Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Amene Amaona Kuti Ndife Ofunika Kwambiri

Amene Amaona Kuti Ndife Ofunika Kwambiri

Yandikirani Mulungu

Amene Amaona Kuti Ndife Ofunika Kwambiri

Luka 12:6, 7

BAIBULO limati nthawi zina ‘mtima wathu umatitsutsa.’ Zimenezi zikutanthauza kuti mtima wathu ungatichititse kuti tizidziona ngati ndife anthu osafunika, oti Mulungu sangatikonde ndi kutisamalira. Koma Baibulo limatitsimikizira kuti “Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziwa zonse.” (1 Yohane 3:19, 20) Iye amatidziwa bwino kwambiri kuposa mmene ife timadzidziwira. Amationa mosiyana kwambiri ndi mmene ifeyo timaganizira. Koma n’chifukwa chiyani Yehova Mulungu amationa kuti ndife ofunika kwambiri? Yankho la funso limeneli tingalipeze m’fanizo logwira mtima limene Yesu anafotokoza panthawi ziwiri zosiyana.

Panthawi yoyamba, Yesu anati: ‘Mpheta ziwiri amazigulitsa kakobili kamodzi kochepa mphamvu.’ (Mateyo 10:29, 31) Malinga ndi Luka 12:6, 7, Yesu anatinso: “Mpheta zisanu amazigulitsa makobili awiri ochepa mphamvu, si choncho nanga? Komatu palibe ngakhale imodzi mwa izo imaiwalika kwa Mulungu. . . . Musachite mantha; ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zambiri.” Fanizo logwira mtima limeneli likutiphunzitsa mmene Yehova amaonera atumiki ake.

Mpheta zinali mbalame zotsika mtengo kwambiri zomwe zinkagulitsidwa monga ndiwo. Ndipo n’kutheka kuti Yesu anali ataonapo azimayi osauka, ngakhale amayi ake amene, akugula timbalame timeneti pamsika kuti akadye ku nyumba kwawo. Kakobili kamodzi kochepetsetsa kwambiri ankagulira mpheta ziwiri. Mbalame zimenezi zinali zotsika mtengo kwambiri moti timakobili tiwiri amagulira osati mpheta zinayi koma zisanu, ndipo mpheta inayo amangoikapo ngati yaulere.

Yesu anafotokoza kuti palibe mpheta ngakhale imodzi imene “imaiwalika kwa Mulungu” kapena “imene idzagwa pansi Atate” osadziwa. (Mateyo 10:29) Yehova amaona mpheta iliyonse ngakhale ikagwa pansi kaya chifukwa choti yavulala kapena ikufunafuna chakudya. Timbalame tomwe Yehova anatilenga ndiponso tomwe tingaoneke ngati tachabechabe, ndi tofunika kwambiri kwa iye ndipo samatiiwala. Iye amationa kuti ndi tamtengo wapatali. Kodi mukuona mfundo yofunika kwambiri m’fanizo la Yesu limeneli?

Nthawi zambiri pophunzitsa, Yesu anali kugwiritsa ntchito mafanizo a zinthu zing’onozing’ono pofuna kuphunzitsa mfundo yaikulu. Mwachitsanzo, iye ananenanso kuti: “Makwangwala, iwo safesa mbewu kapena kukolola, alibe nyumba yosungiramo zinthu kapena nkhokwe, komatu Mulungu amawadyetsa. Kodi inu si ofunika kwambiri kuposa mbalame nanga?” (Luka 12:24) Fanizo limeneli linathandiza kuti anthu amvetse bwino mawu a Yesu onena za mpheta. Ngati Yehova amasamalira timbalame timeneti, kuli bwanji anthu amene amam’konda ndi kum’lambira?

Malinga ndi zimene Yesu ananenazi, si bwino kudziona ngati ndife anthu osafunika oti Mulungu, yemwe ndi “wamkulu kuposa mitima yathu,” sangatisamalire. N’zolimbikitsa kwabasi kudziwa kuti Mlengi wathu amaona mwa ife zinthu zimene ifeyo sitingazione.

[Mawu a Chithunzi patsamba 9]

Sparrows: © ARCO/​D. Usher/​age fotostock