Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Woweruza Amene Amachita Zoyenera Nthawi Zonse

Woweruza Amene Amachita Zoyenera Nthawi Zonse

Yandikirani Mulungu

Woweruza Amene Amachita Zoyenera Nthawi Zonse

Genesis 18:22-32

CHILUNGAMO, kusakondera komanso kupanda tsankho. Kodi inu simukopeka ndi makhalidwe abwino amenewa? Anthufe mwachibadwa timafuna kuchitiridwa chilungamo. Koma n’zomvetsa chisoni kuti chilungamo chikusowa masiku ano. Ngakhale zili choncho, pali woweruza amene tiyenera kumudalira. Iye ndi Yehova Mulungu. Nthawi zonse amachita zoyenera ndipo mfundo imeneyi inasonyezedwa ndi zimene Yehovayo anakambirana ndi Abulahamu, malinga ndi Genesis 18:22-32. *

Yehova atauza Abulahamu zakuti akufuna kukayendera mzinda wa Sodomu komanso Gomora kuti akaone mmene zinthu zilili, Abulahamu anaopa kuti anthu olungama okhala kumeneko, kuphatikizapo m’bale wake Loti, angawonongeke. Abulahamu anafunsa Yehova kuti: “Kodi mudzawononga olungama pamodzi ndi oipa? Kapena alipo olungama makumi asanu mkati mwa mudzi; kodi . . . simudzasiya malowo chifukwa cha olungama makumi asanu ali momwemo?” (Vesi 23 ndi 24) Mulungu ananena kuti sadzawononga mizindayo mutapezeka anthu 50 olungama. Abulahamu anachonderera Yehova maulendo ena asanu, ndipo anatsitsa chiwerengerocho mpaka kufika pa 10. Maulendo onsewa, Mulungu ananena kuti sadzawononga mizindayo mutapezeka anthu olungama onsewo.

Kodi pamenepa Abulahamu anali kukangana ndi Mulungu? Ayi, si choncho. Kuchita zimenezo kukanakhala kupanda ulemu. Mmene Abulahamu ankalankhulira, zinasonyeza ulemu ndi kudzichepetsa. Iye anati: “Ine ndine fumbi ndi phulusa.” (Mavesi 27, 30-32) Ndiponso, mawu a Abulahamu anasonyeza kuti iye ankadziwa kuti Yehova ndi wachilungamo. Kuganiza kuti Mulungu angawononge olungama pamodzi ndi oipa kunali kosatheka kwa Abulahamu. Munthu wokhulupirikayu ananena maganizo ake pofunsa kuti: “Kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?”​—Vesi 25.

Kodi Abulahamu analondola pazinthu zimene ananena? Inde komanso ayi. Iye analakwitsa poganiza kuti ku Sodomu ndi Gomora kungapezeke anthu olungama okwana 10. Koma analondola ponena kuti Mulungu ‘sangaphe olungama pamodzi ndi oipa.’ Mulungu atawononga mizinda yoipayo, anthu olungama amene anapulumuka pothandizidwa ndi angelo anali Loti ndi ana ake awiri aakazi.​—2 Petulo 2:7-9.

Kodi nkhani imeneyi ikutiphunzitsa chiyani za Yehova? Pouza Abulahamu kuti akufuna kuyendera mizindayo, tingatero kuti Yehova anafuna kukambirana ndi Abulahamu. Ndipo pokambiranapo, Yehova anamvetsera moleza mtima pamene bwenzi lake Abulahamu ankafotokoza nkhawa yake. (Yesaya 41:8) Apatu tikuphunzirapo mfundo yofunika kwambiri yakuti Yehova ndi Mulungu wodzichepetsa, yemwe amalemekeza atumiki ake padziko lapansi osati kuwanyoza. Ndiyetu tili ndi zifukwa zomveka zokhulupirira Yehova ndi mtima wonse. Iye ndi Woweruza amene amachita zoyenera nthawi zonse.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 1 Panthawiyi, mngelo ndi amene analankhula ndi Abulahamu poimira Yehova. Mukafuna kuona chitsanzo china, werengani Genesis 16:7-11, 13.

[Chithunzi patsamba 24]

Abulahamu anachonderera Yehova pankhani ya Sodomu ndi Gomora