Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ndinetu Mdzakazi wa Yehova!”

“Ndinetu Mdzakazi wa Yehova!”

Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo

“Ndinetu Mdzakazi wa Yehova!”

MARIYA anayang’ana modabwa kwambiri pamene mlendo ankalowa m’nyumba yawo. Mlendoyu sanabwerere makolo ake, koma anabwerera iyeyo. Ndipo Mariya ankadziwa bwino ndithu kuti mlendoyu sanali wa mumzinda womwewo wa Nazareti. Popeza kuti mzindawu unali waung’ono, zinali zosavuta kuzindikira munthu aliyense. Koma mlendo uyu anali wosiyana kwambiri ndi anthu. Zimene mlendoyo anauza Mariya poyamba kulankhula naye, zinali zachilendo kwambiri. Mlendoyo anati: “Mtendere ukhale nawe, wodalitsika koposatu iwe, Yehova ali nawe.”​—Luka 1:28.

Umu ndi mmene Baibulo limayambira kutiuza za Mariya, mwana wa Heli, yemwe ankakhala mu mzinda wa Nazareti ku Galileya. Panthawi imeneyi n’kuti Mariya akufunika kusankha chochita pankhani zofunika kwambiri zokhudza moyo wake wonse. Iye anali pachibwenzi ndi mmisiri wa matabwa Yosefe, yemwe sanali munthu wolemera koma anali wokhulupirika kwa Mulungu. Choncho, Mariya anali atakonzeratu za mmene moyo wake udzakhalire m’tsogolo. Iye anali kudzakhala moyo wosalira zambiri ndiponso wothandiza mwamuna wake Yosefe polera ana awo. Koma mosayembekezereka, iye anachezeredwa ndi mngelo amene anamuuza uthenga wa ntchito imene Mulungu anafuna kum’patsa. Ntchito imeneyi inali kudzasintha moyo wake wonse.

Mwina mungadabwe kudziwa kuti Baibulo silitiuza zambiri zokhudza Mariya. Silinena zambiri za mmene analeredwera ndiponso makhalidwe ake, ndipo silinena chilichonse chokhudza maonekedwe ake. Komabe, zimene Mawu a Mulungu amanena za iye zimatithandiza kudziwa zambiri za moyo wake.

Kuti tidziwe bwino za Mariya, tiyenera kuiwala kaye zikhulupiriro zambirimbiri zongopeka zimene zipembedzo zosiyanasiyana zimaphunzitsa. Motero, tiyeni tichotse m’maganizo mwathu zithunzi ndi ziboliboli zonse za Mariya. Komanso, tichotse m’maganizo mwathu zinthu zovuta kumvetsa zimene zipembedzo zimaphunzitsa zokhudza mayi ameneyu, zomwe zachititsa kuti apatsidwe mayina monga “Mayi wa Mulungu” ndiponso “Mfumukazi Yakumwamba.” M’malo mwake, tiyeni tione zimene Baibulo limanena. Zimenezi zingatithandize kumvetsa chikhulupiriro chake ndiponso zimene tingachite pomutsanzira.

Mngelo Achezera Mariya

Mwina mukudziwa kuti mlendo wa Mariyayu sanali munthu wamba koma anali mngelo Gabiriyele. Iye anatchula Mariya kuti ‘wodalitsika koposa,’ kutanthauza wokondedwa mwapadera. Ndipo Mariya ‘anadabwa kwambiri’ ndi mawu amenewa moti anayamba kuganizira tanthauzo lake. (Luka 1:29) Kodi anali wokondedwa mwapadera ndi ndani? Mariya sanayembekezere kukondedwa mwapadera ndi anthu. Koma mngeloyu anali kunena za kukondedwa ndi Yehova Mulungu. Imeneyi inali nkhani yaikulu kwa Mariya. Komabe iye sanaganize modzikweza kuti anali wokondedwa kale ndi Mulungu. Pamene nafenso tikuyesetsa kuti Mulungu azitikonda, sitiyenera kuganiza modzikweza kuti ndife okondedwa kale ndi Mulunguyo. Tikatero tidzaphunzira mfundo yofunika kwambiri imene Mariya ankaidziwa bwino yoti: Mulungu amatsutsa odzikweza, koma amakonda ndi kuthandiza anthu odzichepetsa.​—Yakobe 4:6.

