Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Masoka Achilengedwe Ndi Chilango Chochokera kwa Mulungu?

Kodi Masoka Achilengedwe Ndi Chilango Chochokera kwa Mulungu?

Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi Masoka Achilengedwe Ndi Chilango Chochokera kwa Mulungu?

Mulungu salanga anthu pogwiritsa ntchito masoka achilengedwe. Iye sanalangepo ndipo sadzalanga anthu ndi masoka achilengedwe. N’chifukwa chiyani tikutero? N’chifukwa choti pa lemba la 1 Yohane 4:8, Baibulo limati: “Mulungu ndiye chikondi.”

Zonse zimene Mulungu amachita, amazichita chifukwa cha chikondi. Chikondi sichichititsa kuti anthu osalakwa avulazidwe. Ndipo Baibulo limati, “chikondi sichikuchititsa zoipa kwa mnansi wako.” (Aroma 13:10) Komanso palemba la Yobu 34:12, Baibulo limati: “Ndithu zoonadi, Mulungu sangachite choipa.”

N’zoona kuti Baibulo linalosera kuti masiku ano kuzichitika masoka monga “zivomezi zamphamvu.” (Luka 21:11) Koma sitinganene kuti Yehova ndiye amachititsa kuti zinthu ziwonongeke ndi masokawa monganso mmene zilili kuti katswiri woona zanyengo si amene amachititsa kuti zinthu ziwonongeke ndi mphepo yamkuntho. Popeza kuti si Mulungu amene amachititsa kuti anthu azivutika ndi masoka achilengedwe, kodi ndani amene amawachititsa?

Baibulo limanena kuti: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo,” amene ndi Satana Mdyerekezi. (1 Yohane 5:19) Iye wakhala akupha anthu kungoyambira pamene anagalukira Mulungu, anthu atangolengedwa kumene, mpaka pano. (Yohane 8:44) Satana sawerenga za moyo wa anthu m’pang’ono pomwe. Iye amachita zinthu modzikonda, motero n’zosadabwitsa kuti anthu ambiri padziko lonse ndi odzikonda. Anthu masiku ano akuponderezana kwambiri mpaka kufika pochititsa anthu oponderezedwawo kukakhala m’malo oopsa amene mungachitike masoka achilengedwe kapena masoka amene amayambika chifukwa cha zochita za anthu. (Aefeso 2:2; 1 Yohane 2:16) Motero anthu adyera ndi omwe amachititsa ena mwa mavuto amene anthu amakumana nawo. (Mlaliki 8:9) Kodi amachita motani zimenezi?

Pali masoka ambiri ndithu amene amachitika chifukwa cha zochita za anthu. Mwachitsanzo, taganizirani za mavuto amene anthu okhala mu mzinda wa New Orleans, ku United States anakumana nawo madzi atasefukira. Taganiziraninso za mavuto amene anthu okhala m’mphepete mwa mapiri a m’mbali mwa nyanja m’dziko la Venezuela anakumana nawo nyumba zawo zitakokoloka ndi matope. M’zitsanzo zimenezi ndi zinanso, zochitika zachilengedwe monga mphepo ndi mvula, zinawononga zinthu makamaka chifukwa choti anthu sankadziwa bwino za nyengo, anamanga nyumba mosasamala, analibe mapulani olongosoka, sanamvere chenjezo ndiponso chifukwa choti aboma sanayendetse bwino zinthu.

Taganiziraninso za tsoka linalake lotchulidwa m’Baibulo. M’nthawi ya Yesu, nsanja ina inagwa mwadzidzidzi n’kupha anthu 18. (Luka 13:4) Tsoka limeneli linachitika osati chifukwa choti Mulungu anafuna kulanga anthuwo. Koma n’kutheka kuti nsanjayo inagwa chifukwa cha vuto lina limene anachititsa ndi anthu, kapena chifukwa cha ‘zotigwera’ mwadzidzidzi kapenanso tsokali linachitika chifukwa cha zonse ziwirizi.​—Mlaliki 9:11.

Kodi Mulungu anayamba wachititsapo masoka alionse? Inde, komabe mosiyana ndi masoka amene amachitika chifukwa cha zochita za anthu, masoka amene Mulungu anachititsa sankawononga aliyense, ankakhala ndi cholinga ndipo sankachitika kawirikawiri. Zitsanzo za masoka amenewa ndi Chigumula cha m’nthawi ya Nowa chimene chinachitika padziko lonse, ndiponso kuwonongedwa kwa mizinda ya Sodomu ndi Gomora m’nthawi ya Loti. (Genesis 6:7-9, 13; 18:20-32; 19:24) Masoka amenewa anawononga anthu onse omwe sankafuna kulapa, koma sanawononge anthu olungama.

Yehova Mulungu adzathetsa mavuto onse omwe amachitika chifukwa cha masoka achilengedwe. Iye ali ndi mphamvu zochitira zimenezi ndipo akufunitsitsa kutero. Ndipotu lemba la Salmo 72:12 linalosera kuti Yesu Khristu yemwe ndi Mfumu yoikidwa ndi Mulungu, “adzapulumutsa waumphawi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi.”