Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Ndi “Mpulumutsi” Wathu

Yehova Ndi “Mpulumutsi” Wathu

Yehova Ndi “Mpulumutsi” Wathu

“Yehova adzawathandiza ndi kuwapulumutsa.”​—SAL. 37:40, NW.

1, 2. Kodi ndi mfundo iti yonena za Yehova imene ndi yotonthoza ndiponso yolimbikitsa kwambiri?

DZIKO likamazungulira, mthunzi umene umabwera chifukwa cha dzuwa sukhala malo amodzi, umasunthasuntha. Koma Mlengi amene analenga dziko ndi dzuwa sasintha. (Mal. 3:6) Baibulo limatiuza kuti: “Iye sasintha ngati kusuntha kwa mthunzi.” (Yak. 1:17) Mfundo yonena za Yehova imeneyi, ndi yotonthoza komanso yolimbikitsa kwambiri makamaka pamene tikukumana ndi mavuto kapena mayesero aakulu. N’chifukwa chiyani tikutero?

2 Monga tinaonera m’nkhani yoyamba ija, Yehova ‘anapulumutsa’ anthu ake m’nthawi za m’Baibulo. (Sal. 70:5) Iye sasintha ndipo amakwaniritsa mawu ake. Choncho, atumiki ake masiku ano angamudalire kuti “adzawathandiza ndi kuwapulumutsa.” (Sal. 37:40, NW) Kodi Yehova wapulumutsa bwanji atumiki ake masiku ano? Nanga angatipulumutse bwanji ifeyo aliyense payekha?

Amatipulumutsa kwa Adani

3. Kodi tikudziwa bwanji kuti adani sangaletse anthu a Yehova kulalikira uthenga wabwino?

3 Mulimonse mmene Satana angachitire, sangaletse Mboni za Yehova kulambira Yehova. Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti: “Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m’chiweruzo udzalitsutsa.” (Yes. 54:17) Adani ayesetsa kuletsa anthu a Mulungu kulalikira koma alephera. Taganizirani zitsanzo ziwiri izi.

4, 5. Kodi n’chiyani chinachitikira atumiki a Mulungu mu 1918, nanga zotsatirapo zake zinali zotani?

4 Mu 1918, atsogoleri achipembedzo anatsogolera kuzunza anthu a Yehova kuti asiye ntchito yawo yolalikira. Pa May 7, boma la United States, linalamula kuti M’bale J. F. Rutherford, amene ankayang’anira ntchito yolalikira ya padziko lonse ndi anthu ena ogwira ntchito kulikulu la Mboni za Yehova amangidwe. Pasanathe miyezi iwiri, M’bale Rutherford ndi anzake anawapeza olakwa powanamizira kuti anali oukira boma ndipo analamulidwa kukhala m’ndende nthawi yaitali. Kodi adaniwa anathetsa ntchitoyi? Ayi.

5 Kumbukirani kuti Yehova analonjeza kuti: “Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula.” Zinthu zinasinthadi mwadzidzidzi. Atatha miyezi 9 m’ndende, M’bale Rutherford ndi anzake anatulutsidwa pabelo pa March 26, 1919. Chaka chotsatira, pa May 5, 1920, mlandu wawo unatha. Ndi ufulu umenewu, abalewa analimbikira kugwira ntchito ya Ufumu. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Kuyambira nthawi imeneyi, chiwerengero cha ofalitsa chinayamba kuwonjezereka kwambiri. Tikaganizira zimene zinachitikazi, timathokoza “mpulumutsi” wathu, Yehova.​—1 Akor. 3:7.

6, 7. (a) Kodi boma la Germany linali ndi cholinga chotani ndi Mboni za Yehova, nanga zinthu zinatha bwanji? (b) Kodi mbiri ya makono ya Mboni za Yehova imatitsimikizira chiyani?

6 Tsopano tiyeni tione chitsanzo chachiwiri. Mu 1934, Hitler anatsimikiza mtima kuthetsa Mboni za Yehova ku Germany. Zimenezi sizinali zongonena. Anthu ambiri anamangidwa ndipo Mboni za Yehova zambiri zinazunzidwa komanso zina zinaphedwa mu ndende zozunzirako anthu. Kodi Hitler anakwanitsa cholinga chake? Kodi Mboni zinalekadi kulalikira uthenga wabwino ku Germany? Ayi ndithu. Panthawi yovuta imeneyi, abale athu anapitiriza kulalikira uthenga wa Ufumu mobisa. Ulamuliro wa Hitler utatha, Mboni za Yehova zinapitiriza kulalikira. Masiku ano ku Germany kuli Mboni zoposa 165,000. Apanso, “mpulumutsi” wathu anakwaniritsa zimene analonjeza zakuti: “Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula.”

