Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalanibe ndi “Chingwe cha Nkhosi Zitatu” M’banja Lanu

Khalanibe ndi “Chingwe cha Nkhosi Zitatu” M’banja Lanu

Khalanibe ndi “Chingwe cha Nkhosi Zitatu” M’banja Lanu

“Chingwe cha nkhosi zitatu sichiduka msanga.”​—MLAL. 4:12.

1. Kodi ndani anakwatitsa anthu awiri oyamba?

ATALENGA zomera ndi nyama, Yehova Mulungu analenga munthu woyamba, Adamu. Kenako anagonetsa Adamu tulo tatikulu ndipo anatenga nthiti yake n’kupanga mkazi womuthandiza. Atangomuona mkaziyo, Adamu anati: “Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga, ndi mnofu wa mnofu wanga.” (Gen. 1:27; 2:18, 21-23) Yehova anasangalala chifukwa chomulengera Adamu mkazi ndipo anakwatitsa anthu awiri oyambawo ndi kuwadalitsa.​—Gen. 1:28; 2:24.

2. Kodi Satana anasokoneza bwanji banja la Adamu ndi Hava?

2 N’zomvetsa chisoni kuti pasanapite nthawi yaitali, banjalo linasokonekera. Kodi chinachitika n’chiyani? Mngelo woipa amene anadzakhala Satana, ananamiza Hava kuti adye chipatso cha mtengo woletsedwa. Adamu nayenso anadya chipatsocho ndipo anapandukira ulamuliro wa Mulungu. (Gen. 3:1-7) Yehova atawafunsa zimene anachitazo, zimene anayankha zinasonyeza kuti banja lawo linayamba kuvuta. Adamu anaimba mlandu mkazi wake kuti: “Mkazi amene munandipatsa ine kuti akhale ndi ine, ameneyo anandipatsa ine za mtengo, ndipo ndinadya.”​—Gen. 3:11-13.

3. Kodi Ayuda ena anali ndi maganizo olakwika otani pankhani ya banja?

3 Kuyambira nthawi imeneyo, Satana wakhala akusokoneza mabanja pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, nthawi zina amagwiritsa ntchito atsogoleri achipembedzo kulimbikitsa mfundo zosagwirizana ndi Malemba pankhani ya banja. Atsogoleri ena achipembedzo achiyuda ankanyozera malamulo a Mulungu, polola amuna kusudzula akazi awo pazifukwa zazing’ono monga kuwawitsa mchere mu ndiwo. Koma Yesu anati: “Aliyense wosudzula mkazi wake ndi kukwatira wina achita chigololo, kupatulapo ngati am’sudzula chifukwa cha dama.”​—Mat. 19:9.

4. Kodi mabanja asokonekera bwanji masiku ano?

4 Satana akusokonezabe mabanja ndipo zikuoneka kuti akupambana, chifukwa maukwati a amuna kapena akazi okhaokha, kukhalira pamodzi kwa mwamuna ndi mkazi amene sanakwatirane ndiponso kusudzulana pa zifukwa zosamveka, n’kofala kwambiri masiku ano. (Werengani Aheberi 13:4.) Kodi Akhristufe tingapewe bwanji kutengera maganizo olakwika amenewa? Tiyeni tione zinthu zimene zimapangitsa banja kukhala losangalala.

Yehova Azikhala M’banja Lanu

5. Kodi mawu akuti “chingwe cha nkhosi zitatu” amaimira chiyani m’banja?

5 Kuti banja liziyenda bwino, Yehova ayenera kukhala m’banjalo. Baibulo limati: “Chingwe cha nkhosi zitatu sichiduka msanga.” (Mlal. 4:12) Mawu akuti “chingwe cha nkhosi zitatu” ndi ophiphiritsa. Tikamanena za banja, zingwe ziwiri zoyamba zimaimira mwamuna ndi mkazi wake, amene amapotedwa pamodzi ndi chingwe chachikulu, Yehova Mulungu. M’banja mukakhala Mulungu, banjalo limakhala lolimba mwauzimu ndipo limatha kupirira mavuto. Chimenechi ndi chinsinsi cha banja losangalala.

6, 7. (a) Kodi Akhristu angatani kuti Mulungu akhale m’banja lawo? (b) Kodi mlongo wina anati amakonda mwamuna wake chifukwa chiyani?

6 Koma kodi anthu okwatirana angachite chiyani kuti banja lawo likhale ngati chingwe cha nkhosi zitatu? Wamasalmo Davide anaimba kuti: “Kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga; ndipo malamulo anu ali m’kati mwamtima mwanga.” (Sal. 40:8) Kukonda Mulungu kumatilimbikitsa kumutumikira ndi mtima wonse. Choncho, onse awiri ayenera kukhala paubwenzi wabwino ndi Yehova komanso ayenera kusangalala kuchita zimene Iye amafuna. Anthu okwatirana ayeneranso kuyesetsa kulimbikitsana kuti azikonda Mulungu.​—Miy. 27:17.

