Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mkwiyo wa Kaini

Mkwiyo wa Kaini

Zoti Achinyamata Achite

Mkwiyo wa Kaini

Malangizo: Chitani zotsatirazi muli pa malo opanda phokoso. Mukamawerenga mavesiwo, muziyerekezera kuti pamene zinthuzo zinkachitika inuyo munalipo. Yesani kuona nkhanizi m’maganizo mwanu. Yerekezerani kuti mukumva mawu a m’nkhanizi. Yesani kuganizira mmene anthu otchulidwa m’nkhaniyi ankamvera.

ONANI BWINOBWINO NKHANI IYI.​—WERENGANI GENESIS 4:1-12.

Kodi mukuganiza kuti Kaini ankaoneka bwanji, ndipo anali ndi makhalidwe otani? Nanga bwanji Abele?

․․․․․

Kodi Kaini anaonetsa “ntchito za thupi” zotani, ndipo tikudziwa bwanji zimenezi? (Agalatiya 5:19-21)

․․․․․

FUFUZANI MOZAMA.​—WERENGANINSO MAVESI 4 MPAKA 7.

Kodi panalinso zinthu zina zimene Yehova anaganizira polandira kapena kukana nsembezi? (Miyambo 21:2)

․․․․․

Kodi mkwiyo ungakhale woyenera pazinthu zotani, koma n’chifukwa chiyani zinali zolakwika kuti Kaini ‘akwiye kwambiri’?

․․․․․

Kodi nsanje ingakhale yoyenera panthawi yotani, koma n’chifukwa chiyani nsanje ya Kaini inali yolakwika? (1 Mafumu 19:10)

․․․․․

Kodi Kaini akanachita chiyani kuti ‘alamulire’ mkwiyo wake?

․․․․․

GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA PONENA ZA . . .

Mkwiyo.

․․․․․

Nsanje.

․․․․․

Mmene mungalimbanirane ndi zizolowezi zoipa.

․․․․․

M’NKHANIYI, KODI NDI MFUNDO ZITI ZIMENE ZAKUKHUDZANI KWAMBIRI NDIPO N’CHIFUKWA CHIYANI?

․․․․․