7 Mbiri ya makono ya Mboni za Yehova ikutitsimikizira kuti Yehova sadzalola kuti anthu ake onse monga gulu awonongedwe. (Sal. 116:15) Koma kodi Yehova amateteza aliyense wa ife payekha? Ngati ndi choncho, amatiteteza bwanji?

Kodi Amatiteteza Mwakuthupi?

8, 9. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti Mulungu sanalonjeze kuti adzatiteteza mwakuthupi? (b) Kodi tiyenera kuzindikira chiyani?

8 Timadziwa kuti Mulungu sanalonjeze kuti adzateteza aliyense wa ife mwakuthupi. Tili ndi maganizo ofanana ndi anyamata okhulupirika a Chiheberi amene anakana kugwadira fano la golide la Mfumu Nebukadinezara. Anyamata oopa Mulungu amenewa analibe maganizo akuti Yehova awateteza mozizwitsa. (Werengani Danieli 3:17, 18.) Koma Yehova anawapulumutsa mu ng’anjo yotentha yamoto. (Dan. 3:21-27) Ngakhale m’nthawi za m’Baibulo, kupulumutsa anthu mozizwitsa sikumachitikachitika. Ndipo atumiki ambiri a Yehova okhulupirika anaphedwa ndi adani awo.​—Aheb. 11:35-37.

9 Nanga bwanji masiku ano? Yehova monga “mpulumutsi” wathu, akhozadi kutipulumutsa pamavuto. Pazinthu zimene zingatichitikire, kodi tinganene motsimikiza kuti Yehova watithandiza kapena sanatithandize? Ayi. Komabe, munthu amene wapulumuka pangozi inayake akhoza kunena kuti ndi Yehova amene wam’pulumutsa. Ngati akunena choncho, sibwino kumutsutsa. Koma tiyenera kuzindikiranso kuti Akhristu okhulupirika ambiri azunzidwa mpaka imfa, monga mmene zinalili ku Germany. Ndipo ena afa momvetsa chisoni kwambiri. (Mlal. 9:11) Ndiyeno tingafunse kuti, ‘Kodi Yehova analephera kukhala “mpulumutsi” wa anthu okhulupirika amenewa? Ayi, si choncho.

10, 11. Kodi n’chifukwa chiyani munthu sangadziteteze ku imfa, koma kodi Yehova ali ndi mphamvu zotani?

10 Taganizirani izi: Munthu sangadziteteze ku imfa, chifukwa Baibulo limati, palibe munthu “amene adzapulumutsa moyo wake ku mphamvu ya manda.” (Sal. 89:48) Koma bwanji Yehova? Mlongo wina amene anapulumuka mu ulamuliro wa Hitler, anakumbukira zimene mayi ake a Mboni anamuuza pomutonthoza, abale awo atafera mu ndende zozunzirako anthu. Iwo anamuuza kuti: “Zikanakhala kuti imfa siidzatha, ndiye kuti ikanakhala yamphamvu kuposa Mulungu.” Zoonadi, imfa si yamphamvu kuposa Mlengi wathu wamphamvu zonse. (Sal. 36:9) Yehova amakumbukira onse amene ali kumanda ndipo adzawapulumutsa.​—Luka 20:37, 38; Chiv. 20:11-14.

11 Masiku ano Yehova amasamalira atumiki ake okhulupirika. Tiyeni tikambirane njira zitatu zimene Yehova amakhala “mpulumutsi” wathu.

Amatiteteza Mwauzimu

12, 13. Kodi chitetezo chauzimu n’chofunika kwambiri chifukwa chiyani, ndipo Yehova amatiteteza bwanji mwauzimu?

12 Yehova amatiteteza mwauzimu, ndipo chimenechi ndi chitetezo chofunika kwambiri. Ife Akhristu oona timadziwa kuti pali chinthu china chofunika kuposa moyo umene tili nawo panopa. Chinthu cha mtengo wapatali kwambiri kwa ife ndicho ubwenzi wathu ndi Yehova. (Sal. 25:14; 63:3) Popanda ubwenzi umenewu, moyo wathu ukanakhala wopanda tanthauzo komanso bwenzi tilibe chiyembekezo.

