Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulimbikitsa Odwala Amene Ali ndi Matenda Oti Afa Nawo

Kulimbikitsa Odwala Amene Ali ndi Matenda Oti Afa Nawo

Kulimbikitsa Odwala Amene Ali ndi Matenda Oti Afa Nawo

“Sindinakhulupirire nditamva kuti mayi anga ali ndi matenda oti afa nawo. Ndinasokonezeka maganizo kwambiri ndipo zinandivuta kuvomereza kuti akhoza kumwalira nthawi ina iliyonse.”​—Anatero Grace, wa ku Canada.

MUNTHU akapezeka ndi matenda oti afa nawo, achibale ndiponso anzake amavutika maganizo kwambiri ndipo angasowe chochita. Ena sadziwa ngati akufunikira kumuuza wodwalayo zoona zenizeni zokhudza vuto lakelo. Ndipo ena amaona kuti angavutike kuona mnzawoyo akuzunzika ndi matendawo ndipo mwinanso kufika polephera kudzichitira yekha zinthu zina. Ambiri amada nkhawa kuti adzasowa chonena kapena chochita munthuyo akatsala pang’ono kumwalira.

Ngati mnzanu kapena wachibale wapezeka ndi matenda oti afa nawo, kodi zimene mungachite zingakukhudzeni bwanji inuyo komanso wodwalayo? Ndipo mungasonyeze bwanji kuti ndinu “bwenzi” lake lenileni n’kumulimbikitsa ndiponso kum’thandiza panthawi yovuta imeneyi?​—Miyambo 17:17.

Mwachibadwa Timamva Chisoni

Aliyense amasokonezeka maganizo munthu amene amam’konda akadwala matenda aakulu. Nawonso madokotala, nthawi zambiri amavutika kusamalira ndiponso kulimbikitsa odwala amene ali ndi matenda oti afa nawo. Izi zimachitika ngakhale kuti kwa iwo si zachilendo kuona munthu akufa ndiponso kulankhula ndi anthu nkhani yokhudza imfa.

N’kutheka kuti nanunso mumavutika maganizo kwambiri mukaona munthu amene mumam’konda akudwala. Mayi wina yemwe amakhala ku Brazil dzina lake Hosa, yemwe mng’ono wake anadwala matenda aakulu anati: “N’zopweteka kwambiri kuona munthu amene umam’konda akuvutika kwa nthawi yaitali.” Nayenso Mose, yemwe anali munthu wokhulupirika, ataona kuti mlongo wake wakanthidwa ndi khate anachonderera Mulungu kuti: “M’chiritsenitu, Mulungu.”​—Numeri 12:12, 13.

Chifukwa chakuti tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu wathu wachifundo, Yehova, anthufe timamva chisoni kuona munthu amene timam’konda akuzunzika ndi matenda. (Genesis 1:27; Yesaya 63:9) Kodi Yehova amamva bwanji akamaona anthu akuvutika? Taonani zimene Yesu, yemwe anatengera kwambiri khalidwe la Atate, wake anachita. (Yohane 14:9) Ataona anthu odwala, iye “anagwidwa chifundo.” (Maliko 1:40, 41; Mateyo 20:29-34) Monga momwe tafotokozera m’nkhani yapitayi, Yesu anakhudzidwa kwambiri panthawi ya maliro a mnzake Lazaro, ataona chisoni chimene achibale ndiponso anzake a Lazaroyo anali nacho. Iye anamva chisoni kwambiri ndipo “anagwetsa misozi.” (Yohane 11:32-35) Baibulo limalongosola kuti imfa ndi mdani ndipo limalonjeza kuti posachedwapa matenda ndiponso imfa zidzatha.​—1 Akorinto 15:26; Chivumbulutso 21:3, 4.

N’zomveka kuti mwina mungamaimbe mlandu munthu wina chifukwa choti munthu amene mumam’konda akudwala kwambiri. Komabe, Dr. Marta Ortiz, amene pomaliza maphunziro ake a ku yunivesite analemba nkhani yokhudza kusamalira anthu odwala kwambiri, anapereka malangizo awa: “Musadziimbe mlandu kapena kuimba mlandu anthu ena, monga madokotala ndi manesi chifukwa cha mmene wodwalayo alili. Kuimba mlandu anthu ena kungathe kuwononga ubwenzi wanu ndi anthu enawo ndiponso kukulepheretsani kuganizira zimene wodwalayo akufunikira kwambiri.” Kodi mungachite chiyani kuti muthandize wodwalayo kupirira matenda akewo ndiponso kum’thandiza kuti avomereze zoti angathe kumwalira?