Mariya anafunikadi kudzichepetsa malinga ndi mwayi wapadera kwambiri womwe anali nawo. Mngeloyo anafotokoza kuti Mariya adzabereka mwana amene adzakhale wofunika kwambiri pa anthu onse. Gabiriyele anati: “Yehova Mulungu adzam’patsa mpando wachifumu wa Davide atate wake, ndipo adzalamulira monga mfumu pa nyumba ya Yakobo kwa muyaya, mwakuti ufumu wake sudzatha konse.” (Luka 1:32, 33) Mosakayikira, Mariya ankadziwa zimene Mulungu analonjeza Davide zaka zoposa 1,000 zimenezi zisanachitike. Lonjezolo linali lakuti mmodzi mwa mbadwa zake adzalamulira kwamuyaya. (2 Samueli 7:12, 13) Choncho mwana wakeyo anali kudzakhala Mesiya amene anthu a Mulungu anakhala akumuyembekezera kwa nthawi yaitali.

Kuwonjezera pamenepo, mngeloyo anamuuza kuti mwana wakeyo ‘adzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba.’ Kodi zingatheke bwanji kuti munthu abereke Mwana wa Mulungu? Ndipo zikanatheka bwanji kuti Mariya akhale ndi mwana? Chifukwatu, ngakhale kuti anali pachibwenzi ndi Yosefe koma anali asanagonanepo. Motero anafunsa mosapita m’mbali kuti: “Zimenezi zidzatheka bwanji, pakuti sindikugona ndi mwamuna?” (Luka 1:34) Taonani kuti Mariya sanachite manyazi kutchula kuti anali asanagonanepo ndi mwamuna ndipo ankanyadira kuti anali namwali. Koma masiku ano, achinyamata ambiri saona vuto lililonse kugonana asanalowe m’banja, ndipo amanyoza anzawo omwe sanagonanepo ndi wina aliyense. Dzikoli lasintha kwambiri, koma Yehova sanasinthe. (Malaki 3:6) Mofanana ndi mmene zinalili m’masiku a Mariya, Mulungu amasangalala ndi anthu amene amatsatira mfundo zake zamakhalidwe abwino.​—Aheberi 13:4.

Ngakhale kuti anali mtumiki wokhulupirika wa Mulungu, Mariya anali wopanda ungwiro. Ndiyeno zikanatheka bwanji kuti abereke mwana wangwiro, Mwana wa Mulungu? Gabiriyele anati: “Mzimu woyera udzafika pa iwe, ndipo mphamvu ya Wam’mwambamwamba idzakuphimba. Pa chifukwa chimenechinso, wodzabadwayo adzatchedwa woyera, Mwana wa Mulungu.” (Luka 1:35) Kukhala woyera kumatanthauza “kusadetsedwa” kapena “kukhala wopatulika.” Mwachibadwa, anthu amapatsira ana awo kupanda ungwiro. Koma pankhani ya Mariya, Yehova anali kudzachita chozizwitsa chapadera kwambiri. Iye anali kudzasamutsa moyo wa Mwana wake kuchoka kumwamba ndi kuuika m’mimba mwa Mariya ndiponso kugwiritsa ntchito mzimu wake ‘kuphimba’ Mariya, kuti mwanayo asatengere uchimo uliwonse. Kodi Mariya anakhulupirira lonjezo la mngeloyo? Kodi iye anayankha bwanji?

