Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Amishonale Analalikira Kum’mawa Mpaka Kukafika Kuti?

Kodi Amishonale Analalikira Kum’mawa Mpaka Kukafika Kuti?

Kodi Amishonale Analalikira Kum’mawa Mpaka Kukafika Kuti?

PASANATHE zaka 30 kuchokera panthawi imene Yesu anafa, mtumwi Paulo analemba kuti uthenga wabwino unali kulalikidwa “m’chilengedwe chonse” cha pansi pa thambo. (Akolose 1:23) Sikuti Paulo anatanthauza kuti munthu wina aliyense amene anali moyo panthawiyo anali atamva uthenga wabwino. Ngakhale zili choncho, mfundo ya Paulo ndi yomveka: Amishonale achikhristu anali kulalikira m’madera ambiri odziwika panthawiyo.

Kodi amishonalewa analalikira mpaka kukafika kuti? Malemba amanena kuti sitima zamalonda zinathandiza Paulo kulalikira mpaka kukafika kumadzulo, ku Italiya. Mmishonale wakhama ameneyu ankafunanso kukalalikira ku Sipaniya.​—Machitidwe 27:1; 28:30, 31; Aroma 15:28.

Nanga bwanji za kum’mawa? Kodi Akhristu oyambirira analalikira kum’mawa mpaka kukafika kuti? Sitikudziwa kwenikweni, chifukwa Baibulo silinena. Koma mwina mungadabwe kudziwa kumene njira zamalonda zapakati pa dera lozungulira nyanja ya Mediterranean ndi mayiko a kum’mawa zinkafika m’zaka zapakati pa 1 C.E. ndi 100 C.E. Ngakhale kuti sitikudziwa zambiri, njira zimenezi zimasonyeza kuti zinali zotheka kupita kum’mawa.

Zotsatirapo za Nkhondo za Alesandro

Nkhondo zimene Alesandro Wamkulu anamenya zinam’fikitsa kum’mawa, kudutsa dera lonse la Babulo ndi Perisiya mpaka ku Punjab, kumpoto kwa Indiya. Maulendo a Alesandro anathandiza kuti Agiriki adziwe magombe a pakati pa matsiriro a mtsinje wa Firate, ku nyanja ya Perisiya, ndi matsiriro a mtsinje wa Indus.

Posapita nthawi, zinthu monga zokometsera chakudya ndiponso lubani zinayamba kufika m’madera olamulidwa ndi Girisi, kuchokera kutsidya lina la nyanja yamchere ya Indiya kudzera ku Nyanja Yofiira. Poyamba, malonda amenewa ankayendetsedwa ndi Amwenye komanso Aluya. Koma mafumu a ku Iguputo abanja la Tolemi atazindikira kayendedwe ka mphepo ya monsoon, nawonso anayamba kuchita nawo malonda a panyanja yamchere ya Indiya.

Kuyambira mwezi wa May mpaka September, panyanja imeneyi mphepo imaomba kuchokera kum’mwera chakumadzulo. Mphepoyi inkathandiza sitima kuyenda kuchokera kumene Nyanja Yofiira imakumana ndi nyanja yamchere ya Indiya, kutsata gombe la kum’mwera kwa Arabiya kapena kulunjika kum’mwera kwa Indiya. Kuyambira November mpaka March, mphepoyi imaomba kuchokera kumpoto chakum’mawa, zomwe zinkathandiza kuti abwerere bwino paulendo wawo. Chifukwa chodziwa kwa zaka zambiri mmene mphepoyi imayendera, akatswiri apanyanja achimwenye ndi achiluya ankadalira mphepoyi poyenda pakati pa Indiya ndi Nyanja Yofiira, atanyamula katundu monga kasya, sinamoni, nado ndi tsabola.

Njira Zapanyanja Zopita ku Alesandiriya ndi Roma

Aroma atagonjetsa madera olamulidwa ndi mafumu amene analowa m’malo mwa Alesandro, dziko la Roma linakhala msika waukulu wa zinthu zamtengo wapatali zochokera kum’mawa. Zinthuzo ndi monga minyanga kuchokera ku Africa, lubani ndi mule kuchokera ku Arabiya, zinthu zokometsera chakudya ndi miyala yamtengo wapatali kuchokera ku Indiya ndiponso nsalu yasilika kuchokera ku China. Sitima zonyamula malonda zinkafika pa madoko awiri aakulu a ku Iguputo, ku Nyanja Yofiira. Mayina a madokowa ndi Berenice ndi Myos Hormos. Kuchokera ku madoko awiriwa, kunali njira zamalonda zapamtunda zopita ku Coptos, m’dera la Nile.