7 Ngati chilamulo cha Mulungu chili mumtima mwathu, timasonyeza chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi, ndipo zimenezi zimathandiza kuti banja lathu likhale lolimba. (1 Akor. 13:13) Mwachitsanzo, Mkhristu wina dzina lake Sandra, amene wakhala m’banja zaka 50 anati: “Ndimakonda kwambiri mwamuna wanga chifukwa amandilangiza mwauzimu ndiponso chifukwa chakuti amakonda Yehova kuposa mmene amandikondera.” Kodi amunanu, akazi anu anganene zimenezi ponena za inu?

8. Kodi chofunika n’chiyani kuti tipeze “mphoto yabwino” m’banja?

8 Kodi m’banja mwanu mumaika zinthu zauzimu ndiponso za Ufumu patsogolo? Ndipo kodi mumaona mwamuna kapena mkazi wanu monga mnzanu wothandizana naye potumikira Yehova? (Gen. 2:24) Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Awiri aposa mmodzi; pakuti ali ndi mphoto yabwino m’ntchito zawo.” (Mlal. 4:9) Inde, mwamuna ndi mkazi wake ayenera kulimbikira kuti apeze “mphoto yabwino,” yomwe ndi banja lokondana ndi lolimba limene Mulungu amasangalala nalo.

9. (a) Kodi amuna ali ndi udindo wotani? (b) Malinga ndi Akolose 3:19, kodi amuna sayenera kuwachitira chiyani akazi awo?

9 Banja limene muli Mulungu limadziwika ngati mwamuna ndi mkazi wake amayesetsa kutsatira malamulo a Mulungu. Amuna ali ndi udindo wopezera banja lawo zinthu zofunika pamoyo wawo komanso zauzimu. (1 Tim. 5:8) Amalimbikitsidwanso kuganizira mmene mkazi wawo akumvera. Pa Akolose 3:19, timawerenga kuti: “Amuna inu, musaleke kukonda akazi anu ndipo musawapsere mtima.” Katswiri wina wa Baibulo anafotokoza kuti mawu akuti ‘kuwapsera mtima’ amatanthauza “kuwakalipira, kapena kuwamenya ndiponso kusawakonda, kusawasamalira, kusawapatsa zimene akufunika, kusawateteza komanso kusawathandiza.” Ndithudi, amuna achikhristu safunika kusonyeza khalidwe limeneli. Ngati mwamuna amakonda mkazi wake, mkaziyo savutika kugonjera mwamunayo.

10. Kodi akazi achikhristu ayenera kukhala ndi khalidwe lotani?

10 Akazi achikhristu amene akufuna kuti Yehova akhale m’banja lawo ayeneranso kumvera malamulo a Mulungu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Akazi agonjere amuna awo monga kugonjera Ambuye, chifukwa mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake monganso Khristu alili mutu wa mpingo.” (Aef. 5:22, 23) Satana ananamiza Hava kuti akhoza kukhala wosangalala popanda kugonjera Mulungu. Ndipo kusagonjerana ndi kofala m’mabanja ambiri. Koma akazi achikhristu sakana kugonjera amuna awo. Iwo amakumbukira kuti Yehova anapanga Hava kuti ‘azithangata’ mwamuna wake, ndipo Mulungu anaona kuti umenewu ndi udindo wolemekezeka kwambiri. (Gen. 2:18) Mkazi wachikhristu amene amatsatira makonzedwe a Mulungu amenewa amakhala “korona” kwa mwamuna wake.​—Miy. 12:4.

11. Kodi m’bale wina anati n’chiyani chathandiza banja lake?

11 China chimene chingathandize kuti Mulungu akhale m’banja lanu ndi kuphunzirira limodzi Mawu a Mulungu. Mwachitsanzo, Gerald amene wakhala mosangalala m’banja zaka 55, anati: “Kuti banja likhale losangalala liyenera kuwerenga ndi kuphunzira Baibulo pamodzi.” Iye ananenanso kuti: “Kuchitira zinthu pamodzi, makamaka zinthu zauzimu, kumapangitsa anthu okwatirana kukondana komanso kukonda Yehova.” Kuphunzira Baibulo pamodzi kumathandiza anthu okwatirana kukumbukira malamulo a Yehova komanso kukonda kwambiri zinthu zauzimu.

12, 13. (a) Kodi n’chifukwa chiyani mwamuna ndi mkazi wake ayenera kupempherera pamodzi? (b) Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zimalimbitsa banja?