Yankho la Mariya kwa Gabiriyele

Anthu omwe amakayikira nkhani imeneyi, kuphatikizapo akatswiri a maphunziro a zaumulungu m’Matchalitchi Achikhristu, zimawavuta kukhulupirira kuti namwaliyu anabereka mwana. Ngakhale kuti ndi anthu ophunzira kwambiri, iwo amalephera kumvetsa mfundo ya choonadi yosavuta imeneyi. Malinga ndi zimene Gabiriyele ananena, “zimene Mulungu wanena, sizilephereka.” (Luka 1:37) Mariya sanakayikire zimene Gabiriyele ananena chifukwa chakuti iye anali ndi chikhulupiriro cholimba. Komabe izi sizikutanthauza kuti anali munthu wongokhulupirira zilizonse. Mofanana ndi munthu wina aliyense woganiza bwino, Mariya anafuna umboni wowonjezera pa chikhulupiriro chake. Ndipo Gabiriyele anam’patsa umboni wotero. Anam’fotokozera za Elizabeti, yemwe anali wachibale wake wokalamba ndipo anali wosabereka. Mulungu anachita chozizwitsa chimene chinapangitsa kuti Elizabeti akhale woyembekezera.

Tsopano, kodi Mariya akanachita chiyani? Iye anali atapatsidwa ntchito yoti achite ndipo anali ndi umboni wakuti Mulungu adzachita zonse zimene Gabiriyele ananena. Tisaganize kuti ntchito imeneyi inali yophweka kapena kuti yopanda mavuto alionse. Mwachitsanzo, iye anali atatomeredwa ndi Yosefe, ndipo anafunika kuganizira zimenezo. Kodi Yosefe akanam’kwatira ngakhale atadziwa kuti ndi woyembekezera? Komanso n’kutheka kuti Mariya ankaona kuti ntchitoyi sinali yamasewera. Anali kudzabereka Mwana wa Mulungu, wokondedwa kwambiri komanso wamtengo wapatali pa zolengedwa zonse. Ndipo akanafunika kum’samalira ali wakhanda ndiponso kum’teteza ku dziko loipali. Kunena zoona, imeneyi inalidi ntchito yaikulu kwambiri.

Baibulo limasonyeza kuti ngakhale anthu achikhulupiriro cholimba kwambiri nthawi zina anali kuopa kuti Mulungu awapatse ntchito zovuta kwambiri. Mwachitsanzo, Mose ananena kuti sangakhale wolankhulira Mulungu chifukwa chakuti sankatha kulankhula bwinobwino. (Eksodo 4:10) Yeremiya ananena kuti anali “mwana” wamng’ono kwambiri moti sangakwanitse ntchito imene Mulungu anam’patsa. (Yeremiya 1:6) Ndipo Yona anathawa ntchito yomwe anapatsidwa. (Yona 1:3) Nanga Mariya akanatani?

Zimene iye analankhula zikusonyeza kuti anali wodzichepetsa kwambiri ndiponso womvera. Mariya anauza Gabiriyele kuti: “Ndinetu mdzakazi wa Yehova! Zimene mwanenazo zichitike ndithu kwa ine.” (Luka 1:38) Mdzakazi anali mtumiki wotsika kwambiri ndipo moyo wake wonse unali kulamulidwa ndi mbuye wake. Umu ndi mmene Mariya ankaonera moyo wake kwa Yehova. Iye ankaona Yehova monga Mbuye wake. Ankadziwa kuti ndi wotetezeka m’manja mwake ndiponso kuti Yehova ndi “wachifundo,” kutanthauza kuti wokhulupirika kwa anthu okhulupirika kwa iye. (Salmo 18:25) Ankadziwanso kuti Yehova adzam’dalitsa ngati atayesetsa kugwira ntchito yomwe wapatsidwa.

Nthawi zina Mulungu angatiuze kuti tichite zinthu zinazake zimene ifeyo tikuona kuti n’zovuta ndipo mwina n’zosatheka n’komwe. Komabe, kudzera m’Mawu ake, iye watipatsa zifukwa zomveka zom’khulupirira ndiponso kuti tim’dalire ndi moyo wathu wonse ngati mmene Mariya anachitira. (Miyambo 3:5, 6) Kodi ifeyo tidzachitadi zimenezo? Ngati titatero, iye adzatidalitsa ndipo tidzapeza zifukwa zina zotithandiza kumukhulupirira kwambiri.