13 Tikuthokoza kuti Yehova amatipatsa zonse zofunika kuti tikhale naye paubwenzi wabwino. Iye watipatsa Mawu ake, mzimu woyera, ndi gulu lake la padziko lonse kuti zitithandize. Kodi tingatani kuti zinthu zimenezi zitithandize? Tiziphunzira Mawu ake mwakhama nthawi zonse kuti chikhulupiriro chathu chilimbe. (Aroma 15:4) Tizipempha mzimu wake ndi mtima wonse, kuti tipewe kuchita zinthu zoipa. (Luka 11:13) Tiyenera kumvera malangizo amene gulu la kapolo limatipatsa kudzera m’mabuku ofotokoza za m’Baibulo, m’misonkhano ya mpingo, yadera ndi yachigawo. Ndipo tikamatero ndiye kuti tikudya ‘chakudya chauzimu panthawi yoyenera.’ (Mat. 24:45) Zinthu zimenezi zimatiteteza mwauzimu ndiponso zimatithandiza kuti tiyandikirane ndi Mulungu.​—Yak. 4:8.

14. Fotokozani chitsanzo chimene chikusonyeza kuti Yehova amatiteteza mwauzimu.

14 Chitsanzo chimodzi chosonyeza kuti Yehova amatiteteza mwauzimu ndi cha makolo amene tinawatchula koyambirira kwa nkhani yoyamba ija. Mwana wawo Theresa atasowa kwa masiku angapo, analandira uthenga womvetsa chisoni kwambiri wakuti waphedwa. * Bambo ake ananena kuti: “Ndinapempha Yehova kuti amuteteze. Titamva kuti wapezeka atafa ndinadzifunsa kuti, n’chifukwa chiyani Mulungu sanayankhe pemphero langa? Ndikudziwa kuti Yehova sanalonjeze zoteteza mozizwitsa munthu aliyense payekha. Ndinapitiriza kupempha Mulungu kuti andithandize kumvetsa nkhani imeneyi. Ndalimbikitsidwa kudziwa kuti Yehova amateteza anthu ake mwauzimu mwa kuwapatsa zinthu zofunikira kuti apitirize kukhala naye paubwenzi. Chitetezo chimenechi n’chofunika kwambiri, chifukwa chimakhudza tsogolo lathu losatha. Choncho, ndinganene kuti Yehova anamuteteza Theresa, chifukwa anatumikira Yehova mokhulupirika mpaka pamene anafa. Ndimasangalala kudziwa kuti moyo wake uli m’manja mwa Mulungu.”

Yehova Amatithandiza Tikamadwala

15. Kodi Yehova angatithandize bwanji tikamadwala?

15 Yehova amatisamalira “pa kama wodwalira” ngati mmene anachitira ndi Davide. (Sal. 41:3) Iye amatithandiza, ngakhale kuti masiku ano satichiritsa mozizwitsa tikadwala. Kodi amatithandiza bwanji? Mfundo zopezeka m’Mawu ake zingatithandize kusankha mankhwala ndi zinthu zina mwanzeru. (Miy. 2:6) Tingapeze malangizo othandiza okhudza matenda athu m’nkhani za mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mwa mzimu wake, Yehova angatipatse “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti tipirire vuto lathu komanso kuti tipitirizebe kukhala okhulupirika zivute zitani. (2 Akor. 4:7) Ndi thandizo limeneli, tingapewe kuganizira kwambiri za matendawo kuposa zinthu zauzimu.

16. Kodi n’chiyani chathandiza m’bale wina kupirira matenda ake?

16 Taganizirani za m’bale wachinyamata amene tamutchula kumayambiriro kwa nkhani yoyamba ija. Mu 1998, anam’peza ndi matenda oopsa amene anachititsa kuti afe ziwalo. * Kodi chinamuthandiza n’chiyani kuti apirire matendawa? Iye anafotokoza kuti: “Nthawi zina ndimawawidwa mtima ndipo ndimangofuna kufa basi. Ndikakhala ndi maganizo amenewa, ndimapemphera kwa Yehova kuti andithandize kukhala ndi zinthu zitatu izi: Kuleza mtima, kudekha ndi kupirira. Ndikuona kuti Yehova anayankha mapemphero anga. Mtima wodekha umandithandiza kuganizira mmene zinthu zidzakhalire m’dziko latsopano pamene ndidzathenso kuyenda, kusangalala ndi chakudya komanso kulankhula bwinobwino ndi abale anga. Kuleza mtima kumandithandiza kuthana ndi mavuto okhudzana ndi matenda anga. Kupirira kumandithandiza kukhalabe wokhulupirika komanso kukhala ndi ubwenzi wolimba ndi Yehova. Ndimamva ngati mmene anamvera wamasalmo Davide, chifukwa inenso ndikuona kuti Yehova wandisamalira pa matenda anga.”​—Yes. 35:5, 6.

