7 C.E. (Mac. 5:37) Kureniyo anali bwanamkubwa wa Suriya panthawi imene kulembetsa konse kuwiriko kunachitika. Zikuoneka kuti iye anakhala bwanamkubwa kawiri. Popeza Luka akunena kuti Yesu anabadwa panthawi ya kulembetsa m’kaundula koyamba, zikutanthauza kuti Yesu anabadwa mu 2 B.C.E.

2:35—Kodi mawu akuti “lupanga lalitali” lidzapyoza moyo wa Mariya anali kutanthauza chiyani? Apa anali kunena za mmene mtima wa Mariya unawawira poona anthu ambiri atamukana Yesu kuti si Mesiya, ndiponso chisoni chimene Mariya anakhala nacho chifukwa cha imfa yowawa ya mwana wake.​—Yoh. 19:25.

9:27, 28—Luka akunena kuti Yesu anasandulika patapita “masiku asanu ndi atatu” kuchokera pamene iye analonjeza ophunzira ake kuti ena a iwo “sadzalawa imfa m’pang’ono pomwe” kufikira atamuona akubwera mu Ufumu wake. Koma Mateyo ndi Maliko amanena kuti panapita “masiku asanu ndi limodzi.” Chifukwa chiyani? (Mat. 17:1; Maliko 9:2) Zikuoneka kuti Luka anawonjezerapo masiku awiri, tsiku limene Yesu anapereka lonjezolo ndi tsiku limene anasandulika.

9:49, 50—Kodi n’chifukwa chiyani Yesu sanaletse mwamuna wina kutulutsa ziwanda, ngakhale kuti mwamunayo sanali kumutsatira? Yesu sanachite zimenezo chifukwa chakuti anali asanakhazikitse mpingo wachikhristu. Choncho, panthawiyo munthu sanali kufunikira kuti azichita kuyenda ndi Yesu kuti asonyeze chikhulupiriro chake mwa Yesu ndi kutulutsa ziwanda.​—Maliko 9:38-40.

Zimene Tikuphunzirapo:

1:32, 33; 2:19, 51. Mariya anasunga mu mtima mwake zochitika ndi mawu amene anakwaniritsa ulosi. Kodi ife timakumbukira zimene Yesu analosera zokhudza “mapeto a dongosolo lino la zinthu” ndi kuyerekeza zimene ananenazo ndi zimene zikuchitika masiku ano?​—Mat. 24:3.

2:37. Chitsanzo cha Anna chikutiphunzitsa kuti tisasiye kulambira Yehova, ‘tizilimbikirabe kupemphera’ ndipo tisasiye “kusonkhana kwathu pamodzi” pamisonkhano yachikhristu.​—Aroma 12:12; Aheb. 10:24, 25.

2:41-50. Pamoyo wake, Yosefe anaika zinthu zauzimu patsogolo ndipo anasamala banja lake mwakuthupi ndi mwauzimu. Mwanjira imeneyi, anapereka chitsanzo chabwino kwa mitu ya mabanja.

4:4. Tisalole tsiku kudutsa popanda kuganizira zinthu zauzimu.

6:40. Mphunzitsi wa Mawu a Mulungu amapereka chitsanzo chabwino kwa ophunzira ake. Iye amachita zimene amalalikira.

8:15. Kuti ‘tisunge mawu ndi kubereka zipatso mwa kupirira,’ tifunikira kumvetsa Mawu a Mulungu, kuzindikira ubwino wake ndi kuwaphunzira. Powerenga Baibulo ndi mabuku olifotokoza, tizipemphera ndi kusinkhasinkha.

MAPETO A UTUMIKI WA YESU

(Luka 10:1–24:53)

Yesu anatumiza anthu ena 70 kuti atsogole kupita ku Yudeya ndi kukalowa m’mizinda ndi malo osiyanasiyana. (Luka 10:1) Iye anayenda “mu mzinda ndi mzinda, komanso mudzi ndi mudzi, kuphunzitsa.”​—Luka 13:22.