12 Chinthu chinanso chimene chingathandize mabanja kukhala osangalala ndi kupempherera pamodzi. Mwamuna ‘akamatsanulira mtima wake’ kwa Mulungu popempha zinthu zokhudza banja lake, banjalo limalimba. (Sal. 62:8) Mwachitsanzo, sizivuta kuthetsa mkangano ngati mwamuna ndi mkazi wake apempha Mulungu kuti awatsogolere. (Mat. 6:14, 15) Mukapemphera, ndi bwino kuti nonse ‘mupitirize kulolerana ndi kukhululukirana wina ndi mnzake ndi mtima wonse.’ (Akol. 3:13) Musaiwale kuti pemphero limasonyeza kuti mukudalira Mulungu. Mfumu Davide ananena kuti: “Maso a onse ayembekeza Inu.” (Sal. 145:15) Tikapemphera kwa Mulungu timayembekezera kuti atithandiza ndipo sitimakhala ndi nkhawa zambiri podziwa kuti Iye ‘amatisamalira.’​—1 Pet. 5:7.

13 Chinanso chimene chingathandize kuti Yehova akhale m’banja lathu ndi kupezeka pa misokhano ya mpingo ndiponso kuyendera limodzi muutumiki. Pa misonkhano m’pamene anthu okwatirana amaphunzira zimene angachite polimbana ndi “machenjera” amene Satana amagwiritsa ntchito posokoneza mabanja. (Aef. 6:11) Ndipo amuna amene nthawi zonse amayenda ndi akazi awo muutumiki amakhala “ochirimika, osasunthika.”​—1 Akor. 15:58.

M’banja Mukakhala Mavuto

14. Kodi ndi zinthu ziti zimene zimachititsa mavuto m’banja?

14 Mwina mfundo zimene takambiranazi sizachilendo kwa inu, komabe n’zofunika kuti mukambirane ndi mwamuna kapena mkazi wanu. Ndipo onani mbali zimene mungafunike kusintha m’banja lanu. Baibulo limanena kuti ngakhale anthu amene Mulungu ali m’banja lawo, “adzakhala ndi nsautso m’thupi mwawo.” (1 Akor. 7:28) Mabanja a atumiki okhulupirika a Mulungu amakhalanso pa mavuto aakulu chifukwa chopanda ungwiro, makhalidwe oipa a m’dziko loipali ndiponso misampha ya Mdyerekezi. (2 Akor. 2:11) Koma Yehova amatithandiza kulimbana ndi mavuto amenewa. Zimene zinachitikira munthu wokhulupirika Yobu zimasonyeza kuti n’zotheka kuthana ndi mavuto amenewa. Mwachitsanzo, ana, ziweto ndi antchito a Yobu anaphedwa. Komabe Baibulo limati: “Mwa ichi chonse Yobu sanachimwa, kapena kunenera Mulungu cholakwa.”​—Yobu 1:13-22.

15. Kodi mavuto angachititse anthu kuchita chiyani, nanga tizitani ngati mwamuna kapena mkazi wathu akuchita zimenezo?

15 Mkazi wa Yobu anamuuza kuti: “Kodi uumiriranso kukhala wangwiro? Chitira Mulungu mwano, ufe.” (Yobu 2:9) Ndithudi, munthu ukakumana ndi mavuto, umatha kuchita zinthu mosokonekera. Munthu wina wanzeru anati: “Nsautso iyarutsa wanzeru.” (Mlal. 7:7) Ngati mwamuna kapena mkazi wanu akulankhula mokalipa chifukwa cha mavuto enaake kapena “nsautso,” dekhani. Kuyankhanso mokalipa kungapangitse wina kapena nonse kunena zinthu zimene zingawonjezere vutolo. (Werengani Salmo 37:8.) Choncho, muzinyalanyaza mawu amene mnzanu wanena ‘mwasontho’ chifukwa chokwiya kapena kukhumudwa.​—Yobu 6:3.

16. (a) Kodi mawu a Yesu a pa Mateyo 7:1-5 amagwira ntchito bwanji m’banja? (b) Kodi n’chifukwa chiyani timafunika kukhala ololera m’banja?

16 Anthu okwatirana sayenera kuyembekezera kuti mwamuna kapena mkazi wawo sangalakwitse zinthu. Mwamuna kapena mkazi angaone khalidwe linalake mwa mnzake ndipo anganene kuti, ‘Ndimusintha ameneyu.’ Mwachikondi komanso moleza mtima, mungathandize mnzanuyo kusintha pang’onopang’ono. Komabe, musaiwale kuti Yesu anayerekezera munthu amene amaona zolakwa zing’onozing’ono za mnzake ndi munthu amene amaona “kachitsotso” m’diso la m’bale wake koma osaona “mtanda” umene uli m’diso lake. Yesu anatilangiza kuti: “Lekani kuweruza ena kuti inunso musaweruzidwe.” (Werengani Mateyo 7:1-5.) Zimenezi sizikutanthauza kuti tizinyalanyaza zolakwa zazikulu. Mwachitsanzo, Robert amene wakhala m’banja pafupifupi zaka 40, anati: “Mwamuna ndi mkazi wake ayenera kulankhulana momasuka ndi moona mtima komanso onse amafunika kusintha maganizo kuti avomereze zimene mnzawo akunena.” Choncho, tifunika kukhala ololera. M’malo moipidwa chifukwa chakuti mwamuna kapena mkazi wanu alibe makhalidwe enaake, yesetsani kuyamikira makhalidwe abwino amene ali nawo.​Mlal. 9:9.