Amatipatsa Chakudya

17. Kodi Yehova akutilonjeza chiyani, nanga kodi lonjezo limeneli limatanthauza chiyani?

17 Yehova analonjeza kuti adzatipatsa zimene timafunika pamoyo wathu. (Werengani Mateyo 6:33, 34 ndi Aheberi 13:5, 6.) Zimenezi sizikutanthauza kuti tisamagwire ntchito. (2 Ates. 3:10) Koma zimatanthauza kuti, ngati timatsogoza Ufumu wa Mulungu pamoyo wathu komanso ngati timagwira ntchito mwakhama, Yehova adzatithandiza kupeza zinthu zofunika pamoyo. (1 Ates. 4:11, 12; 1 Tim. 5:8) Iye angatipatse zinthu zofunika pamoyo wathu m’njira imene sitimayembekezera, mwina kudzera mwa okhulupirira anzathu amene angatipatse zinthuzo kapena angatithandize kupeza ntchito.

18. Fotokozani chitsanzo chosonyeza kuti tingathandizidwe panthawi imene tilibe chakudya.

18 Taganizirani mlongo amene tamutchula kumayambiriro kwa nkhani yoyamba ija. Iye ndi mwana wake wamkazi atasamukira kumalo ena, anavutika kupeza ntchito. Iye anafotokoza kuti: “M’mawa uliwonse ndinkapita mu utumiki wa kumunda, ndipo masana ake ndinkapita kukafunafuna ntchito. Ndikukumbukira tsiku lina nditapita kukagula mkaka, ndinaonakonso ndiwo zamasamba koma ndinalibe ndalama zogulira. Izi zinandikhumudwitsa kwambiri. Nditabwerera kunyumba, ndinapeza pakhonde pathu pali ndiwo zosiyanasiyana zakudimba. Ndiwo zimenezi zinali zotikwanira kudya miyezi ingapo. Nditaziona, ndinagwetsa misozi ndipo ndinathokoza Yehova.” Kenako mlongoyo anauzidwa kuti ndiwozo zinabwera ndi m’bale wa mu mpingo mwawo amene amalima ndiwo zamasamba. Nthawi ina iye analembera kalata m’baleyo kumuuza kuti: “Ngakhale kuti ndinakuthokozani tsiku lija, ndinathokozanso kwambiri Yehova pogwiritsira ntchito mtima wanu wabwino kundikumbutsa za chikondi chake.​—Miy. 19:17.

19. Kodi atumiki a Yehova adzakhala ndi chikhulupiriro chotani pa chisautso chachikulu, ndipo panopa tiyenera kutani?

19 Choncho, zimene Yehova anachita m’nthawi za m’Baibulo komanso zimene wachita masiku ano, ndi umboni wakuti iye ndi Mthandizi wathu. Posachedwapa, chisautso chachikulu chikadzayamba m’dziko la Satanali, tidzafunikira kwambiri thandizo la Yehova kuposa kale. Panthawi imeneyi, atumiki a Yehova adzadalira kwambiri Mulungu kuti awathandize. Iwo adzatukula mitu yawo mosangalala, podziwa kuti chipulumutso chawo chayandikira. (Luka 21:28) Panopa, kaya tikumane ndi mavuto otani, tiyeni titsimikize mtima kukhulupirira Yehova. Tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro chonse kuti Mulungu wathu amene sasintha ndi “mpulumutsi” wathudi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Onani nkhani yakuti, “Coping With an Unspeakable Tragedy,” mu Galamukani! ya Chingelezi ya July 22, 2001, masamba 19-23.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi Yehova amakhala bwanji mpulumutsi kwa anthu amene anaphedwa?

• Kodi chitetezo chauzimu n’chofunika kwambiri chifukwa chiyani?

• Kodi lonjezo la Yehova lotipatsa chakudya limatanthauza chiyani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 8]

M’bale Rutherford ndi anzake anamangidwa mu 1918, kenako anamasulidwa ndipo milandu yawo inatha

[Chithunzi patsamba 10]

Yehova angatisamalire “pa kama wodwalira”