Ganizirani za Munthuyo Osati Matenda Akewo

Chinthu choyamba chimene mungachite ndicho kupewa kumangoganizira za mmene munthuyo akuonekera chifukwa cha matenda akewo. M’malo mwake muziganizira kwambiri za munthu weniweniyo. Kodi mungachite motani zimenezi? Sarah yemwe ndi nesi ananena kuti: “Ndimapatula nthawi yoona zithunzi zimene wodwalayo anajambulitsa adakali wathanzi. Ndimamvetsera bwinobwino akamandifotokozera zimene ankachita kale. Izi zimandithandiza kuganizira za mmene moyo wake unalili kale, osati kumangoganizira za mmene alili panopa.”

Nesi winanso, dzina lake Anne-Catherine, anafotokoza zimene amachita kuti asamangoganizira za mmene wodwala akuonekera. Iye anati: “Ndimamuyang’ana m’maso wodwalayo, n’kuyesetsa kuganizira zimene ndingachite kuti ndim’thandize.” Buku lina lofotokoza mmene tingalimbikitsire wodwala amene watsala pang’ono kumwalira limati: “Anthu ambiri amathedwa nzeru akaona munthu amene amam’konda atasintha chifukwa cha matenda kapena ngozi. Panthawi yotereyi, chinthu chabwino kwambiri chimene tingachite ndicho kumuyang’anitsitsa m’maso wodwalayo. Popeza kuti maso sasintha, tingathe kuganizira bwino za munthuyo osati za matenda akewo.”​—The Needs of the Dying​—A Guide for Bringing Hope, Comfort, and Love to Life’s Final Chapter.

N’zoona kuti m’pofunika kukhala odziletsa ndiponso kuchita khama kwambiri kuti tithe kuona zinthu motere. Georges, yemwe ndi mkulu mumpingo wa Mboni za Yehova ndipo nthawi zambiri amachezera odwala matenda oti afa nawo, anafotokoza izi: “Kuti tithandize wodwalayo, tiyenera kum’konda kwambiri, m’malo modera nkhawa kwambiri za matenda akewo.” Mukamaganizira kwambiri za wodwalayo, osati matenda akewo, nonse awiri mumapindula. Yvonne amene anasamalirapo ana odwala matenda a khansa anati: “Munthu ukamazindikira kuti ungathandize odwalawo kuti azipatsidwabe ulemu zimakuthandiza kuti uyesetse kulimbana ndi matenda awowo.”

Khalani Wokonzeka Kuwamvetsera

Anthu nthawi zina safuna kulankhula ndi munthu yemwe watsala pang’ono kumwalira ngakhale kuti amam’konda kwambiri. Chifukwa chiyani amatero? Amada nkhawa kuti angasowe chonena. Komabe, Anne-Catherine, yemwe posachedwapa anasamalira mnzake yemwe ankadwala matenda aakulu kwambiri, anafotokozapo kuti tingathe kulimbikitsa wodwala ngakhale kuti sitingalankhulepo chilichonse. Iye anati: “Timalimbikitsa wodwala kudzera mu zomwe timanena ndiponso zimene timachita. Kukhala naye pafupi, ndi kugwirana naye dzanja ndiponso kusonyeza mmene takhudzidwira mwa kugwetsa misozi, zimasonyeza kuti tikumuganizira wodwalayo.”

Mwina munthu yemwe akudwalayo angafune kufotokoza zakukhosi kwake. Komabe, nthawi zambiri iye amadziwa kuti anthu ena amakhala ndi nkhawa ndipo safuna kukambirana naye nkhani zikuluzikulu zokhudza iyeyo. Nthawi zina, nawonso anzake ngakhalenso achibale ake angaganize kuti akuchita bwino kusakambirana naye nkhani zimene iye zikum’detsa nkhawa, ndipo mwinanso kum’bisira zinthu zofunika kwambiri zokhudza matenda akewo. Kodi kuchita zimenezi kuli ndi mavuto otani? Dokotala wina amene amathandiza anthu omwe akudwala matenda oti afa nawo, anafotokoza kuti zimenezi “zimawonongetsa nyonga zimene mukanazigwiritsira ntchito pochita zinthu zofunika kwambiri, monga kufotokozera ena za matendawo ndiponso kufunafuna chithandizo.” Choncho, ngati wodwalayo akufuna, muloleni kuti afotokoze zakukhosi kwake pankhani ya matenda akewo.