Kutatsala masiku asanu kuti Pasika wa mu 33 C.E. ayambe, Yesu analowa mu Yerusalemu atakwera mwana wa bulu. Nthawi inali itakwana yakuti mawu ake kwa ophunzira akwaniritsidwe, akuti: “Mwana wa munthu ayenera kukumana ndi mavuto ambiri, ndipo adzakanidwa ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi. Ndiyeno adzaphedwa, ndi kuukitsidwa tsiku lachitatu.”​—Luka 9:22, 44.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

10:18—Kodi Yesu anali kunena za chiyani pamene anauza ophunzira 70 kuti: “Ndinayamba kuona Satana atagwa kale ngati mphezi kuchokera kumwamba”? Apa Yesu sanali kunena kuti Satana anali atathamangitsidwa kale kumwamba. Zimenezo sizinachitike panthawiyo koma zinachitika Khristu atangokhala Mfumu kumwamba mu 1914. (Chiv. 12:1-10) Ngakhale sitinganene motsimikiza, zikuoneka kuti potchula zochitika za kutsogolozo ngati zinachitika kale, Yesu anali kutsindika mfundo yakuti zidzachitikadi.

14:26—Kodi otsatira a Khristu afunika ‘kudana’ ndi achibale m’njira yotani? Nthawi zina m’Baibulo, “kuda” munthu kapena chinthu, kumatanthauza kukonda munthuyo kapena chinthucho pang’ono, poyerekeza ndi mmene umakondera munthu wina kapena chinthu china. (Gen. 29:30, 31) Akhristu afunika ‘kudana’ ndi achibale mwa kuwakonda pang’ono poyerekeza ndi mmene amakondera Yesu.​—Mat. 10:37.

17:34-37—Kodi “ziwombankhanga” ndani, ndipo “chinthu chakufa,” kapena kuti thupi limene amasonkhanako, n’chiyani? Pano anthu amene “adzatengedwa,” kapena kuti amene adzapulumuka, akuwayerekeza ndi ziwombankhanga zimene zimaona patali. Thupi limene amasonkhanako ndi Khristu weniweni panthawi ya kukhalapo kwake komanso chakudya chauzimu chimene Yehova amawakonzera.​—Mat. 24:28.

22:44—Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anazunzika koopsa? Pali zifukwa zingapo. Yesu anali ndi nkhawa ya mmene imfa yake monga mpandu inakhudzira Yehova Mulungu ndi dzina Lake. Ndiponso, Yesu anali kudziwa bwino lomwe kuti moyo wake wosatha ndi tsogolo la anthu onse, zinadalira kukhulupirika kwake.

23:44—Kodi mdima wa maola atatuwo unachitika chifukwa cha kadamsana? Ayi si choncho. Kadamsana amachitika nthawi imene mwezi wangokhala kumene, osati uli wathunthu, ngati mmene umakhalira nthawi ya Pasika. Mdima umene unakhalako tsiku limene Yesu anamwalira, unali chozizwitsa chimene Mulungu anachita.

Zimene Tikuphunzirapo:

11:1-4. Tikayerekeza malangizo amenewa ndi mawu osiyana pang’ono a m’pemphero lachitsanzo, limene linaperekedwa miyezi 18 m’mbuyomo, timapeza mfundo yakuti mapemphero athu asakhale ongobwereza mawu akutiakuti.​—Mat. 6:9-13.

11:5, 13. Ngakhale kuti Yehova ndi wokonzeka kuyankha mapemphero athu, tifunika kukhala akhama popemphera.​—1 Yoh. 5:14.

11:27, 28. Munthu amapeza chisangalalo chenicheni akamachita chifuniro cha Mulungu mokhulupirika, osati chifukwa cha chibale kapena chuma ayi.

11:41. Mtima wachikondi ndi wodzipereka ndi umene uyenera kutilimbikitsa kupereka mphatso za chifundo.

12:47, 48. Munthu amene ali ndi udindo waukulu koma amalephera kuusamala, amakhala ndi mlandu waukulu kuposa munthu amene sakudziwa udindo wake kapena kuumvetsa bwinobwino.

14:28, 29. Si nzeru kufuna zinthu zimene sitingakwanitse.

22:36-38. Yesu sanauze ophunzira ake kunyamula chida kuti adziteteze. Komabe, malupanga amene iwo anali nawo pamene iye anali kuperekedwa usiku, anathandiza kuti Yesu awaphunzitse mfundo yofunika kwambiri yakuti: “Onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.”​—Mat. 26:52.

[Chithunzi patsamba 31]

Yosefe anapereka chitsanzo chabwino cha mutu wa banja

[Chithunzi patsamba 32]

Luka analemba nkhani zambiri zokhudza moyo ndi utumiki wa Yesu kuposa anzake