17, 18. Kodi mavuto akatichulukira, tingapemphe ndani kuti atithandize?

17 Zinthu zikasintha pamoyo wathu pangakhale mavuto. Anthu okwatirana angakhale ndi mavuto pamene abereka ana. Mwina mwamuna kapena mkazi wathu kapenanso mwana wathu angadwale kwambiri. Makolo athu okalamba angafunike kuwasamalira mwapadera. Ana athu amene akula angasamukire kutali. Kusintha kwina kungakhale kokhudza kusamalira maudindo a kumpingo. Zonsezi zingabweretse mavuto m’banja.

18 Kodi mungatani ngati mukuona kuti mavuto a m’banja mwanu afika poipa kwambiri moti simungapirirenso? (Miy. 24:10) Musataye mtima. Satana amasangalala mtumiki wa Mulungu akasiya kulambira koona. Amasangalalanso kwambiri ngati anthu amene achita zimenezi ndi okwatirana. Choncho, chitani zonse zimene mungathe kuti banja lanu likhalebe ngati chingwe cha nkhosi zitatu. M’Baibulo muli nkhani zambiri za anthu amene anakhalabe okhulupirika ngakhale anali pamavuto aakulu. Mwachitsanzo, nthawi ina Davide anapemphera kwa Yehova ndi mtima wonse. Iye anati: “Mundichitire chifundo, Mulungu, pakuti anthu . . . andipsinja.” (Sal. 56:1) Kodi munayamba mwapsinjidwapo ndi zochita za munthu wina? Kaya mavuto anu akuchokera kwa munthu wina, kapena kwa mwamuna kapena mkazi wanu, kumbukirani kuti: Davide anapirira ndipo inunso mungapirire. Davide anati: “Ndinafuna Yehova ndipo anandivomera, nandilanditsa m’mantha anga onse.”​—Sal. 34:4.

Madalitso Amene Timapeza

19. Kodi tingapewe bwanji kugonjetsedwa ndi Satana?

19 M’masiku otsiriza ano, anthu okwatirana afunika ‘kupitiriza kutonthozana ndi kulimbikitsana wina ndi mnzake.’ (1 Ates. 5:11) Musaiwale kuti Satana amanena kuti timakhala okhulupirika kwa Yehova chifukwa cha dyera. Motero amagwiritsa ntchito njira iliyonse imene angathe, kaya kusokoneza mabanja, kuti tisakhale okhulupirika kwa Mulungu. Kuti Satana asatigonjetse, tifunika kukhulupirira kwambiri Yehova. (Miy. 3:5, 6) Paulo analemba kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”​—Afil. 4:13.

20. Kodi timapeza madalitso otani ngati Mulungu ali m’banja lathu?

20 Madalitso amene tingakhale nawo chifukwa chakuti Mulungu ali m’banja lathu ndi ambiri. Zimenezi n’zimene Joel ndi mkazi wake amene akhala m’banja zaka 51 aona. Joel anati: “Ndimathokoza Yehova nthawi zonse chifukwa chondipatsa mkazi wabwino komanso chifukwa chakuti tikukhala mosangalala. Mkazi wanga wakhaladi mnzanga weniweni.” Kodi chinsinsi chawo n’chiyani? Iye anati: “Nthawi zonse timayesetsa kukomerana mtima, kukondana ndiponso kupirirana.” Komabe, palibe angasonyeze makhalidwe amenewa mosaphonyetsa m’dongosolo lino la zinthu. Choncho, tiyeni tilimbikire kutsatira mfundo za m’Baibulo kuti Yehova azikhala m’banja lathu. Ngati tichita zimenezi, banja lathu lidzakhala ngati “chingwe cha nkhosi zitatu [chimene] sichiduka msanga.”​—Mlal. 4:12.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi kukhala ndi Yehova m’banja lanu kumatanthauza chiyani?

• Kodi okwatirana ayenera kuchita chiyani pakakhala mavuto?

• Kodi banja limene muli Mulungu tingalidziwe bwanji?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 18]

Kupempherera pamodzi kumathandiza anthu okwatirana kupirira mavuto