Kuchokera ku Coptos, katundu ankadutsa mu Nile, womwe ndi mtsinje waukulu ku Iguputo, kupita ku Alesandiriya. Kumeneku katunduyu ankapakiridwa mu sitima zopita ku Italiya ndi madera ena. Njira ina yopitira ku Alesandiriya inali yodzera ngalande imene inalumikiza Nyanja Yofiira ndi mtsinje wa Nile. Ngalande imeneyi inali pafupi ndi malo amene pali ngalande yamakono ya Suez. Dziko la Iguputo ndi madoko ake anali pafupiko ndi madera amene Yesu ankalalikirako ndipo kunali kosavuta kufika ku maderawo.

Katswiri wodziwa za malo wa m’zaka zapakati pa 1 C.E. ndi 100 C.E., dzina lake Strabo, ananena kuti m’nthawi yake sitima zokwana 120 za ku Alesandiriya zinkayenda chaka chilichonse kuchokera ku Myos Hormos kukachita malonda ku Indiya. Buku lina la m’nthawi imeneyo lonena za maulendo apanyanja lidakalipobe mpaka pano. N’kutheka kuti linalembedwa ndi wamalonda wa ku Iguputo amene ankalankhula Chigiriki pofuna kuthandiza amalonda anzake. Kodi buku lakale limeneli lingatiphunzitse chiyani?

Bukuli, lomwe limadziwika ndi dzina la Chilatini lakuti, Periplus Maris Erythraei, (Ulendo Wozungulira Nyanja ya Erythraean) limafotokoza za njira zapanyanja zokwana mtunda wa makilomita zikwizikwi kuchokera kum’mwera kwa Iguputo mpaka kukafika ku Zanzibar. Ponena za kum’mawa, wolemba bukuli anatchula mitunda, malo okocheza, misika, katundu yemwe ankagulitsidwa, komanso makhalidwe a anthu amene ankakhala m’mphepete mwa gombe la kum’mwera kwa Arabiya, ndiponso kumadzulo kwa nyanja ya Indiya kukafika ku Sri Lanka kenako kum’mawa kwa nyanja ya Indiya mpaka kukafika ku Ganges. Kufotokoza zinthu molondola ndiponso momveka bwino kwa bukuli kumapangitsa anthu kuganiza kuti munthu yemwe analilemba anafika m’madera amene anatchulawo.

Azungu ku Indiya

Ku Indiya, azungu ochita amalonda ankatchedwa kuti Ayavana. Malinga ndi buku lija lakuti Periplus, malo amene ankakonda kufikako m’zaka zapakati pa 1 C.E. ndi 100 C.E. anali mzinda wa Muziris, kufupi ndi kumapeto kwenikweni kwa Indiya, kum’mwera. * Ndakatulo za anthu otchedwa a Tamil, za m’zaka za m’ma 1 C.E. mpaka 200 C.E., zimanena za amalonda amenewa mobwerezabwereza. Ndakatulo ina imati: “Sitima zokongola za Ayavana zinkabweretsa golide ndipo pobwerera kwawo zinkatenga tsabola, ndiponso ku Muziris kunkakhala phokoso lokhalokha.” Mu ndakatulo inanso, mwana wa mfumu ya kum’mwera kwa Indiya akulimbikitsidwa kumwa vinyo wonunkhira yemwe Ayavana anabweretsa. Wina mwa katundu wobwera ndi azungu yemwe ankayenda malonda kwambiri ku Indiya anali zinthu zagalasi, zitsulo, ngale ndi nsalu.