Atumiki ena akale a Mulungu akadwala, ankafotokozera Yehova Mulungu nkhawa zawo. Mwachitsanzo, Mfumu Hezekiya ali ndi zaka 39 anadziwa kuti watsala pang’ono kufa. Iye anafotokozera Yehova mmene zimenezi zinam’pwetekera mumtima. (Yesaya 38:9-12, 18-20) Nawonso anthu amene adwala matenda oti afa nawo aziloledwa kufotokoza chisoni chimene ali nacho imfa yawo ikayandikira. N’kutheka kuti ndi okhumudwa chifukwa chakuti tsopano akuona kuti sakwaniritsa zolinga zimene anali nazo, monga kukacheza ku malo osiyanasiyana, kukhala ndi ana, kudzaona zidzukulu zawo zikukula kapena kuchita zonse zomwe angathe potumikira Mulungu. Mwina ali ndi mantha poganiza kuti anzawo kapena achibale awo aziwapewa chifukwa choti sakudziwa zimene ayenera kuwachitira. (Yobu 19:16-18) N’kuthekanso kuti ndi othedwa nzeru poganizira zoti azunzika ndi matenda ndipo adzafika pomangodziipitsira kapena kufa kumene.

Anne-Catherine anati: “Ndi bwino kwambiri kuti muzilola wodwalayo kufotokoza zakukhosi kwake, popanda kum’dula mawu, kumuweruza kapena kumuuza kuti palibe chifukwa chodera nkhawa. Imeneyi ndi njira yabwino kwambiri yodziwira maganizo ake, zimene zikum’detsa nkhawa ndiponso zimene akuyembekezera.”

Dziwani Zimene Akufunikira Kwambiri

Poganizira za ululu umene mnzanuyo akumva, womwe mwina wawonjezeka chifukwa cha mankhwala omwe akulandira, n’kutheka kuti mungasokonezeke maganizo kwambiri. Zimenezi mwina zingakuchititseni kufika poiwala chimene wodwalayo akufunikira kwambiri, chomwe ndi kudzisankhira yekha zochita.

Malinga ndi zikhalidwe zina, achibale angayese kuteteza wodwalayo mwa kusamuuza zoona pa matenda akewo, mwinanso kufika mpaka pom’patula pamene akukambirana za chithandizo chimene iye angapatsidwe. Zikhalidwe zina zili ndi vuto lina losiyana ndi limeneli. Mwachitsanzo, Jerry yemwe ndi nesi anati: “Nthawi zina anthu odzaona wodwala amakonda kukambirana za wodwalayo ataimirira pafupi ndi bedi lake. Ndipo amangokambirana okha ngati kuti wodwalayo palibepo.” Zochitika zonsezi zimachotsera ulemu wodwalayo.

Chinthu china chimene wodwala amafunikira kwambiri ndicho kukhala ndi chiyembekezo. M’mayiko amene n’zotheka kulandira chithandizo chabwino kwambiri chamankhwala, nthawi zambiri wodwala amakhala ndi chiyembekezo poganizira kuti adzapeza chithandizo champhamvu kwambiri. Michelle, yemwe anathandiza mayi ake amene adwala matenda a khansa maulendo atatu, anati: “Amayi akafuna kuyesa mtundu wina wa mankhwala kapena kuonana ndi dokotala wina, ndimawathandiza kufufuza zimenezo. Panopa ndimaona kuti ndisamayembekezere kuti achira mwadzidzidzi komabe ndi bwino kuti ndizilankhula zolimbikitsa.”

Koma bwanji ngati palibe chiyembekezo chilichonse choti n’kupeza chithandizo? Kumbukirani kuti wodwalayo amafunika kukhala womasuka kukambirana ndi anthu za imfa yake. Georges, amene tam’tchula kale uja anati: “Ndi bwino kusam’bisira zoti imfa yake yayandikira. Kuchita zimenezi kumathandiza wodwalayo kukonzekera imfa yake komanso kukonzeratu mmene zinthu zidzakhalire iyeyo akamwalira.” Chifukwa choona kuti wachita zonse zimene amafunikira kuchita, mtima wa wodwalayo ungakhale m’malo ndiponso sangakhale ndi nkhawa yoti asiyira anthu ena mavuto.

N’zoona kuti mwachibadwa kukambirana nkhani zoterezi n’kovuta. Komabe kumasukirana motere kungakupatseni mwayi wamtengo wapatali kwambiri wofotokozerana zakukhosi. Mwina wodwalayo angafune kuthetsa kusiyana maganizo kumene kunalipo pakati panu, kukupepesani kapena kukupemphani kuti mum’khululukire. Kukambirana kotereku kungakuthandizeni kuti mugwirizane kwambiri ndi munthuyo.

Kulimbikitsa Wodwala Amene Watsala Pang’ono Kumwalira

Kodi mungalimbikitse motani wodwala amene watsala pang’ono kumwalira? Dr. Ortiz, amene tam’tchula chakumayambiriro kwa nkhani ino anati: “Muloleni wodwalayo kuti anene zinthu zomaliza zimene akufuna kuti mumuchitire. M’mvetsereni mwatcheru. Ngati n’zotheka, yesetsani kuchita zimene akufunazo. Ngati mukuona kuti n’zosatheka kuchita zimene akufunazo, musam’bisire zimenezo.”