Mariya Achezera Elizabeti

Kwa Mariya, zinthu zimene Gabiriyele ananena zokhudza Elizabeti zinali zofunika kwambiri. Kodi ndani mwa akazi onse padziko lapansi amene akanatha kum’mvetsa Mariya? Mofulumira, iye anayamba ulendo wopita ku dera lamapiri la Yuda, womwe mwina unali wamasiku atatu kapena anayi. Atafika ku nyumba ya Elizabeti ndi Zakariya, yemwe anali wansembe, Yehova anapatsanso Mariya umboni wina womwe unalimbitsa chikhulupiriro chake. Elizabeti atangomva mawu a Mariya, nthawi yomweyo mwana amene anali m’mimba mwake analumpha ndi chisangalalo. Elizabeti anadzazidwa ndi mzimu woyera ndipo anatchula Mariya kuti “mayi wa Ambuye wanga.” Mulungu anauza Elizabeti kuti mwana wa Mariya adzakhala Mbuye ndi Mesiya. Ndiponso mouziridwa ndi mzimu, iye anayamikira Mariya chifukwa cha kumvera ndiponso kukhulupirika kwake. Iye anati: “Wosangalalanso ndi mayi amene anakhulupirirayo.” (Luka 1:39-45) Zoonadi, zonse zimene Yehova anam’lonjeza Mariya zinali kudzakwaniritsidwa.

Kenako Mariya analankhula mawu amene amapezeka palemba la Luka 1:46-55. Mawu amenewa ndi aatali kwambiri pa mawu onse opezeka m’Baibulo amene Mariya analankhula ndipo amatithandiza kudziwa zambiri za iye. Mawuwa amasonyeza kuti iye anali ndi mtima woyamikira, chifukwa anatamanda Yehova pom’patsa mwayi wokhala mayi wa Mesiya. Amasonyezanso kuti Mariya anali ndi chikhulupiriro champhamvu chifukwa iye anafotokoza kuti Yehova amatsitsa anthu odzikweza ndi amphamvu ndipo amakweza odzichepetsa amene amafuna kum’tumikira. Komanso mawuwa akusonyeza kuti Mariya ankadziwa Malemba kwambiri. Zikuoneka kuti iye anagwira mawu m’Malemba Achiheberi m’malo oposa 20.

N’zoonekeratu kuti Mariya ankaganizira kwambiri Mawu a Mulungu. Ngakhale zinali choncho, Mariyayo anadzichepetsa mwa kugwiritsa ntchito Malemba m’malo mofotokoza za m’maganizo mwake. Mwana amene anali kukula m’mimba mwake anali kudzasonyezanso mtima ngati womwewu. Panthawi ina Yesu anati: “Zimene ine ndimaphunzitsa si zanga ayi, koma ndi za amene anandituma.” (Yohane 7:16) Tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimasonyeza ulemu ngati umenewu pa Mawu a Mulungu? Kapena ndimakonda kunena za m’maganizo mwanga pophunzitsa?’ Zimene Mariya akanachita n’zodziwikiratu.

Mariya anakhala ndi Elizabeti kwa miyezi itatu ndipo mosakayikira iwo analimbikitsana kwambiri. (Luka 1:56) Akazi awiri onsewa amatikumbutsa za kufunika kokhala ndi mabwenzi. Tikakhala ndi anzathu omwe amakondadi Mulungu wathu yemwe ndi Yehova, tidzakula mwauzimu ndiponso tidzakhala paubwenzi wolimba ndi Mulunguyo. (Miyambo 13:20) Pamapeto pake, Mariya anafunika kubwerera kwawo. Koma kodi Yosefe adzanena chiyani akamva kuti iye ndi woyembekezera?