Akatswiri ofufuza zinthu zakale apeza umboni wakuti ku Indiya kunali katundu wochokera ku mayiko a azungu. Mwachitsanzo, ku Arikamedu, kugombe la kum’mwera chakum’mawa kwa Indiya, anapeza zinthu monga mapale a mitsuko ya vinyo ndi mbale zochokera ku Roma, zolembedwa mayina a anthu amene anaziumba a ku Arezzo, chigawo chapakati cha Italiya. Munthu wina wolemba mabuku anati: “Munthu wofufuza zakale wamasiku ano akapeza mapale m’nthaka ku ndomo ya Bengal olembedwa mayina a anthu amene ankawapanga, amene mauvuni awo anali kufupi ndi ku Arezzo, amaganizira zinthu zambirimbiri zokhudza zinthu zakale.” Umboni winanso wakuti anthu a m’dera la Mediterranean ankachita malonda ndi anthu a ku Indiya ndi ndalama zasiliva ndi zagolide zambirimbiri za ku Roma, zimene zapezedwa kum’mwera kwa Indiya. Zambiri mwa ndalamazi ndi za m’zaka zapakati pa 1 C.E. ndi 100 C.E., ndipo zili ndi zithunzi za mafumu a Roma monga Augusito, Tiberiyo ndi Nero.

Umboni wina wosonyeza kuti n’zotheka kuti nzika za Roma zinakhazikitsa misika yachikhalire kum’mwera kwa Indiya ndi mapu akale, ndipo mapu okopedwa ku mapu amenewa m’zaka za ma 500 C.E. mpaka 1500 C.E., alipo mpaka pano. Mapu amenewa, omwe amadziwika kuti Peutinger Table, omwe amati amasonyeza madera olamulidwa ndi Roma m’zaka zapakati pa 1 C.E. ndi 100 C.E., amasonyezanso kachisi wa Augusito ku Muziris. Buku lina limati: “Kachisi ameneyu ayenera kuti anamangidwa ndi nzika za ufumu wa Roma, ndipo n’kutheka kuti nzikazo ndi zimene zinkakhala ku Muziris kapena zimene zinkathera nthawi yaitali kumeneku.”​—Rome’s Eastern Trade: International Commerce and Imperial Policy, 31 BC–AD 305.

Kaundula wa Aroma amatchula za akazembe atatu a dziko la Indiya amene anapita ku Roma m’nthawi ya ulamuliro wa Augusito, kuchokera mu 27 B.C.E. mpaka mu 14 C.E. Anthu ena ochita kafukufuku pankhaniyi anati: “Akazembe amenewa anali ndi cholinga chachikulu.” Ndipo cholingacho chinali kukambirana kuti agwirizane za malo kumene anthu a m’mayiko osiyanasiyana angamachitire malonda awo, madera oyenera kupereka msonkho, kumene anthu obwera angamakhale ndi zina zotero.

Choncho, m’zaka za pakati pa 1 C.E. ndi 100 C.E., zinali zosavuta ndipo sizinali zachilendo kuti anthu ayende maulendo kuchokera m’madera ozungulira Mediterranean kukafika ku Indiya. Sizikanavuta kuti mmishonale wachikhristu amene anali kumpoto kwa Nyanja Yofiira akwere sitima yopita ku Indiya.

Kodi Anapitirira Indiya?

Ndi zovuta kunena kuti amalonda a ku Mediterranean komanso anthu ena apaulendo anafika kutali bwanji kulowera kum’mawa. Ndi zovutanso kudziwa kuti anayamba liti. Komabe, akatswiri amakhulupirira kuti pomafika m’zaka zapakati pa 1 C.E. ndi 100 C.E., azungu ena anakafika mpaka ku Thailand, Cambodia, Sumatra ndi Java.

Kaundula wotchedwa Hou Han-Shou (Kaundula wa Ufumu Wotsatira wa Han), amene amafotokoza zochitika zapakati pa 23 C.E. ndi 220 C.E., amanena za nthawi imene ulendo wina unachitika. Mu 166 C.E., kazembe wotumidwa ndi mfumu An-tun ya ku Daqin, anafika ku nyumba ya mfumu ya ku China atanyamula mtulo wa Mfumu Huan-ti. Dzina lakuti Daqin ndi limene anthu a ku China ankatchulira ufumu wa Roma, pamene An-tun likuoneka kuti ndi dzina la Chitchaina lotanthauza Antoninus. Dzinali linali la banja la Marcus Aurelius, yemwe anali mfumu ya Roma panthawiyo. Akatswiri a mbiri yakale amaganiza kuti ulendo umenewu sanatumidwe ndi boma koma kungoti azungu amalonda ankafuna azipeza okha nsalu zasilika ku China, osati kuchita kugula kwa anthu ena.

