Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

M’kalata imene mtumwi Paulo analembera Aheberi anatchula za “kuika manja.” Kodi pamenepa amanena za kuikidwa kwa akulu kapena amanena chiyani?​—Aheb. 6:2.

Palibe chifukwa chokakamirira mbali imodzi, koma ziyenera kuti Paulo amanena zoika manja popereka mphatso za mzimu.

N’zoona kuti nthawi zina Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti kuika manja pankhani yoika munthu paudindo m’gulu la Mulungu. Mwachitsanzo, Mose ‘anaika manja ake’ pa Yoswa pamene ankamusankha kukhala womulowa m’malo. (Deut. 34:9) Mumpingo wachikhristu, amuna ena oyenerera anasankhidwa mwa kuikidwa manja. (Mac. 6:6; 1 Tim. 4:14) Paulo anachenjeza kuti sibwino kufulumira kuika manja munthu wina aliyense.​—1 Tim. 5:22.

Komabe, Paulo analimbikitsa Akhristu Achiheberi ‘kuyesetsa mwakhama kufika pa uchikulire’ popeza anali atasiya “chiphunzitso choyambirira.” Ndiyeno anatchula za ‘kulapa ntchito zakufa, chikhulupiriro mwa Mulungu, chiphunzitso cha maubatizo ndiponso kuika manja.’ (Aheb. 6:1, 2) Kodi pamenepa akutanthauza kuti kuikidwa kukhala mkulu kuli m’gulu la zinthu zoyambirira zimene Mkhristu ayenera kuyesetsa mwakhama kuzikwaniritsa kuti akule mwauzimu? Ayi. Chifukwa amene amasankhidwa kukhala akulu mu mpingo amakhala abale okhwima mwauzimu.​—1 Tim. 3:1.

Koma kuika manja kunali ndi cholinga chinanso. M’nthawi ya atumwi, Yehova anakana Aisiraeli akuthupi ndipo anasankha Aisiraeli auzimu, omwe ndi mpingo wa Akhristu odzozedwa, kukhala anthu ake. (Mat. 21:43; Mac. 15:14; Agal. 6:16) Mphatso zapadera za mzimu, monga kulankhula m’malilime, zinali umboni wa zimenezi. (1 Akor. 12:4-11) Koneliyo ndi banja lake atakhala okhulupirira, analandira mzimu woyera, ndipo zimenezi zinadziwika chifukwa ‘cholankhula m’malilime.’​—Mac. 10:44-46.

Nthawi zina, anthu ankalandira mphatso zapadera mwa kuikidwa manja. Filipo atalalikira uthenga wabwino ku Samariya, anthu ambiri anabatizidwa. Ndiyeno bungwe lolamulira linatumizako mtumwi Petulo ndi Yohane. Chifukwa chiyani? Baibulo limati: “Chotero [awiriwa] anayamba kuwaika manja [anthu amene anabatizidwa kumenewo], ndipo analandira mzimu woyera.” Zimenezi zinatanthauza kuti iwo analandira mphatso za mzimu zimene anthu anatha kuziona. Tikudziwa zimenezi chifukwa Simoni, amene poyamba anali wamatsenga, anaona mmene mzimu umagwirira ntchito ndipo mwadyera anafuna kugula luso limeneli kuti akaika anthu ena manja, anthuwo azichita zozizwitsa. (Mac. 8:5-20) Kenako, anthu 12 a ku Efeso anabatizidwa. Baibulo limati: “Pamene Paulo anawaika manja, mzimu woyera unafika pa iwo, ndipo anayamba kulankhula malilime ndi kunenera.”​—Mac. 19:1-7; yerekezani ndi 2 Timoteyo 1:6.

Choncho, pa Aheberi 6:2, Paulo ayenera kuti amanena zoika manja popereka mphatso ya mzimu kwa anthu okhulupirira kumene.