Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Munthu Amene Mumam’konda Akamwalira

Munthu Amene Mumam’konda Akamwalira

Munthu Amene Mumam’konda Akamwalira

Lachiwiri, pa July 17, 2007, cha m’ma 7 koloko madzulo, ndege yonyamula anthu inasiya msewu wake pabwalo la ndege la mu mzinda wa São Paulo, lomwe ndi lalikulu kwambiri ku Brazil. Ndegeyo inakadutsa msewu wina waukulu wa magalimoto n’kukaomba nyumba zina zofikira katundu. Ndipo anthu pafupifupi 200 anafa pangoziyi.

NGOZIYI, yomwe akuti ndi yoopsa kwambiri pangozi zonse za ndege zomwe zachitikapo ku Brazil, sidzaiwalika makamaka kwa anthu amene panafa abale ndi anansi awo. Claudete ndi mmodzi mwa anthu amenewa ndipo iye anali akuonera TV panthawi yomwe anamva za ngoziyi. Mwana wake wamwamuna Renato, anali m’ndegeyo. Renato anali ndi zaka 26 ndipo anali atakonza zokwatira m’mwezi wa October. Atamva za ngoziyi, Claudete anayesayesa kuimbira mwana wakeyo foni yam’manja, koma sanayankhe. Kenako mayiyu anagwa pansi n’kuyamba kulira kwambiri.

Mnyamata yemwe anali pachibwenzi ndi Antje anamwalira pa ngozi ya galimoto mu January 1986. Mtsikanayu atangouzidwa za ngoziyi, anangoti kakasi. Iye anati: “Nditamva za ngoziyi, sindinakhulupirire. Ndinkangoona ngati ndikulota. Ndinanjenjemera kwambiri ndipo ndinamva kupweteka ngati kuti wina wandimenya m’mimbamu.” Antje anavutika maganizo kwambiri kwa zaka zitatu zotsatira. Ngakhale kuti tsopano padutsa zaka zoposa 20 chichitikireni zimenezi, iye amanjenjemerabe akakumbukira za ngoziyo.

N’zovuta kufotokoza mmene munthu amamvera, munthu amene amam’konda akamwalira mwadzidzidzi. Komabe, ngakhale munthu atamwalira pambuyo podwala nthawi yaitali, anthu amene ankamukonda amamvabe chisoni kwambiri. Palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene amakonzekera bwinobwino za imfa ya m’bale kapena mnansi wake. Mwachitsanzo, amayi ake a Nanci atamwalira mu 2002, iye anathedwa nzeru kwambiri n’kungokhala pansi m’chipatala momwe amayi akewo anamwalirira. Anachita izi ngakhale kuti amayi akewo anali atadwala nthawi yaitali. Nanci ankangoona kuti moyo wake wasokonezekeratu. Ngakhale kuti tsopano padutsa zaka zoposa zisanu, iye amalirabe akakumbukira za amayi akewo.

Dr. Holly G. Prigerson anati: “Anthu sangaiwale imfa ya munthu amene amam’konda, koma amangoipirira.” Ngati munthu amene munali kumukonda anamwalira, kaya mwadzidzidzi kapena ayi, mwina munadzifunsapo kuti: ‘Kodi anthu enanso amamva chisoni ngati mmene ndikumvera inemu? Kodi ndingatani kuti ndipirire imfa ya munthu ameneyu? Kodi ndidzaonana nayenso?’ Nkhani yotsatirayi iyankha mafunso amenewa ndi enanso amene mungakhale nawo.

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

EVERTON DE FREITAS/​AFP/​Getty Images