Tsopano tibwerere ku funso lathu lija. Kodi sitima kalelo zinatenga amishonale achikhristu n’kuwapititsa kum’mawa mpaka kukafika kuti? Kodi zinakawafikitsa ku Indiya kapenanso kupitirira? Mwina. Koma n’zodziwikiratu kuti uthenga wachikhristu unafalikira kutali mwakuti mtumwi Paulo n’kunena kuti uthengawo unali ‘kubala zipatso ndiponso kuwonjezeka m’dziko lonse,’ kutanthauza madera akutali kwambiri odziwika nthawi imeneyo.​—Akolose 1:6.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 Malo enieni amene kunali mzinda wa Muziris sadziwika, komabe akatswiri amati ndi pafupi ndi matsiriro a mtsinje wa Periyar, m’boma la Kerala.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 22]

Dandaulo la Mfumu

Mu 22 C.E., Mfumu Tiberiyo ya Roma inadandaula kuti anthu ake ankawononga kwambiri chuma. Chuma cha dzikoli chinkawonongeka chifukwa cha mtima wongofuna zinthu zapamwamba wa anthu a kumeneku ndiponso mtima wa akazi olemera a ku Roma omwe ankafuna kwambiri majuwelo. Zimenezi zinkachititsa kuti chuma cha ufumuwo chipite “kumayiko achilendo kapena a adani awo.” Wolemba mbiri wa ku Roma, dzina lake Pliny Wamkulu (23-79 C.E.), anadandaulanso za kuwononga chuma kotereku. Iye analemba kuti: “Mayiko monga Indiya ndi Seres ndiponso dera la Arabiya akati awononga zochepa, amawononga ndalama zokwana masesitasi 100 miliyoni za dziko lathu chaka chilichonse. Timawonongera ndalama zankhaninkhani pazinthu zapamwamba komanso akazi athu.” *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 28 Akatswiri owerengera ndalama amati masesitasi 100 miliyoni anali okwana pafupifupi 2 peresenti ya chuma chonse cha ufumu wa Roma.

[Mawu a Chithunzi]

Museo della Civiltà Romana, Roma; Todd Bolen/​Bible Places.com

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 23]

Kumene Amalonda Ankapeza Katundu Wawo

Yesu ananena za “wamalonda woyendayenda amene akufunafuna ngale zabwino.” (Mateyo 13:45) Buku la Chivumbulutso limatchulanso za “amalonda oyendayenda” amene katundu wawo ankaphatikizapo miyala yamtengo wapatali, nsalu zasilika, mitengo yafungo lokoma, minyanga, sinamoni, lubani ndi amomo. (Chivumbulutso 18:11-13) Katundu ameneyu ankapezeka m’misika imene inali m’njira zamalonda zopita kum’mawa kwa Palestina. Matabwa onunkhira, monga a mtengo wa sandalwood, ankachokera ku Indiya. Ngale zamtengo wapatali zinkapezeka ku nyanja ya Perisiya, Nyanja Yofiira ndiponso, malinga ndi wolemba buku lakuti Periplus Maris Erythraei, zinkapezekanso kufupi ndi mzinda wa Muziris ndi ku Sri Lanka. Ngale zochokera kunyanja yamchere ya Indiya ziyenera kuti zinali zabwino kwambiri ndiponso zokwera mtengo.

[Mapu pamasamba 20, 21]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Zina mwa njira zamalonda zimene zinali pakati pa Roma ndi Asiya m’zaka zapakati pa 1 C.E. ndi 100 C.E.

Arezzo

Roma

NYANJA YA MEDITERRANEAN

AFRICA

Alesandiriya

IGUPUTO

Coptos

Mtsinje wa Nile

Myos Hormos

Berenice

Zanzibar

Nyanja Yofiira

Yerusalemu

ARABIYA

Mtsinje wa Firate

BABYLONIA

Nyanja ya Perisiya

PERISIYA

Mphepo ya kumpoto chakum’mawa

Mphepo ya kum’mwera chakumadzulo

Mtsinje wa Indus

PUNJAB

Mtsinje wa Ganges

Ndomo ya Bengal

INDIYA

Arikamedu

Muziris

SRI LANKA

NYANJA YAMCHERE YA INDIYA (NYANJA YA ERYTHRAEAN)

CHINA

UFUMU WA HAN

THAILAND

CAMBODIA

VIETNAM

Sumatra

Java

[Chithunzi patsamba 21]

Sitima yonyamula katundu ya Aroma

[Mawu a Chithunzi]

Ship: Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.