Mwina, kusiyana ndi m’mbuyo monsemo, wodwalayo angafune kulankhulana ndi anthu amene amaona kuti ndi ofunika kwambiri pamoyo wake. Georges anati: “Thandizani wodwalayo kupeza anthu amenewo, ngakhale kuti mwina sangalankhule nawo kwambiri chifukwa chosowa mphamvu.” Ngakhale atangolankhulana patelefoni, zimenezo zingawathandize kuti alimbikitsane ndiponso kuti apempherere limodzi. Christina, yemwe amakhala ku Canada, ananena zotsatirazi anthu atatu omwe anali kuwakonda atamwalira motsatizana: “Pamene imfa yawo inkayandikira kwambiri, iwo anali kudalira kwambiri mapemphero a abale awo achikhristu.”

Kodi ndi bwino kulira pamaso pa munthu amene mumam’kondayo? Inde. Mukamalira, mumapatsa mwayi mnzanu amene watsala pang’ono kumwalirayo woti akulimbikitseni. Buku lofotokoza mmene tingalimbikitsire wodwala amene watsala pang’ono kumwalira lija limati: “Kulimbikitsidwa ndi munthu amene watsala pang’ono kumwalira kumakhudza mtima kwambiri. Ndipo zingakhale zothandiza kwambiri kwa munthu amene akudwalayo.” Mwa kulimbikitsa ena, munthu amene wakhala akusamalidwa kwambiriyo amakhala ndi mwayi wodzionanso monga bwenzi, tate kapena mayi wachikondi kwambiri.

M’pomveka kuti nthawi zina sizingatheke kukhala limodzi ndi munthu amene mumam’kondayo pamene watsala pang’ono kumwalira. Komabe, ngati n’zotheka kutero, kaya ndi kuchipatala kapena kunyumba, yesetsani kum’gwira dzanja mpaka pamene watsirizika. Panthawi yotereyi mungakhale ndi mwayi wolankhula zinthu zimene simulankhula kawirikawiri. Ngakhale kuti panthawiyi wodwalayo mwina sangachite chilichonse, musalole kuti zimenezo zikulepheretseni kutsanzikana naye, ndiponso kumusonyeza chikondi ngakhalenso chiyembekezo chodzaonana nayenso ataukitsidwa.​—Yobu 14:14, 15; Machitidwe 24:15.

Mosakayikira, ngati mutayesetsa kugwiritsa ntchito bwino nthawi yotereyi, mungapewe kudzanong’oneza bondo m’tsogolo. Komanso, n’kutheka kuti m’tsogolo mwake zochitika panthawi yotereyi, zimene kawirikawiri zimakhudza mtima kwambiri, zingadzakulimbikitseni. Mukamadzaganizira zimene munachita, polimbikitsa wodwalayo, mudzaona kuti munali bwenzi lenileni panthawi ya ‘tsokalo.’​—Miyambo 17:17.

[Mawu Otsindika patsamba 27]

Kuganizira kwambiri za munthuyo, osati matenda akewo, kumapindulitsa nonse awiri

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 29]

Njira Yolemekezera Ufulu wa Wodwala

M’mayiko ambiri, anthu akuyesetsa kulemekeza ufulu wa munthu amene akudwala matenda oti afa nawo. Iye ali ndi ufulu wofa mwamtendere ndiponso mwaulemu. Wodwalayo amayenera kulemberatu chikalata chofotokoza zofuna zake, ndipo zimenezi zimathandiza kuti ufulu wake ulemekezedwe ndiponso kuti aloledwe kukafera kunyumba kapena kumalo osamalirira odwala.

Chikalata choterechi chingathandize m’njira izi:

• Kuti pakhale kulankhulana momasuka pakati pa madokotala ndi achibale a wodwalayo

• Kuti wodwalayo adzisankhire yekha chithandizo chimene angalandire m’malo moti achibale ake ndiwo achite zimenezi

• Kuti wodwalayo asapatsidwe chithandizo chimene sakufuna, chomwe chilibe phindu kwa iyeyo, chopweteka kwambiri, chofuna ndalama zambiri

Kuti chikalatachi chizigwira ntchito bwino chiyenera kukhala ndi izi:

• Dzina la munthu wokuimirani pa za thandizo la mankhwala

• Chithandizo chimene mungalole kapena kukana ngati zaonekeratu kuti simuchira

• Dzina la dokotala amene akudziwa zosankha zanuzo, ngati n’zotheka kutero

[Chithunzi patsamba 26]

Ganizirani za mmene moyo wa wodwalayo unalili kale, osati za mmene alili panopa