Mariya ndi Yosefe

Mariya sanadikire kuti Yosefe achite kuzindikira yekha kuti iye ali ndi pakati. Iye anamuuza yekha za nkhaniyo. Koma asanamuuze, ayenera kuti anaganizira mozama zimene Yosefe angachite akamva za nkhaniyi, ngakhale kuti ankadziwa zoti Yosefe anali munthu wokhulupirika ndiponso woopa Mulungu. Komabe, iye analimba mtima n’kumuuza zonse zimene zinamuchitikira. Mosakayikira, nkhani imeneyi inam’vutitsa maganizo kwambiri Yosefe. Iye anafuna kukhulupirira bwenzi lakelo, komabe zimene anamuuzazo zinali zachilendo. Baibulo silinena zimene zinali m’maganizo mwa Yosefe panthawiyi atamva nkhaniyi. Koma, limanena kuti ataganizira za nkhaniyi, anakonza zom’sudzula, popeza kuti anthu omwe ali pachibwenzi ankaonedwa ngati ali pabanja. Komabe, iye sanafune kum’chititsa manyazi kapenanso kuti alandire chilango, motero anasankha zom’sudzula mwamseri. (Mateyo 1:18, 19) Ziyenera kuti zinam’pweteka kwambiri Mariya kuona bwenzi lake, yemwe anali munthu wokoma mtima, akuvutika maganizo chifukwa cha nkhaniyi. Komabe, Mariya sanakhumudwe ndi zimenezi.

Yehova sanalole kuti Yosefe achite zimene anaganizazo. Mngelo wa Mulungu anauza Yosefe kudzera m’maloto kuti Mariya anatengadi pathupi mozizwitsa. Zimenezi ziyenera kuti zinam’limbikitsa kwambiri Yosefe, ndipo anatsatira malangizo a Yehova monganso mmene Mariya anachitira poyamba paja. Anakwatira Mariya ndipo anakonzekera kugwira ntchito yapadera yosamalira Mwana wa Yehova.​—Mateyo 1:20-24.

Anthu omwe ali pabanja ndiponso amene akufuna kulowa m’banja ayenera kuphunzirapo kanthu pa zimene Yosefe ndi Mariya anachita zaka 2,000 zapitazo. Pamene Yosefe anali kuona mkazi wake akusamalira bwino banja lake, mosakayikira iye ankathokoza kuti mngelo wa Yehova uja anam’patsa malangizo abwino. Zimenezi ziyenera kuti zinam’thandiza kwambiri kuona ubwino wodalira Yehova akamasankha zoti achite pankhani zikuluzikulu. (Salmo 37:5; Miyambo 18:13) Mosakayikira, iye monga mutu wa banja anapitirizabe kuchita zinthu mosamala ndiponso mwachifundo posankha zinthu zochita.

Kodi ifeyo tikuphunzirapo chiyani pa zimene Mariya anachita pololera kuti akwatiwe ndi Yosefe? Ngakhale kuti poyamba Yosefe anavutika kuti akhulupirire zimene Mariya anali kumuuza, Mariyayo anadekha n’kudikirabe Yosefe yemweyo kuti ndiye adzakhale mwamuna wake. Zimenezi zinam’thandiza kwambiri Mariya ndipo zimapereka phunziro labwino kwambiri kwa akazi achikhristu masiku ano. Mosakayikira, nkhani zimenezi zinaphunzitsa Yosefe ndi Mariya mfundo yofunika kwambiri yokhudza kufunika kolankhulana mosabisirana kanthu.

Yosefe ndi Mariya anayala maziko abwino a banja lawo. Onse ankakonda Yehova Mulungu ndipo ankafunitsitsa kum’sangalatsa mwa kuchita zinthu monga makolo achikondi ndiponso osamalira bwino ana awo. Iwo anali kuyembekezera madalitso aakulu ndiponso mavuto. Anali kuyembekezeranso kulera Yesu yemwe anali kudzakhala munthu wofunika kwambiri kuposa wina aliyense padziko lonse lapansi.

[Chithunzi patsamba 17]

Kukonda Mulungu ndi maziko abwino a banja